Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g96 2/8 tsamba 3-4
  • Kodi Pali Amene Angadaliridwe?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Pali Amene Angadaliridwe?
  • Galamukani!—1996
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chidaliro Chawonongedwa Kulikonse
  • Kukhulupirira Ena N’kofunika Kwambiri Kuti Munthu Akhale Wosangalala
    Nsanja ya Olonda—2003
  • Kodi Pali Amene Tingamukhulupirire?
    Nsanja ya Olonda—2003
  • Muzikhulupirira Abale Anu
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2022
  • Kodi Ndingatani Kuti Makolo Anga Azindikhulupirira?
    Zimene Achinyamata Amafunsa
Onani Zambiri
Galamukani!—1996
g96 2/8 tsamba 3-4

Kodi Pali Amene Angadaliridwe?

“Anali mmodzi wa anthu oŵerengeka osakhala a m’banja amene makolo anga anamdalira kotheratu. . . . Anadzisonyeza kukhala munthu wabwino ndi wosamala za ena amene sangachite kanthu kena kalikonse kotivulaza. . . . Anali mmodzi wa anthu oŵerengeka m’moyo wanga amene ndinamdalira kwambiri.”

UMU ndi mmene msungwana wina analongosolera za chidaliro chimene anali nacho mwa dokotala wa m’banja lawo. Mwachisoni, icho chinali chidaliro cholakwika mowopsa. Kuyambira pamene anali ndi zaka 16, dokotala ameneyu anagona msungwanayo. “Anali kundinamiza ndi kundinyenga,” msungwanayo anauza akuluakulu abwalo lamilandu, amene anapereka chilango.—The Toronto Star.

Chidaliro Chawonongedwa Kulikonse

Chidaliro, mofanana ndi duŵa lokongola komabe lofuna kusamaliridwa, chingazulidwe mosavuta ndi kuponderezedwa. Chikuwonongedwa kulikonse! Michael Gaine, amene anali mlembi wa khadinala ndi akibishopu ku England anati: “Panali nthaŵi ina pamene aliyense anali kudalira wansembe. Pamene mabanja ankaikiza ana awo m’manja mwawo kuti awayang’anire. Sindiganiza kuti zimenezo zingachitike tsopano. Kudalirana kumeneko kwatheratu tsopano.”—The Guardian Weekend.

Anthu amalonda amaberana. Osatsa malonda amanyenga ndi kulima pamsana makasitomala. Mkulu wantchito wina wouma mtima anatenga molanda ndalama za opuma pa ntchito a m’makampani ake, kubera antchito ake ndalama zawo zosungidwa. Antchito amabera owalemba ntchito awo nthaŵi zonse. Mwachitsanzo, lipoti lina linanena kuti, “magulu amalonda a ku Canada amataya ndalama zoyerekezeredwa kukhala $20 biliyoni pachaka chifukwa cha kuba kwa antchito.”—Canadian Business.

Si andale onse amene ali osadalirika. Koma malipoti onga lotsatirali samadabwitsa anthu ambiri: “Patapita milungu iŵiri pambuyo pa kuphedwa kwa mmodzi wa akazi andale wotsutsa kwambiri ku France, apolisi ayamba kuvumbula chinyengo ndi chiŵembu chaupandu wandale zimene zaphimba zochita za boma kwa nthaŵi yaitali ku gombe la ku Mediterranean.”—The Sunday Times, London.

Kaŵirikaŵiri, chidaliro chimatha m’maunansi apafupi. Amuna ndi akazi amachitirana mosakhulupirika. Makolo amachitira ana nkhanza. Ana amanamiza makolo awo. Pamene mosungiramo zolembedwa za Stasi, apolisi achinsinsi a amene kale anali East Germany, munatsegulidwa, anapezamo “njira zowanda za chinyengo” zogwiritsiridwa ntchito ndi anthu amene anaonedwa ngati mabwenzi. M’njira zocholoŵana za kupereka munthu zimenezo, lipoti lina linati, “Mphamvu ya Stasi inaloŵerera m’makalasi asukulu, pagome latchalitchi, m’chipinda chogona, ngakhale m’zipinda zoululiramo machimo.”—Time.

Ku Ireland wolemba nkhani wina analemba kuti: “Tanamizidwa, tasocheretsedwa ndipo atigwiritsa ntchito mwaphunzo ndipo aja amene tinawaika m’malo olamulira atichitira chipongwe.” (The Kerryman) Anthu ambiri samadalira aliyense chifukwa chakuti nthaŵi zambiri anamizidwa. Kodi tingachitenji kuti titsimikizire kuti chidaliro chathu sichinaikidwe pamalo olakwika? Nkhani ziŵiri zotsatira zidzayankha funso limeneli.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena