Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g95 7/8 tsamba 22-25
  • Kodi Mungadalire Malonjezo a Mulungu?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mungadalire Malonjezo a Mulungu?
  • Galamukani!—1995
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kuyamba ndi Kugwa kwa Maulamuliro a Dziko
  • Mesiya Alonjezedwa
  • Palibe Deti Lodziŵika la Mapeto
  • Kuwongolera Lingaliro Kufunika
  • Maulosi Amene Anakwaniritsidwa
    Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu?
  • Kodi Maulosi Abaibulo Ngodalirika Motani?
    Nsanja ya Olonda—1993
  • Mneneri Amene Anali ku Ukapolo Anaona Masomphenya a Zimene Zidzachitike M’tsogolo
    Kodi Baibulo Lili Ndi Uthenga Wotani?
  • Ndani Angalimbane ndi Kalonga wa Akalonga?
    Samalani Ulosi wa Danieli!
Onani Zambiri
Galamukani!—1995
g95 7/8 tsamba 22-25

Kodi Mungadalire Malonjezo a Mulungu?

YEHOVA MULUNGU, Mlengi wathu, nthaŵi zonse wakhala wokhulupirika pa mawu ake. “Ndanena,” iye anatero. “Ndidzachionetsa.” (Yesaya 46:11) Atatsogolera Aisrayeli kuloŵa m’Dziko Lolonjezedwa, Yoswa mtumiki wa Mulungu analemba kuti: “Sikadasoŵa kanthu konse ka zinthu zokoma zonse Yehova adazinenera nyumba ya Israyeli; zidachitika zonse.”—Yoswa 21:45; 23:14.

Kuyambira tsiku la Yoswa mpaka kudza kwake kwa Mesiya, maulosi mazanamazana ouziridwa ndi Mulungu anakwaniritsidwa. Chitsanzo cha zimenezo ndi chija cha pamene womanganso Yeriko analandira chilango choloseredwa zaka mazana ambiri pasadakhale. (Yoswa 6:26; 1 Mafumu 16:34) China ndicho lonjezo, looneka kukhala losakwaniritsika, lakuti nzika zanjala za Samariya zidzalandira chakudya cha mwana alirenji choti adzadye patsiku lotsatira kunenerako. Mu 2 Mafumu chaputala 7, mungaŵerenge mmene Mulungu anakwaniritsira lonjezolo.

Kuyamba ndi Kugwa kwa Maulamuliro a Dziko

Mulungu anauzira olemba Baibulo kulemba zochitika zatsatanetsatane za kuyamba ndi kugwa kwa maulamuliro a dziko. Mwachitsanzo, Mulungu anagwiritsira ntchito mneneri wake Yesaya kulosera za kugwa kwa Babulo wamphamvuyo zaka pafupifupi 200 iko kusanachitike. Kwenikweni, Amedi, amene anagwirizana ndi Aperisi, anatchulidwa kuti ndiwo adzamugonjetsa. (Yesaya 13:17-19) Komabe, zodabwitsa kwambiri nzakuti, mneneri wa Mulungu anatchula kuti Koresi mfumu ya Perisiya ndiye anali kudzatsogolera pa kugonjetsako, ngakhale kuti Koresi anali asanabadwe nkomwe pamene ulosiwo unalembedwa! (Yesaya 45:1) Koma pali zambiri.

Mneneri Yesaya analoseranso mmene kugonjetsedwa kwa Babulo kudzachitikira. Iye analemba kuti madzi otetezera mzindawo, a mtsinje wa Firate, ‘adzauma’ ndi kuti “zipata [za Babulo] sizidzatsekedwa.” (Yesaya 44:27–45:1) Zochitika zatsatanetsatane zimenezi zinakwaniritsidwa, monga momwe wolemba mbiri Herodotus anasimbira.

Pamene Babulo anali ulamuliro waukulube, Mulungu anagwiritsiranso ntchito mneneri wake Danieli kunena za maulamuliro a dziko amene anali kudzamtsatira. Danieli anaona masomphenya a nkhosa yamphongo ya nyanga ziŵiri imene inagonjetsa “zilombo” zina zonse. Popanda kusiya chikayikiro ponena za amene nkhosa yamphongo ya nyanga ziŵiri inaimira, Danieli analemba kuti “ndi[y]o mafumu a Mediya ndi Perisiya.” (Danieli 8:1-4, 20) Inde, monga momwe kunaloseredwera, Amedi ndi Aperisi anakhala ulamuliro wotsatira wa dziko pamene anagonjetsa Babulo mu 539 B.C.E.

M’masomphenya ameneŵa ochokera kwa Mulungu, Danieli anaonanso “tonde . . . [wokhala] ndi nyanga yooneka bwino pakati pa maso ake.” Danieli anapitiriza kufotokoza kwake: ‘Ndinamuona wayandikira pafupi pa nkhosa yamphongo, naigunda nkhosa yamphongo, nathyola nyanga zake ziŵiri; ndipo panalibe wakupulumutsa mphongoyo. Ndipo tondeyo anadzikulitsa kwakukulu, koma atakhala wamphamvu, nyanga yake yaikulu inathyoka; ndi m’malo mwake munaphuka nyanga zinayi.’—Danieli 8:5-8.

Mawu a Mulungu samasiya chikayikiro chilichonse ponena za tanthauzo la zonsezi. Taonani malongosoledwewa: “Tonde wamanyenje ndiye mfumu ya [Girisi, NW ], ndi nyanga yaikulu ili pakati pa maso ake ndiyo mfumu yoyamba. Ndi kuti zinaphuka zinayi m’malo mwake mwa iyo itathyoka, adzauka maufumu anayi ochokera mu mtunduwu wa anthu, koma osakhala nayo mphamvu ya uja.”—Danieli 8:21, 22.

Mbiri imasonyeza kuti “mfumu ya Girisi” imeneyi inali Alexander Wamkulu. Atamwalira mu 323 B.C.E., ufumu wake potsirizira pake unagaŵidwa pakati pa akazembe ake anayi—Seleucus I Nicator, Cassander, Ptolemy I, ndi Lysimachus. Monga momwedi Baibulo linaloserera, “zinaphuka zinayi m’malo mwake.” Ndiponso monga momwe kunaloseredwera, palibe aliyense wa ameneŵa amene anali nayo mphamvu yonga ya Alexander. Zoonadi, kukwaniritsidwa kwake kwakhala kodabwitsa kwambiri kwakuti maulosi otero a Baibulo atchedwa “mbiri yolembedwa pasadakhale.”

Mesiya Alonjezedwa

Mulungu sanangolonjeza Mesiya wodzalanditsa anthu ku ziyambukiro za uchimo ndi imfa komanso anapereka maulosi ambiri odziŵikitsa Wolonjezedwayo. Tangolingalirani angapo a maulosi ameneŵa, amene Yesu sakanalinganiza kuti awakwaniritse.

Kunaloseredwa zaka mazana ambiri pasadakhale kuti Wolonjezedwayo adzabadwira ku Betelehemu ndi kuti adzabadwa kwa namwali. (Yerekezerani ndi Mika 5:2 ndi Mateyu 2:3-9; Yesaya 7:14 ndi Mateyu 1:22, 23.) Kunaloseredwa kuti adzaperekedwa ndi ndalama zasiliva 30. (Zekariya 11:12, 13; Mateyu 27:3-5) Kunaloseredwanso kuti ngakhale fupa lake limodzi silidzathyoledwa ndi kuti adzalota maere pa zovala zake.—Yerekezerani ndi Salmo 34:20 ndi Yohane 19:36, Salmo 22:18 ndi Mateyu 27:35.

Chofunika koposa nchakuti Baibulo linalosera pamene Mesiya adzabwera. Mawu a Mulungu analosera kuti: “Kuyambira kutuluka lamulo lakukonzanso, ndi kumanga Yerusalemu, kufikira wodzozedwayo, ndiye kalonga, kudzakhala masabata asanu ndi aŵiri; ndi masabata makumi asanu ndi limodzi mphambu aŵiri.” (Danieli 9:25) Malinga ndi kunena kwa Baibulo, lamulo lakukonzanso ndi kumanga malinga a Yerusalemu linaperekedwa m’chaka cha 20 cha kulamulira kwa Mfumu Aritasasta, chimene mbiri yakale imasonyeza kuti chinali chaka cha 455 B.C.E. (Nehemiya 2:1-8) Masabata 69 ameneŵa a zaka anatha patapita zaka 483 (7 x 69 = 483), mu 29 C.E. Munali m’chaka chomwecho pamene Yesu anabatizidwa ndi kudzozedwa ndi mzimu woyera, nakhala Mesiya, kapena Kristu!

Nchifukwa chake anthu m’tsiku la Yesu anali kuyembekezera Mesiya kuonekera panthaŵiyo, monga momwe wolemba mbiri Wachikristu Luka anasonyezera. (Luka 3:15) Olemba mbiri Achiroma Tacitus ndi Suetonius, wolemba mbiri Wachiyuda Josephus, ndi wafilosofi Wachiyuda Philo Judaeus nawonso anachitira umboni za chiyembekezo chimenechi. Ngakhale Abba Hillel Silver, m’buku lake lakuti A History of Messianic Speculation in Israel, akuvomereza kuti “Mesiya anali kuyembekezeredwa cha pambuyo pa zaka makumi aŵiri ndi zisanu zoyambirira za m’zaka za zana loyamba C.E.” Iye anati zimenezi zinali choncho chifukwa cha “kuŵerengera zaka kofala m’tsikulo,” komwe mbali yake inatengedwa m’buku la Danieli.

Polingalira za chidziŵitso chotero, sikungakhale kodabwitsa kuti Baibulo lingasonyezenso pamene Mesiyayo adzabweranso kudzayamba ulamuliro wake waufumu. Umboni wa zaka umene uli mu ulosi wa Danieli unasonyeza nthaŵi yeniyeniyo pamene “Wam’mwambamwamba” adzapereka ulamuliro wa dziko lapansi kwa “wolubukira anthu,” Yesu Kristu. (Danieli 4:17-25; Mateyu 11:29) Nyengo ya “nthaŵi zisanu ndi ziŵiri,” kapena zaka zisanu ndi ziŵiri zaulosi, ikutchulidwa, ndipo nyengo imeneyi yaŵerengedwa kuti inatha m’chaka cha 1914.a

Palibe Deti Lodziŵika la Mapeto

Komabe, chaka cha 1914 changokhala deti la kuyamba kwa ulamuliro wa Kristu “pakati pa adani [ake].” (Salmo 110:1, 2; Ahebri 10:12, 13) Buku la Baibulo la Chivumbulutso limasonyeza kuti panthaŵi imene ulamuliro wa Kristu udzayamba kumwamba, iye adzaponyera Satana Mdyerekezi ndi angelo ake pa dziko lapansi. Asanawononge anthu oipa auzimu ameneŵa, Baibulo limatero, iwo adzadzetsa mavuto aakulu pa dziko lapansi kwa “kanthaŵi.”—Chivumbulutso 12:7-12.

Baibulo, makamaka, silimapereka deti pamene “kanthaŵi” kameneka kadzatha ndi pamene Kristu adzachita monga Wakupha adani a Mulungu pa Armagedo. (Chivumbulutso 16:16; 19:11-21) Kwenikweni, monga momwe taonera m’nkhani yapitayo, Yesu ananena za kudikira chifukwa palibe munthu amene adziŵa deti la chochitikacho. (Marko 13:32, 33) Pamene wina apyola zimene Yesu ananena, monga momwe Akristu oyambirira anachitira ku Tesalonika ndi ena owatsatira, pamakhala kuneneratu konama, kapena kosalondola.—2 Atesalonika 2:1, 2.

Kuwongolera Lingaliro Kufunika

Mbali yomaliza ya chaka cha 1914 isanafike, Akristu ambiri anayembekezera kuti Kristu adzabwera panthaŵiyo ndi kuwatenga kumka nawo kumwamba. Chotero, m’nkhani yoperekedwa pa September 30, 1914, A. H. Macmillan, Wophunzira Baibulo, anati: “Mwinamwake imeneyi ndiyo nkhani yanga yomaliza chifukwa chakuti tidzapita kwathu [kumwamba] posachedwapa.” Mwachionekere, Macmillan anali ndi lingaliro lolakwika, koma chimenecho sindicho chinali chiyembekezo chokha chosakwaniritsidwa chimene iye ndi Ophunzira Baibulo anzake anali nacho.

Ophunzira Baibulo, odziŵika monga Mboni za Yehova chiyambire 1931, anayembekezeranso kuti m’chaka cha 1925 maulosi abwino koposa a Baibulo adzakwaniritsidwa. Iwo analingalira kuti panthaŵiyo chiukiriro cha pa dziko lapansi chidzayamba, chikumabweretsa amuna akale okhulupirika, onga Abrahamu, Davide, ndi Danieli. Posachedwapa, Mboni zambiri zinalingalira kuti zochitika zokhudza kuyamba kwa Ulamuliro wa Kristu wa Zaka Chikwi zidzayamba kuchitika mu 1975. Chiyembekezo chawocho chinazikidwa pa chidziŵitso chakuti zaka chikwi zachisanu ndi chiŵiri za mbiri ya anthu zinali kudzayamba panthaŵiyo.

Malingaliro olakwika ameneŵa sanatanthauze kuti malonjezo a Mulungu anali onama, kuti iye anaphonya. Kutalitali! Zolakwazo kapena malingaliro olakwikawo, monga momwe zinalili kwa Akristu a m’zaka za zana loyamba, anakhalapo chifukwa cha kulephera kulabadira chenjezo la Yesu lakuti, “Simudziŵa nthaŵi.” Malingaliro olakwika otulukapo sanali chifukwa cha njiru kapena kusakhulupirika kulinga kwa Kristu, koma chifukwa cha chikhumbo champhamvu chofuna kuona malonjezo a Mulungu akukwaniritsidwa m’nthaŵi yawo.

Chifukwa chake, A. H. Macmillan pambuyo pake anafotokoza kuti: “Ndinaphunzira kuti tiyenera kuvomereza zolakwa zathu ndi kupitiriza kufufuza Mawu a Mulungu kuti tipeze chidziŵitso chowonjezereka. Masinthidwe alionse amene tidzafunikira kupanga nthaŵi ndi nthaŵi pa malingaliro athu, sadzasintha makonzedwe achisomo a dipo ndi lonjezo la Mulungu la moyo wosatha.”

Inde, tingadalire malonjezo a Mulungu! Anthu ndiwo amaphonya. Chotero, Akristu oona adzapitiriza kuyembekeza momvera lamulo la Yesu. Adzadikirabe ndi kukonzekera kudza kosalephera kwa Kristu monga Wakupha woikidwa ndi Mulungu. Sadzalola kuneneratu konama kuwagoneka tulo ndi kuwachititsa kunyalanyaza chenjezo loona la mapeto a dziko.

Nanga bwanji za chikhulupiriro chakuti dzikoli lidzatha? Kodi palidi umboni wakuti zimenezi zidzachitika posachedwapa, m’moyo wanu?

[Mawu a M’munsi]

a Onani buku lakuti Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi, masamba 138-41, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

[Chithunzi patsamba 23]

Zochitika zatsatanetsatane zokhudza kugwa kwa Babulo zinaloseredwa

[Zithunzi patsamba 25]

Yesu sakanalinganiza zinthu kuti akwaniritse maulosi ambiri onena za iye

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena