Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g96 4/8 tsamba 9-11
  • Kodi Mapeto a Chipembedzo Ayandikira?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mapeto a Chipembedzo Ayandikira?
  • Galamukani!—1996
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Masiku Otsiriza a Chipembedzo?
  • Kukhutiritsa Njala Yauzimu
  • Chipembedzo Choona Nchofunika Kuposa Kale
  • Kumasuka ku Chipembedzo Chonyenga
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Kulondola Chipembedzo Choyera Kaamba ka Chipulumutso
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Gawo 24: Tsopano ndi kwamuyaya—Kukongola Kwamuyaya kwa Chipembedzo Chowona
    Galamukani!—1990
  • Kodi Mwapeza Chipembedzo Cholondola?
    Nsanja ya Olonda—1994
Onani Zambiri
Galamukani!—1996
g96 4/8 tsamba 9-11

Kodi Mapeto a Chipembedzo Ayandikira?

“Dziko lapansi lidzadzala ndi odziŵa Yehova, monga madzi adzaza nyanja.”

YESAYA, MNENERI WACHIISRAYELI WA M’ZAKA ZA ZANA LA 8 B.C.E.

NDIMO mmene mneneri wachihebri Yesaya analoserera kuti tsiku lina aliyense padziko lapansi adzagwirizana m’kulambira Mulungu Wamphamvuyonse. Komabe, lerolino, chiyembekezo chimenecho chingaonekere ngati chapatali kwambiri kuposa ndi kalelonse.

Mwachitsanzo, kuchiyambi kwa zaka za zana lino, magulu osintha zinthu achikomyunisti ku Russia anakhulupirira kuti kuwonongedwa kwa chipembedzo kunali sitepe yofunika pa kumasula anthu osauka. Chiphunzitso chokana Mulungu, iwo anatero, ‘chidzamasula anthu wamba ogwira ntchito pa mtolo wa tsankhu ndi zinyengo zapitazo.’ Podzafika 1939, Stalin anali atachepetsa chiŵerengero cha matchalitchi a Orthodox ololedwa mu Soviet Union kufika pa 100, poyerekezera ndi oposa 40,000 amene analiko 1917 asanafike.

Nayenso Hitler anaona chipembedzo monga chopinga njira yake ya kutenga ulamuliro wonse. “Munthu angangokhala Mkristu kapena Mjeremani. Sangakhale ziŵiri zonsezo,” anatero panthaŵi ina. Iye analinganiza zothetsa mwapang’onopang’ono mitundu yonse ya kulambira imene sanathe kuilamulira. Ali ndi cholinga chimenecho, Anazi anayambitsa mapemphero awoawo onga achipembedzo, mapwando, maubatizo, ndipo ngakhale mapemphero oikira maliro. Hitler anali mesiya wawo, ndipo dziko lawo monga mulungu wawo. Nkhanza iliyonse inali yotheka ngati chinali chifuniro cha Hitler.

Masiku Otsiriza a Chipembedzo?

Stalin kapenanso Hitler sanapambane pa mkupiti wawo wa kuletsa chipembedzo. Koma tsopano, mphwayi ndi imene ikuonekera kukhala ikutenga malo a nkhanza. Kwa ophunzira Baibulo zochitika zimenezi sizimawadabwitsa. Mtumwi Paulo anauza Timoteo kuti mu “masiku otsiriza” anthu adzakhala “okonda zokondweretsa munthu, osati okonda Mulungu.”—2 Timoteo 3:1-4.

Kodi Baibulo limaphunzitsa kuti “masiku otsiriza” ameneŵa odziŵika chifukwa cha mphwayi ya chipembedzo, adzatsogolera ku imfa ya zipembedzo zonse? Ayi. M’malo mwa kuneneratu za mapeto a zipembedzo zonse, Baibulo limalongosola kuti chipembedzo chonyenga—chimene chapatsidwa dzina lophiphiritsira lakuti Babulo Wamkulu—chidzatha.a Buku la Chivumbulutso limati: “Mngelo wolimba ananyamula mwala, ngati mphero yaikulu, naiponya m’nyanja, nanena, Chotero Babulo, mudzi waukulu, udzapasulidwa kolimba, ndipo sudzapezedwanso konse.”—Chivumbulutso 18:21.

Komabe, kuzimiririka kwa chipembedzo chonyenga sikudzabweretsa dziko la anthu osapembedza Mulungu. M’malo mwake, Salmo 22:27 limalosera kuti: “Malekezero onse a dziko lapansi adzakumbukira nadzatembenukira kwa Yehova: ndipo mafuko onse a amitundu adzagwadira pamaso panu.” Tangoganizani za nthaŵiyo pamene “mafuko onse a amitundu” adzagwirizana pamodzi m’kulambira Mulungu mmodzi woona! Pansi pa ulamuliro wa Ufumu wa Mulungu, lonjezo lapadera limenelo lidzakwaniritsidwa mwaulemerero. (Mateyu 6:10) Pamene nthaŵiyo ifika, chipembedzo—chipembedzo choona—chidzakhala chofunika kwambiri. Koma bwanji nanga pa tsopano lino?

Kukhutiritsa Njala Yauzimu

Njala yauzimu imene ili yofala ku Ulaya lerolino ikufanana ndi mkhalidwe umene unali mu Ulamuliro wa Roma m’zaka za zana loyamba. Wolemba mbiri Will Durant akufotokoza mmene Chikristu cha m’zaka za zana loyamba chinakhutiritsira bwino lomwe njala yauzimu yapanthaŵiyo kuti: “Mu mkhalidwe wopanda makhalidwe wa chikunja chomafa, mu mkhalidwe wa chistoiki chosalimbikitsa ndi kuipitsa maganizo kwa chiepekureya, m’dziko lonyansidwa ndi nkhalwe, nkhanza, kupondereza, ndi chiwerewere, mu ulamuliro wamphwayi umene unaoneka kukhala wosafuna kuchita zinthu mwachamuna kapena milungu yankhondo, chinadzetsa mkhalidwe watsopano wa ubale, kukoma mtima, kulongosoka, ndi mtendere.”

Njala ya makhalidwe ndi yauzimu mwa anthu m’nthaŵi yathu ingakhutiritsidwe ndi uthenga wamphamvu umodzimodziwo umene unalalikidwa mu Ulamuliro wa Roma wonse ndi Akristu oyambirira. Ndipo pali anthu omvetsera. Azungu ambiri, ngakhale kuti amaoneka ngati osapembedza, amalingalirabe kuti Mulungu amachita mbali yofunika m’moyo wawo. Angakhale asakufika kumapemphero amwambo atchalitchi, komabe ena akhutiritsa njala yawo yauzimu kumalo ena.

Juan José, mnyamata wina wa ku Palma de Mallorca, Spain, anaphunzira pa sukulu ya Katolika ndi kutumikira monga mnyamata wa kuguwa kufikira pamene anali ndi zaka 13. Anali kupita ku Misa Lamlungu lililonse ndi a m’banja lakwawo, komano anasiya kupita kutchalitchi pamene anakhala wosinkhukirapo. Chifukwa ninji? “Choyamba, kupita ku Misa kunandigwetsa ulesi,” akulongosola motero Juan José. “Ndinaloŵeza mapemphero ake pamtima. Zinthu zonse zinkaoneka ngati kungobwerezabwereza zimene ndinamvapo kale. Ndiponso, wansembe wathu anachitira nkhanza anyamata a kuguwafe. Ndipo ndinaganiza kuti nkulakwa kuti anthu osauka azilipira wansembe kuti awatsogolere m’mapemphero apamaliro.

“Ndimakhulupirirabe Mulungu, koma ndinalingalira kuti ndidzamtumikira m’njira yangayanga, osati m’tchalitchi. Ine pamodzi ndi kagulu ka anzanga, tinayesa kusangalala ndi moyo monga momwe tinathera. Ndiyesa kuti munganene kuti kusanguluka kunakhala chinthu choyamba m’moyo wanga.

“Koma pamene ndinali ndi zaka 18, ndinayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Kodi anandipatsanji chimene sindinapeze m’tchalitchi? Chikhulupiriro chenicheni chozikidwa pa Baibulo m’malo mwa miyambo ndi ‘zinsinsi’ zimene sindinathe kuzimvetsa. Komabe, chikhulupiriro changa chatsopanocho chinatanthauza masinthidwe aakulu kwa ine. M’malo mothera kutha kwa mlungu kulikonse ndikumalinganiza mapwando ku makalabu a disco, ndinayamba kumka kunyumba ndi nyumba kuti ndikauze anansi anga za chikhulupiriro changa chatsopano. Kukhala wotanganitsidwa m’kuthandiza ena kunapereka tanthauzo pa moyo wanga. Kwa zaka zisanu ndi ziŵiri zapitazo, ndakhala mtumiki wanthaŵi yonse wa Mboni za Yehova.”

Si achichepere okha amene akufuna kukhutiritsa njala yawo yachipembedzo. Mkazi wina wokalamba, Antonia, wa ku Extremadura, Spain, anathera nthaŵi yochuluka ya moyo wake “akumafunafuna Mulungu,” monga momwe akunenera. Pa zaka za uchichepere wake, ankapita ku Misa tsiku lililonse ndipo potsirizira pake analoŵa pa mishoni ya Katolika, popeza ankakhulupirira “kuti ngati Mulungu sakhoza kupezeka pamishoni, sangapezekenso kwina.” Koma patapita zaka zitatu anachoka pamishonipo, ali wokhumudwa kwambiri ndi wanjala kuposa kale.

Potsirizira pake, pamene anali m’zaka zake za m’ma 50, anakhala mmodzi wa Mboni za Yehova. “Ndinali wachimwemwe pamene Mboni zinandifikira ndi kuyankha mafunso anga kuchokera m’Baibulo langa,” iye akufotokoza motero. “Kuyambira pamene ndinakhala mmodzi wa Mboni za Yehova, moyo wanga wakhala ndi chifuno. Ndili ndi mavuto, koma ndimatha kulimbana nawo chifukwa chakuti tsopano ndapeza Mulungu woona.”

Si zokumana nazo ziŵiri zokhazi zimene zilipo. Pokana chipembedzo, ziŵerengero za anthu zomakula zikugwirizana ndi Mboni za Yehova ndipo apeza kuti kuchita mogwirizana ndi chikhulupiriro chawo ndi kuchilalikira kwa ena kumapereka tanthauzo ndi chifuno pa moyo wawo.

Chipembedzo Choona Nchofunika Kuposa Kale

Ngakhale kuti tikukhala mu nthaŵi pamene ambiri akukana chipembedzo, kungakhale kupusa kunena kuti zipembedzo zonse nzosayenera. Zoona, m’zaka za zana la 20 lino, anthu akutaya miyambo yopanda pake ndi yachikale ndi ziphunzitso zopanda malemba, ndipo amanyodola kupita kutchalitchi kaamba ka kukaonekerako. Kwenikweni, Baibulo limanena kuti tipeŵe kotheratu chipembedzo chonyenga. Mtumwi Paulo ananeneratu kuti mkati mwa “masiku otsiriza,” anthu ena ‘adzakhala nawo maonekedwe a chipembedzo, koma mphamvu yake adzaikana.’ Anthu amenewo ali ndi maonekedwe onga achipembedzo, koma khalidwe lawo limawatsutsa. Kodi tiyenera kuchita motani ndi chinyengo chachipembedzo chotero? “Kwa iwonso udzipatule,” analangiza motero Paulo.—2 Timoteo 3:1, 5.

Komanso Paulo ananena kuti “chipembedzo . . . chipindulitsa kwakukulu.” (1 Timoteo 6:6) Paulo sanali kungonena za chipembedzo wamba. Liwu lachigiriki lotembenuzidwa pano kukhala “chipembedzo” linali lakuti eu·seʹbei·a, limene limatanthauza kuti “kudzipereka kapena kuchitira ulemu Mulungu.” Chipembedzo choona, kudzipereka kwaumulungu kodalirika, ‘kumakhala nalo lonjezano la ku moyo uno, ndi la moyo ulinkudza.’—1 Timoteo 4:8.

Monga momwe zitsanzozo zikusonyezera, chipembedzo choona chingapereke tanthauzo pa moyo wathu ndi kutithandiza kuyang’anizana ndi mavuto molimbika. Ndiponso, chipembedzo choona chimapereka chitsimikiziro cha mtsogolo mosatha. Mtundu umenewo wa kulambira uli woyenera kutsatiridwa, popeza kuti timatsimikiziridwa kuti potsirizira pake ‘udzadzaza dziko lapansi.’b (Yesaya 11:9; 1 Timoteo 6:11) Ndithudi, inoyo ndiyo nthaŵi pamene chipembedzo choona chili chofunika kwambiri kuposa kale.

[Mawu a M’munsi]

a Baibulo limagwiritsira ntchito mzinda wakale wa Babulo kukhala wophiphiritsira ulamuliro wapadziko lonse wa chipembedzo chonyenga, pakuti m’mzindawu ndimo munachokera malingaliro achipembedzo osiyanasiyana osakhala a m’malemba. M’zaka mazana zapitazi malingaliro ameneŵa achibabulo analoŵerera m’zipembedzo zazikulu zadziko.

b Onani mutu 5 wakuti “Kodi Mulungu Amavomereza Kulambira kwa Yani?” wa buku la Chidziwitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha, kaamba ka nkhani ya mmene mungadziŵire chipembedzo choona, lofalitsidwa mu 1995 ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

[Bokosi/Zithunzi patsamba 10]

Nkhani ya Nyumba Ziŵiri

Spain ngwodzala ndi nyumba zachipembedzo, komano changu chimene panthaŵi ina chinachirikiza kumangidwa kwa matchalitchi aakulu okwera mtengo chichita ngati chatha. Mwachitsanzo, ku Mejorada del Campo, kunja kwa Madrid, kukumangidwa tchalitchi cha Katolika chokongola. Justo Gallego Martínez, yemwe kale anali mmonki wa Benedict, anayamba ntchitoyo zaka pafupifupi 20 zapitazo. Koma nyumbayo ikali yosatha. Martínez, womanga nyumba yekhayo, tsopano ali m’zaka zake za m’ma 60, chotero zikuoneka ngati tchalitchicho sichidzatha. Komabe, kumpoto kwake pamtunda wa makilomita 300, kunachitika nkhani inanso.

“Chikhulupiriro Chisuntha Mapiri” ndimo mmene nyuzipepala yakumaloko inafotokozera kumangidwa kwa Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova kwa masiku aŵiri ku Martos, Jaén, Spain. “Kodi zikutheka bwanji,” nyuzipepala yakumaloko inafunsa motero, “kuti m’dziko lilipoli lozikika pa dyera, antchito odzifunira akumadera osiyanasiyana [a Spain] ayende ulendo mopanda dyera kumka ku Martos kuti akamange nyumba imene yaposa zonse pa kumangidwa kwake kofulumira, kupanda cholakwika, ndi dongosolo?” Poyankha funsoli, nkhaniyo inagwira mawu a wantchito wodzifunira wina kuti: “Zakhala zotheka makamaka chifukwa ndife anthu ophunzitsidwa ndi Yehova.”

[Zithunzi patsamba 10]

Mejorada del Compo

Nyumba ya Ufumu ku Martos

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena