Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g94 9/8 tsamba 20-22
  • Maphunziro Owonjezereka Kapena Ayi?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Maphunziro Owonjezereka Kapena Ayi?
  • Galamukani!—1994
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Lingaliro Lachikatikati
  • Kubwereranso Kusukulu Chifukwa?
    Galamukani!—1994
  • Maphunziro Okhala ndi Cholinga
    Nsanja ya Olonda—1992
  • Kodi Baibulo Limaletsa Maphunziro Akusukulu?
    Galamukani!—1998
  • Makolo—kodi Ana Anu Mukuwafunira Tsogolo Lotani?
    Nsanja ya Olonda—2005
Onani Zambiri
Galamukani!—1994
g94 9/8 tsamba 20-22

Maphunziro Owonjezereka Kapena Ayi?

KODI ndi maphunziro ambiri chotani amene ali ofunika kukhalira moyo? Mayankho ake amasiyanasiyana m’maiko. Kukuonekera kuti m’maiko ambiri maphunziro ofunika kuti munthu adzichirikize ali apamwamba kuposa mmene analiri zaka zingapo zapitazo. M’zochitika zina maphunziro achikatikati ofunidwa ndi lamulo sali okwanira.

Mosakayikira chimenechi ndicho chifukwa chake chiŵerengero chomawonjezereka cha omaliza maphunziro chikubwereranso kusukulu mmalo mwa kupita kuntchito. Ndithudi, mfupo zake zimaonekera kukhala zokopa. The New York Times inatchula za lipoti la Economic Policy Institute imene inapeza kuti “amuna ogwira ntchito okhala ndi madipuloma a sukulu ya sekondale okha anatsitsiridwa malipiro awo ndi 7.4 peresenti kuyambira 1979 kufikira 1987, pamene kuli kwakuti malipiro a amuna omaliza maphunziro ku koleji anakwera ndi 7 peresenti.”

Omaliza maphunziro ku koleji amalandira madigiri amene angawatsegulire mwaŵi wa ntchito. William B. Johnston, wofufuza wamkulu pa Hudson Institute, akunena kuti: “Digiri ya ku koleji, kapena ngakhale umboni wa kukhala utaloŵapo koleji, zakhala mtundu wina wofunika kwambiri wa ziyeneretso za ntchito za dziko lino.”

Komanso, kuyenera kudziŵidwa kuti omaliza maphunziro ambiri amamenyera nkhondo kupeza ntchito, ndipo samapatulidwa pa kuchotsedwa ntchito. “Unyinji wa anzanga amene ndinamaliza nawo maphunziro sugwira ntchito,” akutero Karl wa zaka 22. Jim, wa zaka 55, anamaliza maphunziro ndi kupatsidwa nyota pa yunivesite ina yotchuka kwambiri komabe anachotsedwa ntchito m’February 1992. Dipuloma yake sinampulumutse, kapenanso kumthandiza kupeza ntchito yodalirika. “Maziko ako amasintha ndi kukhala amchenga,” iye akutero.

Mofanana ndi Jim, omaliza maphunziro ku koleji ambiri aloŵa mu mkhalidwe umene U.S.News & World Report imatcha kuti “purigatoriyo wa antchito za m’maofesi”—achichepere kwambiri osafunikira kupuma pantchito, achikulire kwambiri osakhoza kulembedwa ntchito ndi kampani ina.

Chifukwa chake, pamene kuli kwakuti koleji ingakhale ndi mapindu, nkwachionekere kuti sili chothetsera vutolo. Ndiponso sili njira imodzi yokha imene ilipo. Herbert Kohl akulemba mu The Question Is College kuti: “Pali anthu opambana ambiri amene sanapite ku koleji ndi ntchito zambiri zabwino zimene sizimafuna madigiri a ku koleji.” Mwachitsanzo, kampani ina imalemba ntchito anthu osapita ku koleji ndi kuwapatsa malo antchito amene kaŵirikaŵiri amapatsidwa kwa omaliza maphunziro a ku koleji. Mmalo mwa kufunafuna amadigiri, kampaniyo imafunafuna ofunsira ntchito amene amasonyeza luso la kuchita bwino ntchitoyo. “Pamene tipeza munthu wotero,” akutero mneneri wake, “timakhulupirira kuti tingathe kuphunzitsa [munthuyo] maluso apadera antchito.”

Inde, ambiri adzichirikiza bwino lomwe ndi mabanja awo popanda thandizo la digiri ya ku koleji. Ena a ameneŵa achita makosi kusukulu zophunzitsa ntchito, sukulu zophunzitsa maluso a manja, kapena ku makoleji odziimira okha, pa nthaŵi ndi ndalama zochepa.a Ena aphunzira umisiri kapena utumiki wina popanda mtundu wina uliwonse wa maphunziro apadera. Pokhala odziŵika chifukwa cha kudalirika, iwo akhoza kusunga bwino ntchitoyo.

Lingaliro Lachikatikati

Zoonadi, palibe mtundu wa maphunziro—kuphatikizapo a ku koleji kapena maphunziro ena owonjezera—umene umapereka chitsimikizo cha chipambano. Ndiponso, Baibulo limanena molondola kuti “mkhalidwe wa dzikoli ukusintha.” (1 Akorinto 7:31, NW) Zimene zikufunidwa lerolino zingakhale zachabechabe maŵa.

Motero, munthu amene akulingalira zowonjezera maphunziro angachite bwino kupenda mosamalitsa ubwino ndi kuipa kwake. ‘Kodi ndingathe kulipirira mtengo wake? Kodi ndi mtundu wanji wa malo ndi mabwenzi amene ndidzakhala nawo? Kodi makosiwo adzandipatsa maphunziro othandiza amene adzandikhozetsa kudzichirikiza? Kodi adzandithandiza kusamalira banja ngati pambuyo pake ndiloŵa muukwati?’ Makolo othandiza angakhoze kupereka uphungu wofunika mogwirizana ndi thayo limene Baibulo limawapatsa. (Deuteronomo 4:10; 6:4-9; 11:18-21; Miyambo 4:1, 2) Ngati mukulingalira za mapindu a ndalama a maphunziro owonjezera kapena mbali yake ina iliyonse, mawu a Yesu ali oyenerera akuti: “Ndani wa inu amene akafuna kumanga nsanja yaitali, sathanga wakhala pansi, naŵerengera mtengo wake, aone ngati ali nazo zakuimaliza?”—Luka 14:28.

Ndithudi, kulondola maphunziro owonjezera kapena ayi kuli chosankha chimene chiyenera kulingaliridwa mosamalitsa. Nthaŵi zonse Mkristu amakumbukira mawu a Yesu pa Mateyu 6:33 akuti: “Muthange mwafuna Ufumu wake ndi chilungamo [cha Atate wanu wakumwamba], ndipo zonse zimenezo zidzawonjezedwa kwa inu.” Pakati pa Akristu oona, awo amene alibe maphunziro owonjezereka samanyalanyazidwa kapena kuchitiridwa monga onyozeka, chimodzimodzinso awo amene ali ndi maphunziro owonjezereka samapatulidwa kapena kulingaliridwa kukhala apamwamba. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Ndani iwe wakuweruza mnyamata wa mwini wake? Iye aimirira kapena kugwa kwa mbuye wake wa mwini yekha. Ndipo adzaimiritsidwa; pakuti Ambuye ali wamphamvu kumuimiritsa.”—Aroma 14:4.

Yesu anasonyeza lingaliro limeneli lachikatikati. Iye sananyoze awo amene anali “osaphunzira ndi opulukira,” kapenanso kuleka kusankha Paulo wophunzira kwambiriyo kuchita ntchito yaulaliki yamphamvu. (Machitidwe 4:13; 9:10-16) Mu mkhalidwe uliwonse maphunziro ayenera kusungidwa pamalo ake, monga momwe nkhani yotsatira idzasonyezera.

[Mawu a M’munsi]

a Maprogramu a maphunziro owonjezera amasiyanasiyana m’malo ambiri. Sukulu, malaibulale, ndi mautumiki othandizira kulembedwa ntchito a boma ali malo ofunika ofufuzira zimene zilipo m’deralo.

[Bokosi patsamba 22]

Maphunziro Owonjezera Nsanja Ya Olonda Ya November 1, 1992, Inanena Za Mboni Za Yehova Ndi Utumiki Wanthaŵi Yonse Kuti: “Chikhoterero Chochuluka M’maiko Ambiri Nchakuti Mlingo Wa Kuphunzira Wofunikira Kuti Munthu Azilandira Malipiro Oyenera Tsopano Ngwokwera Kuposa Mmene Unaliri Zaka Zingapo Zapitazo. . . . Nkovuta Kupeza Ntchito Za Malipiro Oyenerera Pambuyo Pakumaliza Maphunziro Oyambirira Ofunidwa Ndi Lamulo . . .

“Kodi Mawuwa ‘Malipiro Oyenerera’ Akutanthauzanji? . . . Malipiro Awo Anganenedwe Kukhala ‘Okwanira,’ Kapena ‘Okhutiritsa,’ Ngati Zimene Amalandirazo Zimawalola Kukhala Ndi Moyo Woyenerera Ndi Kuwapatsa Nthaŵi Yokwanira Ndi Mphamvu Kuchita Uminisitala Wawo Wachikristu.”

Chotero Nsanja Ya Olonda Imeneyo Inati: “Sipayenera Kukhala Malamulo Ankhokera Osonkhezera Kapena Kutsutsa Maphunziro Apamwamba.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena