Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g95 3/8 tsamba 12-14
  • Nyengo Yoleka Kusamba—Kuidziŵa Bwino

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Nyengo Yoleka Kusamba—Kuidziŵa Bwino
  • Galamukani!—1995
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chimene Iyo Ili
  • Pamene Imafika ndi Chimene Chimaichititsa
  • Masinthidwe Aakulu m’Moyo
  • Nthaŵi za Kuchita Tondovi
  • Ndi Nthaŵi Yake m’Moyo
  • Kulimbana ndi Nyengo Yoleka Kusamba
    Galamukani!—1995
  • Kupirira Mavuto Amene Azimayi Amakumana Nawo Akamasiya Kusamba
    Galamukani!—2013
  • Nyengo Yoleka Kusamba—Kuvumbula Zinsinsi Zake
    Galamukani!—1995
  • Kodi Nchifukwa Ninji Izi Zikuchitika ku Thupi Langa?
    Galamukani!—1990
Onani Zambiri
Galamukani!—1995
g95 3/8 tsamba 12-14

Nyengo Yoleka Kusamba—Kuidziŵa Bwino

“SINDINGANENE kuti ndi nyengo yabwino kwenikweni m’moyo wa mkazi,” anavomereza motero mkazi wina amene anapyola m’nyengo yoleka kusamba, “koma ndiganiza kuti ungaphunzirepo zinthu. Ndadziŵa mmene ndiyenera kuvomerezera zolephera zanga. Ngati thupi langa lifuna chisamaliro pang’ono kapena kupuma, ndimamvetsera ndi kulipatsa ulemu woliyenera.”

Kufufuza akazi kumene kunasimbidwa m’magazini a Canadian Family Physician kunavumbula kuti “kusadziŵa zimene zingachitike” ndiko kunali chinthu choipa kwambiri ponena za nyengo yoleka kusamba. Komabe, akazi amene anadziŵa kuti nyengo yoleka kusamba ili kusintha kwachibadwa sanali kwenikweni “akuda nkhaŵa, ochita tondovi, ndi amtima wapachala ndipo anali ndi chidaliro chokulirapo ponena za miyoyo yawo.”

Chimene Iyo Ili

Webster’s Ninth New Collegiate Dictionary imamasulira menopause (nyengo yoleka kusamba) motere: “Nyengo yoleka kusamba mwachibadwa yofika [kaŵirikaŵiri] pakati pa misinkhu ya zaka 45 ndi 50.” Menopause yadziŵikanso kukhala kulekekeratu kusamba.

Kwa akazi ena, kuleka kusamba kumangochitika mwadzidzidzi; amati akatsiriza kusamba kwina, kwina sikumachitikanso. Kwa ena, kusambako kumachitika mwa apa ndi apo, kukumachitika pambuyo pa milungu itatu mpaka miyezi ingapo. Pamene chaka chathunthu chipita popanda mkazi kusamba, iye akhoza kugamula mwachidaliro kuti nyengo yoleka kusamba inafika pa nthaŵi ya kusamba kwake kotsirizira.

Pamene Imafika ndi Chimene Chimaichititsa

Mkhalidwe wachibadwa, kudwala, kupsinjika maganizo, mankhwala, ndi opaleshoni zingayambitse nthaŵi ya kuchitika kwake. Ku North America, nyengo yoleka kusamba imafika kwa ambiri pamsinkhu wa zaka za m’ma 51. Nthaŵi pamene imachitika imayambira m’zaka zoyambirira za m’ma 40 mpaka chapakati pa ma 50 ndipo mwa kamodzikamodzi zakazo zisanakwane kapena pambuyo pake. Zofufuza zimasonyeza kuti akazi amene amasuta kaŵirikaŵiri amafikira msanga nyengo yoleka kusamba ndi kuti akazi onenepa kaŵirikaŵiri amaifikira mochedwerapo.

Pobadwa, mkazi amakhala ndi ma ovary okhala ndi mazira onse amene adzakhala nawo nthaŵi zonse, okwanira zikwi mazana angapo. Pakusamba kulikonse kwa pamwezi, mazira oyambira pa 20 mpaka 1,000 amakhwima. Ndiyeno limodzi, kapena nthaŵi zina oposerapo, limatuluka mu ovary ndipo limakhala lokonzekera kugwirizana ndi selo la ubwamuna. Mazira ena okhwimawo amafota ndi kuzimiririka. Ndiponso, mogwirizana ndi kukhwima kwa mazira, milingo ya mahomoni a estrogen ndi progesterone imakwera ndi kutsika nthaŵi zonse.

Pamene mkazi apyola zaka za ma 30, milingo ya estrogen ndi progesterone imayamba kutsika, kaya mwapang’onopang’ono kapena mwa apa ndi apa, ndipo kutulutsa mazira sikungamachitikenso pakusamba kulikonse. Kusamba sikumakhala kwa nthaŵi zonse, kaŵirikaŵiri kukumachitika patapita nthaŵi yotalikirapo; mwazi wotulukawo umasinthasintha maonekedwe, ukumakhala wopepukirapo kapena wolimbirapo. Potsirizira pake mazira amalekekeratu kutuluka, ndipo kusamba kumalekeka.

Kusamba komaliza ndiko mapeto a kusinthasintha kwa milingo ya mahomoni ndi kugwira ntchito kwa ma ovary kumene kwakhala kukuchitika mwina kwa zaka zofika kukhumi. Komabe, milingo yaing’ono ya estrogen imapitirizabe kutulutsidwa ndi ma ovary kwa zaka 10 mpaka 20 panyengo yoleka kusamba. Anabere otchedwa adrenal gland ndi maselo a mafuta amatulutsanso estrogen.

Masinthidwe Aakulu m’Moyo

Minyewa imene imayambukiridwa ndi estrogen kapena imene imadalira pa iyo imayambukiridwa pamene milingo ya estrogen ikutsika. Kutentha thupi kwadzidzidzi kwakanthaŵi kumalingaliridwa kukhala kochititsidwa ndi chiyambukiro cha mahomoni pa mbali ya ubongo imene imalamulira temperecha ya thupi. Njira yochitikira zimenezo njosadziŵika, koma kukuoneka kuti mphamvu yolamulira kutentha ndi kuzizira kwa thupi imachepa kotero kuti matemperecha amene kumbuyoku anali kumveka kukhala bwino mwadzidzidzi amakhala ofunda kwambiri, ndipo thupi limatentha mwadzidzidzi kwakanthaŵi ndi kuchita chitungu kuti lidziziziritse.

M’buku lake lakuti, The Silent Passage—Menopause, Gail Sheehy akuti: “Theka la akazi onse amene amakhala ndi kutentha thupi kwadzidzidzi kwakanthaŵi amayamba kukumva pamene akali kusamba bwinobwino, kukumayamba mwamsanga pamsinkhu wa zaka za makumi anayi. Zofufuza zasonyeza kuti akazi ambiri amakhala ndi kutentha thupi kwadzidzidzi kwakanthaŵi kwa zaka ziŵiri. Gawo limodzi mwa anayi la akazi amakhala nako kwa zaka zisanu. Ndipo 10 peresenti amakhala nako kwa moyo wawo wonse.”

Panthaŵi imeneyi ya moyo wa mkazi, khungu la mkati mwa mpheto yachikazi imayamba kupsapsala ndi kuchepera chinyontho chake pamene milingo ya estrogen icheperachepera. Zizindikiro zina zimene akazi amakhala nazo, akutero Gail Sheehy, zingaphatikizepo “kuchita thukuta usiku, kusoŵa tulo, kulephera kuletsa mkodzo, kutukumuka pamimba kwadzidzidzi, kugunda mofulumira kwa mtima, kulira popanda chifukwa, kuzaza, mutu walitsipa, kuyabwa m’thupi, kunyerenyetsa kwa khungu, [ndi] kuiŵalaiŵala.”

Nthaŵi za Kuchita Tondovi

Kodi kuchepa kwa estrogen kumachititsa tondovi? Funso limeneli lakhala mutu wankhani wochititsa mikangano yochuluka. Yankho lake likuoneka kukhala lakuti kumatero mwa akazi ena, monga aja amene anali a mtima wosinthasintha poyandikira nthaŵi ya kusamba ndi aja osoŵa tulo chifukwa cha kuchita thukuta usiku. Akazi a m’gulu limeneli akuoneka kukhala oyambukiridwa mtima kwambiri ndi kukwera kapena kutsika kwa mahomoni. Malinga ndi kunena kwa Gail Sheehy, akazi ameneŵa kaŵirikaŵiri “amapeza chitonthozo chachikulu pamene apyola nyengo yoleka kusamba” pamene milingo ya mahomoni imakhazikika.

Zizindikiro zowopsa mokulirapo zingakhalepo kwa akazi amene amapyola mofulumira nyengo yoleka kusamba chifukwa cha cheza cha radiation, chemotherapy, kapena opaleshoni yochotsa ma ovary onse aŵiri. Machitidwe ameneŵa angachititse kutsika kwadzidzidzi kwa milingo ya estrogen ndi kuyambitsa zizindikiro za nyengo yoleka kusamba. Zitakhala motero, angalemberedwe mankhwala obwezeretsa estrogen, zikumadalira pa thanzi la mkaziyo.

Kuwopsa ndi mtundu wa zizindikiro zochitikazo kumasiyana kwambiri kwa mkazi ndi mkazi, ngakhale pakati pa akazi okhala pachibale. Zili motero chifukwa chakuti milingo ya mahomoni imasiyana kwa mkazi ndi mkazi ndipo imatsika pamlingo wosiyanasiyana. Ndiponso, akazi amakhudzidwa mosiyanasiyana, kupsinjika maganizo, mphamvu zopiririra, ndi zoyembekezera pamene afikira nyengo yoleka kusamba.

Kaŵirikaŵiri nyengo yoleka kusamba imafikira pamodzi ndi mikhalidwe ina yopsinja maganizo m’moyo wa mkazi, yonga ngati kusamalira makolo okalamba, kuloŵa ntchito, kukulitsa ana kufikira atachoka panyumba, ndi masinthidwe ena a moyo wa chapakati. Zipsinjo zimenezi zingabutse zizindikiro zakuthupi ndi za maganizo, kuphatikizapo kuiŵala zinthu, kulephera kusumika maganizo, nkhaŵa, kunyanyuka, ndi tondovi, zimene zingalingaliridwe molakwa kukhala zochititsidwa ndi nyengo yoleka kusamba.

Ndi Nthaŵi Yake m’Moyo

Nyengo yoleka kusamba sindiyo mapeto a moyo wopindulitsa wa mkazi—ili chabe mapeto a moyo wake wakubala. Pambuyo pa kusamba komaliza kwa mkazi, mtima wake kaŵirikaŵiri umakhala wokhazikikirapo, wosasinthasintha ndi mchitidwe wa mahomoni wa pa mwezi ndi mwezi.

Pamene kuli kwakuti tapenda kulekeka kwa kusamba chifukwa chakuti kuli kusintha kodziŵikiratu, iko kwangokhala chisonyezero cha kusintha kwa mkazi kuchoka ku nthaŵi ya kubala m’moyo wake. Kugwa chinamwali, kukhala ndi pathupi, ndi kuona mwana zilinso nthaŵi za kusintha zochitikira pamodzi ndi masinthidwe a mahomoni, akuthupi, ndi amaganizo. Chotero, nyengo yoleka kusamba ili yomalizira, koma sindiyo nthaŵi yokha ya kusintha kochititsidwa ndi mahomoni m’moyo wa mkazi.

Chifukwa chake, nyengo yoleka kusamba ili nthaŵi yake m’moyo. Mkonzi wamkulu wa Journal of the American Medical Women’s Association analemba kuti, “mwinamwake anthu adzaleka kuona nyengo yoleka kusamba monga vuto, kapena ngakhale monga ‘kusintha,’ ndi kuiona moyenerera monga chabe ‘kusintha kwina.’”

Mopatsa chidaliro, buku lakuti Women Coming of Age limanena kuti mapeto a kubala kwa mkazi “ali achibadwa ndi osapeŵeka mofanana ndi chiyambi chake choikidwiratu. Kufika pa nyengo yoleka kusamba kulidi chizindikiro cha thanzi lakuthupi—chizindikiro chakuti koloko yachibadwa ya thupi [lake] ikugwira bwino ntchito.”

Komabe, kodi nchiyani chimene chingachitidwe kuti kusinthako kuchitike bwinobwino? Ndipo ndimotani mmene mnzanu wa muukwati ndi ziŵalo za banja angakhalire ochirikiza panthaŵi ya kusintha kumeneku m’moyo? Nkhani yotsatira idzapenda mfundo zimenezi.

[Chithunzi patsamba 14]

Kaŵirikaŵiri nyengo yoleka kusamba imafikira pamodzi ndi mikhalidwe ina yopsinja maganizo, kuphatikizapo kusamalira makolo okalamba

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena