Pamene Kwagwa Tsoka
M’ZAKA za zana la 20 mwachitika masoka aakulu, ndipo munthu ndiye amene wachititsa ambiri a iwo. Komabe, ena sindiye wawachititsa. Polosera za masiku athu, Yesu Kristu anati: “Mtundu umodzi wa anthu udzaukirana ndi mtundu wina, ndi ufumu ndi ufumu wina; ndipo kudzakhala njala ndi zivomezi m’malo akutiakuti.” (Mateyu 24:7) Zoona, munthu ali ndi mlandu wochititsa nkhondo ndi njala, koma sindiye amachititsa zivomezi. Mofanana ndi zimenezo, pamene kuli kwakuti zochita za munthu zachititsa kusefukira kwa madzi kowononga m’malo ena, iye sangaimbidwe mlandu wochititsa zivomezi. Ngakhale mikuntho ndi kuphulika kwa mavolokano si mlandu wa munthu.
Kaya akhale otani, masoka achilengedwe amasonyeza kuchepa kwa munthu, kupanda kwake mphamvu pamene akumana ndi mphamvu zazikulu zowopsa zachilengedwe. Nthaŵi zambiri, dzikoli, mudzi wathuwu, limamveka kukhala losungika ndi lolimba kwambiri. Koma pamene ligwedezeka ndi chivomezi, kukokololedwa ndi madzi osefukira, kapena kuwombedwa ndi mphepo zolimba zimene zimalikantha kosaleka ngati kuti pali kuphulika kwamphamvu, mkhalidwewo wa chisungiko umazimirira.
Masoka achilengedwe awononga zinthu kwambiri ndi kutayitsa miyoyo yochuluka m’zaka za zana la 20. Kodi zimenezi zikanapeŵeka? Kodi pali zilizonse zimene zingachitidwe kuchepetsa zotulukapo zake zosakazazo? Kodi ife patokha tingachitenji kuti tidzitetezere? Kodi timasoŵeratu chochita kutagwa tsoka? Kodi anthu adzavutikabe chonchi? Nkhani zotsatira zidzayankha mafunso ameneŵa.