Kupita Patsogolo ndi Manja Amene Amapereka Zizindikiro
KUYAMBIRA mu June 1995 ndi kupitiriza m’chilimwe chonse, Mboni za Yehova m’gawo la nthambi ya United States, zinakhala ndi misonkhano yachigawo 181 yokhala ndi mutu wakuti “Atamandi Achimwemwe.” Pa iŵiri ya imeneyi—umodzi kummaŵa ndipo wina kummadzulo—programu yonse inachitidwa mwachindunji mu American Sign Language (Chinenero Cholankhula ndi Manja cha ku America.) Motero programuyo inamveketsedwa bwino kwambiri—nkhani yokambidwa mwachindunji kwa agonthi m’chinenero cholankhula ndi manja imamveka bwino kwambiri kuposa kumasulira mawu onenedwa.
Nthumwi zinalipo zochokera ku mipingo 11 yachinenero cholankhula ndi manja ndi magulu ena pafupifupi 30 achinenero cholankhula ndi manja ochokera mu United States yense. Koma enanso amene analipo anali nthumwi zochokera ku Britain, Canada, Denmark, Dominican Republic, Ecuador, Germany, Japan, Mexico, Norway, Puerto Rico, ndi Russia. Motero, panali mkhalidwe wa kumaiko osiyanasiyana.
Mawailesi a kanema analinganizidwa kotero kuti programuyo ionekere pamawailesi akanema olunzanitsidwa ndi waya. Komabe, nthumwi zingapo zinali ponse paŵiri agonthi ndi akhungu. Kodi anthuŵa anapindula motani ndi programuyo? Kunali kogwiradi mtima kuona antchito odzifunira oposa zana limodzi akumasinthana kuwauza iwo programu ya tsiku lililonse mwa kumasulira kwa tactile (kukhudza).
Pamisonkhano iŵiri imeneyi, 36 anasonyeza kudzipatulira kwawo kwa Yehova Mulungu mwa ubatizo. Chochitika china chapadera chinali drama yakuti, Kuchitira Ulemu Owuyenerera m’Zaka Zawo Zaukalamba. Mmene kunalili kosangalatsa kuchita drama yonseyi m’chinenero cholankhula ndi manja, ikumalola agonthi kukhalamo ndi mbali yaikulu m’chochitikacho!
Ndiyeno panatulutsidwa buku latsopano lothandizira kuphunzira Baibulo, Knowledge That Leads to Everlasting Life. Osonkhanawo anasangalala makamaka kudziŵa kuti buku limenelo linali kupangidwa m’chinenero cholankhula ndi manja pa matepu a vidiyo! Voliyumu 1, imene inatulutsidwa pamsonkhanopo, ili ndi machaputala atatu oyambirira. Mavoliyumu ena asanu adzatsatira. “Tiyamikira kwambiri kaamba ka vidiyo yatsopanoyi,” inatero nthumwi yochokera ku Ohio. “Idzatithandizira kufulumiza ntchito polalikira kwa agonthi.”
Amene analipo 2,621 pamisonkhano iŵiriyi anapita kwawo atatsitsimulidwa mwauzimu. Kuposa ndi kale lonse, anali otsimikiza kunenanso mawu a wamasalmo akuti: “Zonse zakupuma zilemekeze Yehova. Haleluya.”—Salmo 150:6, NW.