Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g97 9/8 tsamba 9-11
  • Anthu Ophunzitsidwa Kukondana

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Anthu Ophunzitsidwa Kukondana
  • Galamukani!—1997
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • “Dzivekeni Chikondi”
  • Kuchotsa Chidani Nkuikapo Chikondi
  • Posachedwa Chidani Chidzapitiratu Kwamuyaya
  • Njira Yokhayo Yothetsera Chidani
    Nsanja ya Olonda—2000
  • “Nthawi ya Chikondi ndi Nthawi ya Chidani”
    Nsanja ya Olonda—2011
  • Kulani M’chikondi
    Nsanja ya Olonda—2001
  • “Pitirizani Kusonyeza Chikondi”
    Yandikirani Yehova
Onani Zambiri
Galamukani!—1997
g97 9/8 tsamba 9-11

Anthu Ophunzitsidwa Kukondana

CHIKONDI ndicho kukopeka ndi munthu wina, kukoma mtima, kapena anthu aŵiri kuchita chidwi ndi zinthu zofanana. Chikondi ndicho kuyanja wina kwambiri. Chilibe dyera, nchokhulupirika, ndipo chimakhala ndi nkhaŵa yofuna kuthandiza ena. Pali chikondi palibe chidani. Chimene chimalamulira munthu wodzaza chidani ndicho mkwiyo; munthu wolamulidwa ndi chikondi amalingalira ena.

Chikondi kapena chidani—kodi chimalamulira moyo wanu nchiyani? Funso limeneli nlofunika kwambiri chifukwa yankho lake mpamene padalira mtsogolo mwanu mosatha. Pamene akukhala m’dziko limene likuphunzitsidwa kudana, anthu mamiliyoni ambiri akuphunzira kukondana. Akuchita zimenezo mwa kuvala umunthu watsopano. Sakungolankhula za chikondi; akuyesetsa kuchitsata.

Ngati munapezekapo kale pamsonkhano wa Mboni za Yehova, mwina munachita chidwi ndi zimene munaona. Kaya zikhale za dziko liti, Mboni za Yehova nzogwirizana pa kulambira. Zimapangadi ubale wa dziko lonse lapansi. Mutha kuona zimenezi pamipingo yawo yakwanuko ndi pamisonkhano yawo yachigawo koma mwina makamaka m’malo omwe amatcha mabanja a Beteli. Ameneŵa ndi magulu a antchito odzifunira amene amakhala pamodzi ndi kugwira ntchito limodzi monga banja kupanga mabuku ofotokoza Baibulo ndi kuwafalitsa. M’dziko lililonse, ena a iwo amayang’anira ntchito yochitidwa ndi Mboni za Yehova kumeneko. Imeneyi si ntchito yaing’ono ayi, pakuti imakhudza—kuyambira 1997—mipingo yoposa 82,000 m’maiko 233. Kuti akwanitse zimenezi, anthu oposa 16,000 akutumikira m’mabanja a Beteli padziko lonse lapansi, kuphatikizapo kumalikulu a dziko lonse ndi nthambi zina zazing’ono m’maiko 103.

Mabanja ambiri a Beteli apangidwa makamaka ndi nzika za dziko limene muli nthambiyo. Koma si okhawo. Mabanja ena a Beteli apangidwa ndi Mboni za kumaiko kapena mafuko osiyanasiyana ndiponso zimene kale zinali m’zipembedzo zosiyanasiyana. Mwachitsanzo, m’banja la Beteli la anthu pafupifupi 1,200 la ku Selters, Germany, muli anthu a kumaiko ngati 30. Kodi nchiyani chimawatheketsa kukhalira limodzi, kugwira ntchito, ndi kulambira pamodzi mwamtendere ndi umodzi, popanda chidani? Iwo akutsatira uphungu wa Baibulo pa Akolose 3:14, umene umati:

“Dzivekeni Chikondi”

Kulibe munthu amene amabadwa ndi zovala, ndipo munthu samavala zovala mwa kungolankhula za izo. Kuti munthu adziveke afunika kusankha zinthu zotsimikizika ndiyeno nkuyesetsa kuzichita. Momwemonso, palibe amene amabadwa atavala chikondi. Kungolankhula za icho si kokwanira. Pafunikira khama.

Zovala zili ndi ntchito zingapo. Zimateteza thupi, zimabisa mbali za thupi zosaoneka bwino kapena zilema, ndipo pamlingo wina wake zimavumbula umunthu umene munthu ali nawo. Chimodzimodzi ndi chikondi. Chimateteza munthu chifukwa kukonda mapulinsipulo olungama kumamsonkhezera kupeŵa kuyanjana ndi anthu kapena kupeŵa malo amene angakhale angozi. Chimateteza maunansi athu ndi ena, amene timawaŵerengera kwambiri. Amene akonda adzakondedwa nayenso, ndipo iye amene amapeŵa kuvulaza ena nthaŵi zambiri sangavulale.

Chikondi chimabisanso mbali zosaoneka bwino za umunthu wathu, zimene zingasautse anthu anzathu. Kodi sitimakonda kunyalanyaza zophophonya zazing’ono za anthu omwe amakonda ena koposa za anthu omwe ali onyada, odzikuza, odzikonda, omwenso alibe chikondi?

Anthu omwe amadziveka chikondi (NW) amavumbula ukoma wa umunthu wonga wa Kristu. Pamene kukongola kwa kunja nkwachiphamaso chabe, kukongola kwauzimu kumakuta munthu yense. Mwina mukudziŵa anthu ena omwe mumati ngokongola, osati chifukwa cha maonekedwe awo akunja, koma chifukwa cha umunthu wawo wabwino kwambiri. Komanso, ife tonse takumanapo ndi akazi kapena amuna okongola omwe anataya kukongola kwawo konse titadziŵa bwino za umunthu wawo. Zimasangalatsa kwambiri kukhala ndi anthu omwe adziveka chikondi!

Kuchotsa Chidani Nkuikapo Chikondi

Zopezedwa pa kufufuza kochitidwa mu 1994 pa Mboni za Yehova 145,958 ku Germany zikusonyeza kuti chidani chingachokepo nkuloŵedwa m’malo ndi chikondi.

Kumwetsa moŵa, anamgoneka, upandu, juga, ndi kupulupudza kapena chiwawa, zonsezo zili mbali zosiyanasiyana za kudzikonda, zimene mosavuta zingabutse chidani. Koma 38.7 peresenti ya omwe anafunsidwa anatero kuti pofuna kukwanitsa malamulo apamwamba a Baibulo omwe Mboni zimatsata, sanachitire mwina kusiyapo kugonjetsa limodzi kapena ambiri a mavutowa. Kukonda Mulungu ndi malamulo ake olungama a khalidwe kunawasonkhezera kutero. Omwe anawathandiza mwachikondi anali Mboni za Yehova, nthaŵi zambiri payekhapayekha. Pazaka zisanu zapitazo (1992-1996), anthu 1,616,894 m’maiko 233 anathandizidwa kusintha, akumagonjetsa chidani ndi chikondi chopambana pa zonse.

Mwa kugwiritsira ntchito chikondi chopanda dyera m’maukwati awo, Mboni za Yehova zimakhala ndi maunansi olimba. M’maiko ena, ukwati umodzi pa aŵiri kapena atatu alionse umatha. Koma kufufuza kotchulidwako kunasonyeza kuti pakali pano ndi Mboni zokwana 4.9 peresenti zokha zomwe zinasudzulana kapena kupatukana ndi anzawo. Komabe, tisaiŵale kuti chiŵerengero chachikulu mwa ameneŵa anasudzulana asanakhale Mboni za Yehova.

Popeza Mulungu wachikondi ali Mlangizi Wamkulu amene amaphunzitsa omkonda njira zake, Mboni za Yehova choyamba zimakonda iye. Kusiyana ndi anthu ena, amene angakhale “okonda zokondweretsa munthu, osati okonda Mulungu,” Mboni za Yehova zimaika Mulungu patsogolo. (2 Timoteo 3:4) Kusiyana ndi dziko lopanda khalidweli, Mboni iliyonse imawononga maola 17.5 mlungu uliwonse pantchito za chipembedzo. Mwachionekere, Mboni zimakonda zauzimu. Zimenezo nzimene zimawapatsa chimwemwe. Yesu anati: “Achimwemwe ali awo ozindikira kusoŵa kwawo kwauzimu, popeza kuti ufumu wakumwamba uli wawo.”—Mateyu 5:3, NW.

Mtumiki woona wa Mulungu, akutero wolemba Salmo 118, sayenera kuopa anthu. “Yehova ndi wanga; sindidzaopa; adzandichitanji munthu?” (Vesi 6) Kukhulupirira Mulungu kotheratu kumachotsa umodzi wa mizu ya chidani ndi kuopa anthu ena.

Mkristu amene akudziŵa kuti Mulungu ali “wosapsa mtima msanga, ndi wochulukira chifundo ndi choonadi,” adzayesetsa kuchotsa mkwiyo pamoyo wake, popeza ungakhale muzu wina wa chidani. Kukhala ndi zipatso za mzimu wa Mulungu, kuphatikizapo chifatso ndi kudziletsa, kudzamthandiza kukhoza pa zimenezi.—Salmo 86:15; Agalatiya 5:22, 23.

Mkristu woona ngwofatsa ndipo samadzikweza konse. (Aroma 12:3) Amasonyeza chikondi pochita ndi ena. Kusiyana ndi chidani, chikondi “sichipsa mtima, sichilingirira zoipa.”—1 Akorinto 13:5.

Inde, mantha, mkwiyo, kapena kuopa kuvulala zingapangitse anthu kudana. Koma chikondi, mwa kuchotsa maziko a chidani, chimalaka chidani. Ntheradi, chikondi ndicho mphamvu yolimba koposa m’chilengedwe chifukwa “Mulungu ndiye chikondi.”—1 Yohane 4:8.

Posachedwa Chidani Chidzapitiratu Kwamuyaya

Dyera ndi chidani sizingakhaleko kwamuyaya popeza sindizo umunthu wa Yehova Mulungu. Ziyeneradi kuchotsedwapo, kuti chikondi, chimene chidzakhala kosatha, chitenge malo. Ngati mukufuna dziko lopanda chidani, ndipo lodzala chikondi, pemphani Mboni za Yehova zikufotokozereni m’Baibulo zofunika kuti mudzakhalemo m’dzikolo.

Inde, tingachite bwino kudzifunsa yense payekha kuti, ‘Kodi ndi khalidwe liti lomwe limalamulira moyo wanga, chikondi kapena chidani?’ Funso limeneli nlofunika kwambiri. Mtima umene umagunda moyanja mdani wa Mulungu, mulungu wa chidani, sudzagunda nthaŵi yaitali. Mtima umene umagunda moyanja Yehova, Mulungu wachikondi, udzagunda kosatha!—1 Yohane 2:15-17.

[Chithunzi patsamba 10]

Ngakhale makono anthu angadziveke chikondi

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena