Bwenzi Kukanakhala Mpweya Wabwino!
YOLEMBEDWA NDI MTOLANKHANI WA GALAMUKANI! KU BRITAIN
PAMENE mukupuma, kodi mumapuma mpweya wabwino? Kuipitsa mpweya kwamakono kuli “mdani wamkulu kuposa kusuta,” anatero dokotala wogwidwa mawu mu The Times ya London. Ku England ndi Wales, mpweya woipa umapha anthu pafupifupi 10,000 chaka chilichonse. Padziko lonse, makamaka m’mizinda yaikulu, mkhalidwe ngwoipa kowopsa.
Ambiri amaimba mlandu wa kuipitsa mpweya maindasitale a galimoto. Kuti achepetse utsi wowopsa, m’maiko ambiri tsopano galimoto zatsopano zimakhala ndi zipangizo zotsukuluza utsi, zimene zimachepetsa kuipitsa. Ma hydrocarbon mu utsi wa galimoto achepa kufika pa 12 peresenti ya milingo yake ya mu 1970, ndiponso ma nitrogen oxide ndi carbon monoxide achepa mofananamo. Makamaka makanda m’zikuku amakhala pangozi kwambiri chifukwa amayendera pamsinkhu wolingana ndi kotulukira utsi m’galimoto. Koma mpweya woipa umaikanso pangozi okwera m’galimoto. Zamveka kuti mpweya m’galimoto umakhala woipa kuŵirikiza katatu kuposa kunja. Ngozi ina imadza mwa kupuma utsi wa benzene wochokera ku mafuta pamene mukudzaza tanki ya galimoto yanu.
Tsopano mtundu wofala kwambiri wa zoipitsa mpweya padziko lapansi ndiwo “Zinthu Zouluka Mumpweya,” likutero lipoti la malo okhala la United Nations la 1993-94. Zikuoneka kuti, tizidutswa tating’ono ta mwaye, kapena zinthu zouluka, tili ndi mphamvu ya kuloŵa mpaka m’mapapu ndipo mmenemo timaikamo mankhwala owononga.
Kuwonongeka kwa muyalo wa ozoni kuthambo kumabutsa ndemanga zambiri m’nyuzi. Komabe, pansi pano, kuunika kwa dzuŵa kumachititsa ma nitrogen oxide ndi zinthu zina zimene zimaphwa msanga zoipitsa mpweya kutulutsa ozoni wochuluka. Ozoni ameneyo waŵirikiza kaŵiri m’Britain zaka za zana lino. Mipweya imeneyi imawononga utoto ndi mbali zina za nyumba, imadwalitsa mitengo, zomera, ndi zolima, ndipo zikuoneka kuti imachititsa matenda a m’chifuŵa mwa anthu ena. Ngakhale kuti ozoni amaipitsa kwambiri m’mizinda, chodabwitsa nchakuti madera akumidzi ndiwo amavutika kwambiri ndi ziyambukiro zake. M’matauni, ma nitrogen oxide amatsopa ozoni wochuluka, koma kumene kulibe ma oxide ambiri ameneŵa, kulibe chimene chimaletsa ozoni kusakaza zinthu.
Ndiponso, mpweya woipa ngwochuluka “kuŵirikiza nthaŵi ngati 70 m’nyumba kuposa kunja,” ikutero The Times. Umu zimene zimaipitsa mpweya ndizo utsi wa zonunkhiza m’nyumba, ma mothball, ndipo ngakhale zovala zochapidwa ku dry-cleaner. Ndiponso utsi wa fodya umawonjezera ngozi pa thanzi m’nyumba.
Pamenepa, kodi mungachitenji kuti mutetezere banja lanu? The Times ya London inapereka njira zotsatirazi.
• Chepetsani kugwiritsira ntchito kwanu galimoto. Ngati nkotheka, yendani pagalimoto la ena. Yendetsani bwinobwino. Ngati mwaima kwamphindi zingapo chifukwa cha kuchuluka kwa galimoto mumsewu kapena pachifukwa china, zimitsani injini. Ngati nkotheka, patsiku lotentha imikani galimoto lanu mumthunzi kuchepetsa kuipitsa kochitika chifukwa cha kuphwa kwa mafuta.
• Chitani maseŵero olimbitsa thupi mmamaŵa pamene ozoni kunja amakhala wochepa nthaŵi zambiri.
• Letsani kusuta m’nyumba.
• Siyani mazenera otseguka usiku kuchepetsa chinyontho ndipo tulutsani kunja zinthu zokuyambukirani moipa.
Mosakayikira mukuvomereza kuti: Bwenzi kukanakhala mpweya wabwino!