Chitsanzo Chochitsatira Pochita ndi Othaŵa Kwawo
M’CHILAMULO chimene Yehova Mulungu anapatsa mtundu wa Israyeli, Aisrayeli anakumbutsidwa za mkhalidwe wawo monga othaŵa kwawo mu Aigupto. (Eksodo 22:21; 23:9; Deuteronomo 10:19) Chotero analangizidwa kuchitira chifundo alendo omwe anali pakati pawo, inde kuwayesa abale.
Chilamulo cha Mulungu chinati: “Mlendo [amene nthaŵi zambiri anali wothaŵa kwawo] akagonera m’dziko mwanu, musamamsautsa. Mlendo wakugonera kwa inu mumuyese pakati pa inu monga wa m’dziko momwemo; umkonde monga udzikonda wekha; popeza munali alendo m’dziko la Aigupto.”—Levitiko 19:33, 34.
Pozindikira kuti alendo nthaŵi zambiri anali pangozi ndipo osatetezereka, Yehova anapereka malamulo akutiakuti kaamba ka ubwino wawo ndi chitetezo. Talingalirani zoyenera zotsatira zopatsidwa kwa iwo.
KUYENERA KWAWO CHIWERUZO CHOLUNGAMA: “Chiweruzo chanu chifanefane ndi mlendo ndi wobadwa m’dziko.” “Musamaipsa mlandu wa mlendo.”—Levitiko 24:22; Deuteronomo 24:17.
KUYENERA KWAWO KULANDIRAKO CHACHIKHUMI: “Pakutha pake pa zaka zitatu muzitulutsa magawo onse a magawo khumi a zipatso zanu za chaka icho, ndi kuwalinditsa m’mudzi mwanu; ndipo abwere Mlevi, popeza alibe gawo kapena choloŵa pamodzi ndi inu, ndi mlendo, ndi ana amasiye, ndi mkazi wamasiye, okhala m’mudzi mwanu, nadye nakhute.”—Deuteronomo 14:28, 29.
KUYENERA KWAWO MALIPIRO ABWINO: “Musamasautsa [“musamadyerera,” NW] wolembedwa ntchito, wakukhala waumphaŵi ndi wosauka, wa abale anu kapena wa alendo ali m’dziko mwanu, m’midzi mwanu.”—Deuteronomo 24:14.
KUYENERA KWAWO MALO OPULUMUKIRAKO NGATI APHA MUNTHU MWANGOZI: “Midzi isanu ndi umodzi imene ndiyo yopulumukirako ana a Israyeli, ndi mlendo, ndi wokhala pakati pawo; kuti aliyense adamupha munthu osati dala athaŵireko.”—Numeri 35:15.
KUYENERA KWAWO KUKUNKHA: “Pakukolola dzinthu dza m’dziko mwanu, usamakololetsa m’mphepete mwa munda wako, nusamakunkha khunkha. Usamakunkha khunkha la m’munda wako wamphesa, usamazitola zidagwazi za m’munda wako wamphesa; uzisiyire wosauka ndi mlendo; ine ndine Yehova Mulungu wanu.”—Levitiko 19:9, 10.
Inde, Mlengi wathu, Yehova Mulungu, amachitira chifundo othaŵa kwawo, ndipo amakondwera pamene ife tichitanso chimodzimodzi. “Khalani akutsanza a Mulungu,” mtumwi wachikristu Paulo analemba motero, “ndipo yendani m’chikondi.”—Aefeso 5:1, 2.
[Mawu a Chithunzi patsamba 9]
Mnyamata kulamanzere: UN PHOTO 159243/J. Isaac