Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g98 12/8 tsamba 21
  • Kodi Yesu Kristu Anali Yani?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Yesu Kristu Anali Yani?
  • Galamukani!—1998
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Yesu Ankaoneka Bwanji?
    Galamukani!—1998
  • Kodi Yesu Ankaoneka Bwanji?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2017
  • Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
    Nsanja ya Olonda—1992
  • Kodi Yesu Ankaoneka Bwanji?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
Onani Zambiri
Galamukani!—1998
g98 12/8 tsamba 21

Kodi Yesu Kristu Anali Yani?

Panthaŵi ino yachaka m’maiko ambiri padziko lonse lapansi, anthu akuchita mapwando a Khirisimasi. Anthu mamiliyoni osaŵerengeka amakhulupirira kuti Yesu Kristu anabadwa pa December 25 zaka 2,000 zapitazo. Anthu amajambula zithunzi zosiyanasiyana za iyeyo mwa kumjambula kapena kumsema ali khanda m’chodyera ng’ombe. Komabe, anakulatu nkukhala mwamuna ndipo anakhala padziko kwa zaka 33 ndi theka.

Kodi munayamba mwadzifunsapo kuti Yesu ankaoneka bwanji atakula? Nanga nkhope yake inkaoneka bwanji? Kodi anali wanyonga ndi wokongola, kapena anali wofooka ndi wooneka monga wodwala, monga mmene ojambula akhala akumjambulira zaka mazana ambiri zikupitazi? Kodi analibe ndevu kapena ankasunga ndevu? Tsitsi lake nanga, kodi linali lalitali?

Komanso, kodi Yesu anali wowala ndi ulemerero, monga mmene amisiri amamjambulira atamveka nkhata yonyezimira kumutu? Kapena kodi anali wosiyaniratu ndi zimenezo—ndiko kuti, analibe maonekedwe ayekha koma kuti anali wofanana ndi wina aliyense pagulu?

Kwa mibadwomibadwo, olemba mbiri limodzi ndi amisiri ojambula akhala akutsutsana pa za maonekedwe a Yesu. Ndiponso, anthu omwe anali moyo m’zaka za zana loyamba, omwe anamuona ndi maso ndi kucheza naye, polemba Baibulo anasimbanso maumboni odalirika onena za iye.

Komabe, mafunso ofunika kwambiri, osati za mmene iye ankaonekera, ngakuti: Kodi kwenikweni Yesu Kristu anali yani? Kodi ali ndi ntchito yotani pakukwaniritsa chifuniro cha Mulungu? Kodi waitsiriza ntchito imeneyo? Kodi iyeyo lero ngwotani, ndipo ali kuti? Kodi ali ndi udindo wofunika kwambiri moti udzapindulitsa anthu onse, ngakhale amene anamwalira?

Tatiyeni tiyambe ndi kuona maumboni okhudza maonekedwe a Yesu. Kodi ankaoneka bwanji?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena