Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g95 7/8 tsamba 20-21
  • Chifukwa Chake Ambiri Amakhulupirira Kuti Dziko Lidzatha

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chifukwa Chake Ambiri Amakhulupirira Kuti Dziko Lidzatha
  • Galamukani!—1995
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Magwero Ake a m’Baibulo
  • Baibulo ndi Mapeto a Dziko
  • Kumva Molakwa m’Zaka za Zana Loyamba
  • Enanso Afunikira Kuwongoleredwa
  • Kodi Dzikoli Lidzatha? Kodi Baibulo Limanena Kuti Zinthu Zonse Zidzawonongedwa?
    Nkhani Zina
  • Mapeto Osangalatsa a Masomphenya a M’buku la Chivumbulutso
    Mapeto Osangalatsa a Masomphenya a M’buku la Chivumbulutso
  • Mayankho a Mafunso Anayi Okhudza Kutha kwa Dziko
    Nsanja ya Olonda—2010
  • Kodi Dzikoli Lidzapulumuka?
    Kodi Dzikoli Lidzapulumuka?
Onani Zambiri
Galamukani!—1995
g95 7/8 tsamba 20-21

Chifukwa Chake Ambiri Amakhulupirira Kuti Dziko Lidzatha

DZIKO lilidi mumkhalidwe wothetsa nzeru, monga momwe ambiri lerolino amavomerezera msanga. “Ndafunsa anthu akumadera osiyanasiyana a dziko zimene aganiza ponena za mtsogolo mwathu,” mlalikiyo Billy Graham analemba motero. “Ochuluka sakuyembekezera zabwino. . . . Nthaŵi zonse mawuwo ‘Armagedo’ ndi ‘Apocalypse’ amagwiritsiridwa ntchito kufotokozera zochitika padziko.”

Kodi nchifukwa ninji mawuwo “Armagedo” ndi “Apocalypse” amagwiritsiridwa ntchito kaŵirikaŵiri kufotokozera mkhalidwe wa lerolino? Kodi amatanthauzanji?

Magwero Ake a m’Baibulo

Baibulo limalankhula za “nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu, Wamphamvuyonse” ndipo limagwirizanitsa nkhondo imeneyi ndi malo “otchedwa m’Chihebri Harmagedo,” kapena Armagedo. (Chivumbulutso 16:14-16) Webster’s New Collegiate Dictionary imamasulira Armagedo kukhala “nkhondo yomaliza ndi yothetsa mkangano pakati pa magulu abwino ndi oipa.”

Ngakhale kuti liwulo “apocalypse” latengedwa ku liwu la Chigiriki lotanthauza “chivumbulutso,” kapena “kuvundukula,” ilo lakhala ndi tanthauzo lina. Buku la Baibulo la Chivumbulutso, kapena Apocalypse, limasonyeza chiwonongeko cha Mulungu pa oipa ndi Ulamuliro wa Zaka Chikwi wa Mwana wake, Yesu Kristu. (Chivumbulutso 19:11-16; 20:6) Motero, Webster’s New Collegiate Dictionary imamasulira “apocalypse” kukhala “chiwonongeko chowopsa choyandikira pamene Mulungu adzawononga maulamuliro oipa omwe akulamulira ndi kuukitsira olungama ku moyo mu ufumu waumesiya.”

Pamene anthu lerolino alankhula za dziko ndi mkhalidwe wake, iwo mwachionekere amasonkhezeredwa ndi zimene zanenedwa m’Baibulo. Kodi Baibulo limanenanji kwenikweni za mapeto a dziko?

Baibulo ndi Mapeto a Dziko

Baibulo limalosera momveka bwino za mapeto a dziko. Yesu Kristu ndi ophunzira ake analankhula za nthaŵi ya mapeto. (Mateyu 13:39, 40, 49; 24:3; 2 Timoteo 3:1; 2 Petro 3:3; King James Version) Komabe, iwo sanatanthauze kuti dziko lapansi lenilenilo lidzawonongedwa. Ponena za dziko lapansi lenilenilo, Baibulo limati: “Silidzagwedezeka ku nthaŵi yonse.” (Salmo 104:5) Mawuwo “mapeto a dziko” amangotanthauza “chimaliziro cha dongosolo la zinthu.”—New World Translation.

Mtumwi Petro analankhula za dziko lokhalako Chigumula cha m’tsiku la Nowa chisanachitike ndipo anati: “Dziko lapansi la masiku aja [lopangidwa ndi anthu osapembedza], pomizika ndi madzi, lidawonongeka.” Ndiyeno Petro anapitiriza kunena kuti dziko lathuli ‘lasungika kufikira tsiku la chiweruzo ndi chiwonongeko cha anthu osapembedza.’ (2 Petro 3:5-7) Nayenso mtumwi Yohane analemba kuti: “Dziko lapansi lipita, ndi chilakolako chake; koma iye amene achita chifuniro cha Mulungu akhala ku nthaŵi yonse.”—1 Yohane 2:17.

Pamapeto a dzikoli, nayenso wolamulira wake wosapembedza wosaonekayo adzachotsedwa. (Chivumbulutso 20:1-3) Mtumwi Paulo analemba za wolamulira woipa ameneyu: “Mulungu wa nthaŵi ino ya pansi pano unachititsa khungu maganizo awo a osakhulupirira.” Yesu anati za iye: “Mkulu wa dziko ili lapansi [Satana Mdyerekezi] adzatayidwa kunja tsopano.”—2 Akorinto 4:4; Yohane 12:31.

Kodi kuchotsedwa kwa dzikoli ndi wolamulira wake woipa sikudzakhala dalitso? Akristu kwa nthaŵi yaitali apempherera zimenezi kuti zichitike, akumapempha kuti Ufumu wa Mulungu udze ndi kuti chifuniro chake chichitike pa dziko lapansi. Iwo akupemphera kuti Yesu Kristu achite momvera lamulo la Atate wake la kuchotsa kuipa konse pa dziko lapansi!—Salmo 110:1, 2; Miyambo 2:21, 22; Danieli 2:44; Mateyu 6:9, 10.

Komabe, zimenezi zikudzutsa funso: Kodi kunenera konama, kapena kolakwika kwa mapeto a dziko kungakhale kutachitika chifukwa chakuti anthu ananenera za deti la chochitika chimenechi malinga ndi kumva kwawo molakwa maulosi oona a Baibulo kapena kuwatanthauzira molakwa? Tiyeni tione.

Kumva Molakwa m’Zaka za Zana Loyamba

Talingalirani zimene zinachitika m’zaka za zana loyamba. Pamene Yesu anali pafupi kukwera kumwamba, atumwi ake anamfunsa mwachidwi: “Ambuye, kodi nthaŵi ino mubwezera ufumu kwa Israyeli?” Iwo anafuna kulandira madalitso onse a Ufumuwo nthaŵi yomweyo, koma Yesu anati: “Sikuli kwa inu kudziŵa nthaŵi kapena nyengo, zimene Atate anaziika m’ulamuliro wake wa iye yekha.”—Machitidwe 1:6, 7.

Patangotsala masiku atatu imfa yake isanachitike, Yesu analankhula zofanana ndi zimenezo: “Chifukwa chake dikirani, pakuti simudziŵa tsiku lake lakufika Ambuye wanu.” Anawonjezera kuti: “Koma za tsiku ilo, kapena nthaŵi yake sadziŵa munthu, angakhale angelo m’mwamba, angakhale Mwana, koma Atate ndiye. Yang’anirani, dikirani, . . . pakuti simudziŵa nthaŵi yake.” (Mateyu 24:42, 44; Marko 13:32, 33) Miyezi ingapo zimenezo zisanachitike, Yesu analimbikitsanso kuti: “Khalani okonzeka inunso; chifukwa nthaŵi imene simulingirira, Mwana wa munthu akudza.”—Luka 12:40.

Mosasamala kanthu za machenjezo otero operekedwa ndi Yesu, Akristu oyambirira, pofunitsitsa kukhalapo kwa Kristu ndi madalitso amene kudzadzetsa, anayamba kuganizira za nthaŵi pamene malonjezo a Ufumu adzakwaniritsidwa. Chifukwa chake, mtumwi Paulo analembera Atesalonika kuti: “Tikupemphani, . . . chifukwa cha kudza kwake kwa Ambuye wathu Yesu Kristu, ndi kusonkhana pamodzi kwathu kwa iye; kuti musamagwedezeka mtima msanga ndi kutaya maganizo anu, kapena kuwopsedwa, mwa mzimu kapena mwa mawu; kapena mwa kalata, monga wolembedwa ndi ife, monga ngati tsiku la [Yehova, NW] lafika.”—2 Atesalonika 2:1, 2.

Mawu a Paulo akusonyeza kuti Akristu ena oyambirira anakhala ndi ziyembekezo zolakwika. Ngakhale kuti Akristu ku Tesalonika angakhale asananeneretu deti lenileni la ‘kusonkhanitsidwa kwawo kwa Kristu kumwamba,’ iwo mwachionekere anaganiza kuti chochitikacho chinali pafupi. Malingaliro awo anafunikira kuwongoleredwa, ndipo kalata ya Paulo inachita zimenezi.

Enanso Afunikira Kuwongoleredwa

Monga momwe taonera m’nkhani yoyamba, zitapita zaka za zana loyamba, enanso anayembekezera kukwaniritsidwa kwa malonjezo a Mulungu panthaŵi ina yake. Ena ananeneratu kuti pakutha pa zaka chikwi, kuŵerenga kuyambira pa kubadwa kwa Yesu kapena pa imfa yake, mapeto a dziko adzafika. Koma kunenera kwawo nakonso kunakhala konama, kolakwika.

Zimenezi zikubutsa mafunso akuti: Kodi zolakwazo ponena za kukwaniritsidwa kwa malonjezo a Baibulo zatanthauza kuti malonjezowo anali onama? Kodi malonjezo a Mulungu ngodalirika? Ndipo kodi Akristu amakono alandira motani chiwongolero pa nkhaniyi?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena