Njati ya m’Madzi Yokhulupirika ndi Yothandiza
YOLEMBEDWA NDI MTOLANKHANI WA GALAMUKANI! KU BRAZIL
‘Thaŵani, thaŵani! Tiger!’ anyamatawo akufuula motero. Akuthamangira kukakwera njati zawo, akudumphira pamsana pake, ndi kuthaŵa nazo. Mwadzidzidzi, Saïdjah, mmodzi wa anyamatawo, akuphuluzika ndi kugwera m’munda wa mpunga—nyama ya tiger imene ikuyandikira. Komabe, njati ya Saïdjah yaona zimene zachitika. Ikubwerera, niima pa kabwenzi kakeko mophimba ndi thupi lake lalikululo, ndi kuyang’anizana ndi tiger ameneyo. Mphaka wamkuluyo akulumpha kuti agwire nyama yake, komano njatiyo ikuchirimika ndi kupulumutsa moyo wa Saïdjah.
NKHANI imeneyi, yolongosoledwa ndi Eduard Douwes Dekker, wolemba nkhani wa m’zaka za zana la 19 wokhala ku Asia, imasonyeza za mkhalidwe wokondeka wa njati ya m’madzi: kukhulupirika. Lerolino, kukhulupirika ndiko chizindikiro chake. “Njati ya m’madzi,” akutero katswiri wina, “ili ngati galu wa pabanja. Imakukondani kwa nthaŵi yaitali malinga ngati muisamalira bwino.”
Ana ku Asia, ngakhale a zaka zinayi, amadziŵa kuchita zimenezo. Tsiku lililonse amapititsa mabwenzi awo aakuluwo kumtsinje kumene amakawasambitsa ndipo, ndi timanja tawo, amapukuta makutu a nyamayo, maso ndi mphuno. Njatiyo, povomereza zimenezi, imafoya mokhutira. Khungu lake lakudalo limaloŵetsa kutentha kochuluka, ndipo chifukwa chakuti njatiyo ili ndi ma sweat glands ochepa kwambiri poyerekezera ndi ng’ombe, imavutika kuti idziziziritse. Mposadabwitsa kuti imakonda kumizidwa m’madzi kumeneku kwa tsiku ndi tsiku! “Itadzimiza m’madzi kapena m’matope, ikumatafuna itatsinzina pang’ono,” akutero wolemba buku wina, njatiyo “imaoneka kukhala yachimwemwe.”
Komabe, kukonda kwake madzi, kwangokhala mbali ina ya makhalidwe ake. Kodi izo zili ndi mikhalidwe ina yotani? Kodi nchifukwa ninji zili zothandiza? Choyamba, kodi zimaoneka bwanji?
Nyama Yamphamvu Yopezeka ku Mbali Zosiyanasiyana za Dziko
Njati ya m’madzi (Bubalus bubalis) imaoneka ngati ng’ombe yaikulu mopambanitsa ndipo imalemera makilogalamu 900 kapena kuposa pamenepo. Ili ndi khungu lopanda bweya wambiri longa ngati loyerera. Pokhala ndi mamita 1.8 itaima kufikira paphewa lake—ndi nyanga zotayana, msana woongoka, thupi lalitali, khosi lokhuthuka, ndi thupi lojintcha—imaonekadi kukhala yamphamvu. Miyendo yake yamphamvu ili ndi mapazi oyenerera kuyenda m’matope: mapazi aakulu onga mabokosi okhala ndi mfundo zofeŵa. Kufeŵa kotero kumakhozetsa njatiyo kupinda mapazi ake kumbuyo, kuponda pa zinthu zopinga, ndi kuyenda m’minda ya thope mmene ng’ombe zimatererekamo.
Njati za m’madzi 150 miliyoni zofuyikazo za padziko lonse zili m’mitundu iŵiri: za kudambo ndi za kumtsinje. Kuchokera ku Philippines mpaka ku India, njati za mtundu wa kudambo, za nyanga zake zazitali zogonera kumbuyo za mamita oyambira pa 1.2 mpaka pa 1.8, zimakhala zithunzithunzi zokondedwa za pa positikhadi. Pamene zisakujambulidwa, zimakhala zikuyenda m’minda ya mpunga ya matope ofika m’mawondo kapena kukoka ngolo m’njira zimene woyendetsa lole aliyense angachite nazo mantha.
Njati ya kumtsinje njofanana ndi ya kudambo. Thupi lake nlocheperapo pang’ono ndipo nyanga zake nzofupikirapo—zankhata pang’ono kapena zozyolikira pansi. Ngakhale kuti njolemera makilogalamu 900, nayonso njochititsa chidwi. Kale, Aluya amalonda anapititsa mitundu imeneyi kuchokera ku Asia mpaka ku Middle East; ndipo pambuyo pake, Asilikali a Nkhondo za Mtanda obwerera kwawo anailoŵetsa mu Ulaya, kumene ikali kubalana kwambiri.
Ngakhale kuti simudzapeza njati ya m’madzi kukhala yaliŵiro—imayenda pa liŵiro labwino la makilomita atatu pa ola—njati za kudambo ndi kumtsinje zomwe zikupezeka padziko lonse. Izo zakhala kugombe la kumpoto kwa Australia, zayenda pa mtunda pa zisumbu za Pacific, ndipo zikupanga mikwaso mu nkhalango ya Amazon. Ya Amazon?
Osamuka Omawonjezereka
Alendo ophunzira za chilengedwe oyendayenda mu Amazon kaŵirikaŵiri amafufuza ma jaguar obisala m’mbali mwa mitsinje kapena a anaconda aakuluwo mosaphula kanthu. Komabe, iwo samafunikira ma binocular, kapena ngakhale mandala, kuti aone ofika chatsopano m’nkhalangomo—njati za m’madzi—zikwizikwi.
Ngati mulingalira kuti osamuka a ku Asia ameneŵa oyendayenda mu Amazon akuwononga chilengedwe, mungalingalire zokadandaula ku polisi ya Marajó, chisumbu cha pamathiriro a mtsinje. Chenjerani! Sadzakumvetserani pamene mufika pasiteshonipo, popeza kuti ofesala wa chipani cha nthaŵiyo angakhale akufuna kuchoka kumka kukalonda misewu atakwera pamsana pa wantchito waboma wothupsayo. Inde, njati ya m’madzi—ndiponso mtundu wa kudambo! Ndi iko komwe, kodi ndani amene angafune kukapereka dandaulo limenelo?
Kwenikweni, njati ya m’madzi ndi chuma ku chigawo cha Amazon, akutero Dr. Pietro Baruselli, wantchito ya vetenale wa pa amodzi a malo aŵiri ofufuzira za njati za m’madzi ku Brazil. Anauza Galamukani! kuti njatizo zili ndi dongosolo lapamwamba logaya chakudya limene limazikhozetsa kunenepa ndi udzu umene umawondetsa ng’ombe. Alimi a ng’ombe nthaŵi zonse amafunikira kugwetsa nkhalango kuti apange malo atsopano odyera zifuyo, koma njatizo zimanenepa ndi udzu wa m’malo odyeramo omwe alipo kale. Dr. Baruselli akuti njati ya m’madzi “ingathandize kusungitsa nkhalango ya mvula.”
Komabe, kuti ikhalabe ndi moyo mu nkhalango, njatiyo iyenera kukhala yosintha—ndipo ili yotero kumene. Buku lakuti The Water Buffalo: New Prospects for an Underutilized Animal likusimba kuti m’nyengo ya mvula, pamene Amazon amiza malo odyera, njatizo zimasintha kuti zigwirizane ndi malo ake amadziwo. Pamene kuli kwakuti ng’ombe, zoikidwa m’malo ang’onoang’ono pa zitunda, zimayang’ana mosirira zili ndi njala, njati zozizingazo, zikumayenda m’madzi, zikumadya zomera zoyandama ndipo ngakhale kudya udzu wokhala pansi pa madzi. Pamene malowo aphwa, njatizo zimaoneka zili zosalala thupi monga momwe zinalili.
Mfumukazi
Njati za m’madzi zikuwandanso kumbali zina za Brazil. Chiyambire kuchiyambi kwa ma 1980 chiŵerengero chake m’dzikolo chachoka mofulumira pa mazana zikwi zinayi kufikira pa mamiliyoni angapo. Kwenikweni, njatizo zikuwonjezereka pamlingo waukulu kwambiri kuposa ng’ombe. Chifukwa ninji?
Wanderley Bernardes, wofuya njati wa ku Brazil, akulongosola kuti njati zimayamba kukwerana zili ndi zaka ziŵiri. Pambuyo pa miyezi khumi ya kukhala ndi pakati, imabala likonyani lake loyamba. Patapita miyezi 14, likonyani lachiŵiri limabadwa. Pokhala ndi malikonyani ochepa akufa ndi osagwidwa kwambiri ndi matenda, njatizo zimakhala ndi moyo wautali wobala ana. Zaka zingati? Avareji ya zaka zoposa 20. Kodi nzokhoza kubala kufikira pati?
“Ndikusonyezani,” akutero a Bernardes pamene akupita kubusa la famu yawo yazitunda ya mahekita 300, makilomita pafupifupi 160 kumadzulo kwa São Paulo. “Uyu ndi Rainha (Mfumukazi),” iwo akutero mokondwera pamene akuloza nyama imene khungu lake lokalamba ndi nyanga zobenthuka zikusonyeza umboni wa kukhalitsa kwa njatiyo. “Ali ndi zaka 25, gogo wachikazi wa ambiri, koma,” iwo akuwonjezera motero, momwetulira, “wangobala kumene likonyani lake la 20.” Pokhala ndi agogo achikazi onga Raihna, mposadabwitsa kuti akatswiri ena amaneneratu kuti m’zaka za zana lotsatiralo, chiŵerengero chachikulu koposa cha padziko cha njatizo chidzakhala chikudya udzu ku Brazil!
Talakitala ya Moyo Ndiponso ya Zambiri
Komabe, patsopano lino, anthu amanena mawuwo ponena za India, kwawo kwa njati pafupifupi theka la njati za padziko lonse. Kumeneko ndi kumaiko ena a ku Asia, mabanja osauka akumidzi ambiri amadalira pa nthaka yosabala kwenikweni, chifukwa cha njati. ‘Talakitala yawo ya moyoyo’ yosafuna dizilo kapena zitsulo zina, imakoka zinthu, kulima, kusalaza, kukoka ngolo, ndi kuchirikiza banja kwa zaka zoposa 20. “M’banja lathu,” anatero mkazi wina wokalamba wa ku Asia, “njati njofunika kwambiri kuposa ine. Pamene ndifa, adzandilira; koma ngati njati ifa, iwo angafe ndi njala.”
Kuwonjezera pa kukhala yothandiza paulimi, njatiyo ndi chakudyanso. Pafupifupi 70 peresenti ya mkaka wotulutsidwa ku India umachokera ku njati za ku Asia za kumtsinje, ndipo mkaka wa njati umafunidwa kwambiri kwakuti mkaka wa ng’ombe umakhala wovuta kuugulitsa. Kodi nchifukwa ninji ambiri amaukonda? “Mkaka wa njati,” buku lakuti The Water Buffalo: New Prospects for an Underutilized Animal, likufotokoza motero, “uli ndi madzi ochepa, uli ndi zinthu zambiri, uli ndi mafuta ambiri, uli ndi lactose yochulukirapo, ndi proteni yambiri kuposa mkaka wa ng’ombe.” Umapatsa mphamvu yochuluka, umakoma, ndipo amapangira mozzarella, ricotta, ndi tchizi china chokoma.
Bwanji nanga za nyama ya njatiyo? “Imachepa poyerekezera ndi oifuna,” akutero wofuyayo Bernardes. Pofufuza nyama imene anthu amakonda ku Australia, Venezuela, United States, ndi ku maiko ena, panapezeka kuti ambiri amakonda mnofu wa njati kuposa wa ng’ombe. Kwenikweni, anthu ambiri padziko lonse amadya nyama ya njati pamene kaŵirikaŵiri amaganiza kuti akuluma mnofu wang’ombe wochititsa nkhuli. “Kaŵirikaŵiri anthu amakayikira,” akutero Dr. Baruselli, “koma nyama ya njati njokoma, ndipo kaŵirikaŵiri yokoma kwambiri kuposa ya ng’ombe.”
Kuchepetsa Kulemera kwa Njati
Ngakhale kuti chiŵerengero cha njatizo chikukula, izo zili pamavuto. “Nkhunzi zazikulu zimene zinafunikira kukhala zobalitsira,” ikutero Earthscan Bulletin, “kaŵirikaŵiri zimasankhidwa kukhala nyama zokoka ngolo ndi kufulidwa, kapena kukaphedwa monga nyama.” Mwanjira imeneyo, mbewu zake zazikulu zikutayika, ndipo njatizo zikuchepa ukulu wake. “Zaka khumi zapitazo ku Thailand,” akutero akatswiri ena, “kunali kofala kupeza njati yolemera 1,000 kg [2,200lb]; tsopano nkovuta kupeza mitundu yolemera 750 kg [1,700lb].” Kodi vuto limeneli lingathetsedwe?
Inde, likutero lipoti lina lolinganizidwa ndi asayansi ya nyama okwanira 28, koma “kufulumira nkofunika . . . kuti tisunge ndi kutetezera mtundu wapadera wa njatiwo.” Komabe, iwo akuvomereza kuti, njati zanyalanyazidwa, koma “kudziŵa bwino njati ya m’madzi kungakhale kopindulitsa maiko ambiri osatukuka.” Iwo akunena kuti kufufuza kowonjezereka kudzathandiza kudziŵa “mikhalidwe yake yeniyeni imene idzakhalapo.”
Potsirizira pake, asayansi padziko lonse akupeza zimene alimi a ku Asia adziŵa kwa zaka mazana ambiri: Njati ya m’madzi yokhulupirikayo ndi yothandiza ili bwenzi lina labwino koposa la munthu.
[Bokosi patsamba 28]
Kulakwitsa
“AMBIRI amakhulupirira kuti,” likutero buku lakuti The Water Buffalo: New Prospects for an Underutilized Animal, “njati ya m’madzi njachipongwe ndi yaukali. Mainsaikulopediya amachirikiza lingaliro limeneli.” Komabe, kunena zoona, njati ya m’madzi yokhoza kufuyidwayo ndiyo “imodzi ya nyama zaulimi zofatsa koposa. Ngakhale kuti ili ndi maonekedwe othupsa, iyo makamaka ili ngati chiŵeto cha panyumba—yaubwenzi, yofatsa ndi yabata.” Nangano, kodi ndimotani mmene njati ya m’madzi inakhalira ndi mbiri yosaiyenererayo? Mwinamwake anthu amaganiza kuti ndi njati ya African Cape (Synceros caffer), imenedi ili yachipongwe ngakhale kuti ili wachibale wake wapatali. Komabe, njati za m’madzi sizimakwerana nazo. Zimasankha kusayandikana ndi achibale amisalawo.