Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g98 9/8 tsamba 16-17
  • Kumvetsera ndi Maso Anu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kumvetsera ndi Maso Anu
  • Galamukani!—1998
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chinenero Chimalimbitsa Ubwenzi
  • Muziona Kuti Abale ndi Alongo Anu Osamva Ndi Ofunika Kwambiri
    Nsanja ya Olonda—2009
  • Chinenero Chochita Kuona ndi Maso!
    Galamukani!—1998
  • ‘Yehova Wawalitsa Nkhope Yake pa Iwo’
    Nsanja ya Olonda—2009
  • “Kuphunzira Baibulo Kukuthandiza Anthu Osamva”
    Galamukani!—2010
Onani Zambiri
Galamukani!—1998
g98 9/8 tsamba 16-17

Kumvetsera ndi Maso Anu

KODI nchiyani chingakuthandizeni kulankhulana bwino ndi munthu Wogontha? Kuyang’anana kumaso. Nkofunikadi kutero pamene anthu Ogontha akulankhula. Tingoti ngati anthu aŵiri akulankhulana ndi manja, wina amamuona mnzakeyo ngati wamwano ngati wayang’ana kumbali osamuyang’ananso kumaso. Ndiyeno kuti munthu Wogontha akuyang’aneni mungatani? M’malo momtchula dzina, ndi bwino kwambiri kumkodola mwa kumgwira papheŵa kapena pamkono, kutambasulira mkono wanu chapafupi ndi diso lake, kapena ngati ali kutali, ingokodolani munthu wina kuti nayenso amkodole munthuyo. Malinga ndi mmene mkhalidwewo ulili, mungagogode pansi kapena kuyatsa magetsi ndi kuwazimitsanso. Njira zimenezo limodzi ndi njira zina zoyenera zimapangitsa anthu Ogontha kukuyang’anani ndipo ndiwo mkhalidwe wa anthu Ogontha.

Chinenero Chimalimbitsa Ubwenzi

Ena akakumana ndi munthu Wogontha, amalakwa mwa kuganiza kuti kumvetsera mwa kungoyang’ana milomo ndi nkhani yapafupi. Komabe, anthu ambiri Ogontha amaona kuti njira imeneyo simakwaniritsa kwenikweni kulankhulana. Nzoona kuti kwa ena zingakhale zosiyana, chifukwa anthu ena ngaluso pakuzindikira tanthauzo la zimene milimo ikunena, komabe nthaŵi zonse kungakhale kukoma mtima kusaganiza kuti aliyense angalote zimene milomo yanu ikunena. Mwina kupempha munthu wina kuti azikumasulirani kapena kulemba papepala zimene mukufuna kunenazo zingathandize ndithu kulankhulana bwino ndi munthuyo.

Komabe, ngati mumakumanakumana ndi anthu Ogontha, kodi sizingakhale bwino nanu mutaphunzirako kulankhula ndi manja? Mutaterotu mungakhaledi mabwenzi, makamaka ngati anthunu muli ndi chikhulupiriro chimodzi! Zingofanana ndi kuphunzira mawu ofunika a chinenero china kumalo kumene kuli zinenero ziŵiri. Kwa nthaŵi yaitali Mboni za Yehova zakhala zikufuna kuthandiza onse kudziŵa za Yehova Mulungu. Ngati tadziŵa kuti anthu Ogontha sangafike pakumva monga anthu ena onse, zingakhale bwinotu zedi kulankhula nawo ndi manja!—1 Akorinto 9:20-22.

Antonino anasimba kuti pamene anayamba kumapezeka pamisonkhano yachikristu ku Italy, poyamba “sizinali kutheka kulimbikitsana mwa kukambitsirana ndi abale Akumva. Chifukwa sitinali kumvana, ndinkaona ngati ndinali ndekha.” Ambiri mumpingowo anaona kuti ndi bwino kungophunzira chinenero cholankhula ndi manja cha Italian Sign Language (LIS). Okondwerera ena Ogontha anayamba kuphunzira Baibulo, ndipo misonkhano inayamba kuchitika m’chinenerocho cha LIS. Zimenezo zinamlimbikitsa Antonino ndipo tsopano akufuna “kumauza anzake onse Ogontha za misonkhanoyo ndiponso za chikondi chimene anthu a Yehova ali nacho.”

Padziko lonse Mboni za Yehova zikupanga mipingo yolankhula ndi manja, kumeneko anthu Ogontha amasangalala ndi anzawo mwachikondi. Ku Spain, magulu a Ogontha olankhula ndi manja akhalako kwa zaka zoposa 20. Ku United States, pakali pano kuli mipingo yokangalika yokwana 19 ya Ogontha ndiponso magulu aang’ono 47.

Anthu Ogontha amatha kukhala atumiki anthaŵi zonse (apainiya), atumiki otumikira, ndi akulu ngakhalenso kukamba nkhani pamisonkhano yachigawo, kuphunzitsa pa Sukulu Yautumiki Waupainiya, ndi kutsogolera m’njira zina zosiyanasiyana. Kwa iwowo palibe chowalepheretsa pazochitika zimenezi, koma amangopeza mipata yambiri yotamanda Yehova ndi maluso awo.

Chikhumbo chathu chapansi pamtima chakufuna ubwenzi ndi kulankhulana chimaonekera m’zikhalidwe ndi zinenero zambiri padziko lonse lapansi. M’malo moona anthu Ogontha monga olemala kapena opanda nzeru, zimakhala bwino zedi kuona zochita zawo, ndi maluso awo, ndi mikhalidwe imene imatipanga tonsefe kukhala anthu! Tikamalemekeza ena ndi kufunitsitsa kusintha kuti tigwirizane nawo, tonsefe timakhala banja la anthu osiyanasiyana komabe ogwirizana.

[Chithunzi patsamba 16]

Polankhula ndi manja ndi munthu wina, muyenera kumyang’ana kumaso

[Chithunzi patsamba 16]

Anthu Ogontha amatumikira mwachimwemwe monga atumiki anthaŵi zonse

[Chithunzi patsamba 17]

Kuimba nyimbo za Ufumu ndi manja ku Spain

[Chithunzi patsamba 17]

Kukamba nkhani pamsonkhano wachigawo m’chinenero cha Korean Sign Language

[Chithunzi patsamba 17]

Mabuku onena za Baibulo osonyezedwa pavidiyo m’chinenero cholankhula ndi manja

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena