Lingaliro la Baibulo
Kugonjera kwa Mkazi Kodi Kumatanthauzanji?
MAWU A MULUNGU, Baibulo, pa Aefeso 5:22, NW amati: “Akazi agonjeretu amuna awo monga kwa Ambuye.” Kodi kwenikweni zimenezi zimatanthauzanji? Kodi mkazi ayenera kugonjera pa zonse zimene mwamuna akufuna, mosasamala chilichonse? Kodi sangagwiritsire ntchito luntha lake kapena kukhala ndi malingaliro osiyana ndi a mwamuna?
Lingalirani za nkhani ya m’Baibulo ya Abigayeli. Iyeyo anachitapo kanthu mwanzeru koma motsutsana ndi zofuna za mwamuna wake wachuma, Nabala. Ngakhale kuti otsata Davide, munthu amene Mulungu anamsankha kukhala mfumu ya Israyeli, anasonyeza kukoma mtima kwa Nabala, iye “anawakalipira.” Atakwiya ndi kusayamikira kwa Nabala, Davide anakonzekera kukakhetsa mwazi wake. Abigayeli anazindikira kuti nyumba yake yonse inali pangozi. Anafeŵetsa mtima wa Davide. Motani?—1 Samueli 25:2-35.
Abigayeli anavomera kwa Davide kuti Nabala anali “munthu . . . woipa” ndipo anapatsa Davide zinthu zimene Nabala anakaniza. Mwachibadwa, si bwino kwa mwamuna kapena mkazi kudziŵikitsa zophophonya za mnzake. Kodi Abigayeli anali wopanduka polankhula ndi kuchita m’njira imeneyi? Ayi. Iye anali kuyesa kupulumutsa moyo wa Nabala ndi nyumba yake. Palibe lingaliro lililonse lakuti mkaziyo anali ndi chizoloŵezi cha kupanda ulemu kapena kudzigangira. Ndiponso Nabala wovutayo sananenepo za kusakhutira kulikonse ndi mmene mkaziyo anamthandizira kuyang’anira chuma chake chambiri. Komano mu mkhalidwe uwu wovuta, nzeru yake inamlamulira kuti achitepo kanthu payekha. Ndiponso, Baibulo limalankhula moyanja zimene Abigayeli anachita.—1 Samueli 25:3, 25, 32, 33.
Kalekale tsiku la Abigayeli lisanafike, panali nthaŵiyo pamene akazi a makolo anasonyeza malingaliro ndi kuchitapo kanthu mosiyana ndi zimene amuna awo anafuna. Komabe, “akazi oyera mtima, akuyembekezera Mulungu” ameneŵa amasonyezedwa kukhala zitsanzo za kugonjera kwa mkazi wachikristu. (1 Petro 3:1-6) Mwachitsanzo, pamene Sara anazindikira kuti Ismayeli mwana wa Abrahamu anali wangozi pa mwana wake, Isake, anasankha kuti athamangitse Ismayeli. “Mawuwo anaipira Abrahamu.” Koma Mulungu anati kwa Abrahamu: “Usaipidwe nawo, chifukwa cha mnyamatayo, . . . momwe monse akunenera iwe Sara umvere iwe mawu ake.”—Genesis 21:11, 12.
Luntha Lili Lofunika
Pamenepo, si bwino kuti mkazi atsenderezeke kuchita zimene akudziŵa kuti zili zopanda nzeru kwambiri kapena zakuswa mapulinsipulo aumulungu, m’dzina la kugonjera. Ndiponso sayenera kumva liwongo chifukwa cha kuchitapo kanthu pa nkhani ina yofunika, monga momwe anachitira Abigayeli ndi Sara.
Kugonjera kwa mkazi sikumatanthauza kuti mkaziyo nthaŵi zonse ayenera kuvomera zonse zimene mwamuna akufuna. Kodi kusiyana kwake kuli pati? Ngati mapulinsipulo abwino angasweke, mkaziyo sangavomerezane ndi mwamuna wake. Komabe, iye ayenera kusonyeza mzimu wonse wa kugonjera kwaumulungu.
Zoonadi, mkazi ayenera kusamala kuti sakunyalanyaza zofuna za mwamuna wake mwadala, chifukwa cha dumbo, kapena zolinga zina zoipa. Ayenera kukhala waluntha, “wa nzeru yabwino,” monga momwe analili Abigayeli.—1 Samueli 25:3.
Pamene Mwamuna Apeŵa Thayo
Cholinga chachikulu ndi mzimu wa kugonjera kwaumulungu kwa mkazi ndicho kukondweretsa Yehova mwa kuchita mogwirizana ndi mwamuna wake ndi kuchirikiza zosankha zake. Zimenezi zimakhala zosavuta kwambiri ngati mwamuna ali wokula msinkhu mwauzimu. Zingakhale zovuta ngati mwamunayo sali wotero.
Zitatero, kodi mkazi angachite motani? Angamchonderere mwakhama kapena kupempha ngati angamsonyeze zosankha zimene zidzapindulitsa kwambiri banjalo. Ngati mkaziyo alola mwamuna ‘kuwongolera sitima,’ mwina mwamunayo angakhale waluso kwambiri. Kulongololera mwamuna nthaŵi zonse kumawonongetsa mzimu wa kugonjera koyenera. (Miyambo 21:19) Komabe, ngati ubwino wa banja uli pangozi yachionekere chifukwa cha njira yake, mkazi angasankhe zotchula njira yoyenera, monga momwe Sara anachitira.
Ngati mwamuna ali wosakhulupirira, chitokosocho chimakhala chokulirapo kwa mkazi wake. Ngakhale zili choncho, mkaziyo ayenera kugonjera malinga ngati sakumpempha kuswa malamulo a Baibulo. Ngati achita zimenezo, mchitidwe wa mkazi wachikristu ukhale ngati uja wa ophunzira pamene bwalo lamilandu linawauza kuswa malamulo a Mulungu: “Tiyenera kumvera Mulungu koposa anthu.”—Machitidwe 5:29.
Komabe, chifukwa cha kusoŵa chidziŵitso ndi kukhala ndi nzeru zochepa, ngakhale amuna ndi akazi okhala ndi zolinga zabwino angachite mopambanitsa m’mathayo awo. Mwamuna angakhale wosalingalira za mnzake; mkazi angakhale woumiriza kwambiri pa zokonda zake. Kodi nchiyani chimene chingathandize? Lingaliro lodzichepetsa nlofunika kwa onse aŵiri, pakuti “timakhumudwa tonse pa zinthu zambiri.”—Yakobo 3:2.
Amuna ambiri amafikira pa kuyamikira nzeru yoona mtima ya mkazi ngati aigwiritsira ntchito bwino. Ndipo kugwirizana kumakuzidwa ngati aŵiriwo apepesa pamene aphophonya. Monga momwe Yehova amakhululukira zolakwa zathu tsiku lililonse, nafenso tiyenera kukhululukira ena. “Mukasunga mphulupulu, Yehova, adzakhala chiriri ndani, Ambuye? Koma kwa Inu kuli chikhululukiro.”—Salmo 130:3, 4.
‘Kugonjerana Wina ndi Mnzake’
Pamenepo, kaamba ka ubwino wathu tonse, Malemba amalangiza kuti: “Gonjeranani wina ndi mnzake powopa Kristu.” Patsanani ulemu wachikondi wogwirizana; musadodometsane kapenanso kupikisana. Lembalo limapitiriza kuti: “Akazi agonjeretu amuna awo monga kwa Ambuye, chifukwa mwamuna ndiye mutu wa mkazi wake monganso Kristu ali mutu wa mpingo.”—Aefeso 5:21-23, NW.
Liwu lachigiriki limene Paulo anagwiritsira ntchito pa Aefeso 5:21, 22 limapereka lingaliro la kudzigonjetsera, osati kuumirizidwa kugonjera. Ndipo kugonjerako kuli kaamba ka Ambuye, osati chabe kaamba ka kumvana mu ukwati. Mpingo wa odzozedwa wa Kristu umagonjera mwaufulu, mwachimwemwe kwa Kristu. Ngati mkazi achita chimodzimodzi kwa mwamuna wake, pamenepo nkotheka kuti ukwatiwo udzakhala wachimwemwe ndi wachipambano.
Malemba amati: “[Mwamuna] yense akonde mkazi wake wa iye yekha, monga adzikonda yekha.” (Aef. 5:33; 1 Petro 3:7) Mwamuna ayenera kukumbukira kuti nayenso ayenera kugonjera mutu wake, pakuti Baibulo limati: “Mutu wa munthu [“mwamuna,” NW] yense ndiye Kristu.” Inde, mwamuna ayenera kugonjera ku ziphunzitso za Kristu. Kristu nayenso, amagonjera mutu wake: “Mutu wa Kristu ndiye Mulungu.” Chotero, aliyense kusiyapo Yehova ali ndi mutu. Ndipo ngakhale iye amatsatira malamulo ake.—1 Akorinto 11:3; Tito 1:2; Ahebri 6:18.
Kugonjera kwachikristu nkolinganizidwa ndi kopindulitsa kwa onse aŵiri mwamuna ndi mkazi. Kumabweretsa chimvano ndi chikhutiro mu ukwati chimene Mlengi wathu wachikondi yekha ndiye angapereke.—Afilipi 4:7.
[Mawu a Chithunzi patsamba 26]
Leslie’s