“Mutha Kusiya—Ifenso Tinasiya!”
YOSIMBIDWA NDI MTOLANKHANI WA GALAMUKANI! KU JAPAN
Mbiri zina zimati, sitima za ku Ulaya zinkakocheza padoko la Japan chakumapeto kwa m’ma 1500 ndipo zinkabwera ndi alendo omwe ankasuta fodya, omwe ankaoneka ngati kuti anali ndi “moto m’mimba mwawo.” Anadabwa kwambiri ndipo analakalaka kudziŵa chomwe chimachitika, motero pofika m’ma 1880, kusuta fodya kunakhala chizoloŵezi m’Japan. Ndani ankadziŵa kuti mbadwa za anthu a ku Japan omwe ankadabwawo adzakhala ena mwa anthu osuta fodya kwambiri padziko lapansi?
“TINKAFUNA kuti tizidzimva kuti ndife akuluakulu, kuti tizoloŵere zachikulu.”—Akio, Osamu, ndi Yoko.
“Ndinkafuna kuti ndichepetseko thupi.”—Tsuya.
“Ndinkangofuna kuti ndidziŵe mmene zimakhalira.”—Toshihiro.
“Sitinkadziŵa kuti fodya adzationonga chonchi.”—Ryohei, Junichi, ndi Yasuhiko.
“Ndinkafuna kuthetsa mseru umene unkandigwira m’mawa pamene ndinali ndi mimba yachiŵiri.”—Chieko.
“Ndinayamba kusuta kuti ndiziiŵala nthaŵi yomwe sinkandikondweretsa panthaŵi yamisonkhano yazamalonda.”—Tatsuhiko.
Zimenezi ndizo zifukwa zimene kagulu ka anthu kanapereka pamene anafunsidwa zifukwa zake anayamba kusuta. Zifukwazi nzomveka polingalira mfundo yakuti ena amatcha Japan kukhala paradaiso wa osuta. Chokondweretsa nchakuti anthu onse amene atchulidwa maina pamwambapa anasiya chizoloŵezi chosuta fodya. Kusiyaku ndi chinthu chapamwamba kwambiri polingalira za zinthu zimene zikanawalepheretsa kuti asatero. Kodi mukudabwa kuti zimenezi zinatheka bwanji? Choyamba tiyeni tilingalire kaye mmene kusuta fodya kulili kofala ku Japan lerolino.
Vuto la Fodya
Mwa amuna onse a ku Japan, 56 peresenti amasuta, poyerekeza ndi 28 peresenti ya amuna azaka zosachepera 15 ku America. Mwa anthu 34,000,000 a ku Japan amene amasuta, 22 peresenti ndi akazi, amene ambiri mwa iwo ndi achitsikana. Iwo amatsanzira akuluakulu ndiponso chifukwa cha osatsa malonda. Kusatsa ndudu pa TV ndi pa wailesi, kumene kunaletsedwa ku United States zaka makumi aŵiri zapitazo tsopano nkoletsedwa ku Japan.
Kuwonjezera apo, ndudu zimapezeka mosavuta kwa ogulitsa m’misewu ku Japan. Akangoligwira paketi la fodya m’manja, ndi ochepa chabe amene amagwiritsa ntchito chenjezo lopanda mphamvu kwenikweni limene limalembedwa pa paketilo. Limangolembedwa kuti: “Tisamasute kwambiri; kungathe kuwononga thupi.” Ndiye kuwonjezera pamfundo yakuti anthu sadziŵa kuopsa kwa kusuta fodya, palinso chitsanzo choipa choperekedwa ndi anthu apamwamba ambiri chimene chimalimbikitsa anthu ku Japan kuti azisuta, kumawapangitsa iwo kuona kuti palibe vuto.
Nzosadabwitsa kuti, magulu olimbikitsa kuti anthu aleke kusuta amadandaula kuti boma la Japan silichitapo kanthu kwenikweni kupangitsa nzika zake kuleka kusuta fodya. Koma azamaphunziro ayamba kuona kufunika kwake kwa kuchenjeza anthu kuti kusuta kumawononga thanzi ndi moyo wawo. Anthu osuta a ku Japan amasonyeza zizindikiro za matenda zomwe anthu osuta a kwina kulikonse amasonyeza—mselu, kupuma mobanika, chifuwa, kupweteka kwa m’mimba, kusakhala nchilakolako chakudya, kudwaladwala chimfine, ndipo mwinanso, nkupita kwa nthaŵi, kumwalira mwamsanga chifukwa cha kansa ya m’mapapo, nthenda ya mtima, kapena mavuto ena.
Pa April 1, 1985, kampani yokonza ndudu za fodya ku Japan anaigulitsa kwa anthu wamba boma linasiya kuiyendetsa. Komabe imagwirizana kwambiri ndi boma ndipo zimenezi zimalepheretsa kuti pasapezeke njira zolimbikitsira anthu kuleka kusuta. Izi zimatithandiza kumvetsa chifukwa chake magulu olimbikitsa kuti anthu aleke kusuta amaona Japan lerolino monga malo okomera kwambiri anthu osuta. Ndipo zingatithandize kuona chifukwa chake The Daily Yomiuri inanena kuti madokotala akudandaula kuti Japan ndi “dziko limene limalimbikitsa kusuta.”
Kuti muone mmene ena anakwanitsira kusiya, onani bokosi lakuti “Mmene Tinasiyira.”
Ndi Motani Mmene Mungasiyire?
Langizo lomwe tingaphunzirepo kwa anthu omwe ankakonda fodya, monga awo amene nkhani yawo ili m’bokosiwo, nlakuti: muzikhala ncholinga chofuna kulekadi. Chifukwa chimodzi chabwino kwambiri ndi kufuna kukonda Mulungu ndi kumkondweretsa. Ndipo china ndicho kukonda anansi anu. Khalani ndi cholinga ndipo tsimikizani kuchichita. Dziŵitsani onse kuti mufuna kuleka—uzani anzanu, ndipo pemphani chithandizo kwa a m’banja lanu. Ngati nkotheka, lekani mwadzidzidzi. Ndipo chitani zonse zomwe mungathe kupewa kukhala pafupi ndi anthu osuta.
Ngati mukuphunzira Baibulo, limbikirani kugwirizana ndi Mboni za Yehova. Ngati mukhala pamodzi ndi iwo, posapita nthaŵi chilakolako chanu chosuta chidzatha. Komanso, ngati ndinu wa Mboni za Yehova ndipo mukuphunzira Baibulo ndi munthu wosuta, osamlekera kuti athane nazo yekha. Mthandizeni kukonda kwambiri Yehova kuposa chizoloŵezi chake choipacho.
[Bokosi pamasamba 16, 17]
“Mmene Tinasiyira”
Mieko: “Pamene ndinayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova, ndinali wotsimikiza kuti sindingathe kuleka kusuta fodya. Cholinga changa pophunzira chinali chakuti mwina ana anga okha, aphunzire njira yabwino ya moyo. Koma posapita nthaŵi ndinazindikira kuti kholo liyenera kupereka chitsanzo, motero ndinayamba kupemphera kwambiri kwa Yehova Mulungu kuti andithandize. Ndinayesetsa kuti ndizichita zimene ndinkapemphera, ndipo kwa kanthaŵi ndinali wolefuka. Koma sindidzaiŵala chimwemwe chomwe ndinali nacho potsirizira pake pamene ndinasiya khalidwe laumveli.”
Masayuki: “Pambuyo pakuti ndinali kusuta mapaketi atatu patsiku ndiponso nditayesayesa koma mosaphula kanthu, ndinasiya ndudu yanga yomaliza ndikunena kuti basi sindidzasutanso fodya. Am’banja langa, Mboni zinzanga, ndiponso Yehova Mulungu anandithandiza kuti ndileke. Palibe aliyense mwa anzanga amene ndimagwira nawo ntchito ku banki anatsimikiza kuti ndinalekadi. Ndinapereka ganizo lakuti popereka ulemu kwa makasitomala athu, aliyense asamasute pa malo ogwirira ntchito panthaŵi yantchito. Lingaliro langa linayamba kugwira ntchito, ngakhale kuti 80 peresenti mwa ogwira ntchitowo anali anthu osuta fodya. Zimenezi tsopano zinafalikira m’nthambi 260 za banki yathu.”
Osamu: “Pamene ndinayamba kuphunzira choonadi m’Mawu a Mulungu, Baibulo, ndinazindikira kuti ndinayenera kusiya kusuta. Zinanditengera pafupifupi chaka chimodzi. Ngakhale pamene ndinali nditaleka, kwa miyezi isanu ndi umodzi, ndinkafunikira kumalimbana ndi chilakolako chakuti ndisute. Ndinkadziŵa kuti ine mwini ndiyenera kukhala ndi cholinga choleka kusuta.”
Toshihiro: “Nsembe ya dipo ya Yesu inandichititsa chidwi kwambiri mwakuti ndinaona kuti nanenso ndingathe kuchitapo kanthu kuleka kusuta.”
Yasuhiko: “Chifukwa chosankha kuyamba kumvera Yehova Mulungu ndi kusiya kusuta, moyo wanga unatetezeka. Tsiku lina, m’chipinda mmene ndinkagwira ntchito munadzala gas ya propane yomwe inkakha m’chinthu china. Mwachizoloŵezi, ndiye kuti ndikanayatsa ndudu ndipo zimenezi zikanapangitsa kuti chipinda chonsecho chigwire moto. Koma popeza ndinali nditaleka kusuta masiku angapo, nchifukwa chake ndili pano kumalongosola zimenezi.”
Akio: “Pamene ndinayamba kumva mseru nthaŵi ndi nthaŵi, ndinayamba kukayikira kuti mwina kusuta ndiko kunkandivulaza. Koma sindinasiye. Nkhani yoyamba yokhala ndi mfundo zomveka yonena za kuopsa kwa kusuta fodya anandiuza ndi mkazi wanga, amene anali atakhala wa Mboni za Yehova. Posapita nthaŵi ndinayamba kuphunzira Baibulo, ndipo ndinaphunzira m’zofalitsa za Watch Tower kuti osuta sikuti amadzivulaza iwo okha chabe komanso ena m’banja mwawo. Ndinasiya nthaŵi yomweyo!”
Ryohei: “Mkazi wanga ndiye amene ankandigulira ndudu—ankagula mapaketi 20 nthaŵi imodzi. Koma atangophunzira Baibulo ndi Mboni, ankakana kugula chinthu chilichonse chimene ankazindikira kuti chindiwononga. Choncho ndinatsegula golosale yangayanga ya fodya. Tsiku lirilonse ndinkasuta mapaketi atatu ndi theka. Ndiye kenaka ndinayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni. Posapita nthaŵi ndinayamba kulakalaka kumakamba nkhani za m’Baibulo. Choncho ndinasiya kusuta kuti ndiyeneretsedwe monga wophunzira m’Sukulu ya Utumiki Wateokalase.”
Junichi: “Mwana wanga wamkazi wamng’ono amene ndi wa Mboni, anali kudera nkhaŵa za moyo wanga. Iye anandipangitsa kulonjeza kuti ndileka kusuta, ndipo ndinalekadi.”
Tsuya: “Pamene ndinapita ku Nyumba ya Ufumu koyamba, ndinapempha choikamo phulusa la ndudu ndiponso machisa. Ndinadabwa kumva kuti panalibe aliyense amene ankasuta mmenemo. Ndinazindikira kuti ndinayenera kuleka kusuta. Masiku asanu ndi atatu amene ndinathera m’chipatala anandipangitsa kutsimikiza mtima kuti sindiyeneranso kudzavutika kachiŵiri chifukwa cha kufuna kuleka kusuta.”
Yoko: “Ndinaŵerenga nkhaniyo m’magazini ndi mabuku ena a Mboni za Yehova, kuona mmene Yesu anakanira mankhwala osokoneza bongo amene anampatsa pamene anakhomeredwa pamtengo wozunzirapo. Ndinapemphera kwa Yehova Mulungu, kumuuza kuti ndinkafuna kukhala womlambira waukhondo. Pambuyo pake, sindinasutenso. Pamene anthu amene ndayandikana nawo anali kusuta, ndinali pafupi kumeza utsi umene amatulutsa, koma mwamsanga ndinathaŵapo, popeza sindinkafuna chizoloŵezi changa kuti chiyambirenso.”
Anthu onsewa omwe kale ankasuta tsopano ali ndi maganizo akuti sadzasutanso. Kodi inu ndinu mmodzi mwa osuta amene mukufuna kusiya chizoloŵezichi?
Mieko
Osamu
Yasuhiko
Akio ndi mkazi wake, Sachiko
Junichi ndi mwana wake Meri
Yoko