Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g95 3/8 tsamba 23-27
  • Ulendo Wobwereza wa ku Russia

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ulendo Wobwereza wa ku Russia
  • Galamukani!—1995
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kukumbukira za ku Russia
  • Banja Lachikondi Lachirasha
  • Ozikika Bwino pa Baibulo
  • Kuyerekezera ndi Chikristu Choyambirira
  • Kuyesayesa Kuyendera Limodzi ndi Chiwonjezeko
  • Anthu a ku Russia Akuyamikira Ufulu wa Kulambira
    Galamukani!—2000
  • Anthu a Yehova Awina Milandu Imene Yatenga Nthawi Yaitali
    Nsanja ya Olonda—2011
  • Anthu Okonda Mtendere Akuyesetsa Kuti Anthu Asaipitse Mbiri Yawo
    Nsanja ya Olonda—2011
  • Msonkhano Wamitundu Yonse wa Mboni za Yehova Woyamba mu Russia
    Galamukani!—1993
Onani Zambiri
Galamukani!—1995
g95 3/8 tsamba 23-27

Ulendo Wobwereza wa ku Russia

KUMODZI KWA KUSINTHA KWAKUKULU KOPOSA MU YEMWE KALE ANALI SOVIET UNION NDIKO UFULU WA KUKAMBITSIRANA ZA CHIPEMBEDZO. ARASHA AMBIRI AGWIRITSIRA NTCHITO UFULU UMENEWO KUPENDERA ZIPHUNZITSO ZA BAIBULO. CHOTULUKAPO CHAKE CHAKHALA CHOZIZWITSA CHAMAKONO.

NDINADABWA chotani nanga pa July 28, 1993, pamene ndinatenga New York Times ya mmaŵa ndi kuona patsamba lakunja chithunzithunzi chachikulu cha ubatizo chojambulidwa ku Moscow! Chinali ndi mawu akuti: “Kumasulidwa kwa chipembedzo mu Russia kudzetsa otembenuzidwa mu Locomotive Stadium ya Moscow ku ubatizo wa aunyinji kukhala Mboni za Yehova.”

Ine ndi mkazi wanga tinali titangobwera kuchokera ku Russia dzulo lake. Tinaonerera ubatizo umenewo wa anthu 1,489. Chikondi cha Chikristu chosonyezedwa ndi Arasha ndi kukondwerera kwawo zinthu zauzimu zinatichititsadi chidwi. Chokumana nacho china chimene tinali nacho pambuyo pa gawo lomaliza la msonkhanowo pa Sande madzulo chikusonyeza zimenezi.

Pamene tinali kubwerera ku hotelo yathu ndi Metro, ndinakhala pafupi ndi mnyamata wina mwina mwake wa zaka 18 kapena 19. Ndinampatsa trakiti lonena za Baibulo lakuti Kodi Pali Chiyembekezo Chotani Kaamba ka Akufa Okondedwa?a, m’Chirasha. Ataliona pang’ono, analipereka kwa amake. Chotero ndinapatsa mnyamatayo linanso. Nditatero analoza pa funso lakuti, “Atafa munthu, adzakhalanso ndi moyo kodi?” ndipo, ndi liwu losonyeza chikayikiro, anafunsa m’Chingelezi kuti, “Kodi mumakhulupirira zimenezi?”—Yobu 14:14.

Potembenuka ndi kuyang’anizana naye, ndipo ndi chikhutiro, ndinayankha kuti: “Ndimazikhulupiriradi!” Ndinawonjezerapo mofulumira kuti: “Tangoganiza. Moyo wathu monga anthu anzeru ndi oganiza uli chozizwitsa. Munthu wina Wapamwamba ayenera kukhala mwini malamulo amene amalamulira kuyambika kwathu kuti tikhale anthu amoyo. Chotero ndimakhulupirira kuti Munthu Wapamwambamwamba ameneyu angalengenso munthu wakufa kuti akhalenso ndi moyo.”

Nthaŵi yomweyo mnyamatayo anayamba kuŵerenga trakitilo. Pamene anamaliza, ndinampatsa brosha lakuti Kodi Mulungu Amatisamaliradi?*, m’Chirasha. Anafuna kudziŵa zambiri, koma ulendo wathu unali kuthera pasiteshoni yotsatira. Ngakhale kuti mnyamatayo ndi amake anafunikira kukapeza sitima ina usiku umenewo, anatuluka nafe pasiteshonipo kuti tikambitsirane pang’ono. Nditafotokoza mwachidule za programu yathu ya phunziro la Baibulo, ndinamsonyeza keyala kuseri kwa brosha imene angalembereko kuti adziŵe zambiri.

Tinachoka m’Russia tsiku lotsatira, koma zokumana nazo zonga chimenechi zinakhomerezeka kwambiri m’maganizo.

Kukumbukira za ku Russia

Ndinapitirizabe kuganiza za ziŵerengero zazikulu za atsopano amene anabatizidwa pamene chiletso cha Mboni za Yehova chinachotsedwa mu yemwe kale anali Soviet Union m’March 1991. Misonkhano yaikulu isanu ndi iŵiri inalinganizidwa mwamsanga kaamba ka chilimwe cha 1991, ndipo 7,820 anamizidwa m’madzi. Ndiyeno, pamisonkhano yaikulu ya m’chilimwe cha 1993—kuphatikizapo umene tinakaloŵa ku Moscow—11,238 anamizidwa.

Changu cha kulalikira cha Mboni za ku Russia chakhala choonekera kwa anthu ambiri Achirasha. Pamene uganiza za kulabadira ziphunzitso za Baibulo kwa Arasha, zimaoneka kukhala zozizwitsa.

‘Kodi kukula kwa chiŵerengero kofulumira kotere kukutheka bwanji?’ tinadabwa motero. ‘Kodi Arashawa ngozama mizu motani m’ziphunzitso za Chikristu?’

Pamene okwatirana ena aŵiri okhala m’Moscow ananena kuti adzatilinganizira malo okhala tikadzabweranso ku Russia, tinayamba kupanga makonzedwe aulendowo. Chiyembekezo chathu cha ulendowo chinakula pamene tinalandira malipoti owonjezereka onena za chikondwerero chapadera cha Arasha cha choonadi cha Baibulo.

Banja Lachikondi Lachirasha

Tinafika pa July 24 ndi masutikesi m’manja kumalo kumene anatikonzera kukakhala mu Moscow—chipinda chachiŵiri cha nyumba yosanja imene inatalikirana ndi mphindi khumi za kuyenda kuchokera pa nyumba ya mabwenzi athu. Ponena za banja limene tinali kudzakhala nalo, Katia yekha wa zaka 15 ndiye amene anali panyumbapo kuti atilandire. Linali Sande madzulo, ndipo ena onse a m’banjalo anali adakali mu utumiki Wachikristu.

Posapita nthaŵi, ziŵalo zina za banjalo zinayamba kubwerera panyumba—Galina, amayi; mwana wamkazi wamng’ono wa zaka 13 Zhenia; ndipo pomalizira pake, Viktor, atate. Palibe aliyense wa iwo amene anali kudziŵa Chingelezi mokwanira, ndipo ifeyo tinkadziŵa Chirasha pang’onodi kwambiri. Kulankhulana kunali kosavuta kwenikweni pamene mabwenzi athu olankhula Chingelezi analipo monga omasulira koma kunali kovuta pamene anachoka. Tinkagwiritsira ntchito dikishonale ya Chirasha ndi Chingelezi ndi majesichala ofotokoza. Katia ndi Zhenia anali odziŵa bwino pa kulankhulanaku, pokhala ataphunzira chinenero cha anthu ogontha.

Banja lonselo linabatizidwa panthaŵi yofanana, zaka ziŵiri zokha zapitazo. Viktor anali mtumiki wotumikira mumpingo, ndipo asungwanawo anagwiritsira ntchito matchuthi awo asukulu kuti athere nthaŵi yambiri mu utumiki. Pamene anali kusukulu, sanazengereze kunena za chikhulupiriro chawo. Kwenikweni, kulalikira kwawo kunadzutsa chidwi cha akuluakulu a boma losakhala la chigawo chawo. Tinachita chidwi kudziŵa kuti banjalo linali kuchititsa maphunziro a Baibulo apanyumba 28 mlungu ndi mlungu kwa okondwerera!

Mwachionekere, chiŵalo chilichonse cha banjalo chinasumika maganizo pa phunziro la Baibulo ndi utumiki Wachikristu, ndipo tinaona kuti miyoyo yawo inalemeretsedwadi. Anasonyeza kukhala achimwemwe.—Machitidwe 20:35.

Ozikika Bwino pa Baibulo

Tisanakagone usiku, ndinkafunsa banjalo mavesi a Baibulo. Choyamba ndinafunsa zimene Chivumbulutso 21:3, 4 amanena. Nthaŵi yomweyo, mogwirizana, asungwanawo anagwira mawu ake. Kenako, ndinafunsa za Yesaya 2:4. Anadziŵanso limenelo, akumagwiritsira ntchito ngakhale majesichala osonyeza kusula malupanga kukhala zolimira.

Ndinapitiriza kufunsa malemba a mu Yesaya amene amafotokoza za ulamuliro wa Ufumu ndi madalitso a dziko latsopano, ndiko kuti, Yesaya 9:6, 7; 11:6-9; 25:8; 33:24; 35:5, 6; ndi 65:21, 22. Banjalo linkatha kudziŵa mawu a vesi lililonse popanda kuyang’ana m’ma Baibulo awo. Panthaŵi ndi nthaŵi asungwanawo ankasonyeza kuti amadziŵa lemba ndi majesichala ofotokoza, onga osonyeza mwana akutsogolera mkango.

Pamadzulo ena tinakambitsirana za malemba onena za amene Mulungu ali, tikumasumika maganizo pa amene amasonyeza Yesu kukhala wocheperapo kwa Mulungu ndi kuti Mulungu ndi Yesu sali munthu mmodzi koma ali amodzi m’chigwirizano. A banjalo ankafotokoza mawu a malemba onga Yohane 10:30, Yohane 17:20, 21, ndi 1 Akorinto 11:3. Mkazi wanga ndi ine tinadabwa ndi mmene ankadziŵira bwino Baibulo.

Pa Lachiŵiri mmaŵa pafupifupi khumi ndi aŵiri a ife tinakumana ndi kuyendera pamodzi pa Metro kumka ku paki ina yokongola kumene tinathera maola aŵiri ndi theka tikulankhula ndi anthu za Baibulo. Tinagaŵanika ndi kugwira ntchito tili aŵiriaŵiri. Mmodzi wa ogwira naye ntchito wanga anali Nadia, msungwana Wachirasha amene anali wodekha pofikira anthu ndi kuwaloŵetsa m’makambitsirano. Anali waluso pochititsa anthu kutchera khutu pamalingaliro a Mulungu a m’Baibulo. Ndinaganiza kuti, ‘Ameneyu ndi wofalitsa wodziŵa bwino wanthaŵi yaitali.’ Pambuyo pake ndinadabwa kwambiri kudziŵa kuti anali ndi zaka 17 zokha ndipo anali atangobatizidwa miyezi iŵiri yapitayo!

Tinali ndi zokumana nazo zotero zambiri, zimene zinatisonkhezera kunena kuti mkhalidwewo ku Russia unali wapadera. Kuyambira pa kugwa kwa Chikomyunizimu, Arasha aonetsa kukhala ofunitsitsa kupenda ziphunzitso za Baibulo. Ambiri a iwo ngophunzira bwino, ndipo amakonda kuŵerenga. Ngakhale ana aang’ono amaŵerenga ndi kumvetsetsa bwino, monga momwe tinaonera pamene tinakachezera banja lina Lachirasha limene linali litadziŵa choonadi cha Baibulo pamene Mboni zinali pansi pa chiletso.

Mwana wamng’ono wamwamuna wa okwatiranawo ananena kuti anafuna kufunsa funso. Iye anapempha motero kupyolera mwa womasulira. Ndinasonkhezereka nalo kwakuti ndinati ngati alilemba, ndidzalipereka kwa afalitsi a Galamukani! Nthaŵi yomweyo anakhala pansi nalemba kalata. Naku kutembenuzidwa kwa kalatayo. Kalatayo yatulutsidwanso patsamba 25.

“Serosha akulembera kalata Watchtower Society ali ku Russia. Ndili ndi zaka zisanu ndi ziŵiri, ndipo ndinayamba kale kumapita kukalalikira ndi Atate ndi Amayi. Ndimakonda kulankhula ndi anthu za Ufumu wa Mulungu. Ndimakondanso kuŵerenga magazini a Galamukani! Amafika ku Russia m’Chirasha kamodzi kokha pamwezi koma m’chinenero cha Chingelezi kaŵiri pamwezi. Ndingakonde kwambiri kuti ndizikhala ndi magazini ameneŵa kaŵiri pamwezi, chifukwa ndimawakonda kwambirimbiridi. Chitani zimenezi chonde.”

Kusiyana ndi mabwenzi amene tinadziŵana nawo ku Moscow kunali kovuta. M’nthaŵi yaifupi yotero, tinafikira pa kuwakonda kwambiri.

Kuyerekezera ndi Chikristu Choyambirira

Tinanyamuka kumka ku Tallinn, Estonia, ndi sitima yausiku. Kumeneko tinaonako nyumba zokongola zatsopano kumene ntchito yolalikira ikuyang’aniridwa tsopano m’limene kale linali lipabuliki la Soviet Union limenelo. Masiku atatu pambuyo pake tinayenda pa sitima kumka ku St. Petersburg. M’malo aŵiri onsewo Akristu anzathu anafunsa za ntchito yolalikira ku Moscow. “Kukhalako kumeneko ndi kuona chiwonjezeko,” ndinayankha motero, “kunandithandiza kumvetsetsa bwinopo zimene zalembedwa kumbali yoyambirira ya Machitidwe 17 ndi m’makalata omka kwa Atesalonika.”

Ndinkadabwa nthaŵi zonse mmene mpingo unakhazikitsidwira mu Tesalonika mkati mwa milungu yoŵerengeka ya utumiki wa mtumwi Paulo kumeneko. Chondidabwitsanso chinali chakuti mkati mwa chaka chimodzi kapena kuposerapo, Paulo analemba makalata aŵiri kwa Akristu atsopano ameneŵa ponena za nkhani zazikulu zauzimu monga ngati za chiukiriro ndi ‘kukwatulidwa nawo pamodzi m’mitambo,’ “tsiku la Yehova,” mfuu ya “mtendere ndi chisungiko!,” ndi “kukhalapo kwa Ambuye wathu Yesu Kristu.” (1 Atesalonika 4:13-17; 5:1-3, NW; 2 Atesalonika 2:1, 2, NW) Kwenikweni, ntchito yachangu ya Akristu oyambirira amenewo inachita chozizwitsa cha m’zaka za zana loyamba—gulu la padziko lonse lokhwima, lolimba mwazimu la alaliki m’nthaŵi yaifupi kwambiri. Pafupifupi zaka khumi pambuyo pake, Paulo analemba kuti “mbiri yabwino” (NW), inali ‘italalikidwa cholengedwa chonse cha pansi pa thambo.’—Akolose 1:23.

Zimene zinali kuchitika mu Russia zinaonekera kwa ine kukhala zofanana ndi zimene zinachitika m’zaka za zana loyamba.

Kuyesayesa Kuyendera Limodzi ndi Chiwonjezeko

Russia ndi dziko lalikulu koposa onse padziko lapansi, motero kupereka chitsogozo ku zikwi zambiri za kumeneko zimene zikulalikira mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu mwachionekere ndiko ntchito yaikulu.—Mateyu 24:14.

Baibulo limati ponena za awo amene anamva za Chikristu m’zaka za zana loyamba: “Dzanja la [Yehova, NW] linali nawo; ndi unyinji wakukhulupira unatembenukira kwa Ambuye.” (Machitidwe 11:21) Ha, mawu amenewo tinawapeza kukhala ogwira ntchito bwino chotani nanga kwa abale athu Achikristu a ku Russia! Munda wa Russia upitirizebetu kukhala wakucha kaamba ka kututa kwauzimu, ndipo zikwi zina zambiri zigwirizanetu m’mwaŵi wamtengo wapatali wa kuthandiza enanso kuyenda panjira ya kumoyo.—Yoperekedwa.

[Mawu a M’munsi]

a Lofalitsidwa ndi Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania.

[Zithunzi pamasamba 24, 25]

Pamwamba: Banja limene tinkakhala nalo. Pamwamba kulamanja: Kulalikira m’paki. Pansi kulamanja: Serosha ndi kalata yake

[Chithunzi patsamba 26]

Malo atsopano a Watch Tower, mu Tallin, Estonia

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena