Nkhalango Yamvula ya Amazon—Yobisika m’Nthanthi
YOLEMBEDWA NDI MTOLANKHANI WA GALAMUKANI! KU BRAZIL
AMWENYE Achiirimarai okhala m’mphepete mwa mtsinje wa Napo m’Peru sanathe kukhulupirira zimene anaona! Zombo ziŵiri zazikulu kwambiri moti mabwato awo osakhalanso kanthu powayerekezera ndi izo, zinatulukira zitalunjika mudzi wawo. Anaona asilikali andevu m’zombozo—osiyana ndi mtundu uliwonse wa anthu umene anaonapo. Pochita mantha ndi zimenezo, Amwenyewo anabalalika kukabisala napenya alendo akhungu loyerawo akulumphira pagombe, nadya zakudya za pamudzipo, kenako nakweranso zombo zawo ndi kupita—changu chitawadya chofuna kutchuka atadziŵika kukhala oyamba kudutsa m’nkhalango yonseyo yamvula, kuchokera ku Andes Mountains mpaka ku Atlantic Ocean.
M’chaka chimenecho, 1542, umodzi ndi umodzi wa mitundu ya Amwenye unaona zodabwitsa zofananazo pamene Azungu ozonda malowo, posonyeza mauta awo ndi mfuti zagogodera moopseza, analoŵerera mkati mwenimweni mwa nkhalango ya kumalo otentha ku South America.
Posapita nthaŵi, Francisco de Orellana, kaputeni wa ku Spain wotsogolera ogonjetsawo, anadziŵa kuti mbiri ya kufunkha zinthu ndi kuwombera anthu kwa asilikali ake inayenda mofulumira kuposa zombo zawo ziŵirizo. Mitundu ya Amwenye yokhala kumunsi kwa mtsinje (pafupi ndi mzinda wamakono wa Manaus m’Brazil) anali chire ndi mivi yawo akuyembekezera oloŵererawo pafupifupi 50 kuchuluka kwawo.
Ndipo mmodzi wa oloŵererawo, Gaspar de Carvajal anavomereza kuti Amwenyewo analidi akatswiri pa uta ndi muvi. Analankhula zoona ndi maso, pakuti umodzi wa mivi ya Amwenyewo unamgwaza m’nthiti. “Bwenzi si chovala changa chochindikala chausilikali,” analemba motero fulaya wovulalayo, “mapeto anga akanakhala omwewo.”
‘Akazi Omenya Nkhondo Ngati Amuna Khumi’
Carvajal anapitiriza kufotokoza mphamvu yosonkhezera Amwenye olimba mtimawo. ‘Tinaona akazi akumenya nkhondo patsogolo pa amuna monga akaputeni achikazi. Akaziwa ngoyera ndi aatali, ataluka tsitsi lawo ndi kulikulunga m’mitu yawo. Ngolimba, ndipo ndi mauta ndi mivi m’manja, amamenya nkhondo ngati amuna khumi.’
Sitikudziŵa kaya wozonda dzikoyo anaona akazi enieni, kapena anali “mazangazime a malungo a m’nkhalango,” malinga ndi kunena kwa ena. Koma malinga ndi kunena kwa zolembedwa zina, panthaŵi imene Orellana ndi Carvajal anafika kumatsiriro a mtsinje waukuluwo ndi kuloŵa m’nyanja ya Atlantic Ocean, anakhulupirira kuti anaona zachilendo za Dziko Latsopano la Aamazoni, asilikali aakazi oopsawo olongosoledwa m’nthanthi zachigiriki.a
Fulaya Carvajal anasungira mibadwo yakutsogolo nthanthi ya Aamazoni a ku America mwa kuiphatikiza m’nkhani imene analemba yonena za umboni wake woona ndi maso wa ulendo wa Orellana wa miyezi isanu ndi itatu. Kaputeni Orellana, anapita ndi chombo ku Spain, kumene analongosola tsatanetsatane wa ulendo wake wotsatira mtsinje umene anakonda kuutcha Río de las Amazonas, kapena mtsinje wa Amazon. Posapita nthaŵi, opanga mapu a m’zaka za zana la 16 anali kulemba dzina latsopano pamapu atsopano a South America—Amazon. Choncho nkhalango ya Amazon inabisala m’nthanthi, koma tsopano m’nkhalango imeneyo mukuchitika zenizeni zodetsa nkhaŵa.
[Mawu a M’munsi]
a Liwu lakuti “Aamazon” likuoneka kuti likuchokera ku liwu lachigiriki lakuti a, lotanthauza “alibe,” ndipo ma·zosʹ, limatanthauza “maŵere.” Malinga ndi nthanthi zakale, Aamazoni anachotsa bere lawo la kulamanja kuti azigwira bwino uta ndi muvi.
[Mawu a Chithunzi patsamba 11]
Pamwamba kumbuyoko: The Complete Encyclopedia of Illustration/J. G. Heck