Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g94 11/8 tsamba 15-17
  • Nanga Bwanji za Maulendo a Kalasi?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Nanga Bwanji za Maulendo a Kalasi?
  • Galamukani!—1994
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kuŵerengera Mtengo
  • Kukondweretsa Mulungu Mokwanira
  • Maulendo a ku Yerusalemu
    Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
  • Yosefe ndi Banja Lake Anapita ku Yerusalemu
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Achichepere Achikristu Khalani Olimba M’chikhulupiriro
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Ana a Sukulu a Mboni Ayamikiridwa
    Nsanja ya Olonda—1988
Onani Zambiri
Galamukani!—1994
g94 11/8 tsamba 15-17

Achichepere Akufunsa Kuti . . .

Nanga Bwanji za Maulendo a Kalasi?

“UMAPUMULAKO ku za kusukulu.” “Umasinthako ndi kukaonako zatsopano.” “Umadziŵa bwinopo anzako a m’kalasi.”

Anatero achichepere atatu Achijeremani pofotokoza chifukwa chimene amakondera maulendo a kalasi. Maulendo oterowo amakondedwa kwambiri ndi achichepere kuzungulira dziko lonse.

Komabe, si ophunzira okha omwe amaona maulendo a kalasi kukhala ofunika kwambiri. “Ulendo wa kalasi wolinganizidwa bwino umakhala waphindu kwenikweni kwa wachichepere, popeza umakulitsa kalingaliridwe kake ndi kumthandiza kukhala wodzidalira,” akutero mphunzitsi wina. “Ndiponso, unansi wa mphunzitsi ndi kalasi umalimbitsidwa.” Nzosakayikitsa kuti aphunzitsi ozindikira bwino limodzi ndi kalasi lodzisunga akhoza kugwirizana ndi kupangitsa ulendo wa kalasi kukhala wophunzitsa ndi wosangalatsa.

Chikhalirechobe, pangakhale zinthu zingapo zoloŵetsedwamo zimene moyenerera zimadetsa nkhaŵa achichepere Achikristu ndi makolo awo. Mwachitsanzo, mu Germany ndi maiko ena a ku Ulaya, ophunzira achinyamata ndi achitsikana kaŵirikaŵiri amayendera pamodzi pa maulendo a kalasi akutali. Zimenezi kaŵirikaŵiri zimaphatikizapo kugonera komweko. Zimenezi nthaŵi zambiri zimabutsa mavuto. Anna-Laura wa zaka 14 akukumbukira kuti: “Pambuyo pa masiku angapo tili paulendo, zinthu zinafika poipa. Ngakhale usiku sitinapeze mtendere ndi bata. Ochuluka a kalasi anachita mwadyera ndi mosalingalira ena.”

Pamenepo, kodi muyenera kuchitanji ngati mwapatsidwa mwaŵi wakupita pa ulendo wa kalasi?

Kuŵerengera Mtengo

Pa Luka 14:28, Yesu Kristu anati: “Ndani wa inu amene akafuna kumanga nsanja yaitali, sathanga wakhala pansi, naŵerengera mtengo wake, aone ngati ali nazo zakuimaliza?” Inuyo ndi makolo anu musanasankhe kaya ngati ulendo wa kalasiwo uli woyenera kwa inu kapena iyayi, pendani mosamalitsa zonse zoloŵetsedwamo. Nawa mafunso ena owalingalira:

Kodi ulendowo udzakufikitsani kuti? Kaya uli wa tsiku limodzi lokaona myuziyamu yapafupi kapena ulendo wotalikirapo wogonera konko pangakhale kusiyana kwakukulu. Ndiponso, ngati makolo anu ndiwo adzalipirira ulendowo, adzafuna kunena ngati angakwanitse.

Kodi paprogramu pali chiyani? Ngati tsiku lililonse lili lolinganizidwa bwino ndi zochita zabwino zosangalatsa, zimenezi zidzachititsa kalasilo kukhala lotanganitsidwa ndi kuchepetsa mpata wa chinthu choipa kuchitika. Chotero pendani programu mosamalitsa musanasankhe za ulendo wa kalasiwo. Kukaona mamyuziyamu kapena kupita paulendo wamaphunziro wokaona zinthu zachilengedwe kungakhale kophunzitsa. Koma kukaphunzira za machitachita a Yoga ndi zipembedzo za ku Asia—konga kumene kunalinganizidwapo monga ulendo wa kalasi wina—kuli kosayenera mpang’ono pomwe kwa Mkristu.—1 Akorinto 10:21.

Kodi padzakhala uyang’aniro wotetezera ndi wanthaŵi zonse? Mtsikana wina Wachikristu wa zaka 15 wotchedwa Julia akukumbukira kuti: “Ndinali m’kalasi lodzisunga kwambiri, motero Amayi ndi Atate sanandiletse kupita paulendowo. Aphunzitsi anatiyang’anira mosamala kwambiri.” Komabe, chiyang’aniro chotero sichimapezeka kaŵirikaŵiri masiku ano. Zili monga momwe mphunzitsi wina Wachijeremani anavomerezera kuti, uyang’aniro wosamala ndi wodalirika “suli wotsimikizirika kukhalapo.” Indedi, wachichepere wina anadzitama pambuyo pa ulendo wa kalasi kuti: “Pamene tinanyenga aphunzitsi onse aŵiriwo, tinachita monga momwe tinafunira.”

Ophunzira ena amapulupudzabe ngakhale pamene aphunzitsi ayesa zolimba kuwayang’anira bwino. Yemwe kale anali mphunzitsi akukumbukira kuti: “Achicheperewo anapeza njira zoloŵetsera moŵa mobisa, motero kufufuza zipinda zawo kunali kosaphula kanthu. Ndinazindikira kuti ankamwa moŵa kwambiri pamene mmodzi wa atsikana anayamba kusanza.” Mwachionekere, kungakhale kovuta kwambiri kutsimikizira kuti ulendowo udzayang’aniridwa bwino. Komabe, kungakupulumutseni ku nkhaŵa zambiri ndi zonyazitsa ngati inu ndi makolo anu mupenda mosamala kuti muone kuti ndi makonzedwe otani a uyang’aniro omwe apangidwa. Miyambo 22:3 imati: “Wochenjera aona zoipa, nabisala; koma achibwana angopitirira, nalipitsidwa.”

Kodi ambiri a anzanu apasukulu amalabadira motani malangizo a mphunzitsi wanu? Zimenezi zidzakupatsani lingaliro labwino la mmene adzadzisungira pa ulendo wa sukulu. Zasimbidwa kuti sukulu ina ya sekondale ku Germany inakakamizika kulekeza panjira ulendo wa kalasi wa masiku atatu chifukwa chakuti ophunzira opulupudza ananyalanyaza “malangizo abwino ndi oleza mtima” a aphunzitsi.

Mtsikana wina Wachijeremani wotchedwa Stephanie anapita pa maulendo oterowo kale ndipo chifukwa cha zokumana nazo zake amanena kuti ndibwino kudzifunsa mafunso otsatirawa: ‘Kodi anzanga a m’kalasi ali ndi nzeru za kumvetsera kwa aphunzitsi? Kodi sukulu likuyesayesa kusunga mbiri ya khalidwe labwino? Kodi aphunzitsi ali olimba pakupereka chitsogozo choyenera? Kodi achichepere akuona khalidwe labwino kukhala lofunika? Kodi amamwa moŵa ndi anamgoneka?’ Zoona, Stephanie akuvomereza kuti kwenikweni “zimadalira pa munthuwe, kuti ugonje mosavuta kapena kukana.” Koma kodi mungapemphere motani kuti Yehova ‘asakutengereni kokakuyesani’ ndiyeno nkudziika dala pamkhalidwe wopereka chiyeso?—Mateyu 6:13.

Motero, Petra wa zaka 17 anakana kupita paulendo wa kalasi. Iye akufotokoza kuti: “Ndinadziŵa mmene anzanga a m’kalasi akachitira. Ndinaoneratu kuti mikhalidwe yoloŵetsamo moŵa ndi chisembwere ikaikadi chikumbumtima changa pachiyeso. Monga momwe zinakhaliradi, anyamata asanu anavula mtsikana wina ndi kumjambula zithunzithunzi, zimene pambuyo pake zinkasonyezedwa kwa ena pasukulupo.”

Kodi zikhulupiriro zanu zachipembedzo zidzalemekezedwa? Mwachitsanzo, Timon wachichepere, ananena kuti: “Kaŵirikaŵiri pamakhala phwando la tsiku lakubadwa, limene limakhala lovuta kupeŵa.” Monga mmodzi wa Mboni za Yehova, iye amakana kutengamo mbali m’mapwando oterowo.a Kodi aphunzitsi ndi anzanu a m’kalasi akalemekeza lingaliro lanu ngati ulendo wa kalasi ungaphatikizepo phwando loterolo?

Kodi mudzakhala ndi mayanjano otani? Akristu amadziŵa kuti Mulungu amatsutsa kusuta fodya, kumwa anamgoneka, kumwa moŵa kosayenera, kapena kugonana ukwati usanakhale. (1 Akorinto 6:9, 10; 2 Akorinto 7:1) Nchifukwa chake kuli kwanzeru kupeŵa kuyanjana ndi achichepere amene amachita zinthu zoterozo. (1 Akorinto 15:33) Miyambo 13:20 imachenjeza kuti: “Mnzawo wa opusa adzapwetekedwa.” Paulendo wa kalasi, mumakhala pamodzi ndi achichepere oterowo kwa nthaŵi yaikulu kwambiri, ndipo zimenezo zimachitikira mumkhalidwe womasuka. Andreas wachichepere ananena motere: “Paulendo wa kalasi, umakhala ukuona mzimu wa dziko tsiku lonse, ndi nyimbo zaudziko zonse ndi malankhulidwe onyansa.”

Chinthu china nchakuti nkwapafupi kusungulumwa pamene muli kutali ndi kunyumba. Maulendo a kalasi ayambitsa kukondana kwa anyamata ndi atsikana ambiri. Kodi pangakhale ngozi yakuti mungagwere m’chikondi ndi wosakhulupirira? Akorinto Woyamba 10:12 amachenjeza kuti: “Iye wakuyesa kuti ali chilili, ayang’anire kuti angagwe.” Ndipo ngakhale ngati munali wolimba moti nkukhoza kukaniza chiyeso, kodi kukhalapo kwanu pa ulendo woterowo kungakhale chokhumudwitsa kwa achichepere ena Achikristu?—Yerekezerani ndi 1 Akorinto 8:7-13; 10:28, 29.

Yvonne wazaka 14 anakana kupita paulendo wa kalasi wokachita maseŵera oterereka pachipale chofeŵa. Iye akufotokoza kuti: “Ndikanatha mlungu wonse ndi achichepere ndi aphunzitsi akunja okhaokha. Ndiponso, ndikanalakalaka kuyanjana ndi abale anga, ntchito yolalikira, ndi misonkhano. Chifukwa china ndicho mmene achichepere ena amachitira ngati palibe wowayang’anira.”

Kukondweretsa Mulungu Mokwanira

Popeza kuti si nthaŵi zonse pamene maulendo a kalasi amaloŵetsamo zachipembedzo, ndale, kapena machitachita ena oletsedwa kwa Akristu, wophunzira pamodzi ndi makolo ake adzafunikira kusankha kaya kukakhala bwino kupita. (Yerekezerani ndi Yesaya 2:4; Chivumbulutso 18:4.) Mikhalidwe ndi zochitika zimasiyana m’malo ndi malo ndi pa kalasi ndi kalasi; chifukwa chake, Akristu a m’dera lina angalimbane ndi mavuto osiyana ndi a m’dera lina.

“Amayi ankadziŵa bwino achichepere a m’kalasi langa ndipo ankadziŵanso kuti mphunzitsi wanga anali wodziŵa kuyang’anira ana. Motero ulendo wa kalasi unali wopindulitsa,” akutero Stephan. “Koma nditasinkhukirapo pamene ulendo womaliza unafika, lingaliro langa la kupita linali losiyana kotheratu.” Chifukwa ninji? Iye akupitiriza kuti: “Zaka zitatu zokha zapitazo, anzanga a m’kalasi anali abwino ndi aulemu. Komano chiyambire panthaŵiyo anamgoneka ndi chisembwere zinadzakhala khalidwe la moyo wawo. Motero sindinapite nawo paulendowo. Ndiponso, ulendo womalizawo anaulekezera pakati.”

Komabe, polingalira zonsezi, inuyo ndi makolo anu muyenera kupenda zoloŵetsedwamo zonse ndi kupanga chosankha chanuchanu. Tsimikizirani kuti, chilichonse chimene musankha, cholinga chanu ndicho ‘kuyenda koyenera [Yehova, NW] kukamkondweretsa monsemo.’—Akolose 1:10.

[Mawu a M’munsi]

a Onani “Krisimasi—Kodi Imakutayitsani Zoposa Zimene Mungaganizire?” m’kope lathu la December 8, 1993.

[Chithunzi patsamba 17]

Kodi mudzakhala ndi mayanjano otani ngati mupita paulendo wa kalasi wokagonera kumeneko?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena