Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g94 9/8 tsamba 25-27
  • Kodi Nchifukwa Ninji Atate Anamwalira?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Nchifukwa Ninji Atate Anamwalira?
  • Galamukani!—1994
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • ‘Ndine Wokwiya Kwambiri’
  • ‘Tsopano Ndikudzimva Waliwongo Kwambiri’
  • Kupweteka kwa Chisoni
  • Kupeza Chitonthozo
  • Kodi Ndingaiŵale Motani Imfa ya Atate?
    Galamukani!—1994
  • Kodi Ndingatani Ngati Mayi Kapena Bambo Anga Amwalira?
    Galamukani!—2009
  • N’chiyani Chingandithandize Kupirira Ngati Mayi Kapena Bambo Anga Anamwalira?
    Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Loyamba
  • Kodi Ndingakhale Motani ndi Chisoni Changa?
    Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira
Onani Zambiri
Galamukani!—1994
g94 9/8 tsamba 25-27

Achichepere Akufunsa Kuti . . .

Kodi Nchifukwa Ninji Atate Anamwalira?

ALIYENSE anadabwa pamene atate ake Al, mwamuna wodziŵika kukhala wanyonga ndi wathanzi, anapita kuchipatala. Ngakhale kuti zinali choncho, Al anakhulupirira kuti atate ake akabwerera kunyumba posapita nthaŵi. Koma mwadzidzidzi matenda awo anakula, ndipo anamwalira. “Sindinakhulupirire kuti munthu wanyonga kwambiri angamwalire,” Al anadandaula motero.

Atate ake Kim anali mwamuna Wachikristu wachikondi. Panthaŵi ina anagonekedwapo m’chipatala chifukwa cha nthenda yosachiritsika, koma anaoneka ngati akuchira. Ndiyeno tsiku lina anagwa m’chipinda chosambira. “Pamene ndinawaona ndinadziŵa kuti anali akufa,” Kim akumbukira motero. “Amayi ndi achimwene anga mosaphula kanthu anayesayesa kuwatsitsimutsa ndi mchitidwe wosakhala wongoyeserera wa CPR. Ndinathamangira m’chipinda changa ndi kupemphera kuti: ‘Yehova, musalole zimenezi kuchitika. Chonde asiyeni akhale ndi moyo!’ Koma iwo sanatsitsimuke konse.”

M’dziko lino imfa ili mkhalidwe wopweteka. Baibulo limati: “Kanthu kalikonse kali ndi nthaŵi yake . . . mphindi yakubadwa ndi mphindi yakumwalira.” (Mlaliki 3:1, 2) Ngati munaleredwa monga Mkristu, mumadziŵa ziphunzitso za Baibulo ponena za chifukwa chake anthu amafa, mkhalidwe wa akufa, ndi chiyembekezo cha chiukiriro.a

Komabe, mungakhale mutataya mtima chifukwa cha kutayikidwa kholo lanu. Chimenecho chili chimodzi cha zokumana nazo zovuta koposa m’moyo. Chingakuchititseni kuona ngati kuti mwasiyidwa ndi kuti muli pangozi. Mukali kukula, ponse paŵiri mwakuthupi ndi mwamalingaliro, ndipo pamene kuli kwakuti mungakhale mutapeza ufulu wakutiwakuti wodzichitira zinthu, mudzafunabe makolo anu m’njira zambiri.b

Pamenepa, mposadabwitsa kuti kufufuza kwina kunavumbula kuti nkhaŵa yaikulu koposa ya wazaka zapakati pa 13 ndi 19 ili ya kutayikidwa makolo ake. Wachichepere wina anavomereza kuti: “Makolo anga amandikwiyitsadi nthaŵi zambiri, komatu sindingakondwe ngati choipa chilichonse chingawachitikire. Zimenezo zimandidetsa nkhaŵa.”—The Private Life of the American Teenager.

Nchifukwa chake kuli kosadabwitsa kuti ngati mmodzi wa makolo anu wamwalira, mungathedwe mphamvu ndi chisoni. Inde, mwina poyamba, mungafooke kwambiri moti simungathe kulira nkomwe. Zimenezi sizachilendo. Atapsinjika kwambiri, wamasalmo anati: “Ndafoka ine, ndipo ndachinjizidwa.” (Salmo 38:8) Buku la Death and Grief in the Family limati: “Munthu amene watemeka kwambiri kapena kuthyoka fupa amachita dzanzi. Dzanzi limeneli lili ngati chiŵiya chotetezera chimene chimaletsa kumva kupweteka kwakukulu [panthaŵi yomweyo]. Chisoni chimachita mwanjira imodzimodziyo.” Komabe, kodi nchiyani chimene chingachitike pamene dzanzilo lizimiririka?

‘Ndine Wokwiya Kwambiri’

Pa Luka 8:52, timaŵerenga kuti pambuyo pa imfa ya buthu lina, “anthu onse analikumlira iye ndi kudziguguda pachifuwa.” Inde, pamene imfa itenga wokondedwa, kuli kwachibadwa kuvutika mtima kwambiri, kuphatikizapo kuchita chisoni, kumva liwongo, kuchita mantha—ngakhale kukwiya.

Kukwiyiranji? Chifukwa chakuti makolo athu amatichititsa kukhala otetezereka, osungika. Pamene mmodzi wa iwo afa, nkwachibadwa kuchita mantha ndi kuona ngati kuti tasiyidwa. Sikuti kholo lanu linakusiyani dala. Koma chifukwa chakuti imfa ili mdani wathu. (1 Akorinto 15:26) Pamene imfa itenga wokondedwa, kutayikidwako kumakhala kwenikweni ndipo kupweteka kwake kumakhala kosapeŵeka. Tamverani mmene Wendy wazaka 18 ananenera: “Ndinamva ngati kuti ndinali ndekha m’dziko ndipo ndinachita mantha pambuyo pa imfa ya atate. Nthaŵi zambiri ndinalakalaka kuti bwenzi atate anali nane kuti andithandize.” Polingalira za zimene mwatayikidwa—chikondi, chichirikizo, malangizo—nzomvekera kuti mungakhale wokwiya.

Mwachitsanzo, Debbie wachichepere anali kukondana kwambiri ndi amalume ake. Iwo atamwalira iye analemba kuti: “Sikunaoneke kukhala koyenera kuti munthu wabwino motero, wokondedwa kwambiri, ndi yemwe anakonda Yehova kwambiri avutike ndi kufa imfa yoŵaŵa yotero. Ngakhale kuti ndinaleredwa monga Mkristu ndipo ndidziŵa chifukwa chake anthu amakalamba ndi kufa ndi chifukwa chake anthu abwino amavutika, sindinayembekezere kukhala ndi mkwiyo umene ndinakhala nawo.”

Ena amakwiyiradi ngakhale kholo lakufalo. Victoria wachichepere akuvomereza kuti: “Agogo wanga aamuna anamwalira chaka chatha. Ndinawakwiyira kwambiri kuti angafe bwanji, ndiyeno pamene mkwiyowo unatha, ndinachita chisoni kwambiri.” Ndithudi, ena ayesedwa kukwiyira wam’mwambamwambayo. “Ndakwiyira Mulungu,” Terri wazaka 14, amene atate wake anafa ndi nthenda ya mtima yadzidzidzi, anavomereza motero. “Ndi iko komwe, kodi nchifukwa ninji Atate anamwalira pamene kuli kwakuti ndinali kuwakonda ndi kuwafuna kwambiri?”

‘Tsopano Ndikudzimva Waliwongo Kwambiri’

Kumva liwongo kuli chiyambukiro china chofala pa imfa ya kholo. “Onse anachimwa, napereŵera pa ulemerero wa Mulungu,” Baibulo limatero. (Aroma 3:23) Monga chotulukapo chake, azaka zapakati pa 13 ndi 19 ochuluka amakangana ndi makolo awo nthaŵi ndi nthaŵi. Koma pamene kholo lifa, kukumbukira kulimbana ndi mikangano yakale imeneyo kungakhale magwero a kuvutika kwambiri.

Mwina kungathandize kukumbukira kuti ngakhale anthu amene amakondana amasemphana kwambiri nthaŵi zina. “Ndinkakonda amayi,” Elisa wachichepere akuvomereza motero, “ndipo ndidziŵa kuti iwonso ankandikonda, koma miyezi ingapo iwo asanadwale, tinali kuvutana. Ndinkawakwiyira—pa zinthu zimene tsopano zimaoneka kukhala zopanda pake—koma zimene zinali zofunika kwa ineyo panthaŵiyo. Tsiku lina, pamene ndinawakwiyira kwambiri, ndikumbukira kuti ndinakwera mwaukali kumka m’chipinda changa ndikumalakalaka mumtima kuti akanangofa. Pamene Amayi anadwala ndi kufa mwadzidzidzi, ndinalingalira za mikangano yonseyi yosathetsedwa imene inali pakati pathu. Tsopano ndikudzimva waliwongo kwambiri.” Mosasamala kanthu za zimene mungakhale munanena kapena kulingalira, simunachititse imfa ya kholo lanu. Sichinali chifukwa chanu.

Kupweteka kwa Chisoni

Ngakhale zili choncho, mungakhale mukumva chisoni chachikulu. Pezani chitonthozo podziŵa kuti amuna ndi akazi achikhulupiriro m’nthaŵi za Baibulo anakhalanso ndi malingaliro otero. Pamene Yosefe anataya atate ake okondedwa mu imfa, “anagwa pa nkhope ya atate wake, namlirira iye nampsompsona iye.” (Genesis 50:1) Ndiponso, Yesu Kristu “analira” chifukwa cha imfa ya Lazaro bwenzi lake.—Yohane 11:35.

Ndithudi, pamene wina akulira maliro a kholo, kuli kwachibadwa kuthedwa mphamvu ndi chisoni nthaŵi zina. Poyesa kufotokoza kuvutika kwake, wamasalmo anadziyerekezera ndi ‘munthu wakulira maliro amayi wake, woŵeramira pansi polira.’ (Salmo 35:14) Pothedwa mphamvu ndi chisoni, ‘simungagone tulo chifukwa cha chisoni.’ (Salmo 119:28, NW) Mungasiye kudya kapena mwadzidzidzi mungayambe kupeza vuto la kusumika maganizo pamene muli kusukulu. Mwina mungachitedi tondovi.

Zinthu zingaipirepo ngati kholo lanu lotsalalo ndi abale anu angakhale othedwa mphamvu kwambiri ndi chisoni chawo kwakuti sakhoza kukuthandizani ndi kukuchirikizani. Kim akukumbukira motere: “Titaika maliro a atate, tinayesa kukhalabe ndi moyo monga mwamasiku onse. Tsopano amayi anakhala mutu wa banja. Koma panali nthaŵi zina pamene iwo ankayamba kulira phunziro lathu la Baibulo labanja lili mkati. Ndinkawamva akulira usiku, akumaitana dzina la atate.”

Kupeza Chitonthozo

Panthaŵi ina mneneri Yeremiya anati: “[Chisoni chimene chili chosachiritsika chadza mwa ine, NW]. Mtima wanga walefuka mkati mwa ine.” (Yeremiya 8:18) Nanunso mungamve ngati kuti kupwetekako sikudzatha konse. Koma tamverani mawu a mtumwi Paulo: “Wolemekezeka . . . Mulungu wa chitonthozo chonse, wotitonthoza ife m’nsautso yathu yonse.” (2 Akorinto 1:3, 4) Mulungu amapereka chitonthozo chimenechi makamaka m’masamba a Mawu ake olembedwa, Baibulo. Ndiponso, mzimu wake ungasonkhezere mabwenzi ndi ziŵalo za banja kupereka thandizo ndi chichirikizo zofunika.

Musalole mkwiyo wolakwika kukulepheretsani kupeza chitonthozo cha Mulungu chimenechi. Yobu wolungama anaphonya mwa kuimba Mulungu mlandu chifukwa cha zoŵaŵa zimene zinamgwera. Mopwetekedwa mtima iye ananena kuti: “Ndinali kukhala pamtendere, koma Mulungu anandigwira pakhosi nandikantha ine nanditswanya ine.” (Yobu 16:12, 13, Today’s English Version) Koma Yobu analakwa. Satana, osati Mulungu, ndiye anali wochititsa mavuto a Yobu. Elihu wachichepere anakumbutsa Yobu kuti “Mulungu sangachite choipa, ndi Wamphamvuyonse sangaipse mlandu.” Pambuyo pake Yobu analapa pa mawu ake ansontho.—Yobu 34:12; 42:6.

Mofananamo, mungafunikire wina kukuthandizani kuona zinthu ndi lingaliro lachikatikati. Kim akukumbukira motere: “Mkulu Wachikristu wachikulirepo anatikumbutsa za chiyembekezo cha chiukiriro, akumatisonyeza malemba onga Yohane 5:28, 29 ndi 1 Akorinto 15:20. Iye anati: ‘Atate wako adzabwera, koma uyenera kukhalabe wokhulupirika ngati uti udzawaone m’Paradaiso.’ Sindidzaiŵala zimenezo! Iye ananenanso kuti imfa sinali chifuno cha Mulungu kwa munthu. Ndinazindikira kuti si Mulungu amene anachititsa imfa ya atate wanga.”

Kulingalira zinthu mwa Malemba sikunathetse kupweteka mtima kwa Kim panthaŵiyo, koma kunali kuyamba. Nanunso mungayambe kulimbana ndi kupweteka mtima ndi chisoni. Njira yeniyeni imene mungachitiremo zimenezi ndiwo mutu wa nkhani yotsatira mu mpambowu.

[Mawu a M’munsi]

a Kuti mupeze mawu owonjezereka, onani buku la Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

b Nkhani imeneyi ikuphatikizapo achichepere amene atayikidwa achibale awo ena, monga agogo, azakhali, amalume, amene anali kukondana nawo kwambiri.

[Chithunzi patsamba 26]

Imfa ya kholo ingakhale chimodzi cha zokumana nazo zovuta koposa m’moyo

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena