Mpunga—Kodi Mumakonda Wophika Kapena Wosaphika?
YOLEMBEDWA NDI MTOLANKHANI WA GALAMUKANI! KU INDIA
‘KODI mumadya mpunga wophika kapena wosaphika?’ Mwina limenelo ndilo funso limene mungafunsidwe monga mlendo m’nyumba ya Aindiya. Mu India pafupifupi 60 peresenti ya mpunga umadyedwa wofutsa (wophika pang’ono mwa kuŵiritsa). Koma mwina zingakudabwitseni kudziŵa kuti m’maiko Akumadzulo, pafupifupi aliyense amadya mpunga umene Aindiya amatcha wosaphika!
Zonsezi sizingakhale zachilendo kwenikweni pamene muzindikira kuti sitikunena za mmene mpunga umaphikidwira usanaikidwe pa thebulo, koma za njira imene Aindiya amagwiritsira ntchito pokonza mpunga pamene aukolola. Chotero, kodi chimene chimachitika pa ntchitoyo nchiyani, ndipo nchifukwa ninji? Kupenda mpunga mosamalitsa ndi mmene umakonzedwera monga chakudya kudzapereka mayankho otsegula maso.
Chakudya cha Mamiliyoni Ambiri
Zofukulidwa m’mabwinja ndi zolembedwa zakale zimasonyeza kuti mpunga unali kulimidwa mu India ndi China kalelo m’zaka za chikwi chachitatu B.C.E. Nzika zakale za India zinautcha dhanya, kapena “mchirikizi wa fuko la anthu.” Dzina limenelo lidakali loyenera chifukwa chakuti anthu ambiri amadya mpunga kuposa chakudya china chilichonse cholima. Ochuluka mwa anthu ameneŵa amakhala ku Asia, kumene, molingana ndi chidziŵitso china, anthu oposa 600 miliyoni amapeza theka la nyonga yawo ya chakudya tsiku ndi tsiku mumpunga wokha ndi kumenenso mpunga wa padziko lonse woposa 90 peresenti umalimidwa ndi kudyedwa.
Matsiriro achinyontho ndi otentha a Ganges ali amodzi a madera a padziko lonse amene amatulutsa mpunga wambiri koposa. Mvula yochuluka ndi mphepo yofunda, limodzinso ndi antchito ochuluka, zimachititsa malo ameneŵa kukhala oyenera kulimidwako mpunga. Tiyeni tivomere chiitano cha mabwenzi athu okhala kumidzi m’derali ndi kudzionera tokha kukolola ndi kukonzedwa kwa mpunga.
Kukolola Minda ya Mpunga
Basi yathu ikutipititsa ku Jaidercote ku West Bengal, ndipo ulendo wathu ukupitiriza kuloŵa mkati panjinga yotchedwa ricksha. Posapita nthaŵi tikuona anthu otanganitsidwa m’mindayo. Kunoko sitikuonako makina okolola dzinthu! M’malo mwake, atate, ana aamuna, amalume, ndi achimwene ali otanganitsidwa m’minda ya mpunga, mwaluso akumadula ndi mazenga aang’ono chitsakata panthaŵi imodzi. Wina mwa omwetawo, poona kamera yathu, amaliza msangamsanga kumanga mtolo wake ndi udzu nautukulira m’mwamba, naima bwino. Tikuseka kufuna kujambulidwa kumene anthu akumudzi akhala nako.
Mitoloyo imasiyidwa padzuŵa tsiku limodzi kapena aŵiri kuti iume. Ndiyeno achichepere a m’banjamo angathe kuthandiza, akumapititsa kunyumba mitolo yaing’ono youma yochita tswatswatswayo ataidendekera bwinobwino pa mitu pawo.
Tsopano, tafika pamudzi. “Muli bwanji, a Dada?” tikupereka moni kwa woticherezayo, tikumagwiritsira ntchito dzina la ulemu. Kumwetulira kwake kukutisonyeza kuti zonse zili bwino, ndipo mkazi wake tamuona akunyamuka ndi liŵiro kupita kukakonza tiyi.
Pamene tikumwa tiyi wathu wa mmaŵa, tifunsa kuti ulimi wayenda bwanji chaka chino. “Unalipo bwino,” iye akuyankha mwankhokera malinga ndi chizoloŵezi cha alimi, komano akudandaula kuti mwa kugwiritsira ntchito mbewu zopatsa kwambiri m’zaka za posachedwapa, nthaka ikuguga. Poyamba zinkatulutsa mbewu zimene zinaoneka kukhala zabwino koposa, koma tsopano mkhalidwe wasintha. Fataleza wofunikira kaamba ka mbewu zopatsa kwambiri ngwokwera mtengo, ndipo iye sangathe kumugula.
Kuomba ndi Kufutsa
Pamene tikumaliza chakudya chathu chotolera, tilimbikitsa banjalo kupitiriza ntchito yawo yokolola, imene tabwera kudzaona. M’nyumbayi atha kale kuomba. Chakumunsi kwa kanjira, panyumba ina ya pafupi, akazi ali otanganitsidwa. Akuomba mtolo umodzi ndi umodzi pa thandala la nsungwi ndipo ngala zake zikuyoyokera pansi m’mipata mwake. Udzu wotsala ukuunjikidwa mulu.
Mpunga wosapuntha, wotchedwanso paddy, uli ndi mankhusu, olimba amene ali ovuta kupukusa m’mimba. Chotero awo amene amakonda mpunga wosaphika, amangofunikira kuupuntha, kapena kuchotsa mankhusu ake, ndipo mwinamwake kusinjitsa pang’ono ndi kuchotsa mankhusu ngati udzagulitsidwa kunja kwa dziko kumene amafuna wabwino.
Komabe, zokolola za kunoko sizogulitsidwa kunja koma zimadyedwa ndi mabanja ozilimawo. Iwo amasunga mpunga mu tikri, kapena nkhokwe yaudzu yaikulu bwino. Anthu akumatsiriro a Ganges kaŵirikaŵiri amadya mpunga wophika, koma ife mwaulemu tikulankhula mwanjerengo ndi woticherezayo, tikumamuuza kuti chaka chino ayenera kukonza mpunga wosaphika.
“Sindingatero ayi,” iye akuyankha motero. “Kwathu kuno tinazoloŵera mpunga wophika ndipo wosaphika sitimaukonda kwenikweni.”
Tinamva kuti mpunga wophika umakonzedwa mwa kuviika ndi kufutsa, koma sitidziŵa mmene amachitira zimenezi. Tili okondwa chifukwa chakuti bwenzi lathu lifuna kutisonyeza njira imene banja lake limatsatira. Sipafunikira makina apadera chifukwa chakuti amangokonza wochuluka pang’ono panthaŵi imodzi kuti ukwanire banjalo mlungu umodzi kapena iŵiri. Iwo amadzaza hanri yaikulu, kapena mphika wophikira, ndi mpunga wa mankhusu wosungidwa mu tikri ndiyeno amaikamo madzi pafupifupi lita imodzi. Zimenezo zimaterekedwa pa sitovu yophikira, yotchedwa oonoon, yosonkhezeredwa ndi moto wa udzu wochuluka bwino, kufikira madziwo ataphwa. Ndiyeno mpungawo umaviikidwa m’madzi abwino m’beseni usiku wonse, ndipo madziwo atatsanulidwa, amauikanso mu hanri kuti utukutire kufikira madzi ataumanso. Potsirizira pake, mpungawo amauyanika pansi kuti ulimbe ndi dzuŵa, akumaupapasa ndi phazi nthaŵi ndi nthaŵi.
Ife tinaona zimenezi monga kungochulukitsa ntchito, koma njira imeneyi ili ndi mapindu ake kuwonjezera pa kuyenerana kwake ndi zimene banja limakonda. Kufutsa kumachititsa mavitamini ena ndi zomanga thupi za m’mbewu za mpunga kuloŵa kwambiri mu endosperm, kapena mbali imene timadya, ya paddy. Zimenezi sizimasukuluka wamba ndi kutsuka ndi kuphika kotsatirapo. Potsirizira pake pamakhala chakudya chomanga thupi kwambiri. Kukhalapo kapena kusakhalapo kwa phindu lowonjezera la chakudya limenelo kungatanthauze moyo kapena imfa kwa awo amene mpunga uli chakudya chawo chachikulu.
Phindu lina limene alimi iwo okha amazindikira mosavuta nlakuti mpunga wofutsa umasungika mosavuta ndipo mankhusu ake ngosavuta kuchotsa. Chifukwa cha zimenezo, limodzi ndi kulimbitsidwa kwake, umakhala wosadukaduka.
Kulaŵa Mpungawo
“Tsopano ndi nthaŵi yakuti timwe tiyi wina ndi zomwera zake,” akutero woticherezayo. Tikubwerera kunyumba kwake kumene a Dida (Agogo) akukonza moori. Mpunga wa mbuluuli wokonzedwa chatsopano umenewu onse amaukonda kwambiri, makamaka ana. A Dida anyonyomala pafupi ndi oonoon, akumakazinga mpunga wofutsa wochulukirapo wopanda mankhusu umene anali ataviika ndi kuthirako mchere pang’ono. Tsopano mpungawo wauma ndipo uli wosagwirana ndipo atengapo pang’ono panthaŵi ndi nthaŵi naumwazira m’chiwaya chachitsulo chokhala ndi mchenga wotentha. Pamene akutenthetsabe mchengawo, mpungawo ukufufuma kuŵirikiza kangapo kuposa ukulu wake weniweni. Ndiyeno moori wakupsawo auchotsa mwamsanga pamchengapo ndi matsatsa kuti usapserere. Matsatsawo amagwiranso ntchito yokwapulira manja a ana ofuna kutenga moori wotentha m’lichero.
Tikudya moori wathu ndi zibenthu za ngole yophwanyidwa kumene, koma tikusamala kuti tisadyetse, pokumbukira kuti chakudya cha masana chili pafupi.
Ntchito yomalizira imene tikuona ndi ya kupuntha. Kufikira posachedwapa imeneyi inali kuchitidwa ndi munsi ndi mtondo zotchedwa dhenki, mwa kugwiritsira ntchito phazi, koma tsopano, ndi kumidzi komwe, makina opuntha amachita ntchitoyo mwamsanga. Amvula zakale ena amadandaula ndi kusintha kumeneku, popeza mpunga wopunthidwa ndi dhenki umakhalabe ndi mbali yaikulu ya khungu lake la mkati lofiira (epidermis), ukumakhala ndi kukoma kwake ndi zomanga thupi zowonjezereka za chakudyacho. Komabe, makina amachotsa zonse—mankhusu, madeya, ndi mbali yaikulu ya mphumu—kusiya endosperm yokha yoyera yokhala ndi sitachi wambiri imene anthu ambiri amafuna lerolino.
Tsopano akaziwo akufunitsitsa kuti tidye madyerero amene akhala akukonza. Aphika mpunga wofutsa mwa kuuŵiritsa, ndipo tsopano akuuunjika miyulumiyulu wotentha pa masamba a nthochi. Ndiyeno abweretsa mphodza, ndiwo za masamba za komweko, ndi nsomba za m’dziŵe zodyera limodzi ndi mpungawo. Ife tonse tikuvomereza kuti mbali imeneyi ya ulendo wathu ndi imene takondwera nayo koposa.
Inde, kaya umadyedwa uli wophika kapena wosaphika, mpunga ndi chakudya chokoma, wina wa udzu wobiriŵira umene Mulungu anameretsa monga “zitsamba achite nazo munthu.”—Salmo 104:14.
[Bokosi patsamba 18]
Jhal Moori
Kumadera ambiri a India, mpunga wa mbuluuli wotolera umagulitsidwa m’makwalala ndi amalonda ovala zokongola. Jhal moori wokomayo ndi womanga thupi angakonzedwe mosavuta ndipo amasiyana kwambiri ndi zakudya zotolera za masiku onse zolongedwa m’mapaketi.
Kuyamba ndi kapu yodzala mpunga wofufuma wosathiridwa shuga ndi wouma, thirani pang’ono zotsatirazi, molingana ndi zimene mungakonde: matimati oduladula bwino, anyenzi, nkhaka, tsabola wosapsa (ngati mufuna), mtedza pang’ono, chick-peas (ngati mufuna), chaat masala (ufa wa zokoleretsa zosiyanasiyana, wopezeka m’sitolo za Aindiya) kapena mchere ndi tsabola pang’ono, mafuta a mustard kapena mafuta ophikira alionse theka la tiyisupuni. Khutchumuzani mwamphamvu msanganizowo, ndi kudya nthaŵi yomweyo.
Popeza munthu aliyense ali ndi zimene amakonda, ogulitsa moori amalola wakudyayo kusankha pa ndiwo zawo zamasamba zoduladula ndi zokoleretsa zosiyanasiyana zimene akufuna kuti ziwonjezedwe ndi kuchuluka kwake. Mukhoza kupereka zakudya zotolerazo ndi zosanganizira zake pazokhapazokha, kulola alendo anu kusanganiza moori wawo.
[Zithunzi pamasamba 16, 17]
(1) Kuomba mpunga (2) Kupeta (3) A Dida akukonza “moori” (4) Lichero la “moori” ndi zosanganiza zamitundumitundu