Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g98 11/8 tsamba 26-27
  • Kuzunza Nyama—Kodi Nkulakwa?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuzunza Nyama—Kodi Nkulakwa?
  • Galamukani!—1998
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Nchifukwa Chiyani Kuzunza Nyama Kuli Kulakwa?
  • Nyama Zidzapumula
  • Nyama
    Galamukani!—2015
  • Kodi Zinyama Zimapita Kumwamba?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Kodi Mulungu Amasamalira Nyama?
    Galamukani!—2011
  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
    Nsanja ya Olonda—2003
Onani Zambiri
Galamukani!—1998
g98 11/8 tsamba 26-27

Lingaliro la Baibulo

Kuzunza Nyama—Kodi Nkulakwa?

M’BWALO lamaseŵera, ku Central America, maso angoti dwii, kuyang’ana atambala aŵiri, mmodzi wofiira, winayo woyera. Khamulo likufuula pamene tambala wofiirayo, kampeni kakuthwa ngati lumo katamangiriridwa pamwendo wake, akukwapula tambala woyerayo. Kenaka kapitawo akuzitola nkhuku ziŵirizo. Woyerayo tsopano wangouma, wafa, ndipo magazi ali chuchuchu. Ndewu ya atambala yatha.

Chakummwera kwa Philippines, akavalo aŵiri akuwamenyanitsa. Openyererawo akuyang’ana nkhondo yoopsayo pamene akavalowo akulumana makutu, pakhosi, mphuno, ndi mbali zina zathupi. Ngakhale kuti onsewo angatuluke m’bwalolo adakali moyo, komabe mmodzi angatulukemo atalemala kapena atathudzulidwa maso kapena atavulala zedi moti angafe nthaŵi ina iliyonse.

Ku Russia agalu aŵiri akulumana. Panthaŵi yaing’ono chabe, upeza kuti maso athudzuka makutu ang’ambika, agaluwo akuyenda ndi miyendo yopunduka, magazi akungochucha pamabala aakulu.

Kwa zaka mazana ambiri anthu akhala akumenyanitsa zinyama, akumaona zimenezo ngati maseŵera, makamaka cholinga chawo chimakhala chili kuseŵera juga. Kuwonjezera pamenepo, ankamenyanitsanso ng’ombe zamphongo, kusaka ankhandwe ngakhale kumenyanitsa akangaude. Ndiponso, nyama zambiri zimazunzidwa ndi anthu a sayansi. Komanso, nyama zina zambirimbiri zimazunzika chifukwa chosasamalidwa ndi eni ake, kaya mwadala kapena mwa njira ina.

M’maiko ena, muli malamulo amene amaletsa anthu kuzunza nyama. Kale kwambiri, mu 1641, a Massachusetts Bay Colony anapanga bungwe la “The Body of Liberties,” limene linati: “Palibe aliyense amene ayenera Kuzunza Nyama iliyonse yomwe munthu amagwiritsira ntchito.” Kuyambira pamenepo, anapanga malamulo ndi kukhazikitsa mabungwe oletsa anthu kuzunza nyama.

Komabe, ambiri amene amachirikiza maseŵera omenyanitsa zinyama omwe tatchula poyamba aja, samadziona ngati ozunzadi zinyama. Ena amanena kuti amakonda zinyama pomwe ndiwonso amazizunza kapena kuzipha. Anthu ambiri okonda kumenyanitsa atambala amanena kuti nkhuku zawo zimakhala moyo wautali kuposa zija zimene amangozisunga kuti zikhale za ndiwo—chipongwe chimenecho!

Kodi Nchifukwa Chiyani Kuzunza Nyama Kuli Kulakwa?

Mulungu amatilola kupindula ndi zinyama. Malamulo a Baibulo amatilola kupha nyama kuti zikhale ndiwo ndi kutinso tipeze zovala kapena kuti nyama zititeteze. (Genesis 3:21; 9:3; Eksodo 21:28) Komabe, moyo ngwopatulika kwa Mulungu. Tiyenera kulamulira zinyama mwa njira yabwino yosonyeza kuti timalemekeza moyo. Baibulo limatsutsa munthu wina wotchedwa Nimrode, yemwe ankangopha nyama mwinanso ndi anthu omwe, chabe chifukwa chakuti zinali kumsangalatsa.—Genesis 10:9.

Mwa mawu otsatiraŵa, Yesu ananenapo za mmene Mulungu amadera nkhaŵa zinyama: “Kodi mpheta zisanu sizigulidwa timakobiri tiŵiri? ndipo palibe imodzi ya izo iiwalika pamaso pa Mulungu.” (Luka 12:6) Ndiponso, atasintha maganizo ake kuti asawonongenso mzinda wodzala ndi anthu ochita zoipa, koma omwe anali atalapa, Mulungu anati: “Ndipo sindiyenera Ine kodi kuchitira chifundo Nineve mudzi waukulu uwu; m’mene muli anthu oposa zikwi zana limodzi mphambu zikwi makumi aŵiri . . ., ndi zoweta zambiri zomwe?” (Yona 4:11) Nzachionekere kuti iye samaganiza kuti nyama zangokhala zinthu zimene ungangowononga mmene ungafunire.

Pamene Mulungu anali kupatsa Aisrayeli malamulo, anawaphunzitsanso kusamala zinyama. Anawalamula kuti akapeza nyama yosochera anayenera kuibweza kwa mbuye wake ndi kutinso anayenera kupepuza nyama yolemedwa ndi katundu. (Eksodo 23:4, 5) Nyamanso zinkafunikira kupuma pa Sabata, monga mmene ankachitira anthu. (Eksodo 23:12) Panalinso malamulo okhudza kusamalira nyama zolimira. (Deuteronomo 22:10; 25:4) Nzachionekere kuti nyama zinafunikira kumasamalidwa ndi kutetezeredwa, osati kuzunzidwa.

Miyambo 12:10 imanena momvekera bwino zimene Mulungu amaganiza, kuti: “Wolungama asamalira moyo wa choweta chake; koma chifundo cha oipa ndi nkhanza.” (Miyambo 12:10) Baibulo lina lokhala ndi ndemanga linatanthauzira vesi limeneli kuti: “Munthu wolungama amachitira chifundo ngakhale nyama zopanda nzeru, koma munthu woipa ngwankhanza, ngakhale pamene akuganiza kuti akuzisamala nyamazo kwambiri.”—Believer’s Bible Commentary, lotembenuzidwa ndi William MacDonald.

Munthu wolungama amachitira nyama chifundo ndipo amafuna kudziŵa chimene zikufuna. Munthu woipa anganene kuti amakonda zinyama, koma “chifundo” chake, kwenikwenidi chili nkhanza. Zochita zake zimasonyeza maganizo ake oipa. Zimenezo zilidi choncho ndi anthu aja amene amamenyanitsa zinyama chifukwa chofuna kupeza ndalama!

Nyama Zidzapumula

Nzoona kuti cholinga choyamba cha Mulungu chinali choti munthu ‘alamulire nsomba za m’nyanja, ndi mbalame za m’mlengalenga, ndi zamoyo zonse zakukwaŵa padziko lapansi.’ (Genesis 1:28) Sipadzakhalanso kuzunza zinyama. Nkhanza imene anthu amachitira zinyama idzatheratu. Tikukhulupirira kuti Mulungu adzathetsa kuvutika konse kosafunikira. Koma motani?

Amalonjeza kuti adzaononga anthu oipa ndiponso ankhanza. (Miyambo 2:22) Hoseya 2:18, ponena za nyama, amati: ‘Ndipo tsiku lomwelo ndidzachita pangano ndi nyama za kuthengo, ndi mbalame za mlengalenga, ndi zokwawa pansi; . . .ndi kuzigonetsa pansi mosatekeseka.’ Zimenezotu zidzakhala zosangalatsa zedi, kukhala m’mikhalidwe yamtendere, anthu oongoka mtima ndi zinyama zomwe!

[Chithunzi patsamba 26]

“Ng’ombe zikumenyana m’mudzi,” chojambulidwa ndi Francisco Goya

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena