Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g94 8/8 tsamba 14-21
  • Kodi Kutchova Juga ndi kwa Akristu?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Kutchova Juga ndi kwa Akristu?
  • Galamukani!—1994
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Nchifukwa Ninji Anthu Amatchova Juga?
  • Lingaliro la Mulungu
  • Kodi Kutchova Njuga Kuli Ndi Vuto Lanji?
    Galamukani!—2002
  • Oseŵera Juga Atsopano—Achichepere!
    Galamukani!—1995
  • Kodi Baibulo Limaletsa Kutchova Juga?
    Nsanja ya Olonda—2011
  • Kodi Kutchova Juga Kulidi Koipa Kwambiri?
    Galamukani!—1991
Onani Zambiri
Galamukani!—1994
g94 8/8 tsamba 14-21

Lingaliro la Baibulo

Kodi Kutchova Juga ndi kwa Akristu?

KUTCHOVA JUGA KULI CHIZOLOŴEZI CHOWONONGA NDALAMA. KAŴIRIKAŴIRI KUMAWONONGA THEKA LA MALIPIRO A MUNTHU NDIPO KUNGACHITITSE NGONGOLE ZAZIKULU. CHIZOLOŴEZI CHIMENECHI CHINGAWONONGE MAUKWATI NDI NTCHITO NDIPO CHINGACHITITSE NGAKHALE ANTHU ENA KULOŴA MU UPANDU. MIKHOLE YAKE NJOMWEREKERA NDIPO INGAKHALE NDI ZIYAMBUKIRO ZA KULEKA ZONGA ZIJA ZIMENE ZIMAKHALA NDI OMWEREKERA ENA.

KUTCHOVA JUGA kuli kofala kwambiri kwakuti maiko ena amakuona monga “maseŵera a maikowo.” Komabe, kodi kwenikweni kutchova juga nchiyani? Kutchova juga ndiko “kubetchera pa zotulukapo za chochitika choyembekezeredwa,” ikutero The World Book Encyclopedia. “Otchova juga kaŵirikaŵiri amabetchera ndalama kapena kanthu kena kamtengo monga pinyolo pa zotulukapo zimene amalosera. Pamene zotulukapozo zitsimikiziridwa, wopambanayo amatenga pinyolo wa olepherawo.”

Kutchova juga sikuli chochitika chatsopano. Amaya akale a ku Central America ankachita maseŵera ofala a mpira otchedwa poktatok—odziŵika kwa Aaztec monga tlachtli—“m’mene ena, pokhala atataya chuma chawo [mwa kubetchera pa maseŵerawo], anapinyolitsa miyoyo yawo yeniyeniyo,” akutero magazini otchedwa Américas. Anthu akale ameneŵa anagwidwa ndi msala wakubetchera, nthaŵi zina “akumadziika pangozi ya kukhala ndi moyo waukapolo chifukwa cha kutanuka koipa kwa mpira.”

Kodi nchifukwa ninji ambiri agwidwa ndi msala wakutchova juga? Malinga ndi kunena kwa Duane Burke, prezidenti wa Public Gaming Research Institute ku United States, “anthu ambirimbiri akuona kutchova juga monga mtundu wovomerezeka wa machitachita akupuma.” Ngakhale magulu ena achipembedzo amavomereza kutchova juga monga njira yopezera ndalama.

Ngakhale kuti kutchova juga nkofala ndipo kwakhalako kwanthaŵi yaitali m’mbiri, kodi kungangokhala maseŵera abwino kwa Akristu? Kapena kodi kumaphatikizapo zambiri kuposa zimenezo?

Kodi Nchifukwa Ninji Anthu Amatchova Juga?

Mwachidule, kuti apambane. Kwa otchova juga, kutchova juga kumaoneka monga njira yofulumira ndi yosangalatsa yopezera ndalama popanda kuvutikira ndi kudziletsa zophatikizidwa m’kugwira ntchito yolembedwa. Nthaŵi yochuluka imatayidwa pa kuyerekezera za “kupambana kwambiri” ndi kutchuka ndi chuma zimene mphothoyo ingawadzetsere.

Koma mwaŵi wakupambana wa wotchova jugayo n’ngwaung’ono kwambiri. Mwachitsanzo, wofufuza za ziŵerengero Ralf Lisch akunena kuti ku Germany “mukhoza kukanthidwa ndi mphezi mkati mwa chaka kuŵirikiza kanayi koposa [kupambana] pa kubetchera [m’lotale ya ku Germany].” Ngati zimenezo sizimveka kukhala zokhutiritsa, iye akuwonjezera fanizo lotsatirali: “Ngati ndinu mwamuna, kukhoza kwanu kwa kukhala ndi moyo kufikira [usinkhu wa zaka] 100 nkokulirapo kuŵirikiza nthaŵi 7,000 kuposa [kuja kwa kupambana lotale].” Nkodabwitsa kuti wotchova juga angakhale akudziŵa zimenezi. Chotero, kodi nchiyani chimene chimamchititsa kupitirizabe kutchova juga?

Malinga ndi kunena kwa Dr. Robert Custer, m’buku lake lakuti When Luck Runs Out, kwa ena amene amatchova juga, “phindu landalama langokhala mbali ina ya kupambana. . . . Kwa iwo chinthu chofunika ndicho kuchititsa kaso, ulemu, kukhumbidwa, ndi thamo, zimene kupata ndalamazo kungachititse.” Iye akuwonjezera kuti kwa ameneŵa kumakhala “kosangalatsa kukhoza kusonyeza mpukutu wa ndalama kapena kungokhoza kunena kuti, ‘Ndinapata zazikulu zisanu’ ndi kukhala muulemererowo.”

Kumbali ina, kupambana—ndi chisangalalo chimene kumakhala nacho—kumakhalabe kosakwanira kwa otchova juga ambiri. Chisonkhezero cha kutchova juga chingakhale champhamvu kwambiri kwakuti amakhala otchova juga otengeka maganizo. M’kufufuza kochitidwa ndi Dr. Custer pa ziŵalo za Gamblers Anonymous, 75 peresenti ya awo ofufuzidwa anati ankadzitama ponena za kupambana ngakhale pamene anali kulephera! Inde, kutchova juga kungakhale kumwerekera koipa ndi kowononga mofanana ndi kumwerekera ndi zakumwa zoledzeretsa kapena namgoneka wina aliyense. Kodi ndi otchova juga angati amene apyola malire akuseŵera nakhala otengeka maganizo? Kodi ndi angati amene atero ndipo sakudziŵa?

Lingaliro la Mulungu

Baibulo silimafotokoza zambiri pa kutchova juga. Komatu, limatipatsa malamulo a mkhalidwe amene amatithandiza kudziŵa mmene Mulungu amaonera kutchova juga.

Zochitika zasonyeza kuti kutchova juga kumasonyeza chisiriro. Baibulo limatsutsa mwamphamvu chisiriro, likumachenjeza kuti ‘wosirira yense alibe choloŵa mu ufumu wa Mulungu.’ (Aefeso 5:5) Chisiriro chimaoneka ngakhale pamene otchova juga alephera. Malinga ndi kunena kwa katswiri wina, wotchova juga “amayesa kupambananso zimene wataya—akumafunafuna ‘kupambana kwambiri.’ Ngati apambana kwambiri, amabetchera mokulirapo, ndipo m’kupita kwa nthaŵi amataya ‘kupambana [kwake] kwambiri.’” Inde, chisiriro chilidi mbali ya kutchova juga.

Ena amagwiritsira ntchito kutchova juga monga njira yokhutiritsira kunyada kwawo. Kufufuza kwina kochitidwa pa otchova juga otengeka maganizo kunasonyeza kuti 94 peresenti anaona kutchova juga kukhala “ntchito yokulitsa kudzitama,” ndipo 92 peresenti anati anadzimva monga “apamwamba” pamene anatchova juga. Komabe, Mulungu amati: “Kunyada, ndi kudzikuza, . . . ndizida.” Chotero, Akristu amafulumizidwa kukulitsa kudekha ndi kudzichepetsa.—Miyambo 8:13; 22:4; Mika 6:8.

Kutchova juga kungasonkhezerenso ulesi, popeza kuti kumaoneka monga njira yosavuta yopangira ndalama popanda kuyesayesa kophatikizidwa m’kugwira ntchito. Koma Mawu a Mulungu momvekera bwino amalimbikitsa Akristu kugwira ntchito mwakhama ndi mwamphamvu.—Aefeso 4:28.

Ndiponso, zimene amati ndi mwaŵi zimakhala zofunika kwambiri kwa otchova juga ena kwakuti iwo amakhala otengeka nazo maganizo, kuzipanga kukhala mulungu wawo. Zimenezi nzofanana ndi nkhani ya Baibulo yonena za amuna amene anali “kukonzera mulungu wamwaŵi gome.” Chifukwa cha kachitidwe kawo kopembedza mafano, iwo anasankhidwiratu “kulupanga.”—Yesaya 65:11, 12.

Kodi bwanji ngati munthu wapatsidwa tikiti yaulere ya lotale kapena ndalama zaulere zotchovera juga? M’zochitika zonse ziŵirizo, kulandira mphatso yotero kungakhalebe kuchirikiza mchitidwe wa kutchova juga—mchitidwe wosemphana ndi malamulo a mkhalidwe aumulungu.

Ayi, kutchova juga sikuli kwa Akristu. Monga momwe mkonzi wina wa magazini ananenera, ‘kutchova juga sikuli chabe kolakwa komanso kuli kopanda nzeru.’

[Mawu a Chithunzi patsamba 14]

Valentin/The Cheaters, Giraudon/Art Resource

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena