Kupweteka Mtima Polola Mwana Kuchoka Panyumba
“Tsiku limene mwana wathu woyamba anabadwa, mwamuna wanga anandichenjeza—‘wokondedwa, kulera anaku ndiyo ntchito yotenga nthaŵi yaitali yokonzekera tsiku lopweteka mtima pamene mwana adzachoka panyumba.’”—Ourselves and Our Children—A Book by and for Parents.
MAKOLO ambiri amakondwa—nasangalala kwabasi—atabadwa mwana wawo woyamba. Ngakhale kuti kukhala kholo kumadza ndi zovuta zina, zopweteka, zokhumudwitsa, ndi nkhaŵa zosiyanasiyana, ana amadzetsa chimwemwe chachikulu. Pafupifupi zaka zikwi zitatu zapitazo, Baibulo linati: “Ana ndiwo cholandira cha kwa Yehova; chipatso cha m’mimba ndicho mphotho yake.”—Salmo 127:3.
Komabe, Baibulo limaneneratunso mawu otonthoza aŵa: “Mwamuna adzasiya atate wake ndi amake.” (Genesis 2:24) Pazifukwa zosiyanasiyana, ana akakula kaŵirikaŵiri amachoka panyumba—kupita kumaphunziro kapena kukagwira ntchito. Kukagwira ntchito yowonjezera utumiki wachikristu, kapena kukapeza banja. Koma makolo ena, zimenezi zimawapweteka mtima kwabasi. Pamene ana awo akuyesa kupeza ufulu wawo wachibadwidwe, iwo amaona ngati kumeneko ndi “kuwanyoza, kuwachita chipongwe, kuwakhumudwitsa, kuwanyazitsa, kuwaopseza kapena kuwanyanyala,” malinga ndi kunena kwa mlembi wina. Zimenezi kaŵirikaŵiri zimayambitsa mkangano ndi kusiyana maganizo kosatha pabanja. Makolo ena, poipidwa ndi tsiku limene ana awo adzachoka panyumba, amalephera kuthandiza anawo kukonzekera kudzadziimira paokha akakula. Zotsatira za kunyalanyaza koteroko zimakhala zomvetsa chisoni: anawo akakula amalephera kusamala nyumba, kusunga banja, ngakhalenso kusunga ntchito.
Kupweteka mtima polekana ndi mwana kumaŵaŵa kwambiri pamabanja a kholo limodzi. Karen, monga kholo lopanda mwamuna anati: “Mwana wanga wamkazi ndi ine timakondana kwabasi; ndife mabwenzi enieni. Kulikonse kumene ndinkapita, ndinkamutenga iye.” Ubwenzi wokondana chotero pakati pa kholo ndi mwana ngwofala m’mabanja a kholo limodzi. Ndithudi, kuganiza zopatukana ndi bwenzi lotero kungakhaledi kodetsa nkhaŵa.
Komabe, buku lakuti Traits of a Healthy Family (makhalidwe a banja labwino) limakumbutsa makolo kuti: “Ndi mmene moyo wa banja wakhalira: umalera khanda lodalira pa iweyo limene tsiku lina lidzakusiya ndi kukadziimira palokha.” Kenako bukulo limachenjeza kuti: “Mavuto ambiri m’mabanja amabuka chifukwa makolo amalephera kulola ndi mtima wonse kuti anawo apite.”
Nanga bwanji za inuyo? Kodi ndinu kholo? Ngati muli kholo, kodi mwalikonzekera tsikulo limene mudzafunikira kulola ana anu kuchoka panyumba? Bwanji nanga za ana anu? Kodi mukuwathandiza kukonzekera kudzadziimira paokha?