Kukumana kwa Usiku ku Tanzania
PAMBUYO pa msonkhano wamitundu yonse wa Mboni za Yehova ku Kenya, mokondwera tinayamba ulendo wathu wokajambula nyama kuloŵa mu Tanzania.
Malo athu oyamba kuima anali Lake Manyara National Park. Tinadabwa poona nyama zosiyanasiyana—apusi obiriŵira, nswala, njati, mbidzi, ndi zina zambiri. Tangolingalirani kuona padziŵe mitu ya mvuwu ili bibibi. Tangolingalirani kuona nyamalikiti ikudya kumbali ina, mkango uli mu udzu chauko, ndipo nsambi wa nyumbu patsogolo pakepo.
Titafika ku Ngorongoro Crater, tinapempha wotitsogolera ndi kubwereka galimoto yamphamvu kaamba ka ulendo woona nyama wa tsiku limodzi kuloŵa mu caldera (chigwa chopangika pamene phiri la volokano linaphwerera). Ulendo wa mabampuwo unali wa pafupifupi mamita 600 kuchokera pamlomo pake kumka pansi pa chigwacho. Ha, ndi malo ochititsadi chidwi chotani nanga! Nyama zinali m’chigwa chonsecho. Misambi ya nyumbu inali kuyenda monga ngati kuti ikusamukira kwina. Mbidzi, ngondo, ndi mphoyo za mtundu wa Thomson ndi Grant nzambiri. Pamalo ena amene tinaima, mkango wamanyenje unakhala pansi pa mthunzi wa galimoto yathu, wosasamala kuti tinali pamwamba pake. Pambuyo pake tinaima kuti tione chipembere chakuda chapatali ndi njovu za m’thengo chapafupi zikumadya m’mitengo. Pamene tinali kukwera kuchoka m’chigawocho, tinakumbukira nyama zambiri zochititsa chidwi. Kodi tinali titaiŵalapo nyama ina?
Oo, inde, nyalugwe wa mu Afirika. Koma chiyembekezo cha kumuona m’thengo chimangokhala chosaphula kanthu. Wojambula zithunzi Erwin Bauer anati: “Alendo odzaona nyama amalondola anyalugwe mwachangu ndipo mwakhama, makamaka chifukwa chakuti nyamazo nzovuta kwenikweni kuzipeza, osanena za kuzijambula. Alendo ambiri odzajambula nyama samaona ngakhale mmodzi. Mkati mwa maulendo anga 15, ndaona anyalugwe okwanira asanu ndi atatu, ndipo mmodzi yekha wokhala pamalo okhoza kujambulidwa.”—International Wildlife.
Pofika madzulo tinali kulingalira za nkhani ina. Pamalo okhala alendo panalibe malo ogona, chotero tinafunikira kufunafuna malo ena ogona. Zimenezi zinatipangitsa kuloŵa m’kamsewu kena kadothi ka mdima wa ndiwe yani. Mwadzidzidzi aŵirife amene tinakhala kumpando wa kutsogolo tinadzidzimuka. Chinthu china chodera chinadumphira kutsogolo kwa magetsi athu. Tinaima mofulumira ndi kupuma mwankhwezakweza tili odabwa!
Patsogolo pathu penipenipo panali nyalugwe wamkulu! Ngati awo amene anali kumipando yakumbuyo anaona ngati analibe mwaŵi, zimenezo zinathera pomwepo. Nyalugweyo anathamangira kumbali kwa msewu kulamanja—naima chiriri. ‘Kodi ndichitenji?’ iye anaoneka ngati kuti akusinkhasinkha motero pamagetsipo ndi pamaso pa ife tonse. ‘Ndiukire, kapena ndingotembenuka kusiya “mdani” wosadziŵikayu ndi kuthaŵira m’tchire?’
Adrian, mmodzi wa mabwenzi athu, ndiye amene anali pafupi kwambiri, kungotalikirana ndi mita imodzi ndi nyama ya nyonga ndi yokongola imeneyi imene ingafwamphuke. “Tandipatsani msanga fulashi ija,” iye ananong’ona motero pamene anali kunyamula kamera yake ya otomatiki. Wina anachenjeza kumbuyo kwake kuti, “Musachite phokoso.” Kamerayo inatcheredwa ndipo chithunzithunzi chinajambulidwa, komano kunaoneka ngati kuti fulashi inathwanimira mkati mwa galimotolo. Pamene mabatire anali kudzitchaja m’fulashiyo, Adrian anatsitsa zenera lake mosamala. Nyalugwe anangoimabe pafupi ngati mkono umodzi, nsonga ya mchira wake ikugwedezeka, atatuzula maso.
Titangojambula chithunzithunzi chachiŵiri, iye anasankha chochita. Nyalugwe wokongolayo anadumphira m’zitsamba nangozimiririka. Munali chikondwerero chachikulu chotani nanga m’galimoto mwathumo! Chokumana nacho chosaiŵalika, chimene pambuyo pake wotitsogolerayo anatiuza kuti sichimachitikachitika. Pamene chithunzithunzi chachiŵiricho chinatuluka bwino kwambiri, tinachitenga kuti tizikumbukira kukumana kwa usiku kokondweretsa kumeneko ku Tanzania.