Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g95 6/8 tsamba 7-8
  • Kodi Anachita Bwanji Zimenezo?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Anachita Bwanji Zimenezo?
  • Galamukani!—1995
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • “Ufumu Wanu Udze”
  • Kodi Mulungu Ankakondwera ndi Malonda a Ukapolo?
    Galamukani!—2001
  • Tinayamba Kalekale Kulimbana Ndi Ukapolo
    Galamukani!—2002
  • Kodi Baibulo Limalimbikitsa Ukapolo?
    Galamukani!—2011
  • Akapolo Anapeza Ufulu M’mbuyomu Komanso Masiku Ano
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2017
Onani Zambiri
Galamukani!—1995
g95 6/8 tsamba 7-8

Kodi Anachita Bwanji Zimenezo?

KODI anthu analungamitsa motani malonda a akapolo? Olemba mbiri amanena kuti kufikira m’zaka za zana la 18, ndi anthu oŵerengeka amene anakayikira kuyenera kwa ukapolo. Buku lakuti The Rise and Fall of Black Slavery limati: “Panthaŵi imene Columbus anafika mwadzidzidzi ku West Indies, tchalitchi ngakhale zolemba zimene chinavomereza sizinasonyeze kwa odzakhala kumeneko kuti kugwiritsira ntchito kwawo akapolo kunali koipa, ngakhale kuti anthu ena atchalitchi oŵerengeka anakayikirapo. . . . Panalibe lingaliro lakuti kuyambika kwa ukapolo, kumene kunali kogwirizana kwambiri ndi Azungu, kunayenera kukayikiridwa.”

Pamene malonda odutsa Atlantic amenewo anafika pachimake, atsogoleri achipembedzo ambiri anagwiritsira ntchito zigomeko zachipembedzo kuchirikizira ukapolo. Buku lakuti American Slavery limati: “Abusa Achiprotesitanti [ku America] anachita zamphamvu kuchirikiza ukapolo . . . Mwinamwake chigomeko chofala ndi champhamvu kwambiri chachipembedzo chinali lingaliro lakuti ukapolo unali mbali ya makonzedwe a Mulungu a kutsegulira anthu akunja panthaŵiyo madalitso a Chikristu.”

Koma nkhanza ndi nkhalwe yochitidwa kaŵirikaŵiri kwa akapolowo inafunikiranso kulungamitsidwa kuposa chinyengo cha kupereka “madalitso a Chikristu.” Chotero atsamunda ndiponso alembi ndi afilosofi ku Ulaya anakhulupirira kuti anthu akuda sanali ofanana ndi achiyera. Edward Long, mlimi amene anali kudzalemba buku lakuti History of Jamaica, anati: “Pamene tilingalira za chibadwa cha anthu ameneŵa, ndi kusiyana kwawo ndi anthu ena onse, kodi sitinganene kuti ali amtundu wosiyana?” Zotulukapo za kulingalira kotero zinatchulidwa ndi bwanamkubwa wa Martinique: “Ndafika pa kukhulupirira zolimba kuti munthu ayenera kuchita ndi Anegro mofanana ndi zilombo.”

Potsiriza pake kufuna phindu la zachuma ndiponso kuthandiza anthu kunathandizira kuthetsa malonda a akapolo odutsa Atlantic. Kuyambira pachiyambi anthu Achiafirika anatsutsa kugwidwa kwawo ukapolo, ndipo pofika chakumapeto kwa zaka za zana la 18, zipanduko zinali zofala. Ambuye awo amantha anapeza kuti mkhalidwe wawo unali wangozi kwambiri. Ndiponso anakayikira ngati, m’malo mwa kuchirikiza akapolo, kukanakhala kotsikirapo mtengo kulemba antchito achikhalire pamene kunali kofunikira.

Panthaŵi imodzimodziyo, zigomeko zachikhalidwe, zachipembedzo, ndi zaumunthu zotsutsa ukapolo zinachirikizidwa kwambiri ku Ulaya ndi ku America. Mabungwe omenyera nkhondo kuletsa ukapolo analimba. Ngakhale kuti malonda a akapolo analetsedwa mwalamulo m’maiko ambiri kuyambira chaka cha 1807 kumka mtsogolo, zotulukapo za ukapolo zinatsalirabe.

Programu ya pawailesi yakanema yakuti, The Africans: A Triple Heritage, inafotokoza molunjika malingaliro a ana aamuna ndi aakazi a Afirika: “Kale masiku aukapolo asanayambe, tinkakhala ku . . . Afirika. Ndiyeno anthu ena achilendo anadza natenga ena mwa ife. Lerolino, ndife omwazikana kwambiri kwakuti dzuŵa silimaloŵa kwa mbadwa za Afirika.” Kupezeka kwa anthu mamiliyoni ambiri Achiafirika ku North ndi South America, ku Caribbean, ndi ku Ulaya kuli chotulukapo chachionekere cha malonda a akapolo.

Anthu amakanganabe pankhani yakuti ndani ali ndi mlandu wa malonda a akapolo odutsa Atlantic. Basil Davidson, katswiri wa mbiri ya Afirika, akulemba m’buku lake lakuti The African Slave Trade: “Afirika ndi Ulaya onse anali ndi thayo.”

“Ufumu Wanu Udze”

Pali kanthu kena kamene tingaphunzirepo—kanthu kokhudza ulamuliro wa munthu. Mwamuna wina wanzeru analemba: “Ndinalingalira ntchito zonse zotsendereza zimene zinachitidwa pansi pano,—ndipo taonani! misozi ya otsenderezedwa, ndipo alibe wowatonthoza, ndipo kwa owatsenderezawo kuli mphamvu.”—Mlaliki 4:1, Rotherham.

Nzachisoni kuti mawu amenewo, olembedwa kale malonda a akapolo a m’Afirika asanayambe, akali oona lerolino. Otsendereza ndi otsenderezedwa tikali nawo, ndiponso m’maiko ena mukali akapolo ndi ambuye awo. Akristu akudziŵa kuti posachedwa, Yehova, kupyolera mwa boma la Ufumu wa Mulungu, “adzapulumutsa waumphaŵi wofuulayo; ndi wozunzika amene alibe mthandizi.” (Salmo 72:12) Pa chifukwa chimenecho ndi zina, iwo amapitiriza kupemphera kwa Mulungu kuti: “Ufumu wanu udze.”—Mateyu 6:10.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena