Achinyamata Akufunsa Kuti . . .
Kodi Ndingakhaledi bwenzi la Mulungu?
KUKHALA bwenzi la Mulungu? Kutalitali, Doris wazaka 20 akukhulupirira motero. “Ndine wosanunkha kanthu ndi wosayenerera chikondi cha munthu,” akudandaula motero mtsikana ameneyu. “Ndaleka ngakhale kupemphera kwa Yehova Mulungu chifukwa chakuti ndiganiza kuti sindili woyenera pamaso pake.” Mumtima, achichepere ena amamva kukhala osayenerera konse ubwenzi ndi Mulungu. Pamene kuli kwakuti angakonde lingaliro la kukhala bwenzi la Mulungu, amalingalira kuti zimenezo nzosatheka kwa iwo. Kodi munayamba mwalingalirapo motero?
Nthaŵi zina, zofooka za wachichepere zingampangitse kukhala ngati wosayenerera ngakhale kufikira Mulungu. Mwachitsanzo, lingalirani za Michael. Iye akuti asanadziŵe njira zaumulungu, anali “ndi malingaliro ndi ntchito zonse zauchimo, ndi zautchisi.” Komabe, zimene anadziŵa m’phunziro lake la Baibulo zinampangitsa kuzindikira za chisoni ndi kugwiritsidwa mwala kumene anadzetsa kwa Mulungu. Anafotokoza kuti: “Msonkhano uliwonse wa mpingo unandisonyeza poyera cholakwa changa china. . . . Sindinathe kuona mmene Yehova akanakhululukira machimo anga ambirimbiri amene ine mwinine sindinathe kudzikhululukira.”
M’zochitika zina, wachichepere angaone kukhala wosayenerera ubwenzi ndi Mulungu chifukwa cha zimene ena amamchitira. Mwachitsanzo, Doris, wogwidwa mawu poyambayo, anasiyidwa ali wamng’ono ndi amake. Iye anaulula kuti: “Ndiganiza kuti palibe amene amandikonda. Ngati mayi wanga enieni ndi banja anganditaye, kodi pali chiyembekezo chakuti winawake adzandisamala?” Pamene wachichepere akhala akunyozedwa ndi kuchitiridwa nkhanza kuyambira paubwana, angakhulupirire ndi mtima wonse kuti Mulungu sangamfune konse kukhala bwenzi lake.
Komanso, munthu wachichepereyo angakhale anali paubwenzi ndi Mulungu, koma chifukwa cha kufooka, nagwera m’tchimo lalikulu. Zimenezi zinachitika kwa Tracy. “Ndimachita manyazi kwambiri,” akudandaula motero wazaka 21 ameneyu, “chisoni changa ndi liwongo nzosapiririka. Ndavulaza kwambiri mtima wa Atate wanga, Yehova.”
Mwinamwake muli mu mkhalidwe wofanana ndi umenewo. Koma musataye mtima: Mulungu angakhale bwenzi lanu!
Chifukwa Chake Mungakhale Bwenzi la Mulungu
Nzoona kuti machimo angaletse munthu kukhala bwenzi la Mulungu. Mwamwaŵi, Atate wathu wachikondi anayambirira kukonza masitepe otithandiza. “Mulungu atsimikiza kwa ife chikondi chake cha mwini yekha mmenemo, kuti pokhala ife chikhalire ochimwa, Kristu adatifera ife,” mtumwi Paulo akulemba motero. (Aroma 5:8) Ndi imfa yake, Yesu analipira dipo loombolera anthu oyamikira ku ulamuliro waukulu wa uchimo. (Mateyu 20:28) Motero, mtumwiyo anawonjezera kuti: “Tinali adani a Mulungu, koma iye anatipanga kukhala mabwenzi ake mwa imfa ya Mwana wake.”—Aroma 5:10, Today’s English Version.
Achichepere ena, asanazindikire miyezo ya Yehova, monga ngati Michael wotchulidwa poyambayo, angakhale ataloŵa m’cholakwa chachikulu. Komabe, kupyolera mu nsembe ya dipo ya Yesu, munthu angakhululukidwe machimo ake akale, mosasamala kanthu kuti anali aakulu motani. Baibulo limapereka chitsimikiziro ichi chosangalatsa mtima: “Ngati tivomereza machimo athu, ali wokhulupirika ndi wolungama iye, kuti atikhululukire machimo athu, ndi kutisambitsa kutichotsera chosalungama chilichonse.” (1 Yohane 1:9) Chikhalirechobe, munthu ayenera kutenga masitepe osonyeza Mulungu kuti akuyamikira kuyeretsa kotero. Mtumwi Paulo akutchula lamulo lina limene lingagwire ntchito pano: “Musakhudza kanthu kosakonzeka,” Yehova akutero, “ndipo ine ndidzalandira inu, ndipo ndidzakhala kwa inu atate.” (2 Akorinto 6:17, 18) Nkotonthoza mtima chotani nanga kudziŵa kuti ngati munthu apatuka pa cholakwa chotero ndi kulapa moona mtima, Mulungu ali wokonzekera kumlandira m’chiyanjo Chake monga bwenzi.
Bwanji nanga za achichepere amene aleredwa mu mkhalidwe wankhanza? Zindikirani kuti Mulungu samalingalira anthu kukhala aliwongo chifukwa cha zinthu zimene anachitiridwa ndi ena mosafuna. Oterowo anangochita tsoka koma analibe liwongo la tchimolo. Kumbukiraninso kuti, kuŵerengeredwa kwanu monga munthu sikumadalira pa mmene munthu wina amakuonerani. Yehova angathe kukhala Bwenzi lanu mosasamala kanthu za mikhalidwe yanu. Maureen analeredwa ndi nakubala Wachikristu pa nyumba yachiwawa chambiri chifukwa cha atate wake auchidakwa. Komabe iye anati: “Pakati pa mkhalidwe wovuta wonsewu, ndinakhozabe kukulitsa unansi ndi Yehova. Ndinafikira pa kumdziŵa monga Uyo amene sangandisiye konse.”
Bwanji Ngati Muloŵa m’Tchimo Lalikulu?
Doug, amene analeredwa ndi makolo opembedza, analoŵa m’chisembwere ali ndi zaka 18. Zimenezi zinachitika chifukwa cha mayanjano ake oipa. “Ndinkadziŵa kuti kunali kulakwa, komano ndinkangochichitabe chifukwa chakuti ndinkafuna kusangalala,” Doug anaulula motero. Patapita nthaŵi, Doug anaona kupanda pake kwa njira yake. Anavomereza kuti: “Ndinayamba kuona kuti onse amene ndinayesa mabwenzi anga anali kungondilima pamsana kuti atenge ndalama zanga kapena kuti azisangalala.” Ndiyeno anayamba kutenga masitepe akupezanso ubwenzi ndi Yehova. Koma chopinga china chachikulu chinatsekereza kupita kwake patsogolo.
“Chimene chinachititsa kukhala kovuta kwambiri kuti ndibwerere chinali chakuti ndinadziyesa wosayenerera,” Doug anaulula motero. “Ndinaona kuti zonse zimene ndinachita zinali zoipa pamaso pa Yehova. Podziŵa za mmene iye alili wabwino ndi mmene anapiririra nane, sindinaone njira iliyonse imene akanandikhululukira nayo chifukwa chakuti ndinali woipa kwambiri.” Komabe, Doug anakhoza kuchotsa chopinga chimenechi ndi thandizo la mkulu wa mumpingo ndi mwa kulingalira mosamalitsa nkhani ya m’Baibulo ya Manase.
Kodi Manase anali yani? Mfumu ya Yuda wakale. Baibulo limasonyeza kuti Hezekiya, atate wake opembedza, anamphunzitsa kukonda Yehova. Koma atate wake atamwalira, iyeyo nakhala mfumu ali ndi zaka 12, anaganiza kuti tsopano adzachita monga momwe anafunira. Anasiya Yehova nalambira Baala. Kulambira kotero kunali kwa makhalidwe oipa kwambiri ndi kwa madzoma akugonana kosalamulirika. Manase “anachita zoipa zambiri pamaso pa Yehova kuutsa mkwiyo wake.” Kupyolera mwa omlankhulira ake okhulupirika, “Yehova analankhula ndi Manase ndi anthu ake, koma sanasamalira.” Ndiyeno, Yehova anapereka chiweruzo mwa kuchititsa Manase kutengedwa monga wandende womangidwa unyolo kumka ku Babulo.—2 Mbiri 31:20, 21; 33:1-6, 10, 11.
Pamene Manase analingalira za zochita zake zakale ndi kuziyerekezera ndi zimene anakumbukira ponena za malamulo a Yehova, anagwidwa ndi chisoni chachikulu napempha chikhululukiro. Anadzichepetsa pamaso pa Mulungu ndipo “anampempha.” Ndipo Mulungu “anapembedzeka, namvera kupembedza kwake, nambwezera ku Yerusalemu mu ufumu wake.” Inde, “Atate wa zifundo” anali wokonzekera kulola wochimwa ameneyu kuyandikira kwa iye kachiŵirinso. Atachitiridwa chifundo chotero, Manase, chifukwa cha zimene zinamchitikira tsopano “anadziŵa . . . kuti Yehova ndiye Mulungu.”—2 Mbiri 33:12, 13; 2 Akorinto 1:3.
Ngati Yehova analandira Manase kachiŵirinso, ndithudi iyeyo angalole wachichepere wopulupudza lerolino kupezanso unansi wake ndi Iye ngati wachichepereyo akusonyeza mkhalidwe wa kulapa. Doug analandira thandizo la abusa auzimu mumpingo wake. Anathandizidwa kuona bwino lomwe kuti Mulungu ‘sadzatsutsana naye nthaŵi zonse; ndipo sadzasunga mkwiyo wake kosatha.’—Salmo 103:9.
Khalanibe Bwenzi la Mulungu
Pamene Mulungu akhala Bwenzi lanu, muyenera kusamalira unansi umenewu kuti ukhalepobe. Mtsikana wina wobatizidwa wazaka 18 anakhala nakubala wosakwatiwa. Komabe, anathandizidwa kuwongolera zinthu ndi Yehova. (Onani Yesaya 1:18.) Kodi anasintha chifukwa cha chiyani? “Ndinaphunzira kuti Yehova anali Atate wachikondi ndipo osati wakupha,” iyeyo anafotokoza motero. “Ndinazindikira kuti ndinamvulaza maganizo ndi zimene ndinachita. Nkofunika kwambiri kuyang’ana kwa Mulungu monga Bwenzi, monga munthu wokhala ndi malingaliro, ndipo osangoti monga Mzimu winawake wofuna kulambiridwa koma wosakondedwa kwenikweni.” Monga Manase, iyeyo anasonkhezeredwa kulambira Yehova mokwanira. (2 Mbiri 33:14-16) Zimenezi zakhaladi chitetezero kwa iye. Iye akulangiza achichepere ena kuti: “Pitirizani kuyesayesa kutamanda Yehova ngakhale pamene zinthu zili zovuta. Mwachikondi Yehova adzawongola njira yanu kachiŵirinso.”
Nkofunikanso kuti mukhale mabwenzi ndi awo amene ali mabwenzi a Mulungu. Komabe, peŵani kotheratu awo amene mwachionekere samalemekeza malamulo aumulungu. (Miyambo 13:20) Linda wachichepere analoŵa m’chisembwere ndi mnyamata wina amene ubwenzi wake unakhala “wofunika kwambiri kuposa chilichonse.” Atachira mwauzimu, Linda anavomereza kuti: “Ukhoza kuwononga moyo wako wonse chifukwa cha kusakhala paubwenzi ndi Yehova.”
Kodi muli ndi ubwenzi wotero? Ngati si choncho, menyerani nkhondo kuti muupeze. Linda akunena mwachidule za phindu la kukhala paubwenzi ndi Mulungu mwa kuti: “Chinthu chofunika koposa m’dziko lonse ndicho unansi wabwino wa munthu mwini ndi Yehova. Palibe mnyamata kapena mtsikana kapena chinthu china chilichonse m’dzikoli chimene chili choposa zimenezo. Ngati ubwenzi ndi Yehova palibe, ndiye kuti palibe chimene chili chofunika.”
[Chithunzi patsamba 31]
Achichepere ena angaganize kuti ali osayenera kukhala bwenzi la Mulungu