Kodi Kuloŵa m’Ngongole Kumathandiza?
“MUSAWONONGE ndalama zanu musanazilandire.” Popeza kuti kwa anthu ambiri kuloŵa m’ngogole ndiko moyo wa masiku ano, kodi uphungu umenewu woperekedwa ndi yemwe kale anali pulezidenti wa United States Thomas Jefferson umamveka kukhala wachikale?
M’maiko ambiri malipiro adakali otsika poyerekezera ndi mitengo ya zinthu, ndi kuchepachepa mphamvu kwa ndalama kumachititsa ndalama za kubanki kukhala zosathandiza kwambiri. Ndiponso, mkhalidwe wa zachuma umasintha makhalidwe abwino a anthu. Komabe, kuona mtima nkofunika. Chifukwa chakuti mikhalidwe yonga kuchita chiyengo pa misonkho ndi kulephera kulipira ngongole njofala, kusungabe chikumbumtima chabwino nkovutadi kwambiri. Pamenepo mposadabwitsa kuti kaŵirikaŵiri nkhani yaikulu ndiyo ya chuma, ndipo malingaliro osungira ndalama kapena opezera ndalama ngambiri m’manyuzipepala ndi m’magazini ndi pa wailesi yakanema pamene anthu akuyesayesa kudziŵa mmene angachitire ndi zovuta zachuma. Panthaŵi imodzimodziyo, nkoyenera kuti mudere nkhaŵa za mmene inuyo ndi banja lanu mungadzisamalirire.—1 Timoteo 5:8.
Popeza kuti ndi anthu ochepa amene ali ndi ndalama zokwanira, kodi mungachitenji kuti mupeŵe mavuto pa banja lanu? Choyamba, pali phunziro lofunika kukumbukiridwa.
Peŵani Ngongole Zambiri
Kodi nchifukwa ninji ena amaloŵa m’ngongole? Sikuti nthaŵi zonse kukongola ndalama kumachitika chifukwa cha mkhalidwe wa mavuto, monga ngati kudwala. Chikhumbo cha kufuna kukhala ndi zinthu zina zakuthupi chingakhale champhamvu kwambiri. Komanso, chochititsa kuloŵa m’ngongolecho sichingakhale choipa. Kwenikweni, kungakhale bwino kulipira ndalama zogulira nyumba kuposa kulipirira lendi nyumbayo, kapena kungakhale kofunikira kugula galimoto. Munthu wodyetsa banja amafuna kuti banja lake likhale lachimwemwe. Amafuna kukhala mwamuna ndi atate wopita patsogolo. Mwachionekere, amalingalira kuti banja lake nloyenerera kupatsidwa zinthu zambiri zakuthupi zimene ena ali nazo.
Zoonadi, munthu angakhale ndi chikhumbo cha kubwereka ndalama zoti agulire chinthu chokhumbidwa koma chimene sichili chofunika kwenikweni. Kupeza zinthu kumasangalatsa munthu, kodi si choncho? Kodi ndani amene sangakondwere ndi diresi lokongola, nsapato zatsopano, kapena ngakhale kanthu kena monga ngati galimoto yatsopano? Ndipo kodi ndani amene sangakonde kukhala ndi nyumba yokongola? Komabe, samalani! Anthu amalonda ali onyengerera, ndipo amapeza ndalama zambiri mwa kugulitsa zinthu kwa anthu amene samazifunikira ndi amene sangathe kuzisamalira.
Kumbukiraninso kuti, kubweza ngongole nthaŵi zonse kungadzetse mavuto pamaunansi a m’banja. Pangakhale kusamvana ndi kupsetsana mitima. Wolemba maseŵero wina Henrik Ibsen analondola pamene anati: “Moyo wa panyumba umaleka kukhala waufulu ndi wokondweretsa pamene uzikidwa pa kubwereka ndalama kapena pa ngongole.” Ngati simukhoza kulipira ndalama zanu panthaŵi yake, mbiri yanu ingaipe. Popeza kuti kugwiritsira ntchito ndalama zobwereka kuli kosavuta kuposa kuzibweza ndi chiwongola dzanja, ambiri amapeza kuti zimene anagula sizimadzetsa chisangalalo chimene anayembekezera.
Kaŵirikaŵiri, maboma amaumirira pa kubwereka ndalama zambirimbiri, akumawonjezera ndalama za chiwongola dzanja zoti alipire. Ngakhale kuti zimenezi zingakhale zoyenera, kodi nkutsanziriranji maiko angongole zambirimbiriwo? Ngongole zambiri zimawonjezera umphaŵi ndi kusasungika kwa zinthu, mmalo mopereka chuma kwa anthu. Kuli monga momwe mwambi wina Wachidanishi umanenera, “kulipirira buledi utamudya kale nkovuta.”
Mwamwaŵi, nkhaŵa ya ngongole imachepa kwambiri pamene mudziŵa mmene mungagwiritsirire ntchito ndalama mwanzeru. Chotero patulani nthaŵi yolinganizira mosamala zokagula zanu kuti mupeŵe chitsenderezo cha kubwereka ndalama. Ngakhale m’maiko mmene muli ndalama zochepa mphamvu kwambiri, muli njira zosungitsira ndalama—mwa kugula zinthu zotsika mtengo ndi mwa kugula zinthu zimene zili zofunika zokha. Zimenezo zimafuna kuti mugwiritsire ntchito ndalama zimene mukhoza kupeza, kukhala wofunitsitsa kuyembekezera kapena kudzimana.
Dzifunseni kuti: Kodi kuloŵa kwanga m’ngongole kudzadzetsa mavuto pa banja langa? Bwanji nanga ponena za mbiri yanga ngati ndilephera kulipira ngongoleyo? Kungatenge nthaŵi yaitali kuti munthuyo akhulupiriridwenso! Ponena za nkhaniyi, uphungu wothandiza ndi wamphamvu ulipo. Bwanji osapenda Baibulo kuti muone kaya ngati lingathandize inu ndi banja lanu kulimbana ndi nkhani ya ngongole?
Kodi Baibulo Lingakuthandizeni?
Chinthu chofunika nchakuti, Baibulo lingathandize tonsefe kukulitsa chidaliro chenicheni mwa Yehova. Ndithudi ife tifunikira thandizo mu “nthaŵi zoŵaŵitsa” zino. (2 Timoteo 3:1) Timalangizidwa kuti: “Mtima wanu ukhale wosakonda chuma; zimene muli nazo zikukwanireni; pakuti iye anati, Sindidzakusiya konse, kungakhale kukutaya, sindidzakutaya ndithu. Kotero kuti tinena molimbika mtima, Mthandizi wanga ndiye [ Yehova, NW ]; sindidzawopa; adzandichitira chiyani munthu?” (Ahebri 13:5, 6) Nkofunika chotani nanga kukulitsa chikhulupiriro champhamvu mwa Mulungu monga Mgaŵiri wathu!
Ngakhale kuti Baibulo silimauza aliyense za mmene angapezere ndalama, limapereka zitsogozo zanzeru. Yesu Kristu analimbikitsa ophunzira ake kusamalira mkhalidwe wawo wauzimu choyamba: “Odala ali osauka mumzimu.” (Mateyu 5:3) Timauzidwanso kuika zonulirapo: “Muyesetse kukhala chete ndi kuchita za inu eni ndi kugwira ntchito ndi manja anu, monga tinakuuzani; kuti mukayende oona mtima pa iwo a kunja, ndi kukhala osasoŵa kanthu.” (1 Atesalonika 4:11, 12) Kodi kukhala chete ndi kukhala ndi mlingo winawake wa bata sikumafuna kuti tikhale ndi moyo mogwirizana ndi zomwe timapeza?
Mawu a Mulungu angatithandize kusintha kalingaliridwe kathu. Mlembi wa Miyambo anasonyeza lingaliro loyenera popempha Mulungu kuti: “Musandipatse umphaŵi, ngakhale chuma, mundidyetse zakudya zondiyenera; ndingakhute ndi kukukanani, ndi kuti, Yehova ndani? Kapena ndingasauke ndi kuba, ndi kutchula dzina la Mulungu wanga pachabe.” (Miyambo 30:8, 9) Chotero musachite manyazi ngati mukhala ndi moyo pa zochepa mwinamwake kwakanthaŵi. Musalole chimwemwe chanu kudalira pa zinthu zakuthupi, monga momwe ambiri amachitira, akumadziyerekezera iwo eni ndi ena kapena akumavutika maganizo mosayenera ndi chuma chakuthupi.—Mateyu 6:31-33.
Ndiponso, Baibulo lingakuthandizeni kukulitsa zizoloŵezi zabwino. Phunzirani kukhala wosinira komanso osati woumira zinthu, mukumakhutiritsidwa ndi zinthu zimene mungathe kupeza. Ngati muli wachichepere, musayembekezere nthaŵi yomweyo kupeza zimene achikulire apeza m’zaka zambiri za kugwira ntchito. Peŵani kuikidwa muukapolo ndi kukondetsa zinthu zakuthupi. Moyenerera, Baibulo limatichenjeza ponena za “chikondi cha pandalama,” osati ndalama, likumati: “Iwo akufuna kukhala achuma amagwa m’chiyesero ndi m’msampha, ndi m’zilakolako zambiri zopusa ndi zopweteka, zotere zonga zimiza anthu m’chiwonongeko ndi chitayiko. Pakuti muzu wa zoipa zonse ndiwo chikondi cha pandalama; chimene ena pochikhumba, anasochera, nataya chikhulupiriro, nadzipyoza ndi zoŵaŵa zambiri.” (1 Timoteo 6:9, 10) Kuli kofunika chotani nanga kuzindikira kusiyana kumene kuli pa zimene mukufunikiradi ndi zimene simukufunikira kwenikweni!
Komabe, kodi mukulingalira kuti malipiro anu ali otsika kwambiri? Zoona, kusoŵa zinthu nkovuta kukupirira popanda kugwiritsidwa mwala. Chikhalirechobe, khalani wofunitsitsa kudzimana zinthu zimene zili zosafunika kwenikweni m’malo mwa kuziloŵera m’ngongole, kumene kungakupatseni mtolo wolemetsa ndipo ngakhale kukuwonongetsani ndalama. Linganizani mosamala, ndipo khalani wosinira. Mwina mungapeze malingaliro othandiza mwa kukambitsirana ndi bwenzi lodziŵa bwino. Kodi kuphunzira kantchito kena kungathandize? Kumbukirani: Kutsatira malamulo a Baibulo, kuika zinthu zauzimu pamalo oyamba, ndi kukhulupirira Yehova kuli zinthu zofunika—pa mkhalidwe uliwonse.—Afilipi 4:11-13.
Inde, kuloŵa m’ngongole kungakhale kosathandiza. Kwanenedwa kuti: “Munthu amene ali m’ngongole ali wogwidwa mu msampha.” Mtolo wa ngongole ungakhale wovulaza banja, thanzi, ndi mkhalidwe wauzimu. Ngongole ingachititse wobwereka ndalamayo kukhala wosaukirapo. Miyambo 22:7 imati: “Wolemera alamulira osauka; ndipo wokongola ndiye kapolo wa womkongoletsa.” Chifukwa chake, peŵani ngongole yosayenera. Ife tingapindulebe ndi lamulo lophatikizidwa m’zimene mtumwi Paulo ananena kwa Akristu: “Musakhale ndi mangawa kwa munthu aliyense, koma kukondana ndiko; pakuti iye amene akondana ndi mnzake wakwanitsa lamulo.”—Aroma 13:8.
Mosasamala kanthu za mkhalidwe wa zachuma m’dziko lanu, yembekezerani mwachidaliro dziko latsopano la Mulungu. Posachedwapa anthu sadzagaŵidwanso kukhala magulu a okongoletsa ndi okongola. Mu Ufumu wa Mulungu, sipadzakhala wosauka. Lonjezo la Yehova lidzakwaniritsidwa: “Adzapulumutsa waumphaŵi wofuulayo; ndi wozunzika amene alibe mthandizi. Adzachitira nsoni wosauka ndi waumphaŵi, nadzapulumutsa moyo wa aumphaŵi.” (Salmo 72:12, 13) M’malo mwa kungomenyera nkhondo pa kukhala ndi moyo, nzika za dziko lapansi panthaŵiyo ‘zidzakondwera nawo mtendere wochuluka.’—Salmo 37:11.
[Chithunzi patsamba 12]
Thomas Jefferson
[Mawu a Chithunzi]
Chithunzithunzi chojambulidwa ndi Gilbert Stuart. Mwachilolezo cha Bowdoin College Museum of Art/Dictionary of American Portraits/Dover
[Chithunzi patsamba 13]
Kuloŵa m’ngongole zambiri kungaloŵetse mavuto m’banja mwanu