Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g95 2/8 tsamba 3
  • Ana Osoŵa Kodi Tsokalo Nlofalikira Motani?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ana Osoŵa Kodi Tsokalo Nlofalikira Motani?
  • Galamukani!—1995
  • Nkhani Yofanana
  • Pamene Ana Abedwa ndi Anthu Osawadziŵa
    Galamukani!—1995
  • Mmene Mungalimbitsire Zomangira za Banja
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Kodi Mungayankhe Bwanji?
    Galamukani!—2009
  • Ana Ayenera Kufunidwa Ndiponso Kukondedwa
    Galamukani!—2000
Onani Zambiri
Galamukani!—1995
g95 2/8 tsamba 3

Ana Osoŵa Kodi Tsokalo Nlofalikira Motani?

‘MWANA WANGA WASOŴA!’

Kuti alankhule mawu amenewo makolo ochuluka angakhale ndi zifukwa zazikulu zingapo zodera nkhaŵa. Pamene kuli kwakuti palibe chiŵerengero chodziŵika cha dziko lonse chimene chingaperekedwe cha ana osoŵa panyumba zawo, tingathe kuzindikira za mmene tsokalo lilili lofalikira kupyolera m’malipoti ofalitsidwa m’maiko ambiri.

MU United States, ana oyambira pa 500,000 kufikira pa oposa 1,000,000, zikumadalira pa mmene akudziŵikitsidwira, amalembedwa kukhala osoŵa panyumba zawo chaka chilichonse. Angakhale osoŵa kwa nyengo yaifupi kapena kusoŵeratu. England akusimba kuti ana pafupifupi 100,000 amazimiririka chaka ndi chaka, ngakhale kuti ena amanena kuti chiŵerengero chake nchachikulu kuposa pamenepo. Yemwe kale anali Soviet Union anasimba za ana zikwi makumi ambiri kukhala osoŵa. Ku South Africa chiŵerengero chake chikunenedwa kukhala choposa pa 10,000. Ndipo ku Latin America, mamiliyoni a ana akuyang’anizana ndi tsoka limeneli.

Mneneri wa Unduna wa Nkhani za m’Dziko wa Italy anasonyeza ukulu wa vutolo kumeneko pamene analemba mu L’Indipendente kuti: “Iwo amachoka panyumba monga mwa masiku onse. Amapita kusukulu kapena kukaseŵera, koma samabwereranso. Amazimiririka, osaonekanso. Ziŵalo zabanja zimawafunafuna mothedwa nzeru, komano pamangokhala zizindikiro zosadziŵika bwino, zosakhutiritsa—ndi mboni zosatsimikizira—zoŵerengeka kwenikweni.”

Kupenda kwina kwaposachedwapa mu United States pa ukulu wa vuto limeneli kunasonyeza kuti mutu wakuti “ana osoŵa” kwenikweni, umaphatikizapo magulu angapo. Gulu limodzi ndilo la ana obedwa ndi anthu osawadziŵa. Lina ndilo la ana obedwa ndi kholo, monga ngati m’zochitika za mkangano wa kuyang’aniridwa kwa ana. Ndiyeno pali otayidwa, ana amene ali osafunidwa ndi makolo kapena owayang’anira. Palinso othaŵa kwawo, gulu lina lalikulu. Ndipo pali awo amene amatayika kapena mwina mwake kulekanitsidwa ndi banja lawo kwa maola oŵerengeka okha kapena kwa tsiku limodzi kapena masiku aŵiri—makamaka ameneŵa ndi ana amene amakhala atachoka panyumba kwanthaŵi yoposa imene analonjeza kapena kuti ana amene makolo awo anamva molakwa zolinga zawo. Ndi ochepa kwambiridi a ameneŵa amene amakhalabe osoŵa.

Komabe, kodi nchiyani chimene chimachitika kwa ana osoŵa a m’magulu okhala paupandu kwambiri? Kodi nchifukwa ninji tsokali limachitika? Kope lino la Galamukani! likupenda mbali zosiyanasiyana za tsokalo ndipo likuyankha funso lakuti, Kodi lidzatha liti?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena