Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g94 7/8 tsamba 7-8
  • Nyenyezi Zilidi ndi Uthenga Wanu!

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Nyenyezi Zilidi ndi Uthenga Wanu!
  • Galamukani!—1994
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Zimene Tingaphunzire ku Nyenyezi
  • Nyenyezi ndi Munthu—Kodi Pali Kugwirizana?
    Galamukani!—1994
  • Kodi Mumakhulupirira Nyenyezi?
    Galamukani!—2012
  • “Monga Nyenyezi za Kumwamba”
    Galamukani!—1988
  • Chilengedwe Chimalengeza Ulemerero wa Mulungu
    Nsanja ya Olonda—2004
Onani Zambiri
Galamukani!—1994
g94 7/8 tsamba 7-8

Nyenyezi Zilidi ndi Uthenga Wanu!

MONGA momwe kwasonyezedwera m’nkhani zapitazo, mosasamala kanthu za ulemerero umene nyenyezi zimasonyeza, munthu anafunikira kuziona monga momwedi zilili—zinthu zopanda moyo zoikidwa m’miyamba ndi Mlengi kaamba ka chifuno chake. Sizinayenera kulambiridwa. Monga mbali yofunika ya chilengedwe chodabwitsa cha Yehova yogonjera ku malamulo ake, nyenyezi zikafunikira ‘kulalikira ulemerero wa Mulungu’ ndipo panthaŵi imodzimodziyo kutumikira monga magwero a kuunika kaamba ka munthu pamene akachita chifuno cha Mlengi kwa iye.—Salmo 19:1; Deuteronomo 4:19.

M’Baibulo timaŵerenga kuti: “Asapezeke mwa inu munthu . . . wosamalira mitambo, kapena wosamalira kulira kwa mbalame, kapena wanyanga. Kapena wotsirika, kapena wobwebweta, kapena wopenduza, kapena wofunsira akufa. Popeza aliyense wakuchita izi Yehova anyansidwa naye; ndipo chifukwa cha zonyansa izi Yehova Mulungu wanu awapitikitsa pamaso panu.” (Deuteronomo 18:10-12) Yesaya anati: “Aimirire tsopano [aphungu ako] openda zam’mwamba, oyang’ana nyenyezi, . . . ndi kukupulumutsa . . . Taona, iwo adzakhala ngati ziputu.”—Yesaya 47:13, 14.

Zimene Tingaphunzire ku Nyenyezi

Komabe, nyenyezi zopanda moyo zingatiuze kanthu kena ngati tifuna kumvetsera. Edwin Way Teale analemba kuti: “Nyenyezi zimalankhula za kusanunkha kanthu kwa munthu ku umuyaya wautali wa nthaŵi.” Inde, pamene tizindikira kuti unyinji waukulu wa nyenyezi zimene timaona ndi maso athu pa usiku watetete unaonedwa ndi makolo athu zaka mazana zapitazo, kodi sikumatichepetsa? Kodi sitimadzimva kukhala aulemu kwa Uyo Wamkulukulu amene anazilenga “pachiyambi” ndi amene pambuyo pake anapanga mtundu wa anthu? Mfumu Davide ya Israyeli inalemba mwaulemu kuti: “Pakuona ine thambo la kumwamba lanu, ntchito ya zala zanu, mwezi ndi nyenyezi, zimene munazikhazika, munthu ndani kuti mumkumbukira? Ndi mwana wa munthu kuti mucheza naye?” Miyamba iyenera kutichepetsa ndi kutichilitsa kulingalira zimene tikuchita ndi miyoyo yathu.—Genesis 1:1; Salmo 8:3, 4.

Panthaŵi ina Davide anapemphera kuti: “Mundiphunzitse chokonda Inu; popeza Inu ndinu Mulungu wanga.” (Salmo 143:10) Mbiri ya moyo wa Davide imasonyeza kuti pemphero lake linayankhidwa. Anadziŵa kuchita chifuniro cha Mulungu monga momwe chinalembedwera m’Chilamulo Chake. Anadziŵanso chifuno cha Mlengi kwa anthu, ndipo analemba za icho. “Katsala kanthaŵi ndipo woipa adzatha psiti: . . . Koma ofatsa adzalandira dziko lapansi; nadzakondwera nawo mtendere wochuluka. . . . Siyana nacho choipa, nuchite chokoma, nukhale nthaŵi zonse. . . . Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.” Limodzi ndi chidziŵitso chimenecho panadza thayo: “Siyana nacho choipa, nuchite chokoma.”—Salmo 37:10, 11, 27-29.

Nyenyezi zili ndi uthenga umodzimodziwo kwa mtundu wonse wa anthu. Popanda kuzilambira kapena ‘kuzifunsira,’ tingaone chikondi, nzeru, ndi mphamvu za Mlengi zosonyezedwa mwa izo. Phunziro la kupenda zakuthambo, mosiyana ndi kupenda nyenyezi, liyenera kukhomereza ulemu m’mitima yathu. Koma koposa zimenezo, kodi silimakhomereza mwa ifeyo chikhumbo cha kuphunzira zambiri ponena za Mulungu? Iye wapereka Mawu ake, Baibulo, kaamba ka chifuno chimenecho. Ngati mwazindikira uthenga umenewu wochokera ku nyenyezi, mungathe kuphunzira zimene Yehova wasungira mtundu wa anthu ndipo, chofunika koposa, mmene mungakhalire ndi phande m’madalitso amene wawakonzera. Ngati muli ndi mafunso ponena za Mulungu ndi chifuno cha moyo, khalani aufulu kufunsa Mboni za Yehova m’dera lanu, kapena lemberani kukeyala yapafupi kwambiri ndi kwanu yosonyezedwa pa tsamba 5.

[Chithunzi patsamba 8]

Nyenyezi zingatiphunzitse kudzichepetsa

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena