Kuteteza Ufulu—Motani?
M’KATAUNI ka Rengasdengklok, ku Indonesia, anthu amafuko osiyanasiyana ankakhala pamodzi mumtendere kwa zaka zambiri. Komabe, ngakhale kuti ankaoneka ngati ololerana pazipembedzo, zimenezo zinatha pa January 30, 1997. Chiwawa chinabuka nthaŵi itatsala pang’ono kukwana 3 koloko m’bandakucha patsiku la phwando lachipembedzo, pamene wokhulupirira wina anayamba kuimba ng’oma yake. Munthu wachipembedzo china, atanyansidwa ndi phokosolo, anayamba kulalatira mnansi wakeyo. Onse anayamba kukalipirana, kugendana ndi miyala. Kutacha, chipolowecho chinakula chifukwa enanso analoŵerera mkanganowo. Pofika madzulo, akachisi aŵiri a Abuda, ndi matchalitchi anayi a Dziko Lachikristu anali atawonongedwa. Nyuzipepala yotchedwa International Herald Tribune inasimba nkhaniyo pamutu wakuti “Chidani cha Kusalolerana Zipembedzo Chibutsa Chipolowe cha Mafuko a Anthu.”
M’mayiko ambiri, mafuko a anthu ochepa omwe ufulu wawo umatetezedwa mwalamulo, kaŵirikaŵiri amaona kuti saloledwa kupembedza. Kulonjeza ufulu mwalamulo sikumachotseratu choyambitsa maganizo akusalolera zina. Chokhacho chakuti maganizo akusalolera zipembedzo zina ngobisika m’mitima ya anthu sichitanthauza kuti maganizowo palibe. Ngati mikhalidwe ingasinthe panthaŵi ina m’tsogolo ndipo mwina n’kupangitsa anthu kukhala a tsankho, maganizo obisika mumtima akusalolera zipembedzo zina angaoneke mosavuta. Ngakhale ngati anthu sakuzunzidwadi, koma angayambe kudedwa kapena malingaliro awo angayambe kutsekerezedwa. Kodi zimenezi zingaletsedwe bwanji?
Kudziŵa Mizu ya Maganizo a Kusalolerana Zipembedzo
Mwachibadwa timakana kapena kukayikira zinthu zina kapena zachilendo, makamaka malingaliro osiyana ndi athu. Kodi zimenezi zikutanthauza kuti kulolera zipembedzo za ena n’kosatheka? Buku la UN lakuti Elimination of All Forms of Intolerance and Discrimination Based on Religion or Belief linatchula umbuli ndi kusazindikira kuti ndiyo “mizu ina yaikulu yakusalolera zipembedzo zina ndiponso tsankho pankhani zachipembedzo ndi chikhulupiriro.” Komabe, monga muzu wamaganizo akusalolera zipembedzo zina, umbuli ungazulidwe. Motani? Mwa maphunziro osakondera. Lipoti la bungwe la Mfundo za Ufulu Wachibadwidwe, la UN Commission on Human Rights, linati: “Maphunziro angakhale njira yopambana yothetsera maganizo a tsankho ndi maganizo akusalolera zipembedzo zina.”
Kodi maphunziro amenewa cholinga chake n’chiyani? Magazini ya UNESCO Courier inati m’malo molimbikitsa anthu kutsutsa ntchito za zipembedzo zina, “cholinga cha maphunzirowo chiyenera kukhala kutsutsa anthu opotoka maganizo amene amapangitsa anthu ena kuopa anthu anzawo ndi kuwapeŵa, ndipo ayenera kuthandiza achinyamata kuganiza mwanzeru ndi kulingalira monga achikulire.”
Mwachionekere, manyuzipepala angachite zambiri pakuthandiza anthu “kuganiza mwanzeru ndi kulingalira za makhalidwe abwino.” Magulu ambiri opezeka m’mayiko onse amadziŵa kuti manyuzipepala ali ndi mphamvu youmba maganizo a anthu ndi kuwalimbikitsa kumamvana ndi anzawo. Komabe, kuti manyuzipepala alimbikitse anthu kulolera zipembedzo za ena m’malo mochirikiza maganizo akusalolera zipembedzo zina monga amachitira manyuzipepala ena, pafunikira atolankhani odalirika, opanda tsankho. Nthaŵi ndi nthaŵi, atolankhani ayenera kutsutsa maganizo a anthu aunyinji. Ayenera kufotokoza bwino nkhani ndiponso mopanda tsankho. Koma kodi zimenezo n’zokwanira?
Njira Yabwino Kwambiri Yothetsera Maganizo Akusalolera Zipembedzo Zina
Kulolera zipembedzo zina sikutanthauza kuti aliyense ayenera kukhala ndi maganizo ofanana ndi a mnzake. Anthu angasiyane maganizo. Ena angaganize kuti zimene ena amakhulupirira n’zolakwika kwambiri. Mwina angamatsutse ngakhale poyera. Komabe, malinga ngati safalitsa mabodza ndi kuyesa kusonkhezera ena kuchita tsankho, amenewo sindiwo maganizo akusalolera zipembedzo zina. Maganizo akusalolera zipembedzo zina amaoneka pamene gulu lina likuzunzidwa, kuikiridwa malamulo okhwima, kuikiridwa malire, kuletsedwa, kapena mwa njira ina kuletsedwa kusonyeza chikhulupiriro chawo. Mtundu wina woipa kwambiri wakusalolera zipembedzo zina ndiwo pamene ena amapha anzawo ndipo ena amafa chifukwa cha chikhulupiriro chawo.
Kodi maganizo akusalolera zipembedzo zina angathetsedwe bwanji? Angavumbulidwe poyera, monga mmene mtumwi Paulo anavumbulira maganizo akusalolera zipembedzo zina a atsogoleri achipembedzo a m’tsiku lake. (Machitidwe 24:10-13) Komabe, njira yabwino kwambiri yoletsera maganizo akusalolera zipembedzo za ena ndiyo kuyamba kuchitapo kanthu inuyo—kuchirikiza maganizo a kulolera zipembedzo zina, ndiko kuti, kuphunzitsa anthu kudziŵana bwino. Lipoti la UN limene tatchula poyamba paja lonena za kuchotsa maganizo akusalolera zipembedzo zina, linatinso: “Popeza kuti mitundu yonse yamaganizo akusalolera zipembedzo zina amayambira m’maganizo a munthu, chonchonso m’maganizo momwemo ndimo mmene muyenera kuyamba kuwongoledwa.” Maphunziro amenewo mwinanso angapangitse anthu kudzifunsa okha pankhani yachikhulupiriro chawo.
Federico Mayor, mkulu wa bungwe la zamaphunziro, zasayansi, ndi zachikhalidwe cha anthu (United Nations Educational, Scientific, and Cultural Organization, analemba kuti: “Maganizo a kulolera zipembedzo zina ndiwo ukoma wa munthu wokhala ndi chikhulupiriro.” Wansembe wa tchalitchi cha Dominican Claude Geffre, polemba m’magazini ya Reformer, anati: “Chinthu chofunika kuti munthu akhale wololera zipembedzo zina ndicho chikhulupiriro champhamvu.” Munthu wokhutira ndi chikhulupiriro chake sadera nkhaŵa ndi chikhulupiriro cha ena.
Mboni za Yehova zimaona kuti njira yabwino kopambana yosonyezera maganizo a kulolera zipembedzo za ena ndiyo kulankhula ndi anthu a zipembedzo zosiyanasiyana. A Mboni amausamala kwambiri ulosi wa Yesu wakuti “Uthenga uwu wabwino wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi, ukhale mboni kwa anthu a mitundu yonse,” ndipo amadziŵika chifukwa cha utumiki wawo wolalikira kwa anthu onse. (Mateyu 24:14) Pantchito imeneyi, amakhala ndi mwayi wakumva anthu a zipembedzo zosiyanasiyana—ngakhale anthu osakhulupirira kuti Mulungu aliko—akufotokoza zimene amakhulupirira. Ndiyeno a Mboni nawonso amafotokozera anthu ofuna kumva zimene amakhulupirira. Choncho, amathandiza anthu kudziŵa zinthu zambiri ndi kuzizindikira. Munthu akadziŵa zinthu ndi kuzizindikira kumakhala kosavuta kukhala ndi maganizo ololera zipembedzo zina.
China Chofunika Pakulolera Zipembedzo Zina
Lerolino, maganizo akusalolera zipembedzo za ena adakali vuto lalikulu, ngakhale kuti ambiri akuyesetsa mogwirizana kuwathetsa. Kuti zinthu zidzasinthedi, pakufunika chinthu chinanso. Nyuzipepala ya ku France yotchedwa Le Monde des débats inalitchula vuto lake, inati: “Anthu amakono akusoŵa kanthu kena kauzimu. Lamulo lingalonjeze kuteteza anthu kwa aja amene amapondereza ufulu wa ena. Lamulolo liyenera kulonjeza anthu kuti adzakhala aufulu ndi olingana, popanda tsankho.” Buku lakuti Democracy and Tolerance linavomerera kuti: “Tidakali ndi zambiri zoti tichite kuti tifikire cholinga chakupangitsa anthu kumvana ndi kufikira muyezo wamakhalidwe oyenera anthu onse.”
Baibulo limalonjeza kuti posachedwapa anthu adzagwirizana pa kulambira koyera kwa Mulungu m’modzi woona. Kugwirizana kumeneku kudzapangitsa ubale weniweni wapadziko lonse, ndipo onse adzakhala olemekezana. Anthu sadzakhalanso mbuli, chifukwa Ufumu wa Mulungu udzaphunzitsa anthu njira za Yehova, choncho udzakhutiritsa zosoŵa zawo zonse zamaganizo ndi zauzimu. (Yesaya 11:9; 30:21; 54:13) Dziko lonse lapansi lidzadzaza anthu aufulu ndi olingana. (2 Akorinto 3:17) Mutadziŵa molongosoka zimene Mulungu akufuna kudzachitira anthu, mungathetse umbuli ndi maganizo akusalolera zipembedzo za ena.
[Bokosi/Chithunzi patsamba 11]
Chipembedzo Chikuponderezedwa
Zaka zaposachedwapa, akuluakulu adziko akhala akuyesa kupondereza Mboni za Yehova ku France mwa kukana kuwapatsa ufulu monga zipembedzo zina. Posachedwapa, ndalama zimene zinalandiridwa kuti zichirikize ntchito zachipembedzo za Mboni, anazidula msonkho waukulu kwambiri. Akuluakulu a France mosayenera anawalipiritsa msonkho waukulu wa madola 50 miliyoni (msonkho limodzi ndi fayindi), ali ndi cholinga chopondereza gulu limeneli la Akristu 200,000 limodzi ndi ena ogwirizana nawo ku France. Tsankho lachipembedzo lapoyera limenelo n’losemphana ndi mfundo zaufulu, chibale, ndi kulingana kwa anthu.
[Chithunzi patsamba 10]
Kusalolera zipembedzo zina kaŵirikaŵiri kumayambitsa chiwawa
[Zithunzi patsamba 12]
Mosasamala kanthu za ntchito yachipembedzo ya Mboni za Yehova, boma la France limati iwo si chipembedzo!