Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g95 10/8 tsamba 8-9
  • Kodi mungathandize Motani Kholo lolera Lokha Ana?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi mungathandize Motani Kholo lolera Lokha Ana?
  • Galamukani!—1995
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Khalani Wochirikiza
  • Perekani Thandizo Labwino
  • Muziganizira Makolo Amene Sali Pabanja
    Nsanja ya Olonda—2010
  • Mabanja a Kholo Limodzi Akhoza Kupambana!
    Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja
  • Makolo Olera Ana Ali Okha Amakhala ndi Mavuto Ambiri
    Galamukani!—2002
  • Kodi Ndingathandize Motani Kholo Langa Limodzi?
    Galamukani!—1991
Onani Zambiri
Galamukani!—1995
g95 10/8 tsamba 8-9

Kodi mungathandize Motani Kholo lolera Lokha Ana?

MAKOLO olera okha ana, aamuna kapena aakazi, ayenera kulingaliridwa. Antchito yothandiza osauka a lerolino amaona kuti kuchirikiza banja la kholo limodzi nkofunika koposa.

“Mabwenzi ochirikiza, achibale amene amasamala, aphunzitsi amene amasonyeza chidwi chachikondi mwa iwo, ntchito zapadera za m’chitaganya cha anthu ndi chipembedzo zolinganizidwira mabanja otero,” akufotokoza motero akatswiri a chikhalidwe cha anthu Letha ndi John Scanzoni, “zingathandize kwambiri pa kutonthoza mtima wa makolo olera okha ana ndi ana awo panthaŵi imene afunikira kwambiri chilimbikitso.” Nangano, kodi mungawathandize motani?

Khalani Wochirikiza

Choyamba, yesani kudziŵa bwino mmene makolo olera okha ana amaonera zinthu. Dziikeni m’malo mwawo. Galamukani! anafunsa Margaret, amene ali ndi ana aŵiri, ausinkhu wa zaka 7 ndi 14. Iye anasudzulidwa zaka zisanu zapitazo ndipo akukhalabe ndi moyo bwino lomwe. Mosakayikira mudzapeza ndemanga zake kukhala zothandiza kwambiri.

Galamukani!: “Monga kholo lolera ana lokha, kodi ndi mavuto otani omwe munalimbana nawo?”

Margaret: “Choyambirira, zinali zondivuta kwambiri kuvomereza kuti ndinakhala kholo lolera ana lokha, chinthu chimene sindinalinganizepo. Ndinavutika maganizo ndi kudziŵidwa kuti ‘kholo lolera ana lokha’ chifukwa ambiri amaona mabanja a kholo limodzi monga anthu opsinjika ndi ovutika maganizo, okhala ndi ana a mbiri yoipa. Choyamba ndinakana kulangizidwa chifukwa chakuti sindinaone zinthu motero. Komano ndazindikira kuti kukhala kholo lolera ana lokha sikuli koipa nthaŵi zonse.”

Kuti muchirikize makolo olera okha ana, mufunikira kudziŵa malingaliro awo. Chitani khama kuwakomera mtima.

Galamukani!: “Simulandira ndalama zosamalirira ana kwa mwamuna wanu wakale. Kodi mumapeza motani ndalama?”

Margaret: “Ndakhala ndikudzimana kwambiri. Ndinazoloŵera kugula zovala zatsopano zovalira pamacheza. Koma, timagulabe zinthu zatsopano, komano sitimawononga ndalama zambiri monga momwe tinali kuchitira. Zoonadi, ndimafuna kuti anawo azivala bwino, chotero ndimalinganiza bwino bajeti. Ndinayamba kusunga ndalama pang’ono sabata lililonse, ndikumazipereka kwa bwenzi limene ndimadalira kuti zisungidwe bwino, chifukwa ndimadziŵa kuti ngati ndizisunga, mwina ndingazigwiritsire ntchito.”

Kodi mungakhale bwenzi lodalirika lotero limene limathandiza kholo lolera ana lokha kuchita bajeti ya ndalama zawo?

Galamukani!: “Kodi mumalimbana motani ndi kusungulumwa?”

Margaret: “Nthaŵi zonse ndimakhala wotanganitsidwa masana. Madzulo, ana akapita kukagona, kumandisautsadi kwambiri. Ndimaimbira telefoni wachibale kapena bwenzi lina. Nthaŵi zina ndimawaululira zakukhosi. Ndimalankhula zimene zachitika masana. Kungomvetseredwa ndi munthu wina kumathandiza kwambiri.”

Mwinamwake mungayambe inuyo kufikira munthu wosungulumwayo kapena kumuimbira telefoni. Pamenepo kumvetsera kwanu kungapereke chitonthozo chachikulu.

Galamukani!: “Kodi nchiyani chimene mumaona kukhala chinthu chovuta koposa monga kholo lolera ana lokha?”

Margaret: “Kulera ana kuti akhale ndi khalidwe lowongoka. Miyezo ya anthu ndi makhalidwe amene akunyonyotsoka zimachititsa anthu kukayikira chifuno changa cha kuloŵetsa makhalidwe abwino mwa ana anga.”

Kupereka kwanu chitsanzo pochirikiza miyezo yaumulungu kudzathandizadi ena kuchita chimodzimodzi.

Galamukani!: “Kulera ana aŵiri kumafuna nthaŵi yanu yochuluka. Kodi mumapeza motani nthaŵi ya kuchita zimene inu mukufuna?”

Margaret: “Ndimayesa kuwombola nthaŵi kaamba ka ine mwini. Mwachitsanzo, pamene bwenzi lina liphunzitsa anawo kuimba, zimenezo zimandipatsa ola limodzi. Ndimakhala pansi ndi kuzimitsa TV. Ndimangokhala duu, ndikumaganiza zimene ndachita patsikulo. Ndimasamala nthaŵi zonse ponena za chabwino kapena choipa, motero ndimakonda kusinkhasinkha pa zimene ndachita kuti ndione ngati ndawongolera.”

Ngati mupereka thandizo la kusamalira ana ake nthaŵi ndi nthaŵi, khololo lolera ana lokha lidzapeza nyengo zofunika za kusinkhasinkha kotero.

Perekani Thandizo Labwino

Galamukani!: “Kodi ndi thandizo lotani limene mwaona kukhala labwino koposa?”

Margaret: “Ndimakondwera pamene ndiitanidwa ndi banja lina. Pamene munthuwe uzindikira kuti ena amasamala za iwe, zimenezo zimakuthandiza kwambiri. Nthaŵi zina umaganiza kuti ndiwe wekha amene uli ndi mavuto. Ndiponso pamene wina andiyamikira chifukwa cha mmene ndikulerera ana anga, zimenezo zimandithandiza kwambiri! Ndiyeno pali mbali inanso yabwino kwambiri, monga ya kukongoletsa malo, kubzala ndi kusamalira maluŵa, kukagula zinthu. . . . Ii, ndinganenedi zambirimbiri!”

Pamene pali kholo limodzi lokha, zinthu zimatenga nthaŵi kuti zichitike ndipo zimakhala zovutirapo. Chotero musanyalanyaze kufunika kwa mphatso yanu ya nthaŵi. Ndiyo imodzi ya mphatso zamtengo wapatali kwa makolo olera okha ana.

[Chithunzi patsamba 9]

Kuti mukhale wothandiza weniweni kwa makolo olera okha ana, chezani nawo

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena