Lingaliro la Baibulo
Kodi Zimene Mumakhulupirira Zili Nkanthu?
“MUNTHU AMAKONDA KUKHULUPIRIRA ZIMENE AMALINGALIRA KUKHALA ZOONA.”—FRANCIS BACON, 1561-1626 WOLEMBA NKHANI ZAZIFUPI WACHINGELEZI NDIPONSO WANDALE.
PONENA za ziphunzitso za chipembedzo, anthu ambiri amaganiza kuti malinga ngati munthu akhulupirira moonadi kuti ‘m’mwambamu muli Winawake’ nakonda munthu mnzake, zinthu zina zimene munthu amakhulupirira sizili nkanthu kwenikweni. Ena angaone zikhulupiriro zowombana zimene magulu achipembedzo amachirikiza ponena za Mulungu, chifuno chake, ndi mmene angamlambirire ndi kunena kuti kusiyanako kwangokhala kwapamwamba, monga masitayelo osiyanasiyana a zovala zimene munthu mmodzimodziyo amavala. Iwo angalingaliredi kuti awo amene amaona kusiyana kotero kukhala nkhani yaikulu aphonya kwambiri mzimu wa Chikristu choona.
Malemba amavomereza kuti si makambitsirano onse a ziphunzitso za chipembedzo amene ali oyenera. Mwachitsanzo, m’kalata yake youziridwa yomka kwa Timoteo, mtumwi Paulo anatchula za amuna ena amene anasonkhezera “makani opanda pake.” Paulo anawafotokoza kukhala ‘oyaluka pa mafunso ndi makani a mawu.’ (1 Timoteo 6:4, 5) Iye analangiza Timoteo ‘kupeŵa mafunso opusa ndi opanda malango, podziŵa kuti abala ndewu,’ ndi kulangiza mipingo ‘kusachita makani ndi mawu osapindulitsa kanthu.’ (2 Timoteo 2:14, 23) Mikangano yambiri yachipembedzo m’nthaŵi yathu imagwirizana ndi malongosoledwe ameneŵa ndipo yakhala yosapindulitsa ndi yotayitsa nthaŵi.
Komabe, kodi zimenezo zikutanthauza kuti makambitsirano onse onena za zikhulupiriro za chipembedzo ali osapindulitsa? Chabwino, ife sitingalekeretu kuvala zovala kokha chifukwa chakuti zovala zina zili zosayenera kuvalidwa, kodi tingatero? Chotero nkuoneranji nkhani ya zikhulupiriro za chipembedzo kukhala yosafunika kokha chifukwa chakuti mafunso ena onena za chiphunzitso ali osayenera kukambitsirana? Mawu a mu nkhani ya Paulo ogwidwawo amasonyeza kuti iye anaona nkhani ya ziphunzitso kukhala yofunika kwambiri. Iye anachenjeza mobwerezabwereza kuti ziphunzitso zonyenga zingapambutse munthu pa chikhulupiriro, ndipo analangiza Timoteo ‘kulamulira ena ajawa asaphunzitse kanthu kena.’ (1 Timoteo 1:3-7; 4:1; 6:3-5; 2 Timoteo 2:14-18, 23-26; 4:3, 4) Ndithudi, iye sakananena mawu amphamvu otero pokhapokhapo ngati zimene Akristu a m’zaka za zana loyamba amenewo anakhulupirira zinali zofunika.
Nangano kodi nchifukwa ninji uphungu wa kupeŵa mafunso pa chiphunzitso unaperekedwa? Chinali chifukwa chakuti m’tsiku la Paulo anthu ena—ofotokozedwa ndi iye monga “oipsika nzeru ndi ochotseka choonadi”—anali kudzutsa mikangano ya chiphunzitso makamaka ndi cholinga cha kuwononga chikhulupiriro cha ena. (1 Timoteo 6:5) Paulo analangiza Timoteo kupeŵa kokha mafunso odzutsidwa ndi anthu oipa amenewo onena za nkhani za zikhulupiriro za chipembedzo.
Kodi Zikhulupiriro Zimayambukira Khalidwe?
Komabe, ena angakayikire kaya ngati zikhulupiriro zathu zachipembedzo zili ndi chiyambukiro chambiri pa mtundu wa munthu amene ife timakhala—mikhalidwe yathu ndi mayendedwe. Iwo angaone zikhulupiriro ndi mayendedwe monga zinthu ziŵiri zosiyana ndiponso zosagwirizana, monga ngati jekete ndi buluku limene silili lake zimene zingavalidwe mosagwirizana kapena mogwirizana malinga ndi mmene wovalayo akufunira. Komabe, m’Baibulo, zikhulupiriro ndi mayendedwe zili ngati suti imene imakhala yogwirizana.
Baibulo limasonyeza za mgwirizano wachindunji pakati pa zimene timakhulupirira ndi mtundu wa munthu amene timakhala. Afarisi odzilungamitsa a m’tsiku la Yesu anali chitsanzo cha anthu okhala ndi chikhulupiriro chosochera choyambukira khalidwe. (Mateyu 23:1-33; Luka 18:9-14) Komanso, Akolose 3:10 amalangiza kuti: “[Valani umunthu, NW ] watsopano, [u]mene [u]likukonzeka watsopano, kuti akhale nacho [chidziŵitso cholongosoka, NW ] monga mwa chifaniziro cha Iye amene [anaulenga, NW ].” Onani kuti m’mavesiwo mphamvu yokhalira ndi moyo waumulungu njogwirizanitsidwa ndi kukhala ndi chidziŵitso cholongosoka cha Mulungu.
Mawu Achigiriki otembenuzidwa kuti “chidziŵitso cholongosoka,” amene amapezeka nthaŵi 20 m’Malemba Achigiriki Achikristu, amanena za chidziŵitso chenicheni, cholongosoka, kapena chokwanira. Katswiri wa Chigiriki Nathanael Culverwel akuchifotokoza monga mkhalidwe wa “kudziŵa bwino kwambiri chinthu chimene ndinangochidziŵa mwawamba; kuona bwino lomwe chinthu chimene ndinali nditaona poyamba chapatali.” Motero monga momwenso wopanga majuwelo amapendera mwala wamtengo wapatali kuti adziŵe mmene ulili ndi mtengo wake, Mkristu ayenera kupenda Mawu a Mulungu kotero kuti afikire pa chidziŵitso chenicheni, cholongosoka, ndi chokwanira cha Mulungu amene amatumikira. Zimenezi zimaphatikizapo kufikira pa kudziŵa mikhalidwe ya Mulungu, zifuno zake, miyezo yake, ndi ziphunzitso zonse zimene zimapanga “chitsanzo cha mawu a moyo”—chinthu chosiyana kwambiri ndi kungokhulupirira kuti ‘m’mwambamu muli Winawake.’—2 Timoteo 1:13.
Chitsanzo cha mtundu wa zipatso zimene zimakhalapo pamene munthu adziŵa Mulungu chapatali chalembedwa m’chaputala choyamba cha kalata youziridwa yomka kwa Aroma. Mmenemo, mukutchulidwa anthu ena amene, “ngakhale anadziŵa Mulungu, . . . anakana kukhala naye Mulungu m’chidziŵitso [cholongosoka, NW ].” Zotulukapo za zikhulupiriro zawo zolakwazo zikufotokozedwa ndi mtumwi Paulo: “Anawapereka Mulungu ku mtima wokanika, kukachita zinthu zosayenera; anadzala ndi zosalungama zonse, kuipa, kusirira, dumbo; odzala ndi kaduka, mbanda, ndewu, chinyengo, udani; akazitape, osinjirira, akumuda Mulungu, achipongwe, odzitama, amatukutuku, oyamba zoipa, osamvera [makolo awo, NW], opanda nzeru, osasunga mapangano, opanda chikondi cha chibadwidwe, opanda chifundo.”—Aroma 1:21, 28-31.
Mosakayikira, zikhulupiriro zimene anthu amenewo anali nazo zinayambukira mwachindunji kukhoza kwawo kulondola miyoyo Yachikristu. Lerolinonso, zikhulupiriro ndi mayendedwe zingayerekezeredwe ndi chovala chopanda msoko, chowombedwera pamodzi. Chotero, nkofunika kuti onse amene amafuna kupeza chiyanjo cha Mulungu atsimikizire kuti zikhulupiriro za chipembedzo chawo zilidi zoona, zozikidwa zolimba pa Mawu a Mulungu. Pakuti “[Mulungu] afuna anthu [a mtundu uliwonse, NW] apulumuke, nafike [pa chidziŵitso cholongosoka cha, NW] choonadi.”—1 Timoteo 2:4.
[Chithunzi patsamba 16]
Kudzilungamitsa kwa Mfarisi kunasonyeza zikhulupiriro zake