Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g96 11/8 tsamba 14-15
  • Kodi Nchitsogozo cha Yani Chimene Mungadalire?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Nchitsogozo cha Yani Chimene Mungadalire?
  • Galamukani!—1996
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Dzanja la Mulungu Lilozera Anthu Ake
  • Gwiritsitsani Dzanja la Mulungu!
  • “Chirimikani, Ndipo Penyani Chipulumutso cha Yehova”
    Nsanja ya Olonda—2007
  • ‘Yehova Wakhala Chipulumutso Changa’
    Nsanja ya Olonda—2006
  • Pa Nyanja Yofiira Panachitika Zodabwitsa Kwambiri
    Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Mulungu Anapulumutsa Ana a Isiraeli
    Kodi Baibulo Lili Ndi Uthenga Wotani?
Onani Zambiri
Galamukani!—1996
g96 11/8 tsamba 14-15

Lingaliro la Baibulo

Kodi Nchitsogozo cha Yani Chimene Mungadalire?

“TIYE kuno!” atate akuuza mwana wake wamwamuna wazaka zisanu. Atateyo akutambasula dzanja lake, ndipo mosazengereza, mwanayo akunyamphira ndi kufumbata zala za atate wake ndi dzanja lake laling’ono. Kulikonse kumene ulendowo udzaloŵera, mwanayo akudalira chitsogozo cha kholo lake ndipo akutsatira ndi mtima wonse. Mosasamala kanthu za chimene chingachitike, mwanayo akangamirabe osaleka.

Pomakhala ndi moyo m’masiku ano a kusatsimikizirika kwa za chuma, za ndale ndi za moyo wa munthu, kodi simukanalandira dzanja lotsogoza la munthu amene mumadalira kotheratu? Komabe, tikukhala ndi moyo m’nthaŵi pamene anthu osaona mtima akudyera masuku pamutu pa osadziŵa. Motero, pali chifukwa chabwino chokhalira wosamala ponena za yemwe tingadalire. Kapena inu munagwiritsidwapo mwala ndi winawake amene munadalira kuti angakutsogozeni.

Komabe, Baibulo limatilimbikitsa kuika chidaliro chathu mwa Mulungu. “Pakuti ine Yehova Mulungu wako ndidzagwira dzanja lako lamanja, ndi kunena kwa iwe, Usaope ndidzakuthandiza iwe,” analemba choncho mneneri Yesaya. (Yesaya 41:13) Ndipo mtumwi Petro anapereka uphungu uwu: “Potero dzichepetseni pansi pa dzanja lamphamvu la Mulungu, kuti panthaŵi yake akakukwezeni; ndi kutaya pa iye nkhaŵa yanu yonse, pakuti iye asamalira inu.”—1 Petro 5:6, 7.

Ngakhale ndi choncho, mungafunse moyenerera kuti, ‘Kodi nchifukwa ninji ndingaike chidaliro m’chitsogozo cha Mulungu?’ Zifukwa zomveka zotsatirazo zikupezeka m’mbiri ya Aisrayeli akale.

Dzanja la Mulungu Lilozera Anthu Ake

Tsatanetsatane wa zochitika zimene zinafika pachimake usiku wa Nisani 14, 1513 B.C.E., zinakhwetemula chitsimikizo cha Farao wotsendereza wankhalwe ndi cha Aigupto, kotero kuti iwo anamasula anthu a Mulungu, Aisrayeli, muukapolo. (Eksodo 1:11-13; 12:29-32) Pa Nisani 15, mtundu wosangalala wa Aisrayeliwo unalunjika kuchipululu pomka ku Dziko Lolonjezedwa. Njira yachindunji kopambana inali cha kumpoto kwa Memphis, motsatana ndi gombe la nyanja ya Mediterranean, cha pafupi ndi dziko lokhalamo Afilisti owopedwawo, mpaka ku Dziko Lolonjezedwalo. Komabe, Mulungu anali ndi njira ina m’maganizo.—Eksodo 13:17, 18; Numeri 33:1-6.

Mulungu anapereka chotsogoza chooneka ku mtundu wa Israyeli wakale umenewo, chomwe chinaoneka ngati mtambo njo masana ndi mtambo njo usiku (Eksodo 13:21, 22) Limodzi ndi chooneka chachilendo chimenechi, Yehova anagwiritsira ntchito monga woimira wake wa padziko lapansi munthu wokhulupirikayo Mose. (Eksodo 4:28-31) Chotero, panali umboni wosatsutsika wakuti dzanja la Mulungu linali kutsogoza Aisrayeli.

Pa chigono chawo chachiŵiri, Etamu, “m’mphepete mwa chipululu,” Yehova analangiza Mose kubwerera m’mbuyo ndi kumanga msasa pa gombe la Nyanja Yofiira, ku Pihahiroti. (Eksodo 13:20) Kachitidwe kooneka kodabwitsa kameneka kanachititsa Farao kuganiza kuti Aisrayeliwo anali “kumangoyendayenda mosokonezeka m’dziko.”[NW] Atalimbikitsika, Farao anasintha maganizo. Tsopano wotsimikizira kuwabwezeretsanso mu ukapolo Aisrayeliwo, iye anasonkhanitsa gulu lake lankhondo nkulithiramo liŵiro kuwatsata.—Eksodo 14:1-9.

Mwakuutsogolera mtunduwo ku njira ina, m’chimene mwachionekere chinali chidikha chotsikira ku Nyanja Yofiira, kunaoneka ngati kuti Mose anali kuwatchera Aisrayeliwo kuti atsekerezedwe ndi mapiri kumbali zonse ziŵiri za msasawo pa Pihahiroti, Nyanja Yofiira, ndi gulu lankhondo la Farao lomayandikiralo. Kunaoneka ngati Aisrayeli anakhala chandamale chokhweka kuti akagonjetsedwa msanga kapena kufafanizidwa.

Kodi izi zinakhala ndi chiyambukiro chotani pa iwo? Kodi iwo akanasonyeza chidaliro m’chitsogozo cha Yehova? Monga mmene kumaonekera, mkhalidwewo unali wopanda chiyembekezo. Chotero, ena anagwidwa mantha. Ngakhale enanso anayamba kung’ung’udza motsutsana ndi Mose. Ena anali okonzekera ngakhale kungobwerera kuukapolo ku Igupto!—Eksodo 14:10-12.

Gwiritsitsani Dzanja la Mulungu!

Mu mkhalidwe uwu Aisrayeli anafunikira kuonetsa chidaliro chonga cha mwana mwa Wamphamvuyonseyo. Yehova anali ndi chifukwa chabwino chosadziŵidwa ndi mtundu wonsewo cha kulangizira Mose kuwoloka Nyanja Yofiira pa Pihahiroti. Mwa kuyendetsa Aisrayeliwo ulendo wa ku Dziko Lolonjezedwa kudzera kummwera kwa dziko la Afilisti, Yehova anasonyeza kuzindikira kwachikondi. Pambuyo pa zaka 215 mu Igupto, panalibe chikayikiro chakuti Aisrayeli anali osakonzekera kumenya nkhondo ndi mtundu wa asilikali owopsawo. Chotero, Yehova anasankha njira imene ikapeŵetsa kulimbana koteroko.a—Eksodo 13:17, 18.

Chilanditso cha mtunduwo ndi kugonjetsedwa kwa Farao ndi gulu lake lankhondo pa Nyanja Yofiira zimapereka umboni wodabwitsa wa mphamvu yopulumutsa ya Mulungu. Ndiponso, mmene analili oyamikira nanga Aisrayeliwo omwe, ngakhale kuti sanamvetsetse chifukwa chake Mulungu anawayendetsa m’njira yakutiyakuti, sanalisiye dzanja la Mulungu! Anagwiritsitsa ndipo anaona kugaŵanika kodabwitsa kwa Nyanja Yofiira ngakhalenso kufafanizidwa kwa adani awo. Chidaliro chawo m’chitsogozo cha Yehova chinafupidwa.—Eksodo 14:19-31.

Kachiŵirinso, tatiyeni tilingalire za chitsanzo cha mwana wogwiriza dzanja la kholo lake. Pamene mwana achita mantha, kodi amachita motani? M’malo mwa kutaya dzanja la atate wake kapena kulisiyirira, mwanayo amalifumbatitsa kwambiri. Mwakutero, amaonetsa chidaliro chosagwedera choti khololo lidzapereka chitsogozo chosalephera ndi nyonga mkati mwa mavuto.

Mofananamo, pamene tikumana ndi zipsinjo m’moyo wathu, tifunikira kugwiritsitsa, tikumadalira mowonjezereka chitsogozo cha Mulungu! Mawu Ake, Baibulo, angathe kukhala nyali yathu yotsogolera. (Salmo 119:105) Ndiponso, kumbukirani kuti limodzi ndi chidaliro kumadza kuleza mtima. Chotero, tiyenera kumpatsa Yehova nthaŵi yoti athetse mavuto, ngakhale ngati kwa nyengo ina tingakhale osamvetsetsa mokwanira chifukwa chake iye akutitsogoza m’njira yakutiyakuti. Inde, tingathe kudalira chitsogozo cha Mulungu.—Eksodo 15:2, 6; Deuteronomo 13:4; Yesaya 41:13.

[Mawu a M’munsi]

a Kuti mudziŵe zowonjezereka ponena za Pihahiroti, onani Insight on the Scriptures, Volume 2, masamba 638-9, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena