Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g99 2/8 tsamba 4-6
  • Kodi Cholinga cha Mulungu N’chiyani?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Cholinga cha Mulungu N’chiyani?
  • Galamukani!—1999
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mulungu Ali ndi Cholinga
  • Cholinga Chake N’chabwinodi
  • Ufumu wa Mulungu wa Zaka Chikwi
  • Dalirani Yehova Kuti Adzakwaniritsa Chifuno Chake
    Nsanja ya Olonda—1994
  • Nthaŵi Yomwe Mulungu Walola Anthu Kuvutika Ili Pafupi Kutha
    Nsanja ya Olonda—2001
  • Ufumu wa Mulungu—Ulamuliro Watsopano wa Dziko Lapansi
    Nsanja ya Olonda—2000
  • Mavuto Onse a Anthu Adzatha Posachedwapa
    Mavuto Onse a Anthu Adzatha Posachedwapa
Onani Zambiri
Galamukani!—1999
g99 2/8 tsamba 4-6

Kodi Cholinga cha Mulungu N’chiyani?

ANTHU ambiri amene amakayikira kuti kuli Mulungu wamphamvuyonse, wachikondi, amafunsa kuti: Ngati Mulungu aliko, kodi akuloleranji anthu kumavutika kwambiri chonchi limodzinso ndi nkhanza nthaŵi yonseyi? Kodi amaloleranji zinthu zomvetsa chisoni kumachitika zimene tikuona lerozi? Nanga bwanji sakuchitapo kanthu kuti athetse nkhondo, uchifwamba, tsankho, umphaŵi, ndi mavuto ena amene akukula mwamsangamsanga kwambiri m’mayiko ambiri padziko lapansi?

Ena amati Mulungu analenga zinthu zonse, n’kuika anthu pa Dzikoli, ndiye kenaka n’kuwasiya kuti azichita zimene akufuna. Ngati zili choncho, ndiye kuti si Mulungu woyenera kuimbidwa mlandu wa mavuto ndi chisoni chimene anthu adziyambitsira okha chifukwa cha umbombo wawo kapena chifukwa cholephera kuyendetsa bwino zinthu.

Komabe, ena amatsutsa mfundo imeneyo. Mwachitsanzo, polofesa wa sayansi ya physics, Conyers Herring, yemwe amavomereza kuti amakhulupirira Mulungu, anati: “Ine ndimakana zoti kale Mulungu anangolenga chilichonse basi n’kuzisiya n’kumangoziyendera zokha, ndiye iyeyo n’kungokhalano n’kumapenyerera anthu n’kumavutika ndi zinthu zimene sazimvetsa. Chifukwa china chimene ndimatsutsira zimenezo n’chakuti zimene ndadziŵa ine pazasayansi sizindipatsa chifukwa chokhulupirira kuti zinthu zakuthambo zimangoyenda mwa zokha ‘ngati koloko.’ Tikufunikira kuwongolerabe kwambiri chidziŵitso chathu pankhani zasayansi, koma ndikuganiza kuti sitidzafikira pakuzindikira kwenikweni. Ndikuganiza kuti zingakhale bwino kukhulupirira kuti pali mphamvu ina ya munthu wamoyo yemwe angatithandize kufikira pakuzindikira.”

Mulungu Ali ndi Cholinga

Pachiyambi, cholinga cha Mulungu chinali chakuti pa Dzikoli pakhale anthu olungama, angwiro. Mneneri Yesaya analemba kuti: “Atero Yehova amene analenga kumwamba, iye ndiye Mulungu amene anaumba dziko lapansi, nalipanga; Iye analikhazikitsa, sanalilenga mwachabe; Iye analiumba akhalemo anthu; Ine ndine Yehova; ndipo palibenso wina.”—Yesaya 45:18.

Mulungu analinga kudzaza dzikoli mwa njira yoti anthu abalane, m’malo moti iye achite kuwalenga mmodzimmodzi. Pamene Adamu ndi Hava anapandukira Mulungu, sanam’lepheretse cholinga chake chapoyamba, komabe anam’pangitsa kusintha zinthu zina ndi zina, kuti akwanitse zolinga zake kwa anthu ndi dziko.

Kwa zaka zoyambirira 6,000, Mulungu walola anthu kumadzichitira okha zinthu mosatsogozedwa ndi iye. Zimenezo n’zimene makolo athu oyamba anadzisankhira. (Genesis 3:17-19; Deuteronomo 32:4, 5) Pamene Mulungu analola anthu kudziimira paokha ndiyeno n’kumadzilamulira okha m’malo molamulidwa ndi Mulungu, zinaoneka kuti munthu sangathe kuwongolera mapazi ake kapena kulamulira bwino munthu mnzake.

Yehova anali atadziŵiratu kuti zinthu zidzakhala choncho. Anauzira anthu kuti alembe zimenezo m’Baibulo. Mwachitsanzo, mneneri Yeremiya analemba kuti: “Ndidziwa kuti njira ya munthu sili mwa iye mwini; sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake.”—Yeremiya 10:23.

Munthu wina wanzeru, wotchedwa Solomo, anatchula mmene zimaipira ngati anthu akuyesa kulamulira anthu anzawo, monga momwe akhala akuchitira kwa zaka mazana ambiri. “Zonsezi ndaziona ndi kuyang’anitsa mtima wanga ntchito zonse zichitidwa pansi pano; nthaŵi yakuti wina apweteka mnzake pom’lamulira.”—Mlaliki 8:9.

Komabe, si kuti Mulungu Wamphamvuyonseyo ‘wangokhala n’kumapenyerera anthu akumavutika ndi zinthu zomwe sazimvetsa’ iyayi, Iye ali ndi chifukwa chabwino chimene walolera kuti zaka zikwi zingapo zipite, Iye osaloŵerera mwachindunji pazochita za anthu.

Cholinga Chake N’chabwinodi

Zaka 6,000 zapitazo chiyambire kukhalapo kwa munthu zingaoneke ngati nthaŵi yaitali poyerekezera ndi zaka zosakwana 100 zimene timakhala ndi moyo. Koma malinga ndi nthaŵi ya Mulungu ndi mmenenso amaionera, zaka zikwi zimenezi zili ngati masiku asanu ndi limodzi—mlungu umodzi sukukwana! Mtumwi Petro anafotokoza kuti: “Ichi chimodzi musaiŵale, okondedwa inu, kuti tsiku limodzi likhala kwa Ambuye ngati zaka chikwi, ndi zaka chikwi ngati tsiku limodzi.”—2 Petro 3:8.

Ndiyeno Petro anatsutsanso mfundo yakuti Mulungu n’ngonyalanyaza zinthu kapena wochedwetsa zinthu, pamene anawonjezera kuti: “Ambuye sazengereza nalo lonjezano, monga ena achiyesa chizengerezo; komatu aleza mtima kwa inu, wosafuna kuti ena awonongeke, koma kuti onse afike kukulapa.”—2 Petro 3:9.

Choncho, zaka zimene zinasankhidwazo zikangotha, Mlengi adzachotsa anthu amene amawononga pulaneti lathu lokongolali. Adzakhala atapereka nthaŵi yokwanira yoti munthu asonyeze kuti sangathe kulamulira kapena kuthetsa nkhondo, chiŵaŵa, umphaŵi, matenda, ndi mavuto ena. Zimenezi zidzapangitsa anthu kuona kuti Mulungu ananena zoona pamene anauza anthu pachiyambi—kuti ayenera kutsogozedwa ndi Mulungu kuti ziwayendere bwino.—Genesis 2:15-17.

Malinga ndi kukwanira kwa ulosi wa Baibulo, tikukhala ‘m’masiku otsiriza’ enieni a dongosolo lino la zinthu la anthu osaopa Mulungu. (2 Timoteo 3:1-5, 13; Mateyu 24:3-14) Nthaŵi imene Mulungu wakhala akulolera anthu kulamulira ndi kudziimira okha ndiponso nthaŵi imene walolera kuipa ndi kuvutika yatsala pang’ono kutha. (Danieli 2:44) Posachedwapa chisautso chachikulu chimene dzikoli silinaonepo chidzafika, chimake chake chidzakhala “nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu, Wamphamvuyonse,” Armagedo. (Chivumbulutso 16:14, 16) Nkhondo yotsogozedwa ndi Mulungu imeneyi siidzawononga ntchito ya Mulungu, dziko lapansili ayi, koma ‘idzawononga iwo akuliwononga dzikoli.’—Chivumbulutso 11:18.

Ufumu wa Mulungu wa Zaka Chikwi

Armagedo itatha, padziko lapansi padzapezeka anthu mamiliyoni ambiri omwe adzakhala atapulumuka. (Chivumbulutso 7:9-14) Ulosi wa pa Miyambo 2:21, 22 udzakhala utakwanira, wakuti: “oongoka mtima adzakhala m’dziko, angwiro nadzatsalamo. Koma oipa adzalikhidwa m’dziko, achiwembu adzazulidwamo.”

Cholinga cha Mulungu n’chakuti, itatha nkhondo yolungama ya Armagedo, padzakhale nyengo yapadera ya zaka chikwi. (Chivumbulutso 20:1-3) Nyengo imeneyo ndiyo idzatchedwa Kulamulira kwa Zaka Chikwi kwa Mwana wa Mulungu, Yesu Kristu, monga Mfumu ya Ufumu wakumwamba. (Mateyu 6:10) M’kati mwa nyengo yosangalatsa imeneyi pamene Ufumu udzakhala ukulamulira padziko lapansi, anthu mamiliyoni osaŵerengeka adzaukitsidwa kutulo tawo taimfa kuti adzakhale ndi anthu ena ambirimbiri amene adzakhala atapulumuka pa Armagedo. (Machitidwe 24:15) Onse pamodzi adzabwezeretsedwa akhalenso angwiro, ndiye kenaka—kumapeto kwa Zaka Chikwi za Kulamulira kwa Kristu—amuna ndi akazi angwiro adzadzaza dziko lapansi, onsewo monga mbadwa za Adamu ndi Hava. Pamenepo Mulungu adzakhala atapambana pakukwaniritsa cholinga chake mwaulemerero.

Inde, cholinga cha Mulungu n’chakuti ‘adzapukute misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; kapena maliro, kapena kulira. Zoyambazo zapita. Ndipo Iye wakukhala pa mpando wachifumu anati: Taonani, ndichita zonse zikhale zatsopano.’ (Chivumbulutso 21:4, 5) Cholinga chimenecho chidzakwanira posachedwapa, sichidzalephereka iyayi.—Yesaya 14:24, 27.

[Zithunzi patsamba 5]

M’dziko latsopano la Mulungu, anthu adzakhala kwamuyaya mwachimwemwe

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena