Lingaliro la Baibulo
Chigumula Chenicheni Kapena Nthano?
‘Ndipo nyama zonse ziŵiriziŵiri zinaloŵa kwa Nowa m’chingalawamo.’—Genesis 7:8, 9.
NDANI nanga yemwe sanamvepo za Chigumula cha m’tsiku la Nowa? Muyenera kuti mwadziŵa nkhaniyo kuyambira paubwana. Ndithudi, ngati mupita ku laibulale ya kwanuko kukafufuza za Chigumulacho, mungapeze mabuku ambiri olembedwera ana pankhaniyo kuposa olembedwera akulu. Chifukwa cha zimenezo, mwina mungaone nkhani ya Chigumula kukhala nthano wamba ya pocheza madzulo. Ambiri amaganiza kuti nkhani ya Chigumula cha Nowa, limodzi ndi nkhani zina zambiri za m’Baibulo, zangokhala nthano basi, kapena phunziro chabe la makhalidwe limene anthu anangopeka.
Chodabwitsa nchakuti, ngakhale ena amene amati zikhulupiriro zawo zazikidwa pa Baibulo amakayikira kuti Chigumula chinachitikadi. Wansembe wachikatolika Edward J. McLean nthaŵi ina anati nkhani ya Nowa sinalembedwe kuti ionedwe monga chochitika chenicheni cha m’mbiri, koma monga “fanizo kapena nkhani wamba ya m’buku.”
Komabe, kodi Chigumulacho chosimbidwa m’Baibulo ndi fanizo chabe, losati kuliona monga chochitika chenicheni? Kodi Baibulo limavomereza lingaliro limenelo?
Maumboni Odalirika
Talingalirani choyamba nkhani imene Mose analemba m’buku la Genesis. Mmenemo, akutchula chaka chenicheni, mwezi, ndi tsiku pamene mvumbiwo unayamba, pamene chingalawacho chinaima paphiri, ndi pamene madzi anauma padziko lapansi. (Genesis 7:11; 8:4, 13, 14) Ngakhale kuti si nthaŵi zonse pamene masiku enieni amalembedwa kwinakwake m’Genesis, masikuŵa akugogomezera mfundo yakuti Mose anaona Chigumula monga chochitika chenicheni. Onani kusiyana kwa choonadi cha Baibulo ndi mawu otsegulira nthano zambiri za akatswiri akuti, “Kale kunali . . .”
Monga chitsanzo china, talingalirani za chingalawa chenichenicho. Baibulo limalongosola chombo chotalika pafupifupi mamita 131, ndi mlingo wa m’litali ndi msinkhu 10 kwa 1 ndipo m’litali ndi m’mimba 6 kwa 1. (Genesis 6:15) Koma Nowa sanali womanga zombo. Ndipo kumbukirani kuti, zimenezi zinachitika zaka zoposa 4,000 zapitazo! Komabe, chingalawacho chinamangidwa m’milingo yoyenera chombo choyandama pamadzi. Ndipo akatswiri amakono a zombo apeza milingo imeneyo kukhala yoyenera kuti chombo chikhale cholimba ndi chokhazikika bwino panyanja zazikulu zatetete. Ngakhale kuti Baibulo silimatchula utali weniweni wa nthaŵi imene Nowa anamanga chingalawacho, nkhaniyo imasonyeza kuti nkotheka kuti chinatenga zaka 50 kapena 60. (Genesis 5:32; 7:6) Mfundo zimenezi zikusiyana kwambiri ndi nthano yodziŵika kwambiri yotchedwa Nthano ya Gilgamesh ya Ababulo. Nthanoyo imalongosola chombo chosapangika bwinobwino cha mbali zonse zolingana monga bokosi, mbali iliyonse mamita 60 chimene chinamangidwa pamasiku asanu ndi aŵiri. Mosiyana ndi nthano yachibabulo imeneyo, nkhani ya Chigumula ya m’Baibulo imasonyeza kuti kulondola kwake nkodalirika.
Kusiyapo nkhani ya m’Genesis, Malemba amatchula Nowa kapena Chigumula cha padziko lonse m’malo khumi. Kodi mavesi ameneŵa amasonyeza kuti alembi ouziridwawo anaona Chigumulacho kukhala chochitika chenicheni cha m’mbiri kapena nthano chabe?
Kuona Kwake Kutsimikiziridwa
M’Malemba, Nowa akuonekera m’mizera iŵiri yobadwira ya mtundu wa Israyeli, wachiŵiriwo umafika mpaka kwa Yesu Kristu. (1 Mbiri 1:4; Luka 3:36) Ezara ndi Luka, olemba mizera yobadwira imeneyo, anali akatswiri olemba mbiri ndipo ayenera kuti anakhulupirira kuti Nowa anali munthu weniweni.
Kwinakwake m’Baibulo, Nowa akundandalikidwa pakati pa anthu a m’mbiri, akumasonyezedwa kukhala munthu wa chilungamo ndi chikhulupiriro. (Ezekieli 14:14, 20; Ahebri 11:7) Kodi kungakhale kwanzeru kwa olemba Baibulo kuphatikiza munthu wa m’nthano monga chitsanzo choti titsatire? Iyayi, pakuti zimenezo zingachititse oŵerenga Baibulo kuganiza kuti chikhulupiriro nchosatheka kwa anthu ndipo chingangosonyezedwa ndi anthu a m’mabuku a nthano. Nowa pamodzi ndi amuna ena ndi akazi achikhulupiriro anandandalikidwa chifukwa chakuti anali anthu okhala ndi zifooko ndi malingaliro onga athu.—Ahebri 12:1; yerekezerani ndi Yakobo 5:17.
M’maumboni otsalawo a m’Malemba, Nowa ndi Chigumula akutchulidwa pofotokoza za chiwonongeko chimene Mulungu anadzetsa pa mbadwo wopanda chikhulupiriro umene unazinga Nowa. Onani kunena kwa Yesu za Chigumulacho, pa Luka 17:26, 27: “Monga kunakhala masiku a Nowa, momwemo kudzakhalanso masiku a Mwana wa munthu. Anadya, anamwa, anakwatira, anakwatiwa, kufikira tsiku lija Nowa analoŵa m’chingalaŵa, ndipo chinadza chigumula, nichiwawononga onsewo.”
Yesu Kristu anali mboni yoona ndi maso zochitika zimene analongosola, pakuti analiko kumwamba asanakhale ndi moyo padziko lapansi. (Yohane 8:58) Ngati Chigumula chinali nthano chabe, ndiye kuti Yesu anali kutanthauza kuti kukhalapo kwake kwamtsogolo kunali kongoyerekezera kapena konama. Koma malingaliro onse aŵiriŵa sakugwirizana ndi Malemba ena onse. (1 Petro 2:22; 2 Petro 3:3-7) Motero, chifukwa cha zimene anadzionera yekha, Yesu Kristu anakhulupirira nkhani ya m’Baibulo ya Chigumula cha padziko lonse kukhala mbiri yakale yoona. Kwa Akristu oona, umenewu ndiwo umboni wodalirika koposa wakuti Chigumula cha m’tsiku la Nowa chinali chenicheni, osati nthano ayi.
[Mawu a Chithunzi patsamba 18]
L. Chapons/Illustrirte Familien-Bibel nach der deutschen Uebersetzung Dr. Martin Luthers