Lingaliro la Baibulo
Zimene Muyenera Kuchita Pamene Mulakwira Ena
CHINA chake chalakwika. Mukudziŵa zimenezo. Mbale wanu wachikristu sakukukondwererani. Sananene zimene zikumvutitsa, koma samakupatsani moni kaŵirikaŵiri—kokha ngati mwayamba ndinu kumpatsa moni! Kodi muyenera kumfikira kuti mudziŵe chimene chalakwika?
‘Limenelo ndi vuto lake,’ mungalingalire motero. ‘Ngati ali nane kanthu, ayenera kubwera kuti tikambirane.’ Zoonadi, Baibulo limalimbikitsa munthu amene walakwiridwa kupeza njira yopangira mtendere ndi mbale wake. (Yerekezerani ndi Mateyu 18:15-17.) Koma bwanji ponena za wolakwayo? Kodi ndi thayo lanji, ngati lilipo nkomwe, limene iye ali nalo?
Pa Ulaliki wake wa pa Phiri, Yesu anati: “Chifukwa chake ngati ulikupereka mtulo wako paguwa la nsembe, ndipo pomwepo ukakumbukira kuti mbale wako ali ndi kanthu pa iwe, usiye pomwepo mtulo wako kuguwako, nuchoke, nuyambe kuyanjana ndi mbale wako, ndipo pamenepo idza nupereke mtulo wako.” (Mateyu 5:23, 24) Onani kuti mawu a Yesu pano akunenedwa kwa wolakwa. Kodi ndi thayo lanji limene ali nalo pothetsa nkhaniyo? Kuti tiyankhe zimenezo, tiyeni tilingalire zimene mawu a Yesu anatanthauza kwa amvetseri ake achiyuda a m’zaka za zana loyamba.
“Ulikupereka Mtulo Wako Paguwa la Nsembe”
Yesu pano akupereka chithunzi chatsatanetsatane: Wolambira wachiyuda wadza ku Yerusalemu kaamba ka limodzi la mapwando apachaka. Iye ali ndi mtulo—mwachionekere nyama—wopereka nsembe kwa Yehova.a Kupereka nsembe sikunali mwambo wopanda tanthauzo ayi. Buku lakuti Judaism—Practice and Belief likufotokoza kuti: “Kusankha nyama zopereka nsembe zonenepa ndi zopanda chilema, kuziona zikuyesedwa ndi akatswiri ngati zili bwino, kupita nazo kufupi ndi guwa la nsembe lomayaka moto, kuzipereka kwa opereka nsembe, kuika manja pamutu pake, kuulula chidetso kapena liwongo, kapena kupatulira nyamayo, kudula mmero wake, kapena kungoigwiririra—zimenezi zinatsimikizira tanthauzo ndi kuwopsa kwa chochitikacho. . . . Palibe amene anakhulupirira kuti Mulungu analamula chochitika chonsecho . . . amene akanatha kuchita zimenezo popanda kutengeka mtima.”
Motero mawu a Yesu pa Mateyu 5:23, 24 akutengera amvetseri ake ku nthaŵi yodzala ndi tanthauzo ndi mantha kwa wolambira wachiyuda. Katswiri wina wa Baibulo akufotokoza chochitikachi m’njirayi: “Wolambira waloŵa m’Kachisi; iye wadutsa m’mabwalo ake ambiri, Bwalo la Akunja, Bwalo la Akazi, Bwalo la Amuna. Patsogolo pa bwalo limeneli panali Bwalo la Ansembe m’mene munthu wamba sanali kuloŵa. Wolambira akuima pa tchinga, wokonzeka kupereka nyama yake kwa ansembe; manja ake ali pa [mutu wa nyamayo] kuti aulule machimo ake.”
Panthaŵi yofunika kwambiri imeneyo, wolambira akukumbukira kuti mbale wake ali naye chakukhosi. Zingakhale kuti chikumbumtima chake chikumuuza zimenezi, kapena zingakhale kuti wadziŵa chifukwa cha mkhalidwe wa mbale wake kwa iye kuti pali kukhumudwa. Kodi ayenera kuchitanji?
“Usiye Pomwepo Mtulo Wako . . . , Nuchoke”
“Usiye pomwepo mtulo wako kuguwako,” Yesu akufotokoza motero, “nuchoke.” Chifukwa ninji? Kodi nchiyani chimene chingakhale chofunika kwambiri panthaŵiyo choposa kupereka nsembe kwa Yehova? “Nuyambe kuyanjana ndi mbale wako,” Yesu akupitiriza kufotokoza, “ndipo pamenepo idza nupereke mtulo wako.” Motero wolambirayo akusiya chopereka chake chamoyo paguwa la nsembe zowotcha ndi kupita kukafunafuna mbale wake wolakwiridwa.
Popeza lili phwando, mbale wake wolakwiridwayo mosakayikira ali pakati pa alendo obwera kudzalambira amene abwera ku Yerusalemu. Yerusalemu, wokhala ndi makwalala opapatiza ndi nyumba zambiri zokhala pafupipafupi, ali ndi chiŵerengero chokwanira bwino. Koma limeneli ndi phwando, ndipo mzinda ngwodzala ndi alendo.b
Ngakhale kuti anthu ochokera ku tauni imodzi anayenda ndi kumanga misasa pamodzi, kuyendayenda mumzinda wodzala anthu kufunafuna munthu kunafuna kuyesayesa kwamphamvu. Mwachitsanzo, mkati mwa Phwando la Misasa, alendo anali kupanga misasa mumzinda wonsewo ndi m’misewu ndi m’minda yozungulira Yerusalemu. (Levitiko 23:34, 42, 43) Ngakhale zinali tero, wolambira wachiyuda anafunikira kufunafuna mbale wake wolakwiridwa mpaka atampeza. Ndiyeno chotsatirapo chake nchiyani?
‘Yanjana ndi mbale wako,’ akunena motero Yesu. Mawu achigiriki otembenuzidwa ‘yanjana ndi mbale wako’ amachokera ku verebu yakuti (di·al·lasʹso) imene imatanthauza “‘kuchititsa kusintha, kusinthanitsa,’ motero, ‘kuyanjanitsa.’” Atayesetsa kupeza mbale wake wolakwiridwa, wolambira wachiyuda akuyanjana naye. Pamenepo, akunena motero Yesu, akhoza kubwerera ku kachisi ndi kupereka nsembe mtulo wake, popeza tsopano Mulungu adzailandira.
Motero mawu a Yesu pa Mateyu 5:23, 24 akuphunzitsa phunziro lofunika kwambiri: Nsembe imadza pambuyo pa kuyanjana, kapena mtendere. Unansi wathu ndi Mulungu umakhudzidwa mwachindunji ndi mmene timachitira ndi olambira anzathu.—1 Yohane 4:20.
Zimene Muyenera Kuchita Pamene Mulakwira Ena
Bwanji nanga mutapezeka mumkhalidwe wofotokozedwa pachiyambi pa nkhaniyi—mwadziŵa kuti mwalakwira wolambira mnzanu? Kodi muyenera kuchitanji?
Mukumagwiritsira ntchito uphungu wa Yesu, pezani njira yofikira mbale wanu. Ndi cholinga chotani? Kukamuuza kuti alibe chifukwa chokhumudwira? Kutalitali! Mwina vuto likuposa pakusamvana wamba. ‘Yanjana naye,’ anatero Yesu. Ngati nkotheka, chotsani udani mumtima mwake. (Aroma 14:19) Pofuna kuchita zimenezo, simudzafunikira kukana koma kuvomereza, kukhumudwa kwake. Mungafunikirenso kufunsa kuti, ‘Kodi ndingachitenji kuti ndiwongolere?’ Nthaŵi zambiri kupepesa koona mtima nkumene kumafunika. Komabe, nthaŵi zina, wolakwiridwayo angafune kukhala ndi nthaŵi yothetsera kukhumudwa kwake.
Koma bwanji ngati mosasamala kanthu za kuyesayesa kwanu kobwerezabwereza simunathe kudzetsapo chiyanjano? Aroma 12:18 amati: ‘Ngati nkutheka, monga momwe mukhoza, khalani ndi mtendere ndi anthu onse.’ Motero mukhoza kukhala ndi chidaliro chakuti pamene mwayesetsa mwamphamvu kupanga mtendere, Yehova adzakonda kuvomereza kulambira kwanu.
[Mawu a M’munsi]
a Nthaŵi yake yobweretsera zopereka zansembe inali mkati mwa madyerero atatu pachaka—a Paskha, Pentekoste, ndi Misasa.—Deuteronomo 16:16, 17.
b Ziŵerengero zongoyerekezera za alendo odzalambira amene anali kupita ku Yerusalemu wakale kaamba ka mapwando zikusiyana. Wolemba mbiri wachiyuda wa m’zaka za zana loyamba Josephus anayerekezera kuti pafupifupi Ayuda mamiliyoni atatu anapezeka pa Paskha.—The Jewish War, II, 280 (xiv, 3); VI, 425 (ix, 3).