Miliri—Chizindikiro cha Mapeto?
KODI miliri ya m’tsiku lathu imasonyeza kuti mapeto a dziko ali pafupi? Tisanayankhe funso limenelo, choyamba tilingalirepo za tanthauzo la mawu akuti “mapeto a dziko.”
Ambiri amakhulupirira kuti mapeto adziko amatanthauza kuti Mulungu adzawononga dziko ndi zamoyo zonse zili pamenepo. Komabe, Mawu a Mulungu amanena kuti iye “analiumba [dziko lapansi kuti] akhalemo anthu.” (Yesaya 45:18) Chifuno chake ndicho kulidzaza ndi anthu athanzi, achimwemwe okhala ndi chilakolako chotsatira malamulo ake olungama. Motero mapeto adziko satanthauza kutha kwa nthaka ndi zonse zokhalapo. M’malo mwake, zimatanthauza kutha kwa dongosolo lino la zinthu ndi okhalamo amene amakana kuchita chifuniro cha Mulungu.
Izi zinasonyezedwa ndi mtumwi Petro yemwe analemba kuti: “Dziko lapansi la masiku aja [m’masiku a Nowa], pomizika ndi madzi, lidawonongeka.” Pamene dziko linawonongeka m’tsiku la Nowa, anali anthu oipa amene anawonongeka. Nthaka ndi Nowa wolungama pamodzi ndi banja lake zinalipobe. Monga momwe Petro akupitirizira, Mulungu adzachitaponso kanthu mtsogolo kubweretsa “chiwonongeko cha anthu osapembedza.”—2 Petro 3:6, 7.
Malemba ena a m’Baibulo amachirikiza lingaliro limeneli mosalekeza. Mwachitsanzo, Miyambo 2:21, 22 imati: “Oongoka mtima adzakhala m’dziko, angwiro nadzatsalamo. Koma oipa adzalikhidwa m’dziko, achiwembu adzazulidwamo.”—Onaninso Salmo 37:9-11.
Miliri ndi Mapeto a Dziko
Koma kodi izi zidzachitika liti? Ophunzira a Yesu anayi anamfunsa choncho. Iwo anati: “Chizindikiro cha kufika kwanu nchiyani, ndi cha mathedwe a nthaŵi ya pansi pano [kapena, monga mmene mabaibulo ena amanenera, “mapeto a dziko lapansi”]?” Yesu anayankha kuti: ‘Mtundu umodzi wa anthu udzaukirana ndi mtundu wina, ndi ufumu ndi ufumu wina; ndipo kudzakhala njala ndi zivomezi m’malo akutiakuti.’ (Mateyu 24:3, 7) M’nkhani yofanana nayo pa Luka 21:10, 11, Yesu anawonjezera kuti: ‘Kudzakhala . . . miliri m’malo akutiakuti, . . . ndipo kudzakhala zoopsa ndi zizindikiro zazikulu zakumwamba.’
Onani kuti Yesu sananene kuti miliri yokha idzasonyeza kuti mapeto ayandikira. M’malo mwake anaphatikizapo nkhondo zikuluzikulu, zivomezi ndi kupereŵera kwa chakudya. Mu ulosi wake watsatanetsatane wopezeka pa Mateyu 24 ndi 25, Marko 13 ndi Luka 21, Yesu ananeneratu zinthu zina zambiri zimene zidzachitika. Zonsezo zinayenera kuchitika pamodzi Mulungu asanachitepo kanthu kuthetsa kuipa padziko lapansi. Pali umboni wokwanira bwino wakuti tikukhala m’nthaŵi imeneyo.
Paradaiso Yemwe Akudza
Sikuti anthu adzatha padziko mtsogolo, kaya ndi miliri kapena mwa dzanja la Mulungu. Yehova Mulungu amalonjeza kusandutsa dzikoli kukhala paradaiso. (Luka 23:43) Adzathetsanso matenda amene amasakaza anthu.
Timatsimikizira zimenezi tikamalingalira za utumiki wa Yesu Kristu, amene anasonyeza mikhalidwe ya Atate wake mwangwiro. Atapatsidwa mphamvu ndi Atate wake wakumwamba, Yesu anachiritsa omwe anali olemala, akhungu, ngakhalenso agonthi. (Mateyu 15:30, 31) Anachiritsanso amene anagwidwa ndi khate. (Luka 17:12-14) Anachiritsa mkazi yemwe anali kukha mwazi, munthu wadzanja lopuwala, ndi munthu wambulu. (Marko 3:3-5; 5:25-29; Luka 14:2-4) Anachiritsa anthu “akhunyu, ndi amanjenje.” (Mateyu 4:24) Katatu anadzutsa akufa!—Luka 7:11-15; 8:49-56; Yohane 11:38-44.
Kuchiritsa kozizwitsa kumeneku kumasonyeza kudalirika kwa lonjezo la Mulungu lakuti mtsogolo mmene iye akukonza, “wokhalamo sadzanena, Ine ndidwala.” (Yesaya 33:24) Sizidzachitikanso kuti miliri iwononge thanzi ndi miyoyo ya anthu. Ndife othokoza chotani nanga kuti Mlengi wathu wachikondi ali ndi mphamvu ndiponso akufuna kuchotseratu matenda, kwamuyaya!—Chivumbulutso 21:3, 4.
[Zithunzi patsamba 9]
Yesu anapatsidwa mphamvu ndi Mulungu kuchiritsa odwala
[Chithunzi patsamba 10]
M’Paradaiso wapadziko lapansi akudzayo, Yehova adzathetsa matenda