Kodi Mudzapezekako?
Chaka chatha, anthu oposa 8,700,000 padziko lonse anapezekapo pa Msonkhano Wachigawo wa “Atamandi Achimwemwe” wa Mboni za Yehova. Kodi mudzapezekako ku umodzi wa Misonkhano Yachigawo ya “Amithenga a Mtendere Waumulungu”? Muli aufulu kudzapezekako.
Kumadera ochuluka, msonkhanowo udzayamba ndi 9:30 pa Lachisanu mmaŵa ndi programu ya nyimbo zamalimba. Programu yotsegulira idzakhala ndi nkhani yolimbikitsa yakuti “Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife?” Imeneyi idzaphatikizapo chidziŵitso chimene tingagwiritsire ntchito kuthandiza anthu ena mamiliyoni kuchita zimene Mulungu amafuna.
Nkhani ya masana yakuti “Kuthandiza Ena Kudziŵa Zofuna za Mulungu” idzakonzekeretsa osonkhanawo kutengamo mbali mokwanira m’ntchito yopanga ophunzira. Pambuyo pake, nkhani yosiyirana ya mbali ziŵiri yakuti “Chenjerani ndi Misampha Yobisika ya Zosangulutsa” idzachenjeza za misampha yauchiŵanda yofunika kupeŵa. Programu ya Lachisanu idzatha ndi nkhani yofunika yakuti “Kuchirikiza Mokhulupirika Kudalirika kwa Mawu a Mulungu.”
Programu ya pa Loŵeruka mmaŵa idzagogomezera kufunika kwa ntchito ya kupanga ophunzira m’nkhani yosiyirana ya mbali zitatu yakuti “Amithenga Obweretsa Uthenga Wabwino wa Mtendere.” Nkhani yomalizira ya programuyo idzakhala ya kudzipatulira ndi ubatizo, ndiyeno padzatsatira ubatizo wa ophunzira atsopano.
Nkhani ya pa Loŵeruka masana yakuti “Lingalirani za Maganizo a Yehova pa Nkhani Zofunika” idzayankha mafunso amene ambiri akhala nawo pankhani zomwe akuganizapo. Mudzakondwa ndi nkhani yosiyirana ya mbali ziŵiri yakuti “Mulungu Wamtendere Amasamala za Inu.” Ndiyeno padzakhala kanthu kapadera m’nkhani yomaliza ya programuyo yakuti “Londolani Mtendere Waumulungu m’Moyo wa Banja.”
Nkhani yosiyirana ya mbali zitatu pa Sande mmaŵa yakuti, “Kudziŵa Mtundu Wabwino wa Amithenga,” idzagogomezera mutu wa msonkhano mwa kugwiritsira ntchito zitsanzo za aneneri a m’Baibulo. Programu ya mmaŵa idzatha ndi seŵero la ovala mikhanjo limene lidzasonyeza maphunziro opindulitsa kuchokera m’nkhani ya Baibulo ya Woweruza Gideoni.—Oweruza 6:11–8:28.
Programu yomalizira ya msonkhano pa Sande masana idzakhala ndi nkhani yapoyera ya mutu wakuti “Mtendere Weniweni Potsirizira Pake!—Kuchokera ku Magwero Ati?” Pomalizira pake, nkhani yosonkhezera yakuti “Kupita Patsogolo Monga Amithenga a Mtendere Waumulungu” idzatsekera msonkhanowo.
Popeza misokhano yalinganizidwa mu Malaŵi, Mozambique, Zambia, ndi Zimbabwe, mosakayikira wina udzakhala pafupi ndi kwanu. Funsani Mboni za Yehova zakumaloko ponena za nthaŵi ndi malo a msonkhano wapafupi ndi kwanu.