Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g98 6/8 tsamba 8-11
  • Mapeto a Umphaŵi Ayandikira

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mapeto a Umphaŵi Ayandikira
  • Galamukani!—1998
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Umphaŵi ndi Chilamulo cha Mose
  • Yesu Ankasamalira Osauka
  • Chitetezo Tsopano
  • Sitidzakhala Nawo Kosatha
  • Tsanzirani Yesu Poganizira Osauka
    Nsanja ya Olonda—2006
  • Posachedwapa, Sikudzakhalanso Mmphaŵi!
    Nsanja ya Olonda—1995
  • Dziko Lopanda Umphawi Layandikira
    Nsanja ya Olonda—2005
  • Akapolo a Umphaŵi
    Galamukani!—1998
Onani Zambiri
Galamukani!—1998
g98 6/8 tsamba 8-11

Mapeto a Umphaŵi Ayandikira

KODI Yesu ankatanthauza chiyani pamene anati: “Nthaŵi zonse muli nawo aumphaŵi pamodzi nanu”? (Mateyu 26:11) Kodi ankatanthauza kuti kwamuyaya umphaŵi sudzatha, palibe njira iliyonse youthetsera?

Yesu ankadziŵa kuti panthaŵi yonse pamene anthu akhale akulamulira, umphaŵi udzakhalapo. Ankadziŵa kuti sungathetsedweretu ndi boma lamtundu uliwonse lopangidwa ndi anthu kaya mwanjira zachuma kapena zakakhalidwe za mtundu uliwonse. Ndipo mbiri yakale imapereka umboni wakuti ndimo zakhalira.

Zaka zonse zikwizikwi za mbiri ya anthu, boma lamtundu uliwonse ndi machitidwe alionse a zachuma ndi kakhalidwe zayesedwa, komabe umphaŵi tidakali nawo. Kunena zoona, ngakhale kuti pakhala kupita patsogolo pa zinthu zina monga sayansi, maindasitale, ndi zamankhwala, choona chake nchakuti padziko lonse chiŵerengero cha anthu osauka chikumka nchiwonjezereka.

Yesu ankadziŵa bwino zinthu zambiri zimene zimachititsa umphaŵi, monga njala, chilala, nkhondo, maboma oipa, kusagwiritsira ntchito bwino chuma, kupondereza osauka ndi ofooka kochitidwa ndi anthu olemera ndi okhala ndi ulamuliro, ngozi ndi matenda, ndi kumwalira kwa mwamuna m’nyumba amene amasiya ana ndi mkazi akumasauka. Ndiponso, ankadziŵa kuti anthu akhoza kumadzibweretsera umphaŵi pa iwo okha ndi mabanja awo chifukwa cha makhalidwe oipa monga ulesi, uchidakwa, juga, ndi kumwa mankhwala osokoneza bongo.

Motero pamene Yesu ankati “muli nawo aumphaŵi nthaŵi zonse pamodzi nanu,” ankatanthauza kuti kuthetsa umphaŵi nkovuta kwakuti mabungwe osiyanasiyana amene alipo m’dziko sangakuthe. Ankatanthauza kuti malinga ngati anthu akupitiriza kulamulira, padzakhala anthu osauka.

Ngakhale kuti vuto la umphaŵi nlakale, sitiyenera kunena kuti Yesu kapena Atate ake akumwamba salabadira za osauka. Komanso sitiyenera kunena kuti umphaŵi sudzatha chifukwa cha mawu a Yesu. Izi nzowonekeratu malinga ndi zimene Baibulo limanena pankhaniyi.

Umphaŵi ndi Chilamulo cha Mose

Mwachitsanzo, talingalirani Chilamulo chimene Mulungu anapereka kwa mtundu wa Israyeli wakale kupyolera mwa Mose. Mfundo imodzi m’Chilamulocho inali yakuti banja lililonse la Chiisrayeli lipatsidwe malo m’Kanani. (Deuteronomy 11:8-15; 19:14) Okha amene sanalandireko anali Alevi. M’malo mwake, chifukwa cha ntchito yapadera imene ankagwira pakachisi, ankathandizika mwa kulandira chachikhumi cha zotuta za m’dzikomo.—Numeri 18:20, 21, 24.

Kuwonjezera apo, malamulo a cholowa pansi pa Chilamulo cha Mose ankati malo amene agaŵiridwa anayenera kupitirizabe kukhala a banjalo kapena a fuko limene linagaŵiridwalo. (Numeri 27:8-11) Ngakhale ngati munthu wagulitsa munda wake, unkakhala wa wogulayo kwa nthaŵi yochepa chabe. Panthaŵi yake mundawo unkaperekedwa kwa banja la amene anagulitsayo.

Kwa amene ankasauka pazifukwa zosiyanasiyana, monga kusatha kusamalira bwino munda wawo kapena kusakaza chuma chawo, Chilamulo chinkati azikunkha chakudya m’minda, m’minda ya zipatso, ndi m’minda yamphesa ya ena. (Levitiko 23:22) Ndiponso, m’Israyeli wosauka , ankatha kukongola ndalama ndipo pobwezera sankapereka chiwongola dzanja. Ndithudi, anayenera kuonetsa mzimu wa kuwolowa manja kulinga kwa osauka.—Eksodo 22:25.

Yesu Ankasamalira Osauka

Zaka mazana ambiri pambuyo pake pamene Yesu anabwera padziko lapansi, anapitiriza kusonyeza mzimu wa kuwolowa manja umene anauphunzira kwa Atate wake, Yehova. Yesu anali ndi chidwi ndi omwe anali osauka mwakuthupi. Iye pamodzi ndi ophunzira ake anali ndi thumba limene ankaligwiritsira ntchito kugaŵira Aisrayeli osauka.—Yohane 12:5-8.

Yesu ataphedwa, Akristu anapitiriza kusonyeza mzimu womwewo kwa osauka pamene ankapereka chithandizo kwa osauka makamaka kwa abale ndi alongo awo auzimu. (Aroma 15:26) Lerolino Akristu oona amasonyezana chikondi mofananamo.

Nzoonadi kuti ngakhale Baibulo limanena za otsenderezedwa mowamvera chisoni, limadzudzula amene, chifukwa cha ulesi, ‘amadya nyama yawo.’ (Mlaliki 4:1, 5) Mtumwi Paulo analemba kuti: “Ngati munthu safuna kugwira ntchito, asadyenso.” (2 Atesalonika 3:10) Mofananamo, amene amawononga ndalama pa makhalidwe oipa monga kumwa mankhwala osokoneza bongo, fodya, uchidakwa amasauka. Izi nzotsatirapo za makhalidwe awo oipa; kwenikweni ‘akututa chimene anafesa.’—Agalatiya 6:7.

Chitetezo Tsopano

Baibulo limasonyeza kuti Mulungu ali ndi chidwi ndi kakhalidwe ka awo amene amayesetsa kuchita chifuniro chake. Mwachitsanzo, pa Salmo 37:25, Davide anati: “Ndinali mwana ndipo ndakalamba: ndipo sindinapenya wolungama wasiyidwa, kapena mbumba zake zilinkupempha chakudya.” Awo amene ali okonda chilungamo salonjezedwa chuma, koma pano pakusonyeza kuti Mulungu adzatsimikizira kuti ali ndi zinthu zofunika kuti akhale ndi moyo. Ndipo vesi 28 la salmo lomwelo limati: “Yehova akonda chiweruzo, ndipo sataya okondedwa.”

Yesu anachita zambiri zoposa kungosonyeza chifundo kwa osauka ndi kuwathandiza mwakuthupi pamene anali ndi moyo padziko lapansi. Anawatsimikizira kuti malinga ngati akuyesetsa kuchita chifuniro cha Mulungu, Mulungu adzaonetsetsa kuti akuwapatsa zinthu zofunikitsitsa pa miyoyo yawo, tsopano ndi mtsogolo. Yesu ananena zotsatirazi:

“Yang’anirani mbalame za kumwamba, kuti sizimafesa ayi, kapena sizimatema ayi, kapena sizimatutira m’nkhokwe; ndipo Atate wanu wa Kumwamba azidyetsa. Nanga inu mulibe kusiyana nazo kuziposa kodi? . . . Ndipo muderanji nkhaŵa ndi chovala? Tapenyetsani maluwa a kuthengo, makulidwe awo; sagwiritsa ntchito, kapena sapota: koma ndinena kwa inu, kuti angakhale Solomo mu ulemerero wake wonse sanavala monga limodzi la ameneŵa. Koma ngati Mulungu aveka chotero maudzu a kuthengo, akhala lero, ndi maŵa oponyedwa pamoto, nanga si inu kopambana ndithu, inu akukhulupirira pang’ono? Chifukwa chake musadere nkhaŵa, ndi kuti, Tidzadya chiyani? kapena, Tidzamwa chiyani? kapena, Tidzavala chiyani? . . . Pakuti Atate wanu wa Kumwamba adziŵa kuti musoŵa zonse zimenezo.”—Mateyu 6:26-32.

Yesu anamaliza mwa kulimbikitsa ophunzira ake kuti: “Koma muthange mwafuna Ufumu wake [wa Mulungu] ndi chilungamo chake, ndipo zonse zimenezo zidzawonjezedwa kwa inu.” (Mateyu 6:33) Ndi chilimbikitso chabwino chotani kwa amene ali osauka koma akufuna kuchita chifuniro cha Mulungu! Onaninso kuti Yesu anasonyeza kuti Ufumu wa Mulungu ndiwo unali woyenera kukhala chinthu chofunika choyamba m’moyo wa otsatira ake. Yesu anadziŵa kuti pamene Ufumu wakumwamba wa Mulungu udzayamba kulamulira dziko lonse lapansi—pokhapo—mpamene umphaŵi ungathetsedweretu.

Sitidzakhala Nawo Kosatha

Motero, Yesu anapereka chiyembekezo chamtsogolo chodabwitsa. Choncho pamene anati “nthaŵi zonse muli nawo aumphaŵi pamodzi nanu,” ankatanthauza za moyo wa nthaŵi ino ya dongosolo la zinthu lolamulidwa ndi anthu. Sankanena za moyo wamtsogolo mu ulamuliro wa Ufumu wakumwamba wa Mulungu. Baibulo limalosera kuti: “Sadzaiŵalika nthaŵi zonse waumphaŵi, kapena chiyembekezo cha ozunzika sichidzawonongeka kosatha.” (Salmo 9:18) Ndipo monga Mfumu mu Ufumu wa Mulungu, Kristu Yesu sadzalekerera aliyense amene adzayese kudyerera anzake masuku pamutu ndi kupondereza ena.

Yesu anapanga ulamuliro wa Ufumu wakumwamba wa Mulungu kukhala mutu wa chiphunzitso chake. (Mateyu 4:17) Mu ulamuliro wa Ufumuwo, zinthu pano padziko lapansi zizidzasonyeza mmene zilili kumwamba. Nchifukwa chake anaphunzitsa ophunzira ake kumapemphera kwa Mulungu kuti: “Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga Kumwamba chomwecho pansi pano.”—Mateyu 6:10.

Kodi zimenezi zidzachitika motani? Ncholinga cha Mulungu kufafaniza dongosolo lonse la zinthu lilipoli padziko lapansi lolamulidwa ndi anthu kuti Ufumu wakumwamba uloŵe mmalo mwake. Ulosi wopezeka pa Danieli 2:44 umati: “Masiku a mafumu aja [amene alipo tsopanoŵa] Mulungu wa Kumwamba adzaika ufumu woti sudzawonongeka ku nthaŵi zonse, ndi ulamuliro wake sudzasiyidwira mtundu wina wa anthu [anthu sadzalamuliranso], koma udzaphwanya ndi kutha maufumu awo onse [alipo leroŵa], nudzakhala chikhalire.”

Ndiye, m’dziko latsopano pansi pa ulamuliro wa Ufumu wa Mulungu, dziko lonse lapansi lidzapangidwa kukhala paradaiso wokhala ndi zinthu zambiri, osaonekanso kachisonyezero kalikonse ka umphaŵi. Onani maulosi ena a Baibulo onena za mmeme zinthu zidzakhalira panthaŵiyo:

“Yehova wa makamu adzakonzera anthu ake onse phwando la zinthu zonona, phwando la vinyo wa pamitsokwe, la zinthu zonona za mafuta okhaokha.” (Yesaya 25:6) “M’dzikomo mudzakhala dzinthu dzochuluka pamwamba pa mapiri; zipatso zake zidzati waa.” (Salmo 72:16) “Padzakhala mivumbi ya madalitso. Ndi mitengo ya kuthengo idzapereka zobala zawo, ndi nthaka idzapereka zipatso zake, ndipo adzakhazikika m’dziko mwawo.” (Ezekieli 34:26, 27) “Dziko lapansi lapereka zipatso zake: Mulungu, Mulungu wathu adzatidalitsa.” (Salmo 67:6) “Chipululu ndi malo ouma adzakondwa; ndipo dziko loti se lidzasangalala ndi kuphuka ngati duŵa.”—Yesaya 35:1.

Ndiponso, Mika 4:4 amalonjeza kuti: “Adzakhala munthu yense patsinde pa mpesa wake, ndi patsinde pa mkuyu wake; ndipo sipadzakhala wakuwaopsa.” Onse adzakhala ndi nyumba: “Iwo adzamanga nyumba ndi kukhalamo . . . Iwo sadzamanga, ndi wina kukhalamo.” (Yesaya 65:21, 22) Nzosadabwitsa kuti Yesu analonjeza amene amakhulupirira ziphunzitso zake kuti: “Udzakhala ndine m’Paradaiso”!—Luka 23:43.

Inde, Mawu ake ouziridwa a Mulungu amatiphunzitsa momvekera bwino kuti umphaŵi udzatheratu. Ndipo nthaŵi imeneyo ikuyandikira, popeza maulosi a Baibulo amasonyeza kuti dzikoli tsopano lili “m’masiku otsiriza,” likukumana ndi “nthaŵi zoŵaŵitsa.” (2 Timoteo 3:1-5, 13) Posachedwapa dongosolo la zinthu lilipoli lidzachotsedwa kwamuyaya ndipo umphaŵi udzachotsedwa kwamuyaya—osati mwa zoyesayesa za anthu koma mwa kuloŵererapo kwa Mulungu. Mfumu Yesu Kristu “adzapulumutsa waumphaŵi wopfuulayo; ndi wozunzika amene alibe mthandizi. Adzachitira nsoni wosauka ndi waumphaŵi, nadzapulumutsa moyo wa aumphaŵi.”—Salmo 72:12, 13.

[Chithunzi pamasamba 8, 9]

M’dziko latsopano la Mulungu, mudzakhala nyumba zabwino ndi chakudya chochuluka cha onse

[Chithunzi patsamba 10]

M’dziko lapansi latsopano, sikudzakhala ana anjala

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena