Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g96 4/8 tsamba 16-17
  • Kodi Akristu Oona Angayembekezere Chitetezero cha Mulungu?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Akristu Oona Angayembekezere Chitetezero cha Mulungu?
  • Galamukani!—1996
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chifuno cha Chitetezero cha Mulungu
  • Chogwiritsiridwa Ntchito pa Kukwaniritsidwa kwa Chifuno cha Mulungu
  • Kodi Mulungu Ngwouma Mtima?
  • Mphamvu Zoteteza—“Mulungu Ndi Pothawira Pathu”
    Yandikirani Yehova
  • Kodi Akristu Ayenera Kuganiza Kuti Mulungu Azingowateteza?
    Galamukani!—2002
  • Jehova Mulungu wa Chifuno
    Nsanja ya Olonda—1994
  • “Osaphunzira Ndiponso Anthu Wamba”
    ‘Kuchitira Umboni Mokwanira za Ufumu wa Mulungu’
Onani Zambiri
Galamukani!—1996
g96 4/8 tsamba 16-17

Lingaliro la Baibulo

Kodi Akristu Oona Angayembekezere Chitetezero cha Mulungu?

KUTI akapereke katundu wachithandizo kwa olambira anzawo, Akristu, atapemphera, anayenda m’galimoto zondondozana kupyola m’dera lankhondo mmene akanaphedwa. Anayenda bwino lomwe, modabwitsa magulu omenyana. Kodi mngelo wa Mulungu anawatetezera?

Akristu aŵiri okwatirana amene anatumikira zaka zambiri anaphedwa pamene ndege inagwera kumene anali kulalikira kukhomo ndi khomo. Kodi nchifukwa ninji mngelo wa Mulungu sanatsogolere iwo kapena ndegeyo kwina panyengo imeneyo?—Yerekezerani ndi Machitidwe 8:26.

Poyerekezera zochitika zimenezi, tingafunse kuti: Kodi nchifukwa ninji Akristu ena amafa pamene akuchita chifuniro cha Mulungu, pamene kuli kwakuti ena, amene kaŵirikaŵiri amapezeka m’mikhalidwe yangozi kwambiri, amapulumuka? Kodi Akristu angayembekezere chitetezero cha Mulungu, makamaka mu “masiku otsiriza” oŵaŵitsa ano?—2 Timoteo 3:1.

Chifuno cha Chitetezero cha Mulungu

Yehova Mulungu walonjeza kudalitsa ndi kutetezera anthu ake. (Eksodo 19:3-6; Yesaya 54:17) Anachita motero mwapadera m’zaka za zana loyamba, pamene mpingo wachikristu unali paubwana wake. Panali zozizwitsa zambiri za mitundu yonse. Yesu anachulukitsa chakudya nadyetsa zikwi za anthu; iyeyo ndi otsatira ake anachiritsa mtundu uliwonse wa matenda ndi zofooka, anatulutsa mizimu mwa anthu ogwidwa ndi ziŵanda, ndipo ngakhale kuukitsa akufa. Pansi pa chitsogozo cha Mulungu mpingo wongobadwa kumenewo unakula ndipo unalimba. Komabe, ngakhale kuti mwachionekere Mulungu anauchirikiza, Akristu ambiri okhulupirika anafa imfa imene tingatche kuti yofulumira.—Yerekezerani ndi Salmo 90:10.

Lingalirani za Yakobo ndi Yohane, ana a Zebedayo. Atasankhidwa kukhala atumwi, iwowo, limodzi ndi Petro, anali pakati pa mabwenzi a Yesu apamtima.a Koma Yakobo anafera chikhulupiriro m’chaka cha 44 C.E., pamene kuli kwakuti mbale wakeyo Yohane anakhala ndi moyo kufikira kumapeto kwa zaka za zana loyamba. Aŵiri onsewo mwachionekere anali kuchita chifuniro cha Mulungu. Kodi nchifukwa ninji Yakobo analoledwa kufa, pamene Yohane anakhalabe ndi moyo?

 Mulungu Wamphamvuyonse ndithudi anali wokhoza kupulumutsa Yakobo. Zoonadi, kufera chikhulupiriro kwa Yakobo kutachitika, Petro analanditsidwa ku imfa ndi mngelo wa Yehova. Kodi nchifukwa ninji mngelo sanalanditse Yakobo?—Machitidwe 12:1-11.

Chogwiritsiridwa Ntchito pa Kukwaniritsidwa kwa Chifuno cha Mulungu

Kuti timvetse chifukwa chimene chitetezero cha Mulungu chimaperekedwa, tiyenera kuzindikira kuti chimaperekedwa osangoti kuti chikhozetse anthu kukhalako kwa nthaŵi yaitali koma kutetezera kanthu kena kofunika kwambiri, kukwaniritsidwa kwa chifuno cha Mulungu. Mwachitsanzo, kupulumuka kwa mpingo wathunthu wachikristu kunachitika chifukwa chakuti nkogwirizanitsidwa ndi kukwaniritsidwa kwa chifuno chimenecho. Komabe, Kristu mosabisa anauza ophunzira ake kuti iwowo monga munthu aliyense payekha adzakumana ndi imfa chifukwa cha chikhulupiriro chawo. Atanena zimenezi, Yesu anagogomezera, osati za kulanditsidwa kozizwitsa, koma za ‘kupirira kufikira chimaliziro.’ (Mateyu 24:9, 13) Kutetezeredwa kwenikweniko kumene ena anali nako, pamene ena analibe, sikumasonyeza kuti Mulungu ngwatsankhu. Mulungu anangogwiritsira ntchito munthu amene anali mu mkhalidwe wabwino koposa kukwaniritsa chifuno chake, chimene potsirizira pake chidzapindulitsa anthu onse.

Popeza kuti imfa yamwamsanga mu utumiki wa Mulungu imachitikadi, Akristu ayenera kukhala ndi maganizo oyenera monga a Ahebri atatu okhulupirika amene anapatsidwa chilango cha imfa chifukwa cha kulambira Mulungu. Anauza mfumu ya Babulo kuti: “Taonani, Mulungu wathu amene timtumikira akhoza kutilanditsa m’ng’anjo yotentha yamoto, nadzatilanditsa m’dzanja lanu, mfumu. Koma akapanda kutero, dziŵani, mfumu, kuti sitidzatumikira milungu yanu, kapena kulambira fano lagolidi mudaliimikalo.”—Danieli 3:17, 18.

Yehova anatetezera moyo wa Petro ndi Yohane chifukwa cha mbali yawo yofunika m’kukwaniritsa chifuno chake. Petro anagwiritsiridwa ntchito “kulimbitsa” mpingo mwa kuchita ntchito yoŵeta, imene inaphatikizapo kulembedwa kwa mabuku aŵiri ouziridwa a Baibulo. (Luka 22:32) Yohane analemba mabuku asanu a Baibulo ndipo anali ‘mzati’ mu mpingo woyambirira.—Agalatiya 2:9; Yohane 21:15-23.

Nkosatheka kuneneratu za nthaŵi ndi mmene Yehova amaloŵererera pa kulanditsa moyo wa atumiki ake. Kokha zimene tinganene motsimikiza nzakuti Kristu analonjeza kukhala ndi otsatira ake “masiku onse, kufikira chimaliziro cha nthaŵi ya pansi pano.” (Mateyu 28:20) Makamaka iye ‘adzakhala nafe’ mwa chitsogozo cha angelo pantchito yolalikira. (Mateyu 13:36-43; Chivumbulutso 14:6) Kusiyapo zisonyezero zodziŵika zimenezi zokha, sitingathe kudziŵa bwinobwino mmene thandizo la Mulungu lingaonetsedwere kapena munthu amene adzalandira chitetezero cha Mulungu. Bwanji ngati Mkristu alingalira kuti walandira chitetezero cha Mulungu ndi chitsogozo? Popeza kuti sitingathe kukana kapena kutsutsa zimenezi, palibe munthu amene ayenera kutsutsa kunena moona mtima kwa munthuyo.

Kodi Mulungu Ngwouma Mtima?

Kodi kulola imfa ya Akristu kwa Mulungu kumeneko kumasonyeza kuti iye mwina ngwankhanza? Kutalitali. (Mlaliki 9:11) Yehova akulinganiza kutetezera moyo wathu osati kwa zaka zingapo chabe kapena ngakhale makumi angapo a zaka koma kwamuyaya. Mwa lingaliro lake lapatali, amachititsa zinthu kuchitika kaamba ka ubwino wosatha wa aliyense amene amamkonda kapena amene amayandikira kwa iye. (Yerekezerani ndi Mateyu 18:14.) Kukwaniritsidwa kwa chifuno chake kudzatanthauza kuchotsedwa konse kwa zovuta zonse zimene tavutika nazo m’dongosolo lino la zinthu—ngakhale imfa. Zochita za Mulungu nzosafotokozeka ndi zangwiro kwambiri kwakuti mtumwi Paulo anasonkhezereka kunena kuti: “Ha! kuya kwake kwa kulemera ndi kwa nzeru ndi kwa kudziŵa kwake kwa Mulungu! Osasanthulikadi maweruzo ake, ndi njira zake nzosalondoleka!”—Aroma 11:33.

Popeza kuti palibe chimene chingatilekanitse ndi chikondi cha Mulungu, funso limene Mkristu aliyense ayenera kufunsa si lakuti ‘Kodi Mulungu adzanditetezera?’ koma lakuti ‘Kodi ndili ndi dalitso la Yehova?’ Ngati tili nalo, adzatipatsa moyo wosatha—mosasamala kanthu za zimene zingachitike kwa ife m’dongosolo lino. Pokuyerekezera ndi umuyaya wa moyo wangwiro, kuvutika kulikonse—ngakhale imfa—m’dongosolo lino kudzaoneka ngati ‘kopepuka kwa kanthaŵi.’—2 Akorinto 4:17.

[Mawu a M’munsi]

a Petro, Yakobo, ndi Yohane anachitira umboni za kusandulika kwa Yesu (Marko 9:2) ndi kuukitsidwa kwa mwana wamkazi wa Yairo (Marko 5:22-24, 35-42); anali pafupi naye m’Munda wa Getsemane mkati mwa kuyesedwa kwake (Marko 14:32-42); ndipo iwo, limodzi ndi Andreya, anafunsa Yesu za chiwonongeko cha Yerusalemu, kukhalapo kwake kwamtsogolo, ndi mapeto adongosolo la zinthu.—Mateyu 24:3, NW; Marko 13:1-3, NW.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena