Kodi Munaonapo Kuŵalima Kobiriŵira?
KUMAKHALA kosangalatsa chotani nanga kumaliza tsiku mwa kupenya kuloŵa kwa dzuŵa kokongola! Kuŵala kofundirira kwa dzuŵa kumatulutsa maonekedwe odabwitsa pamene kuunika kuloŵa mumpweya wophimba dziko lapansi. Chinthu chachilendo chotchedwa green flash (kuŵalima kobiriŵira) chimapangitsa chochitika chozizwitsachi kukhala chapadera kwambiri. Ngati mikhalidwe ili bwino, kuŵalima kwa kuunika kobiriŵira ngati emerald kumeneku kumachitika pamphindi yomaliza pamene dzuŵa likuloŵa. Chochitika chosaonekaoneka chotchedwa blue flash (kuŵalima kwa bluu) amati nchokongola koposa.
Kodi nchiyani chimene chimachititsa kuŵalima kokongola kumeneko? Nchifukwa ninji kumangochitika kwa kamphindi? Ndipo nchifukwa ninji kuli kosaonekaoneka? Kuti tiyankhe mafunso ameneŵa, tiyenera choyamba kukhala ndi chidziŵitso chofunika cha kugwirizana kumene kuli pakati pa kuunika kwa dzuŵa ndi mpweya wophimba dziko lapansi.
Kuunika kwa dzuŵa kumene kumadza kudziko lapansi kuli ndi maonekedwe onse a utawaleza. Pamene kuunika kumeneko kuloŵa mu mpweya wophimba dziko lapansi, mpweyawo umachita ngati galasi lalikulu lochindikala ndi kumwaza kuunikako. Komabe, mlingo wa kumwazika kwa cheza cha kuunika umadalira pa wavelength yake.
Cheza cha kuunika kwa bluu chili ndi wavelength yaifupi ndipo chimamwazika kwambiri mumpweya wophimba dziko lapansi. Nchifukwa chake thambo limaoneka la bluu pamene dzuŵa lili pamwamba pa chizirezire cha dziko tsiku lopanda mitambo. Koma pamene dzuŵa lili pafupi ndi chizirezirecho—monga pakuloŵa kwake—kuunika kwake kumadutsa mbali yaikulu ya mpweya kuti kufike m’maso athu. Chotero, kuunika kwa bluu komwazika kwambiri sikumatifika. Komabe, cheza chotalika, monga chija chofiira, chimaloŵa mosavuta mumpweya wochindikalawo. Zimenezi zimachititsa dzuŵa kuoneka mwachizoloŵezi ngati lofiira kapena lofiirira.a
Komabe, m’mikhalidwe ina, kuŵalima kobiriŵira kapena kwa bluu kungaoneke pamene dzuŵa likuloŵa. Kodi zimenezi zimachitika motani? Pamene mbali yomalizira ya dzuŵa ikuloŵa, kuunika kwa dzuŵa kumamwazika ndi kupanga maonekedwe onga utawaleza. Kuunika kofiira kumakhala kumunsi kwa maonekedwewo, pamene kuunika kwa bluu kumakhala pamwamba pake. Pamene dzuŵa lipitiriza kuloŵa, chigawo chofiira cha maonekedwewo chimaloŵa ku chizirezire cha dziko ndipo chigawo cha bluu nthaŵi zambiri chimamwazika mumpweya. Ndi panthaŵi imeneyi pamene mbali yotsalira ya kuunika ingatulutse kuŵalima kobiriŵira. Koma nchifukwa ninji kumakhala kobiriŵira? Chifukwa kubiriŵira kulinso maonekedwe aakulu a kuunika.
Pamene thambo lili loipitsidwa kwambiri, kuŵalima kobiriŵira sikumaonekaoneka, ndipo kuŵalima kwa bluu kumangooneka pamene thambo lili mbe ndipo kuunika kokwanira kwa bluu kuloŵa m’thambo ndi kuchititsa kuŵalima kwakukulu kuonekera.
[Mawu a M’munsi]
a Kuti mudziŵe zochuluka ponena za kuloŵa kwa dzuŵa, onani Galamukani! wachingelezi wa December 8, 1987, tsamba 16.
[Mawu a Chithunzi patsamba 30]
Kuloŵa kwa dzuŵa: ©Pekka Parviainen/SPL/Photo Researchers