Achichepere Akufunsa Kuti . . .
Kodi Ndiyenera Kuloŵa Timu Yamaseŵero?
“KODI kukhala m’timu kuli ndi ubwino wotani?” inafunsa motero nkhani ya m’magazini a Seventeen. Kuyankha kwake nkhaniyo inati: “Mumamenyera chinthu chimodzi pamodzi, motero mumakhaladi oyandikana. Mumaphunziranso mokhalira ndi anthu ena, monga mothetsera mavuto a pagulu, mokhalira wosauma khosi ndi wolingalira ena, ndi mokhalira wololera.”
Chifukwa cha zimenezi, kuseŵera maseŵero olinganizidwa kumaoneka kukhala ndi mapindu, amene ena a iwo ndi kusangalala ndi kulimbitsa thupi.a Ena amanenanso kuti kuseŵera maseŵero a timu kumathandiza munthu kukulitsa khalidwe labwino. Motero timu ina ya baseball ili ndi mawu akuti, “Khalidwe Labwino, Kulimba Mtima, Kukhulupirika.”
Vuto ndi ili, maseŵero olinganizidwa samakwaniritsa zifuno zabwino zotero nthaŵi zonse. Buku lakuti Kidsports likuti: “Nthaŵi zina achichepere otengeka maganizo msanga amaphunzira kutukwana, kunama, kuchita ndewu, kuwopseza, ndi kuvulaza ena.”
Chipambano Zivute Zitani?
Nkhani ya mu Seventeen inavomereza kuti: “Maseŵero ali ndi mbali yoipa, pamene anthu amaona chipambano kukhala chofunika kwambiri.” Zimenezi nzosiyana kwambiri ndi mawu a Baibulo akuti: “Tisakhale odzikuza, outsana, akuchitirana njiru.” (Agalatiya 5:26) Pamene kuli kwakuti mpikisano pang’ono waubwenzi ungawonjezere chikondwerero ndi chisangalalo pa maseŵero, mzimu wampikisano kwambiri ungayambitse udani—ndi kuthetsa chisangalalo cha kuseŵera.
Jon, yemwe kale anali woseŵera mpira wakusekondale, akukumbukira kuti: “Tinali ndi mlangizi wina amene analidi wotengeka maganizo; nthaŵi zonse ankatikuwira . . . Ndinkachita mantha kupita kokayeseza. . . . Ndinali kumva ngati kuti ndinali m’ndende yachibalo.” Pamene kuli kwakuti si alangizi onse amene amatukwana, ambiri amagogomezera kwambiri pa chipambano. Wolemba wina anati: “Amaseŵera ambiri . . . amafika poti chisangalalo cha kupikisana chimaphimbidwa ndi chikhumbo chosalamulirika chofuna kupambana.” Kodi nchiyani chimene chingatulukepo?
Science News inalemba za kufufuza kumene kunavumbula kuti pakati pa oseŵera mpira ndi basketball akukoleji, “12 peresenti anati amavutika pa mbali ziŵiri mwa zisanu izi: kupsinjika maganizo, kusapeza bwino m’thupi, kuvutika kupeŵa anamgoneka kapena moŵa, kuzunzika maganizo ndi kuchitiridwa nkhanza, ndi kusachita bwino m’maphunziro.” Pankhani imodzimodziyo, buku lakuti On the Mark likuti: “Pafupifupi aliyense amene ali m’maseŵero olinganizidwa angavomereze kuti muli vuto lalikulu la anamgoneka m’maseŵero kwa aliyense woloŵetsedwamo.”
Kutaya Makhalidwe Abwino
Kufunitsitsa kupambana kungachititsenso wamaseŵero wachichepere kuswa miyezo yabwino ya chilungamo ndi kuona mtima. Buku lakuti Your Child in Sports limati: “M’zochitika zamakono za maseŵero, kupambana si kwabwino chabe; ndiko chinthu chokha. Kulephera si koipa chabe, nkosakhululukika.”
Choonadi china chopweteka ndi ichi: Nthaŵi zambiri alangizi a maseŵero amakakamiza kwambiri oseŵera kuti azivulaza opikisana nawo. Nkhani ina mu Psychology Today inati: “Kuti useŵere bwino m’maseŵero, uyenera kukhala woipa. Kapena tinene kuti nzimene amaseŵero, alangizi a maseŵero, ndi okonda kupenyerera maseŵero ambiri amakhulupirira.” Katswiri wina wampira akufotokoza umunthu wake wamasiku onse kukhala “wolankhula mofatsa, wolingalira ena ndi waubwenzi.” Koma pabwalo la maseŵero, amasanduka kotheratu. Pofotokoza umunthu wake ngati ali m’maseŵero, iye akuti: “Panthaŵiyo ndimakhala wovuta ndi wanjiru. . . . Ndimakhaladi woipa. Sindimakhala ndi ulemu uliwonse kwa munthu amene ndikufuna kumenya.” Alangizi a maseŵero kaŵirikaŵiri amalimbikitsa kukhala ndi mkhalidwe wotere.
Baibulo limalimbikitsa Akristu kuti: ‘Valani mtima wachifundo, kukoma mtima, kudzichepetsa, chifatso, ndi kuleza mtima.’ (Akolose 3:12) Kodi mungakulitse mikhalidwe imeneyi ngati masiku onse mumalimbikitsidwa kwambiri kuvulaza, kutswanya, ndi kulemaza wopikisana naye? Robert wazaka 16 akuvomereza kuti: “Ndinaseŵerapo maseŵero olinganizidwa. Sumalingalira kuti wavulaza yani malinga inu mwapambana.” Tsopano popeza ali Mkristu wobatizidwa, malingaliro ake asintha. Iye akuti: “Sindingabwererenso ku zimenezo.”
Chizoloŵezi Chathupi Kapena Chivulazo Chathupi?
Zimenenso siziyenera kunyalanyazidwa ndizo ngozi zakuthupi. Zoona, maseŵero amakhala ndi ngozi ngakhale pamene akuseŵeredwa ndi mabwenzi kokha kaamba ka kusangalala. Koma ngozizo zimakula pamene achichepere amalangizidwa kuti aziyesetsa kuseŵera ngati akatswiri.
Buku lakuti Your Child in Sports limati: “Akatswiri amaseŵero amavulala. Koma ngaluso kwambiri, ali olimba mwakuthupi, ali akulu okhwima amene amakonzekera kukhala pangozi yakuvulala ndipo amapatsidwa malipiro abwino kwambiri chifukwa cha kuchita zimenezo. Ndiponso, nthaŵi zambiri amakhala ndi maphunziro abwino kwambiri, aukatswiri koposa, ziŵiya zabwino koposa, ndi chisamaliro cha mankhwala chabwino kwambiri. . . . Ana a sukulu alibe zinthu zimenezo.” Akristu amauzidwa ‘kupereka matupi awo nsembe yamoyo, yopatulika, yokondweretsa Mulungu.’ (Aroma 12:1) Kodi simuyenera kulingalirapo mosamalitsa pa kuika thupi lanu pangozi zosafunika kapena zopanda nzeru?
Mbali Zina Zofunika Kulingalirapo
Ngakhale pamene ngozi zokhudza thanzi zioneka kukhala zazing’ono, maseŵero olinganizidwa amakhalabe odya nthaŵi. Nthaŵi zakuyeseza sizimangokuchepetserani nthaŵi yanu ya moyo watsiku ndi tsiku koma zimatenganso nthaŵi yanu yaikulu imene mungaiike padera kaamba ka phunziro ndi homuweki. Science News inanena kuti amaseŵero akukoleji amakhala ndi “magiredi apansi pang’ono” kuposa ophunzira ena amene amatengamo mbali m’zochitika za kunja kwa kalasi. Chofunika kwambiri, mudzaona kuti kuseŵera m’timu kumapangitsa kukhala kovuta kulondola zimene Baibulo limatcha “zinthu zofunika kwambiri”—zinthu zauzimu. (Afilipi 1:10, NW) Dzifunseni kuti, ‘Kodi kuloŵa timu kudzafuna kuti ndiziphonya misonkhano yachikristu, kapena kodi kudzandilepheretsa kutengamo mbali mokwanira m’ntchito yolalikira?’
Taganiziraninso mosamalitsa za zimene zingatsatirepo chifukwa chothera nthaŵi yaikulu ndi achichepere ndi achikulire amene malingaliro awo amasiyana ndi anu pa zamakhalidwe abwino, malankhulidwe abwino, kapena kupikisana. Ndiponso, Baibulo limanena kuti “mayanjano oipa aipsa makhalidwe okoma.” (1 Akorinto 15:33) Mwachitsanzo, talingalirani za nkhani ya patsamba la Op-Ed la mu The New York Times imene inati: “Chipinda chosinthira zovala . . . ndicho malo mmene amuna amakambitsirana za matupi a akazi m’mawu okuluŵika odzutsa chilakolako cha kugonana, mmene amadzitama ponena za chipambano chawo pa [kugonana], ndi kuseka ponena za kumenya akazi.” Kodi mkhalidwe wanu wauzimu ungakhale wotani ngati mwasankha kumakhala m’malo otero?—Yerekezerani ndi Yakobo 3:18.
Kupanga Chosankha Chanzeru
Kodi mwakhala mukulingalira zokaloŵa timu yamaseŵero? Ndiye mwinamwake zimene zanenedwazi zidzakuthandizani kuŵerengera mtengo wa kuchita motero. Lingalirani za chikumbumtima cha ena pamene mupanga chosankha chanu. (1 Akorinto 10:24, 29, 32) Komabe, palibe malamulo olimba amene angapangidwe, popeza mikhalidwe imasiyana dziko lonse lapansi. Kumalo ena ophunzira amafunikira kutengamo mbali m’maseŵero. Koma ngati mukukayikira, kambitsiranani ndi makolo anu kapena Mkristu wokhwima.
Achichepere ambiri achikristu apanga chosankha cholimba cha kusaseŵera maseŵero a timu. Zimenezi nzovuta ngati ndinu wamaseŵero ndipo mumasangalaladi ndi maseŵero! Kukakamizidwa ndi aphunzitsi, alangizi a maseŵero, ndi makolo kungawonjezere vutolo. Jimmy wachichepere akuvomereza kuti: “Kumandivuta kusachita maseŵero. Atate wanga amene saali wokhulupirira anali amaseŵero kwambiri m’masiku awo akusekondale. Nthaŵi zina kumakhala kovuta kusaloŵa timu.” Ngakhale zili choncho, chichirikizo cha makolo okhulupirira ndi Akristu okhwima mumpingo chingakuthandizeni kwambiri kumamatira ku chosankha chanu. Jimmy akuti: “Ndikuyamikira amayi. Nthaŵi zina ndimachita tondovi chifukwa cha chikhumbo chachikulu cha kufuna kuseŵera maseŵero. Koma nthaŵi zonse amandikumbutsa za zonulirapo zanga zenizeni m’moyo.”
Maseŵero a timu angaphunzitse oseŵera kugwirizana ndi kuthetsa mavuto. Koma pali mwaŵi waukulu wa kuphunzira zinthu zimenezi mwa kugwira ntchito pamodzi ndi mpingo wachikristu. (Yerekezerani ndi Aefeso 4:16.) Maseŵero a timu angakhalenso chinthu chosangalatsa, koma simufunikira kukhala m’timu kuti musangalale nawo. Maseŵero ena angachitidwe ndi mabwenzi achikristu kuseri kwa nyumba kapena kumalo oseŵerera a kumeneko. Pamene banja lipita kwina kokacheza mwaŵi winanso ungapezeke wa maseŵero abwino. “Kulidi kwabwino kuseŵera ndi ena a mumpingo,” akutero Greg wazaka 16. “Mungoseŵerera kuti musangalale, ndiponso ukuseŵera ndi mabwenzi ako!”
Zoonadi, maseŵero a kuseri kwa nyumba mwachionekere sadzapereka konse chisangalalo chonga cha kukhala m’timu imene yapambana. Komabe, musaiŵale konse kuti pansi pamikhalidwe yabwino kwambiri “chizoloŵezi cha thupi chipindula [kokha] pang’ono, koma chipembedzo [“kudzipereka kwaumulungu,” NW] chipindula zonse.” (1 Timoteo 4:8) Kulitsani kudzipereka kwaumulungu, ndipo mudzakhaladi wopambana pamaso pa Mulungu!
[Mawu a M’munsi]
a Onani “Achichepere Akufunsa Kuti . . . Maseŵero a Timu—Kodi Ali Bwino kwa Ine?” m’kope la March 8, 1996.
[Mawu Otsindika patsamba 20]
“Tinali ndi mlangizi wina amene analidi wotengeka maganizo; nthaŵi zonse ankatikuwira . . . Ndinkachita mantha kupita kokayeseza”
[Chithunzi patsamba 21]
Nthaŵi zonse alangizi a maseŵero amagogomezera kupambana—ngakhale ngati zimenezo zingavulaze ena