Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g97 12/8 tsamba 21-23
  • Kodi Chingamkhalire Bwino Mwana Nchiyani?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Chingamkhalire Bwino Mwana Nchiyani?
  • Galamukani!—1997
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Njira Zina Zosamalira Nkhani ya Woyenera Kusunga Ana
  • Mafunso Omwe Angabukepo
  • Woyenera Kusunga Ana—Kuiona Bwino Nkhaniyo
    Galamukani!—1997
  • Chisudzulo Chiridi ndi Minkhole
    Galamukani!—1991
  • Woyenera Kusunga Anah—Chipembedzo ndi Lamulo
    Galamukani!—1997
  • Mmene Kutha Kwa Banja Kumakhudzira Ana
    Mfundo Zothandiza Mabanja
Onani Zambiri
Galamukani!—1997
g97 12/8 tsamba 21-23

Kodi Chingamkhalire Bwino Mwana Nchiyani?

KODI tisudzulane kapena tisasudzulane? Funso limenelo nlovuta kwambiri kwa anthu ambiri okwatirana amene saali achimwemwe. Zaka zambiri zapitazo anthu anali kunyansidwa nacho chisudzulo, ngakhale kuchitsutsa, pazifukwa za khalidwe ndi chipembedzo. Ndipo makolo ambiri osakondwa ndi ukwati wawo nthaŵi zambiri anali kukhalabe pamodzi chifukwa cha ana. Komabe, zinthu m’dzikoli zasintha kwambiri pazaka zaposachedwapa. Lero ambiri amavomereza chisudzulo.

Komabe, ngakhale kuti amavomereza chisudzulo, makolo ambiri, oweruza, asayansi ya chikhalidwe cha anthu, ndi ena akuda nkhaŵa ndi zimene chisudzulo chimachita kwa ana. Tsopano machenjezo ambiri akumveka. Maumboni ochuluka akusonyeza kuti chisudzulo chingawononge ana. Makolo akulimbikitsidwa kulingalira mmene chisudzulo chingawakhudzire iwo ndi ana awo. Sara McLanahan, katswiri wa za kakhalidwe ka anthu pa Yunivesite ya Princeton, ananena kuti “mwina pakati pa mabanja aŵiri mwa atatu ndi atatu mwa anayi amene amasudzulana ayenera kuyembekeza nthaŵi yaitali ndi kulingalirapo kwambiri ngati zimene akufuna kuchitazo zili zoyenera.”

Kufufuza kwa posachedwa kumasonyeza kuti ana a m’chisudzulo ambiri amatenga mimba, kusiya sukulu, kupsinjika maganizo, maukwati awo amatha, ndipo amakhala pakati pa aja amene amalandira thandizo ku boma. Kumadzulo, mwana mmodzi mwa asanu ndi mmodzi alionse amakhudzidwa ndi chisudzulo. M’buku lake lonena za ufulu wosunga mwana ku United States, wolemba mbiri Mary Ann Mason anati: “Zinali zotheka kuti khoti nkugamula mlandu wa mwana wobadwa mu 1990 wonena za kumene adzakhala ndi amene adzakhala naye.”

Zachisoni nzakuti chisudzulo sichimathetsa ndewu, pakuti makolo angapitirizebe kumalimbana m’makhoti kumenyera ufulu wosunga mwana ndi wocheza ndi mwana, zimene zimawonjezera nsautso ya ana awo. Nkhondo zimenezo m’makhoti odzala chidani zimayesa kukhulupirika kwa ana kwa makolo awo ndipo nthaŵi zambiri iwo amasoŵa chochita ndipo amakhala amantha.

Phungu wina pa zabanja anati: “Chisudzulo sichimapulumutsa ana. Inde, nthaŵi zina chimapulumutsa achikulire.” Koma zimene zimachitikadi nzakuti mwa kusudzulana, makolo amathetsa mavuto awo, kwinaku nkuvulaza ana awo, amene kwa moyo wawo wonse angamayese kuiŵala mavuto awo.

Njira Zina Zosamalira Nkhani ya Woyenera Kusunga Ana

Poti pamakhala chidani ndi kupsinjika maganizo ukwati utatha, nzovuta kwambiri kukambirana modekha ndipo mwanzeru za amene adzasunga mwana mtsogolo. Kuti achepetse kukangana kwa makolo ndi kupewa milandu yaudani, madera ena ali ndi njira zina zothetsera mikangano, monga ija yokambitsirana loya alipo kunja kwa bwalo la milandu.

Kutayendetsedwa bwino, kukambitsirana loya alipo kumalola makolo kupangana m’malo mosiyira mlanduwo woweruza kuti asankhe amene adzatenga ana. Ngati sizitheka kukambitsirana, makolowo atha kupanga makonzedwe ena a wosunga ana ndi kuwachezera kupyolera mwa maloya awo. Makolowo atangopangana ndi kulemberana panganolo, woweruza angasaine chikalata cholembapo zofuna zawo.

Pamene makolo sakuvomerezana pa makonzedwe a kasungidwe ka mwana, kaŵirikaŵiri malamulo m’maiko ambiri amapereka njira yotsimikiza kuti mwanayo adzasamalidwa bwino. Nkhaŵa yaikulu ya woweruza imakhala pa ana, osati pa makolo ayi. Woweruza amapenda mbali zambiri zofunika, monga zofuna za makolo, unansi wa mwanayo ndi makolo aŵiriwo, zimene mwana amakonda, ndi mphamvu ya makolo aŵiriwo yomsamalira tsiku ndi tsiku. Ndiyeno woweruza amasankha kumene mwana adzakhala ndi amene adzakhala naye ndiponso mmene makolowo angasankhire zinthu zazikulu zofunika pa tsogolo la mwanayo.

Ngati makonzedwe ngakuti kholo limodzi lokha lizisunga mwana, kholo limodzilo lingakhale ndi mphamvu yosankha zinthu. Koma ngati pali makonzedwe akuti makolo aŵiriwo angamasunge mwana, iwo ayenera kumvana pankhani zazikulu, monga thanzi la mwana ndi maphunziro ake.

Mafunso Omwe Angabukepo

Atapezeka mumlandu wokhudza kusunga mwana, makolo amene ali Mboni za Yehova ayeneranso kulingalira za zimene zingathandize mwana wawo mwauzimu. Mwachitsanzo, bwanji ngati kholo losakhala Mbonilo silikufuna kuti mwana aphunzitsidwe kalikonse ka m’Baibulo? Kapena bwanji ngati kuti kholo losakhala Mbonilo linachotsedwa mumpingo wachikristu?

Zochitika ngati zimenezi zingachititse kuti makolo achikristu apeze vuto posankha zochita. Amafuna kuchita mwanzeru ndi kuchita zoyenera, ndiponso amafuna kukhalabe ndi chikumbumtima chabwino kwa Yehova pamene alingalira mwapemphero za ubwino wa ana awo.

M’nkhani zotsatira, tidzapenda mafunso otsatirawa: Popatsa kholo ufulu wosunga mwana, kodi lamulo limati chiyani ponena za chipembedzo? Kodi mlandu wokhudza ufulu wosunga mwana ndingauthe bwanji? Kodi ndingapirire bwanji ngati sindinapatsidwe ufulu wosunga mwana? Kodi ndiyenera kuliona motani pangano loti aŵirife, ineyo ndi kholo lochotsedwa, tizisunga mwana?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena