Mavuto ndi Madalitso a Kulera Ana Asanu ndi Aŵiri
Yosimbidwa ndi Bert ndi Margaret Dickman
Ndinabadwa mu 1927, ku Omaha, Nebraska, ku U.S.A., ndipo ndinakulira ku South Dakota. Ndimakumbukira pa unyamata wanga pamene ndinkakhala movutika panthaŵi ya Great Depression (1929-42) pamene chuma chadziko chinatsika kwambiri. Amayi ankakonda kuphika msuzi umene unali wosalimbitsa thupi kwenikweni, choncho iwo ankautcha kuti msuzi wakumanda. Iwo ankangoika mafuta ochepa mu pani n’kuwonjezamo madzi, ndiye timasusamo buledi wathu. Mabanja ambiri ankavutika panthaŵi imeneyo.
A M’BANJA mwathu sankapita kutchalitchi—anali ataona chinyengo m’chipembedzo chachipolotesitanti chakuno. Koma ine, malingaliro anga anali atasokonezeka chifukwa cha zaka ziŵiri zomwe ndinali msilikali panthaŵi ya Nkhondo Yadziko II. Mpamene ndinazoloŵera kumwa moŵa ndi kutchova njuga.
Ndili patchuthi changa ku usilikali, ndinapita kudansi kumene ndinakakumana ndi Margaret Schlaht, mtsikana yemwe makolo ake ndi a ku Germany ndi ku Ukraine. Tinakondana, ndipo titakhala pachibwenzi kwa miyezi itatu, tinakwatirana mu 1946. Zaka zisanu ndi zitatu titakwatirana, tinakhala ndi ana asanu ndi aŵiri, ndipo tinazindikira zinthu zili kale mkati motivuta kuti kulera ana n’kovuta.
Mu 1951, ndinachita ngozi pamakina ochekera matabwa ndipo dzanja langa lakumanzere linatsala pang’ono kuduka. Ndinakhala m’chipatala kwa zaka ziŵiri pamene ankandiika khungu ndi mafupa ena. Panthaŵi imeneyi, Margaret ankalera yekha anyamata asanu. Chifukwa chothandizidwa ndi mabwenzi ndi anansi, Margaret anatha kulimbana ndi mavutowo. Ndili m’chipatala ndinali ndi mpata waukulu wolingalira za chifuno cha moyo. Ndinayesera kuŵerenga Baibulo koma sindinkalimvetsa.
Patangopita nthaŵi pang’ono nditatuluka m’chipatala, tinasamukira ku Opportunity, tauni ina m’Chigawo cha Washington, ndipo ndinayamba ntchito yomanga nyumba ndi mlamu wanga. Tsopano ndifuna Margaret nayenso anenepo mbali yake pankhaniyi.
Ndinali Wotanganidwa Kwambiri!
Ndinakulira pafamu pamene tinkalima dzinthu, tinkaŵeta ng’ombe, ndiponso tinkaika zipatso ndi ndiwo zamasamba m’zitini. Ndinali wolimbikira ntchito kwambiri ndipo linali phunziro londithandiza pazovuta zam’tsogolo m’moyo wanga, zimene zinadzachuluka. Tinapulumuka vuto la kutsika kwa chuma mosiyana ndi ambiri, chifukwa nthaŵi zonse tinkakhala ndi chakudya.
Makolo anga analibe nthaŵi yolingalira za chipembedzo, ngakhale kuti ndinkapita ku Sande sukulu kamodzikamodzi. Ndiye kenaka, ine ndi Bert tinakwatirana tili ndi zaka 19. Sitinapite ku tchalitchi—tinangopanga kaphwando kochepa m’nyumba ya makolo anga ndipo mbusa wa mpingo wa Congregation ndiye ankatsogolera zonse. Patangopita zaka zochepa, ndinakhala ndi ana asanu ndi aŵiri—Richard, Dan, Doug, Gary, Michael, Ken ndi wotsiriza, Scott, mu 1954. Anali ambiri!
Titasamukira ku Opportunity, mkazi wina anabwera pakhomo pathu kufuna kunena za m’Baibulo. Ndinamfunsa ngati ankakhulupirira helo wa moto, chiphunzitso chimene chimandiopsa kwambiri. Ndinasangalala pamene anandiuza kuti helo wa moto si chiphunzitso cha m’Baibulo ndiponso nkhani yakuti munthu ali ndi moyo womwe sufa sizili m’Baibulo! Nthaŵi zonse ndinkakhala mwa mantha kuopa kufa ndipo sindinkatha kugwirizanitsa pakati pa Mulungu wachikondi ndi helo wa moto. Ndinalingalira zakuti sindiyenera kuphunzitsa ana anga bodza limeneli.
Mu 1955, ndinayamba kuphunzira Baibulo mogwiritsa ntchito buku lakuti “Let God Be True.”a Monga mmene mukudziŵira, iyi ndiyo nthaŵi imene mlaliki wina wa tchalitchi cha Pentecost mwadzidzidzi anayamba kusonyeza chidwi chondilalikira kuti ndisamvera za Mboni za Yehova! Iye analakwa kwambiri—chifukwa anayamba kundilalikira za moto wa helo! Anatumiza akazi achipentecostal kuti adzandiletse kuphunzira ndi Mboni.
Panthaŵi iyi, Bert ankangomvetsera phunziro langa la Baibulo m’chipinda china. Pambuyo pake anayamba kumaŵerenga New World Translation of the Christian Greek Scriptures, ndipo anayamba kumamvetsetsa zinthu zina. Kuntchito ankaŵeruka pakati pa usiku. Akamabwera kunyumba ankandipeza nditagona. Usiku wina ndinatsikira mwakachetechete m’chipinda chapansi n’kumpeza akuŵerenga mabuku anga mobisa! Ndinayenda monyang’ama kubwerera ku bedi, ndili wokondwa kuti ankafufuza kuti adzionere yekha. Pambuyo pake nayenso anaphunzira Baibulo, ndipo mu 1956 tinakhala Mboni zobatizidwa.
Popeza ndinakhala ndi ana asanu ndi aŵiri m’zaka zisanu n’zitatu, ndinapeza kuti kuwadyetsa ndi kuwaveka ndikupangitsa nyumba kukhala yaukhondo kunali kovuta. Anyamatawo anaphunzira kumagwira ntchito zapakhomo. Kaŵirikaŵiri ndimanena kuti ndinalibe makina otsukira mbale a otomatiki—koma ndinali ndi asanu ndi aŵiri! Ankalandizanalandizana kugwira ntchito imeneyi. Kunena zoona, Bert anali wothandiza kwambiri. Nthaŵi zonse ankalangiza ndi kumakhazikitsa malamulo a panyumba komabe amasiyabe mpata woti n’kulankhulana uli chitsegukire. Anyamatawo amalemekeza atate wawo komabe sankawaopa. Bert sanalekerere udindo wake wophunzitsa anyamatawo ponena “zakugonana.”
Mwana wathu woyamba, Richard, anapita kukatumikira monga wantchito wodzifunira kulikulu la Watch Tower Society ku Brooklyn, New York mu 1966. Chinali chiyeso kwambiri kwa ine kuona mwana woyamba atachoka panyumba. Nthaŵi zonse zinkandiwawa kuona mpando womwe unkangokhala popanda munthu patebulo tsiku ndi tsiku. Komabe ndinali wosangalala kuti anali kuphunzira zabwino.
Koma ndimulole Bert apitirize.
Kulera Ana Athu Motsatira Mapulinsipulo a Baibulo
Ine ndi Margaret tinabatizidwa pamsonkhano ku Spokane ku Washington. Panthaŵi ino tinali ndi vuto lolera ana athu anyamatawo mogwirizana ndi mapulinsipulo a Baibulo—kaleredwe kamene mwina mungati kachikale. Sindinkalorera kuti wina azinama kapena kumakhala ndi moyo wa paŵiri, ndipo anyamatawo ankadziŵa bwino zimenezi. Tinawaphunzitsa kuti Yehova amafunikira kumpatsa zabwino koposa.
Komabe, ankazindikira kuti ayenera kumandiuza ine zakukhosi kwawo chifukwa tinali ogwirizana kwambiri ndipo tinkachitira zinthu zambiri pamodzi. Monga banja pamodzi, tinkasangalala kumapita kunyanja pamodzi, kukayenda, ndi kuseŵera softball. Tinali ndi ziŵeto ndiponso munda ndipo anyamatawo ankathandiza ntchito iliyonse imene inkafunika kuchitika. Motero anaphunzira kugwira ntchito ndiponso kuseŵera. Tinkayesetsa kuchita zinthu mwachikatikati.
Zochitika zokhudza Utumiki Waufumu
Kunena zauzimu, tonsefe tinkapitira pamodzi kumisonkhano yachikristu ku Nyumba ya Ufumu, ndipo tinkakhala ndi phunziro la Baibulo labanja. Mu 1957 tinapita kumsonkhano wa Mboni za Yehova ku Seattle, ku Washington. Panthaŵi yamsonkhanoyo anapempha kuti mabanja asamukire kumene kuli kusowa kwakukulu kwa Mboni kuti akalalikire uthenga wabwino Waufumu wa Mulungu. Banja lathu linalingalira kuti chinali chinthu chabwino, ndipo tinayamba kukonzekera za kusamuka. Choyamba tinapita ku Missouri mu 1958 ndiye kenaka ku Mississippi mu 1959.
Mu 1958 tinachita chinthu china chokhudza ntchito yathu Yaufumu. Ndinapanga ngolo imene inkakokedwa ndi galimoto yakale ya 1947 yokwera anthu atatu, yotchedwa DeSoto. Chaka chimenecho tonsefe asanu ndi anayi tinapita ku New York m’galimoto imeneyo kuti tikapezeke pamsonkhano wa mitundu yonse. Milungu yambiri inatithera m’njira, tikumaimaima njira yonse kuchokera ku Spokane, ku Gombe la Kummawa, kupita ku New York—mtunda wa makilomita 4,200! Kaŵirikaŵiri anyamataŵa amakumbukira ulendowo kuti unali wosangalatsa.
Kutengera Phunziro pa Keke
Pamsonkhano umenewo tinalandira mabuku a Kucokera ku Paradaiso Wotayika Kunka ku Paradaiso Wopezedwanso.b Buku limenelo, pamodzi ndi Baibulo ndiwo anakhala mabuku ogwiritsa ntchito paphunziro la Baibulo labanja lamlungu ndi mlungu. Anyamata onsewo anaphunzira kuŵerenga adakali ochepa misinkhu. Ankati akaŵeruka kusukulu, Marge amatha nawo nthaŵi kuwamvetsera akuŵerenga Baibulo. Sitinalore kuti TV isokoneze maganizo.
Tinali ndi mwambo ndi ulemu m’banja. Nthaŵi ina Margaret anaphika keke yaikulu—anaiphika bwino kwambiri. Patsikulo china mwa chakudyacho chinali kaloti. Tinkawalimbikitsa anyamata athuwo kuti azidyako zamasamba. Doug sankakonda kaloti. Tinamuuza kuti salandira keke ngati sadya kaye kaloti. Iye anakanabe kudya. Margaret anati, “Ngati siudya kalotiyo, galu ndiye adye keke yako.” Sindiganiza kuti Doug anakhulupiriradi zonena amayi akezo kufikira pamene anaona Blackie akudya keke yake yokomayo! Iye pamodzi ndi anyamata ena onsewo anatengerapo phunziro. Monga makolo, tinkachitadi zimene tanena.
Moyo Unali Wosangalatsa
Ine ndi Margaret tinkatsogozedwa ndi mawu a Yesu opezeka pa Mateyu 6:33: “Koma muthange mwafuna Ufumu wake ndi chilungamo chake, ndipo zonse zimenezo zidzawonjezedwa kwa inu.” Tinkayesetsa kuika zinthu za Ufumu choyamba monga banja. Tonsefe tinkakonda kumapita mu ulaliki pamodzi, ndipo anyamatawa ankasinthanasinthana kupita kunyumba ndi nyumba pamodzi ndi ine. Aliyense anali ndi chikwama chake, Baibulo ndi zofalitsa zofotokoza Baibulo. Tinkawayamikira pa chilichonse chomwe achita bwino. Kaŵirikaŵiri Margaret ankawakumbatira. Tinkawasonyeza chikondi chathu nthaŵi zonse. Sitinkaŵalekerera anyamatawo—moyo unkasangalatsa!
Pamene anyamata athu anakula, ankagwira ntchito monga kutenga anthu kupita nawo kumisonkhano, kutsegula Nyumba ya Ufumu, ndiponso kuthandiza ntchito zina. Iwo anaphunzira kuyamikira Nyumba ya Ufumu monga malo olambirira ndipo ankasangalala kuikonza nyumbayo.
Tinawalimbikitsa kuti azilankhula pamisonkhano yachikristu. Pasukulu ya Utumiki Wateokalase ankakamba nkhani zifupizifupi za ophunzira, mpaka pang’onopang’ono anaphunzira kukhala okamba nkhani. Michael, mwana wathu wachisanu, nthaŵi zonse sankakonda kulankhula pagulu ndipo zinkamvuta kwambiri papulatifomu. Amatheka kuyamba kutuluka misozi nkhani ili mkati chifukwa chakuti walephera kuimaliza ndiye amakhala atakhumudwa kwambiri. Nkupita kwanthaŵi vuto limenelo linamuthera ndipo tsopano ali ndi mkazi ndipo amatumikira monga woyang’anira dera, amachezera mipingo yosiyanasiyana ndi kumapereka nkhani zambiri mlungu ulionse. Uku n’kusintha kwakukulu!
Mmene Anyamatawo Ankaonera Malangizo
Mtolankhani wa Galamukani! anamfunsa Michael kuti amve mmene iye ankaonera kuleredwa mwachikale. “Atate tinkawaona monga mlangizi amene amatifunira zabwino. Ndimakumbukira kuti pamene ndinali wachinyamata, ndinapita kukagwira ntchito panyumba ina youlutsira mawu. Ndinafuna kugula galimoto kuti ndiziigwiritsa ntchito mu upainiya. Manijala anati andigulitsa galimoto yake yamtundu wa Ford Mustang, yampanda denga, yazitseko ziŵiri, mtundu wa galimoto umene achinyamata ambiri ankakonda panthaŵiyo. Ndinaisirira kwambiri, ngakhale ndinkadziŵa kuti siinali yoyenera kuti ndingatengere anthu kupita nawo muutumiki. Ndinapita kwa Atate mwamantha. Pamene ndinawauza zimene manijalayo ananena, iwo anati, ‘Tiyeni tikambirane.’ Ndinazindikira zimene zichitike! Iwo anakambirana nane ndipo anandisonyeza ubwino wogula galimoto yoyenera. Ndiye ndinagula sedan yokhala ndi zitseko zinayi, ndipo nditangoiyendetsa kwa mtunda wa makilomita 160,000 m’gawo langa la ulaliki, ndinati, ‘Apanso Atate anakhoza.’
“Ulendo umene tinayenda tili ang’onoang’ono—kuchokera ku Washington kupita ku Missouri ndiye kenaka ku Mississippi—unali wosangalatsa kwambiri. Unatisangalatsa kwabasi. Ngakhale kuti kwa chaka chonse tonsefe asanu ndi anayi tinkakhala mu ngolo ya mamita 2.5 mlifupi ndi mamita 11 mlitali, zinali zokondweretsa ndipo zinatiphunzitsa kumakhala olinganiza zinthu bwino ndi kumalorerana wina ndi mnzake, ngakhale pamene mukukhala mopanikizana. Nthaŵi zambiri tinkakonda kuseŵera panja.
“Chinthu china chimene ndimakumbukira ndi kusangalala nacho kwambiri ndicho mmene Atate amapangira nafe lemba latsiku. Mu 1966 anakakhala nawo m’sukulu ya akulu ku Kingdom Farm, ku South Lansing, New York, ndipo anaona kuti a Banja la Beteli ankafufuza kaye kuti apereke ndemanga za lemba tsiku ndi tsiku. Iwo anayambitsa zomwezo m’banja mwathu. Aliyense wa anyamata asanu ndi aŵirife ankagaŵiridwa tsiku lakuti apereke ndemanga zimene wapeza atafufuza. Ngakhale kuti nthaŵi zina tinkang’ung’udza, zimenezi zinatithandiza kudziŵa mmene tingafufuzire ndi kulankhula. Ukazoloŵera zotero umapitirizabe kwa moyo wako wonse.
“Ndinkachita chidwi ndi njira imene Atate ndi Amayi ankachitira zinthu. Pamene akulu anga aŵiri Richard ndi Dan anali oti akadatha kulowa ntchito ndi kumapeza ndalama zothandiza pabanjapo, makolo athu anawalimbikitsa kupita ku Brooklyn, New York, kuti akatumikire monga antchito odzifunira palikulu ladziko lonse la Watch Tower Society. Makolo athu anasunganso ndalama kuti tonse anayi tikwere ndege kupita ku New York kukadzionera tokha likulu. Zimenezo zinandikhudza mtima kwambiri. Zinapangitsa kuti ndiyamikire kwambiri gulu la Yehova.
“Tsopano ndiwalole Atate kuti anene.”
Tinali ndi Zovuta Zina
Monga banja lina lililonse, tinali ndi mavuto athu. Pamene anyamata athu anakula kufika poti n’kumafunsira atsikana, ndinafunikira kumawapatsa uphungu kuti asathamangire ukwati pamene angoona mtsikana. Tinkaonetsetsa kuti pamene ali ndi atsikana aziyang’aniridwa bwino. Tinkafuna kuti adziŵe mmene moyo ulili asanasankhe munthu woti akhale naye moyo wawo wonse. Nthaŵi zina pankachitika zomvetsa chisoni mwina ngakhale zokhumudwitsa kwambiri, koma mkupita kwa nthaŵi anazindikira kuti uphungu wa m’Baibulo ndi wanzeru—makamaka kuti ayenera kukwatira “mwa Ambuye.” Tinkawathokoza chifukwa chochita mwanzeru.—1 Akorinto 7:39.
Mwana wathu wachisanu ndi chiwiri, Scott, anatimvetsa chisoni kwambiri mpaka tinalira. Kuntchito kwake anayamba kugwirizana ndi mabwenzi oipa. Potsirizira anachotsedwa mumpingo. Zinatiwawa kwambiri ife tonse, komabe tinalemekeza zimene akulu anagamula. Scott anayenera kuphunzira mwa kumva zowawa kuti kutumikira Yehova ndiyo njira yabwino koposa m’moyo.
Tinapitirizabe kumlimbikitsa kuti abwerere mumpingo. N’chokondweretsa kuti patapita zaka zisanu anabwezeretsedwa mumpingo. Akalingalira za kumbuyo, iye amati, “Chinthu chimodzi chinandilimbikitsa pamene ndinali wochotsedwa n’chakuti ngakhale panali kuyanjana kochepa ndi abale anga, ndinkadziwabe kuti iwo amandikonda.” Scott anapitirizabe kupita patsogolo ndipo wakhala akutumikira monga mkulu kwa zaka zisanu n’zitatu zapitazo.
Zachisoni kuti adzukulu athu aŵiri anachotsedwa m’zaka zaposachedwapa. Koma timatonthozedwa tikalingalira kuti chilango cha Yehova chikhoza kupangitsa munthu kusintha ndi kukhala ndi khalidwe labwino.
Kusintha Kwakukulu M’moyo Wathu
Pofika mu 1978, anyamata onse anali atachoka panyumba. Mkupita kwa nthaŵi, ndadziŵa kukonza zotenthetsera m’nyumba ndi zoziziritsira. Mu 1980, ine ndi Margaret tinaitanidwa kukatumikira kwa miyezi isanu ndi inayi pa likulu la Watch Tower Society ku Brooklyn. Koma tidakali pompano ngakhale kuti tsopano patha zaka 18!
Tadalitsidwa kwambiri. Sizinali zapafupi kulera ana athu m’njira yachikale, mogwirizana ndi mapulinsipulo a Baibulo, koma zatipindulira. Padakali pano, asanu mwa ana athu akutumikira monga akulu m’mipingo, ndipo mmodzi ndi woyang’anira woyendayenda. Tili ndi zidzukulu 20 ndi zidzukulutuvi zinayi—ndipo ambiri mwa iwo ali m’choonadi ndi okhulupirika kwa Mulungu.
Taona kuti mawu a wamasalmo ndi oona akuti: “Taonani, ana ndiwo cholandira cha kwa Yehova; chipatso cha m’mimba ndicho mphotho yake. Ana a ubwana wake wa munthu akunga mivi m’dzanja lake la chiphona.”—Salmo 127:3, 4.
[Mawu a M’munsi]
a Lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc., mu 1946; masiku ano silisindikizidwanso.
b Lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
[Zithunzi pamasamba 20, 21]
Tili ndi ana athu ndi akazi awo (kumanja) ndi zidzukulu kumanja chakumapeto pachikondwerero chakuti patha zaka 50 chikwatirirane, mu 1996