Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g98 7/8 tsamba 10-14
  • Mboni za Yehova—Zinalimba Mtima Poyang’anizana ndi Chiopsezo cha Anazi

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mboni za Yehova—Zinalimba Mtima Poyang’anizana ndi Chiopsezo cha Anazi
  • Galamukani!—1998
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Sizinagwirizane ndi Hitler
  • Kuona pa Zakumbuyo
  • Kodi Chinachitika Nchiyani Pamene Hitler Anatenga Ulamuliro?
  • Mboni Zichitapo Kanthu Molimba Mtima
  • Msonkhano wa Kulimba Mtima Kapena Kugonja?
  • Mawu a Kutsimikiza Mtima
  • Kuvumbula Zoipa za Nazi
    Galamukani!—1995
  • Okhulupirika Olimba Mtima Anapambana Chizunzo cha Nazi
    Nsanja ya Olonda—2001
  • Chimene Matchalitchi Anakhalira Chete
    Galamukani!—1995
  • “Anthu Olimba Mtima Ofunika Kuwayamikira”
    Nsanja ya Olonda—2011
Galamukani!—1998
g98 7/8 tsamba 10-14

Mboni za Yehova—Zinalimba Mtima Poyang’anizana ndi Chiopsezo cha Anazi

YOLEMBEDWA NDI MTOLANKHANI WA GALAMUKANI! KU GERMANY

MBONI ZA YEHOVA zimadziŵika kwambiri chifukwa cha kutsatira kwawo mosamalitsa Mawu a Mulungu, Baibulo. Nthaŵi zambiri zimenezi zimafuna kulimba mtima, ndipotu zimakhudza miyoyo yawo ndi maunansi awo ndi ena.

Mwachitsanzo, Mboni zimalemekeza anthu a mafuko onse. Zimakonda Mulungu ndi anansi awo. (Mateyu 22:35-40) Inde, zimagwirizana kwambiri ndi mtumwi Petro, yemwe anati: “Zoona ndizindikira kuti Mulungu alibe tsankhu; koma m’mitundu yonse, wakumuopa Iye ndi wakuchita chilungamo alandiridwa naye.”—Machitidwe 10:34, 35.

Mboni za Yehova zimadziŵikanso padziko lonse chifukwa cha kumvera kwawo malamulo, kusunga bata, ndi kulemekeza boma. Sizinakhalepo gwero la chipanduko ndipo sizidzatero. Zimenezi zili tero ngakhale pamene zizunzidwa m’maiko ena chifukwa chotsatira kaimidwe ka atumwi kakuti: “Tiyenera kumvera Mulungu koposa anthu.” (Machitidwe 5:29; Mateyu 24:9) Panthaŵi imodzimodziyo, Mboni zimazindikira ufulu wachibadwidwe umene ena ali nawo wolambira mogwirizana ndi zimene chikumbumtima chawo chimawauza.

Mbiri yakale imachitira umboni za kulimba mtima kwachikristu kwa Mboni za Yehova ku Germany ndi maiko ena omwe ankalamuliridwa ndi Adolf Hitler. Chochitika chosaiŵalika ku Berlin, Germany, mu 1933 chimasonyeza kulimba mtima kwawo, kukonda kwawo Mulungu ndi mnansi, ndi kulemekeza kwawo malamulo, bata, ndi ufulu wa chipembedzo.

Sizinagwirizane ndi Hitler

Ulamuliro wa Hitler wazaka 12 umene unali wankhanza, watsankhu, ndi wambanda unatha zaka zoposa 50 zapitazo. Komabe, nkhanza zimene ulamuliro wa Nazi unachita zapweteka anthu mpaka lero.

Mbiri yakale imachitira umboni kuti ndi magulu oŵerengeka okha amene molimba mtima anatsutsa nkhalwe ya Nazi. Ena mwa iwo anali Mboni za Yehova, zofotokozedwa kukhala “kagulu kosagonja [pakhalidwe] pakati pa mtundu wamantha.” Akatswiri olemekezeka olemba mbiri amachitira umboni za kulimba mtima kwawo.

Komabe, otsutsa angapo, kuphatikizapo ena omwe kale ankagwirizana ndi Mboni za Yehova, amanena kuti Mbonizo zinayesa kugwirizana ndi ulamuliro wa Hitler kuchiyambi kwake. Amati oimira Watch Tower Society anayesa mosaphula kanthu kuchita mkomya ku boma latsopanolo ndi kuti, kwanthaŵi ndithu, anavomereza chiphunzitso cha ufuko cha Anazi, chimene pomaliza pake chinaphetsa Ayuda mamiliyoni asanu ndi limodzi.

Zinenezo zoopsa zimenezi ndi bodza lamkunkhuniza. Otsatirawa ndi mafotokozedwe osabisa a zochitika zotchulidwazo, malinga ndi maumboni omwe alipo ndi mbiri yakale.

Kuona pa Zakumbuyo

Mboni za Yehova zakhala zokangalika ku Germany kwazaka zoposa 100. Podzafika mu 1933, m’Germany yense munali Mboni pafupifupi 25,000 zolambira Yehova Mulungu ndi kugaŵira mabuku ofotokoza Baibulo.

Ngakhale kuti malamulo a Germany panthaŵiyo anapereka ufulu, Mboni za Yehova nthaŵi zambiri zinkanenezedwa, makamaka ndi adani awo a zipembedzo zina. Kuyambira mu 1921, Mbonizo, zotchedwa panthaŵiyo Ernste Bibelforscher (Ophunzira Baibulo Akhama), zinanenezedwa kuti zimagwirizana ndi Ayuda pofuna kugwetsa boma. Ophunzira Baibulowo anatchedwa “akapirikoni [oopsa] a Ayuda” ochirikiza Chikomyunizimu, ngakhale kuti panalibe umboni wa zinenezo zimenezo. Katswiri wa zaumulungu wa ku Switzerland Karl Barth pambuyo pake analemba kuti: “Kunena kuti Mboni za Yehova nzogwirizana ndi ochirikiza Chikomyunizimu kungakhale chabe chifukwa chosazimvetsa kapena lingakhalenso dala.”

Magazini ena a tchalitchi ku Germany ananena kuti Mboni ndi Ayuda ankapangira limodzi chiwembu choukira boma. Poyankha, magazini yachijeremani ya The Golden Age ya April 15, 1930 (imene anadzakhala Galamukani!) inati: “Tilibe chifukwa choonera chinenezo chonama chimenechi ngati mwano—popeza ndife okhutira kuti Myuda alidi munthu wofunikabe mofanana ndi Mkristu wadzina lokha; koma tikukana bodza lotchulidwa m’magazini a tchalitchilo chifukwa cholinga chake ndicho kunyozetsa ntchito yathu, monga ngati kuti imachitidwa kuthandiza Ayuda m’malo mofalitsa Uthenga Wabwino.”

Chotero, profesa wa mbiri yakale John Weiss analemba kuti: “Mboni zinalibe utundu wachijeremani ndipo kwazaka mazana ambiri sizinavutike mtima chifukwa cha kusatembenuka kwa Ayuda. Mboni zinatsatirabe mwachangu chikhulupiriro chachikristu choyambirira chakuti zikope onse omwe zikanatha kuti atembenukire kwa Kristu.”

Kodi Chinachitika Nchiyani Pamene Hitler Anatenga Ulamuliro?

Pa January 30, 1933, Adolf Hitler anaikidwa kukhala mtsogoleri watsopano wa Germany. Poyamba, boma la Hitler linayesetsa kubisa chiwawa chake ndi nkhanza. Ndiye chifukwa chake, Mbonizo, limodzi ndi Ajeremani ena mamiliyoni ambiri kuchiyambi kwa 1933, anaona chipani cha National Socialist kukhala ulamuliro woyenera kulamulira panthaŵiyo. Mboni zinkayembekezera kuti boma la National Socialist (Nazi) likazindikira kuti gulu limeneli lachikristu lamtendere ndi lomvera lamulo silinali chiopsezo ku Bomalo. Zimenezi sizinatanthauze kunyalanyaza mapulinsipulo a Baibulo. Monga momwe zachitira m’maiko ena, Mboni zinafuna kudziŵitsa bomalo zenizeni ponena za kusaloŵa m’ndale kwa chipembedzo chawo.

Posakhalitsa zinaonekeratu kuti Mboni za Yehova zidzakhala pakati pa oyamba kuponderezedwa mwankhalwe ndi Anazi. Mboni zinanenezedwanso kuti zimapanga nawo chiwembu ochirikiza Chikomyunizimu ndi Ayuda. Kampeni yozizunza inayamba.

Kodi nchifukwa chiyani kagulu kakang’ono ngati kameneko kanaputa mkwiyo wa boma latsopanolo? Wolemba mbiri Brian Dunn akutchula zifukwa zazikulu zitatu: (1) kupezeka kwa Mbonizo padziko lonse, (2) kutsutsa kwawo ufuko, ndi (3) uchete wawo kulinga ku Boma. Chifukwa cha zikhulupiriro zawo za m’Malemba, Mboni zachijeremani zinakana kuchita suluti ya Hitler, kuchirikiza chipani cha National Socialist, kapena kumenya nawo nkhondo pambuyo pake.—Eksodo 20:4, 5; Yesaya 2:4; Yohane 17:16.

Chotero, Mboni zinapirira ziopsezo, kufunsidwa, kufufuza nyumba zawo, ndi nsautso zina za apolisi ndi a SA (Sturmabteilung ya Hitler, asilikali, kapena a Brownshirts). Pa April 24, 1933, akuluakulu a boma analanda ndi kutseka ofesi ya Watch Tower ku Magdeburg, Germany. Atalephera kupeza umboni wozengera mlandu pambuyo pofufuza, ndipo atakakamizidwa ndi Unduna Woona Nkhani Zakunja wa United States, apolisi anabwezera malowo. Komabe, podzafika mu May 1933, Mboni zinaletsedwa m’zigawo zochulukirapo za Germany.

Mboni Zichitapo Kanthu Molimba Mtima

Kumayambiriro a nyengo imeneyi, Hitler mochenjera anaonetsa kuti anali mchirikizi wa Chikristu. Analengeza kuti adzaonetsetsa kuti pali ufulu wa chipembedzo, nalonjeza kuti adzazichitira zipembedzo zachikristu “mwachilungamo.” Kuti aonetse zimenezo, mtsogoleri watsopanoyo ankaonekera m’matchalitchi. Iyi ndiyo nthaŵi imene anthu ambiri m’maiko amene pambuyo pake anadzachita nkhondo ndi Germany anachita chidwi ndi zipambano za Hitler.

Pakuda nkhaŵa ndi kukula kwa mavuto m’Germany, Joseph F. Rutherford, amene panthaŵiyo anali pulezidenti wa Watch Tower Society, limodzi ndi manijala wa ofesi ya nthambi ya Germany, Paul Balzereit, anaganiza zochita kampeni yodziŵitsa Mtsogoleriyo Hitler, akuluakulu a boma, ndi anthu onse kuti Mboni za Yehova sizimaopseza chitetezo cha Ajeremani ndi cha Boma. Mwachionekere Rutherford anaganiza kuti Hitler sanali kudziŵa za chiwawa chimene Mboni za Yehova zinali kuchitiridwa kapena kuti azipembedzo anamuuza zolakwika ponena za Mboni.

Chotero, ofesi ya ku Magdeburg inakonza msonkhano kuti agwiritsire ntchito ufulu wachibadwidwe wa nzika za Germany wopereka pempho ku boma. Nthaŵi itatha kale, Mboni za Yehova za m’Germany yense zinaitanidwa ku Wilmersdorfer Tennishallen ku Berlin pa June 25, 1933. Anayembekezera osonkhana pafupifupi 5,000. Ngakhale kuti zinthu zinali kuopsa, anthu olimba mtima oposa 7,000 anapezekapo. Osonkhana anavomereza chosankha cha mutu wakuti “Chikalata Cholengeza Mfundo.” Chikalata chimenechi chinatsutsa ziletso zimene zinaikidwa pa ntchito ya Mboni. Chinafotokoza bwino kaimidwe kawo ndi kukana zinenezo zakuti amagwirizana ndi magulu andale amtundu uliwonse ncholinga chopanduka. Chikalatacho chinati:

“Tanenezedwa monama kwa olamulira boma lino . . . Mwaulemu tikupempha olamulira dzikoli ndi anthu kulingalira bwino ndi mopanda tsankhu za mfundo zoperekedwa munomu.”

“Sitikulimbana ndi munthu aliyense kapena aphunzitsi achipembedzo, koma tikufuna kudziŵikitsa mfundo yakuti nthaŵi zambiri amene amati akuimira Mulungu ndi Kristu Yesu ndiwo amene amatizunza ndi kutineneza zonama ku maboma.”

Msonkhano wa Kulimba Mtima Kapena Kugonja?

Ena tsopano amanena kuti msonkhano wa ku Berlin wa 1933 ndi “Chikalata Cholengeza Mfundo” zili umboni wa kuyesetsa kwa Mboni zotchuka kuonetsa chichirikizo chawo ku boma la Nazi ndi kuda kwawo Ayuda. Koma zonena zawo si zoona. Zazikidwa pa chidziŵitso cholakwika ndi kupotoza choonadi.

Mwachitsanzo, otsutsa amanena kuti Mboni zinakometsera Wilmersdorfer Tennishallen ndi mbendera za swastika. Zithunzi za msonkhano wa 1933 zimasonyeza bwino lomwe kuti iwo sanaike mbendera za swastika m’holoyo. Mboni zoona ndi maso zikutsimikizira kuti munalibe mbendera mkatimo.

Komabe, nzotheka kuti kunja kwa nyumbayo kunali mbendera. Asilikali a Nazi anali atagwiritsira ntchito holoyo pa June 21, Lachitatu msonkhanowo usanayambe. Ndiyeno kutangotsala tsiku limodzi kuti msonkhanowo uyambe, makamu a achinyamata limodzi ndi magulu a SS (Schutzstaffel, amene poyamba anali mabodigadi a Hitler otchedwa Blackshirt), a SA, ndi ena anakondwerera tsiku la summer solstice pafupi. Chotero Mboni zofika pamsonkhano Lamlungu ziyenera kuti zinaona nyumbayo ili ndi mbendera za swastika.

Ngati kunali mbendera za swastika kunja kwa holoyo, m’khonde, kapena ngakhale mkati, Mboni zikanangozisiya. Ngakhale lero, pamene Mboni za Yehova zichita lendi nyumba za boma kuti zisonkhaniremo, sizimachotsa zizindikiro za dzikolo. Koma palibe umboni wakuti Mbonizo zinakweza zokha mbendera iliyonse kapena kuti zinazichitira suluti.

Otsutsa amanenabe kuti Mboni zinatsegulira msonkhano wawo ndi nyimbo ya fuko la Germany. Kwenikweni, msonkhanowo unayamba ndi Nyimbo 64 yakuti “Chiyembekezo Chaulemerero cha Ziyoni” ya m’buku la Mboni la nyimbo zachipembedzo. Mawu a nyimbo imeneyi anaimbidwa m’tchuni chopekedwa ndi Joseph Haydn mu 1797. Nyimbo 64 inali itakhala m’buku la nyimbo la Ophunzira Baibulo kuyambira cha m’ma 1905. Mu 1922 boma la Germany linatengera tchuni cha Haydn ndi kuikamo mawu a Hoffmann von Fallersleben kukhala nyimbo ya fuko lawo. Komabe, Ophunzira Baibulo ku Germany anaimbabe Nyimbo 64 yawo nthaŵi ndi nthaŵi, monga momwe anachitira Ophunzira Baibulo m’maiko ena.

Kuimbidwa kwa nyimboyo yonena za Ziyoni sikunganenedwe kukhala kuyesetsa kuchitira mkomya Anazi. Poumirizidwa ndi Anazi otsutsa Ayuda, matchalitchi ena anachotsa m’mabuku awo a nyimbo ndi a mapemphero mawu achihebri onga ngati “Yuda,” “Yehova,” ndi “Ziyoni.” Mboni za Yehova sizinatero. Panthaŵiyo olinganiza msonkhanowo sanayembekezere kupeza chiyanjo cha boma mwa kuimba nyimbo yotama Ziyoni. Mwinamwake, osonkhana ena angakhale atazengereza kuimba “Chiyembekezo Chaulemerero cha Ziyoni,” popeza tchuni cha nyimbo chopekedwa ndi Haydn chinali kufanana ndi cha nyimbo ya fukolo.

Mawu a Kutsimikiza Mtima

Pokhala boma linali kusintha ndipo dzikolo linali m’chipwirikiti, Mboni zinafuna kumveketsa bwino za kaimidwe kawo. Mwa kugwiritsira ntchito “Chikalata,” Mbonizo zinakana kwa mtu wagalu zinenezo zakuti zimalandira thandizo la ndalama kwa Ayuda ndi kuwachirikiza pa zandale. Ndiye chifukwa chake, chikalatacho chinati:

“Adani athu akutineneza monama kuti talandira ndalama kwa Ayuda kuti tithandizike pantchito yathu. Limenelo ndi bodza lamkunkhuniza. Mpaka ola lino, sitinalandirepo ngakhale ndi khobiri lomwe monga chopereka kuchokera kwa Ayuda.”

Pokhala chitafotokoza za ndalama, “Chikalata” chimenecho chinapitiriza kutsutsa ukatangale m’malonda aakulu. Chinati: “Ayuda abizinesi a ku Britain ndi America ndiwo akhala ndi Mabizinesi Aakulu ndipo awachita modyerera ndi kutsendereza anthu a mitundu yambiri.”

Mwachionekere mawu ameneŵa sankanena za Ayuda onse, ndipo nzachisoni ngati amvedwa molakwa ndiyeno nkukhumudwitsa ena. Ena anena kuti Mboni za Yehova zinali ndi chidani pa Ayuda chimene ambiri ankaphunzitsidwa m’matchalitchi a ku Germany panthaŵiyo. Zimenezi nzonama. M’mabuku awo ndiponso mwa khalidwe lawo panthaŵi ya Nazi, Mboni zinakana malingaliro otsutsa Ayuda ndipo zinatsutsa nkhanza imene Anazi ankachitira Ayuda. Ndithudi, kukomera kwawo mtima Ayuda omwe anali nawo m’misasa ya chibalo kumapereka chigomeko chotsutsiratu chinenezo chonama chimenechi.

“Chikalata” chimenecho chinafotokoza kuti ntchito ya Mboni ili yachipembedzo, chikumati: “Gulu lathu si landale ayi. Timalimbikitsa kuphunzitsa za Mawu a Yehova Mulungu kwa anthu.”

“Chikalata” chimenecho chinakumbutsanso boma za malonjezo ake. Mboni zinkachirikiza zolinga zapamwamba, ndipo zimenezo nzimenenso boma la Germany linkachirikiza poyera. Zina mwa zimenezo ndi mwambo wa banja ndi ufulu wa chipembedzo.

Ponena za zimenezi, “Chikalata” chimenecho chinawonjezera kuti: “Kupenda mosamalitsa mabuku athu kumavumbula kuti zolinga zapamwamba zomwe boma lilipoli la dziko lino limakhulupirira ndi kuchirikiza zikufotokozedwa, kuchirikizidwa ndi kugogomezeredwa kwambiri m’zofalitsa zathu, ndipo kumasonyeza kuti Yehova Mulungu adzaonetsetsa kuti onse okonda chilungamo afikira zolinga zapamwamba zimenezi.”

Chotero, Mboni sizinaonetse kuti zikuchirikiza Chipani cha Nazi. Ndiponso, potsata ufulu wa chipembedzo, sizinaganize zosiya kulalikira poyera.—Mateyu 24:14; 28:19, 20.

Malinga ndi nkhani ya mu 1974 Yearbook of Jehovah’s Witnesses, Mboni zina zachijeremani zinakhumudwa kuti mawu a “Chikalata” chimenecho sanali amphamvu. Kodi manijala wa ofesi ya nthambi, Paul Balzereit, angakhale atasukuluza mphamvu ya mawu a chikalatacho? Ayi, pakuti kuyerekezera mawu achijeremani ndi achingelezi kumasonyeza kuti sanatero. Malinga ndi umboni, zakumva zosiyana ndi zimenezo zinazikidwa pa zifukwa zongoganizira za ena amene sanakonzeko “Chikalata” chimenecho. Mbonizo zingakhalenso zitakhumudwa chifukwa choona kuti Balzereit anakana chikhulupiriro chake patangopita zaka ziŵiri zokha.

Tsopano nzodziŵika kuti Mboni za Yehova m’Germany zinali zitaletsedwa Loŵeruka, June 24, 1933, tsiku limodzi kuti msonkhano wa ku Berlin uyambe. Okonza msonkhanowo ndi apolisi anadziŵa za chiletso chimenechi patapita masiku angapo. Poona mmene zinthu zinalili zovuta ndi chidani choonekeratu cha akuluakulu a Nazi, nzodabwitsa kuti msonkhanowo unachitika. Sikukokomeza kunena kuti Mboni 7,000 molimba mtima zinaika chitetezo chawo pangozi mwa kupezeka pamsonkhanopo.

Msonkhanowo utatha, Mboni zinagaŵira makope 2,100,000 a “Chikalata” chimenecho. Mboni zina zinagwidwa nthaŵi yomweyo ndi kutumizidwa kumisasa ya chibalo. Motero, boma la Nazi linavumbuliratu mkhalidwe wake wopondereza ndi wachiwawa, ndipo posakhalitsa, linayamba kampeni youkira kagulu kakang’ono kameneka ka Akristu.

Profesa Christine King analemba kuti: “Anazi anali kudzadziŵa kuti nkhanza yachiwawa singathe kufafaniza Mboni.” Zinali monga momwe “Chikalata” chimenecho chinanenera kuti: “Mphamvu ya Yehova Mulungu njopambana ndipo kulibe mphamvu ina imene ingathe kumtsutsa.”a

[Mawu a M’munsi]

a Malo achepa oti tiperekere umboni wokwanira wa nkhani ya m’mbiri imeneyi. Komabe, pali mpambo wa malifalensi onse amene mungapatsidwe mutapempha ofalitsa magazini ano. Mungadziŵenso zambiri mutaonerera programu yapavidiyo yakuti Jehovah’s Witnesses Stand Firm Against Nazi Assault.

[Zithunzi patsamba 13]

Zithunzi za msonkhano umene Mboni za Yehova zinapezekapo mu 1933 ku Tennishallen

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena