Achinyamata Akufunsa Kuti . . .
Kodi Nchifukwa Chiyani Ndikukhala Wopanda Makolo?
“Kodi popanda makolo moyo unali wotani? Ndinganene kuti unali womvetsa chisoni pazifukwa zambiri. Nzovuta kwambiri kukula popanda kusonyezedwa chikondi ndi makolo ako.”—Joaquín.
“Ndinkavutika kwambiri masiku amene makolo ankafunikira kubwera kudzasaina khadi la lipoti la sukulu. Ndinkamva chisoni ndiponso kusungulumwa. Nthaŵi zina ndimamvabe chimodzimodzi.”—Abelina wazaka 16.
ILI ndi vuto la m’nthaŵi yathu ino—achinyamata mamiliyoni ambiri akukula popanda makolo. Ku Eastern Europe, ambiri ndi amasiye chifukwa cha nkhondo. Mu Afirika, AIDS yapangitsa vuto limodzimodzilo. Ana ena anangosiyidwa ndi makolo awo basi. Mabanja asiyana chifukwa cha nkhondo kapena masoka ena achilengedwe.
Mavuto oterowo anali ofala ngakhale m’nthaŵi za Baibulo. Mwachitsanzo, Malemba amanena mobwerezabwereza za ana amasiye. (Salmo 94:6; Malaki 3:5) Nkhondo ndiponso mavuto ena zinkagaŵanitsa mabanja panthaŵiyo. Motero Baibulo limanena za buthu limene linagwidwa ndi magulu ankhondo Aaramu nkusiyanitsidwa ndi makolo ake.—2 Mafumu 5:2.
Mwinamwake ndinu mmodzi mwa achinyamata mamiliyoni ambiri amene alibe makolo. Ngati ndi choncho ndiye kuti mukudziŵa mmene vuto limeneli limaŵaŵira. Kodi nchifukwa chiyani zimenezi zinakuchitikirani?
Si Inu Amene Munalakwa
Kodi nthaŵi zina mumalingalira kuti mwina mwake Mulungu akukulangani? Mwina mumakwiyira makolo anu chifukwa chakuti anamwalira—ngati kuti anachitira dala. Choyamba zindikirani kuti Mulungu sanakukwiyireni. Ndiponso makolo anu sanachitire dala kukusiyani. Imfa ndi chinthu choipa chomwe chimagwera anthu opanda ungwiro, ndipo nthaŵi zina imaŵagwera makolo pamene ana awo anakali aang’ono. (Aroma 5:12; 6:23) Zimaoneka ngati kuti Yesu anakumana ndi vuto lofananalo lakuti atate ake okondedwa omulera, a Yosefe anamwalira.a Ndithudi zimenezi sizitanthauza kuti Yesu anachimwa.
Komanso, zindikirani kuti tikukhala ‘m’masiku otsiriza owawitsa.’ (2 Timoteo 3:1-5) M’zaka za zana lino, chiwawa, nkhondo ndi upandu zaphetsa anthu mamiliyoni ambiri. Ena amangofa chifukwa cha “zochitika zosadziwika” zomwe zimagwera wina aliyense. (Mlaliki 9:11, NW) Ngakhale kuti imfa ya makolo anu ingakhale yoŵaŵa kwambiri, sikuti inu ndinu wolakwa ayi. M’malo movutika mtima mwakudzimva kukhala wolakwa kapena kukhala ndi chisoni kwambiri, muyenera kutonthozedwa ndi lonjezo la Mulungu lachiukiriro.b Yesu ananeneratu kuti: ‘Musazizwe ndi ichi, kuti ikudza nthaŵi, imene onse ali m’manda adzamva mawu ake, nadzatuluka.’ (Yohane 5:28, 29) Abelina amene tinamtchula poyamba paja anati: “Kukonda kwanga Yehova ndi chiyembekezo chachiukiriro zakhala zothandiza kwambiri.”
Koma bwanji ngati makolo anu adakali moyo koma anakusiyani? Mulungu amafuna kuti makolo azilera ana awo ndi kuwasamala. (Aefeso 6:4; 1 Timoteo 5:8) Mwachisoni, makolo ena modabwitsa asonyeza kuti ndi “opanda chikondi chachibadwidwe” kwa ana awo. (2 Timoteo 3:3) Kwa ena, amaŵasiya ana awo chifukwa chakuti umphaŵi wanyanya, kumwa mankhwala osokoneza bongo, kukhala kundende, kapena uchidakwa. Komanso, pali makolo ena amene amathaŵa ana awo chifukwa chodzikonda chabe. Kaya zifukwa zake zikhale zotani, koma kusiyana ndi makolo ako nkoipa. Komabe izi sizikutanthauza kuti inu mwalakwitsa kena kake kapena kuti muvutike mtima poganiza kuti ndinu wolakwa. Ndi makolo anu amene ayenera kuyankha mlandu kwa Mulungu pazimene anakuchitirani. (Aroma 14:12) Komabe, ngati makolo anu sanachite kufuna kukusiyani koma chabe chifukwa cha mavuto amene iwo sangathe kuwapewa, monga masoka achilengedwe kapena matenda, ndiye kuti palibe amene ayenera kuimbidwa mlandu! Nthaŵi zonse pamakhala chiyembekezo chakuti mukhoza kudzakhalira limodzi ngakhale kuti nthaŵi zina zimakhala ngati zosatheka.—Yerekezerani ndi Genesis 46:29-31.
Vuto Losokoneza Maganizo
Padakali pano, mukhoza kumakumana ndi mavuto ambiri. Kufufuza kochitidwa ndi a United Nations Children’s Fund, kotchedwa kuti Children in War, kunasonyeza kuti: “Ana omwe amakhala okha ndiwo ali pangozi kwambiri—iwo ndiwo . . . amene amavutika kwambiri kuti apulumuke, amasowa wowathandiza kuti akule bwino ndipo amachitidwa nkhanza. Kusiyana ndi makolo kungathe kukhala limodzi mwa mavuto osokoneza mwana maganizo kwambiri.” Mwinamwake inu muli wokhumudwa.
Kumbukirani Joaquin, yemwe tatchula poyamba uja. Makolo ake adalekana ndiponso kusiya iye pamodzi ndi abale ake. Iye anali ndi chaka chimodzi chabe panthaŵiyo ndipo analeredwa ndi achemwali ake aakulu. Iye analongosola kuti: “Ndinkakonda kufunsa kuti nchifukwa chiyani tinalibe makolo monga mmene anzanga analili. Ndipo ndinkati ndikaona bambo wina akuseŵera ndi mwana wake, ndinkangofuna adakakhala bambo wanga.”
Kupeza Chithandizo
Ngakhale kuti nzovuta kukula popanda makolo, sizikutanthauza kuti mudzakhala olephera pazonse. Mwanjira yakuthandizidwa ndi kuchirikizidwa, sikuti mungathe kukula chabe komanso mudzakhala ochita bwino. Izi zingaoneke zovuta kuti mukhulupirire, makamaka ngati muli osakondwa ndiponso achisoni. Komabe zindikirani kuti kudzimva motero nkwachibadwa ndipo kuti sikudzakuvutani kwamuyaya wonse. Pa Mlaliki 7:2, 3, timaŵerenga kuti: “Kunka ku nyumba ya maliro kupambana kunka ku nyumba ya madyerero; . . . chisoni chiposa kuseka; pakuti nkhope yakugwa ikonza mtima.” Ndithudi, pamene vuto lalikulu lakugwera, kulira kumathandiza ndipo nkofunika kuti mtima ukhale pansi. Zidzakuthandizaninso kuuzako mnzanu yemwe angamvetse zinthu kapena wina mumpingo koma wachikulire za mmene zimakuwawirani.
Ndithudi, mukhoza kulakalaka kuyamba kumakhala panokha. Koma Miyambo 18:1 imachenjeza kuti: “Wopanduka [“wodzipatula yekha,” NW], afunafuna chifuniro chake, nakangana ndi nzeru yonse yeniyeni.” Nkwabwino kufunafuna chithandizo kuchokera kwa wina amene ali wokoma mtima ndi womvetsa zinthu. Miyambo 12:25 imati: “Nkhaŵa iweramitsa mtima wa munthu; koma mawu abwino aukondweretsa.” Mungathe kumva “mawu abwino” ngati mutauzako wina “nkhaŵa” zanu.
Kodi ndani amene mungamuuze? Funafunani chithandizo mkati mwa mpingo wachikristu. Yesu analonjeza kuti mmenemo mudzapezamo “abale, ndi alongo, ndi amayi” amene adzakukondani ndi kusamala za inu. (Marko 10:30) Joaquin akukumbukira kuti: “Kukhala pamodzi ndi abale achikristu kunandipangitsa kuona zinthu mosiyana ndi kale. Kupita kumisonkhano nthaŵi zonse kunandipangitsa kuyamba kukonda Yehova kwambiri ndiponso ndinayamba kukhala ndi chilakolako chomtumikira. Abale achikulire ankapatsa banja lathu lonse chithandizo chauzimu ndi uphungu. Lerolino, ena mwa abale anga ali mu utumiki wanthaŵi zonse.”
Kumbukiraninso kuti Yehova ndi “atate wa ana amasiye.” (Salmo 68:5, 6) Kale m’nthaŵi za Baibulo, Mulungu ankalimbikitsa anthu ake kuti azichitira ana amasiye chifundo ndi chilungamo. (Deuteronomo 24:19; Miyambo 23:10, 11) Lerolinonso ali ndi nkhaŵa imodzimodziyo pokhudza achinyamata amene alibe makolo. Choncho pempherani kwa Mulungu, muli ndi chikhulupiriro chakuti iye amadera nkhaŵa za inu ndi kuti ayankha pemphero lanu. Mfumu Davide inalemba kuti: “Pakuti wandisiya atate wanga ndi amayi wanga, koma Yehova anditola. Yembekeza Yehova: Limbika, ndipo Iye adzalimbitsa mtima wako.”—Salmo 27:10, 14.
Ngakhale zili choncho, wachinyamata amene alibe makolo amakumana ndi zovuta zambiri za tsiku ndi tsiku. Kodi muzikhala kuti? Kodi ndalama muzizitenge kuti? Nkhani yam’tsogolo idzalongosola mmene mungalimbanirane ndi mavuto amenewa ndi kuwagonjetsa.
[Mawu a M’munsi]
a Asanamwalire, Yesu anauza Yohane kuti azisamalira amayi ake a Yesuyo, chinthu chimene mwachionekere sichikanachitika ngati atate omlera, Yosefe akanakhala kuti anali moyo.—Yohane 19:25-27.
b Ngati mufuna nkhani zina zonena za mmene mungachitire makolo anu atamwalira, onani nkhani za “Achichepere Akufunsa . . .” za mu Galamukani! wa September 8, 1994.
[Mawu Otsindika patsamba 19]
“Kukonda kwanga Yehova ndi chiyembekezo chachiukiriro zakhala zothandiza kwambiri”
[Chithunzi patsamba 19]
Nthaŵi zina mungakhale wosungulumwa
[Zithunzi patsamba 20]
Mumpingo muli mabwenzi amene angathe kukuthandizani ndiponso kukulimbikitsani