Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g99 3/8 tsamba 30-31
  • Kodi N’kulakwa Kutchula Dzina la Mulungu?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi N’kulakwa Kutchula Dzina la Mulungu?
  • Galamukani!—1999
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Mulungu Amaganizapo Motani?
  • Lamulo Lachitatu
  • Zili Ndi Ntchito Yanji?
  • Tanthauzo la Dzina la Mulungu Ndiponso Mmene Tingaligwiritsire Ntchito
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
  • Dzina la Mulungu
    Galamukani!—2017
  • Muzilemekeza Dzina Lalikulu la Yehova
    Nsanja ya Olonda—2013
  • Mmene Mungadziŵire Dzina la Mulungu
    Galamukani!—2004
Onani Zambiri
Galamukani!—1999
g99 3/8 tsamba 30-31

Lingaliro la Baibulo

Kodi N’kulakwa Kutchula Dzina la Mulungu?

KWA zaka mazana ambiri Chiyuda chaphunzitsa kuti dzina la Mulungu, Yehova, ndi loyera kwambiri kotero kuti silingatchulidwe.a (Salmo 83:18) Akatswiri ambiri a zaumulungu akhala ndi malingaliro akuti ndi mwano kuitana Mulungu motero ngati kuti ukuitana mnzako ndiponso kuti ndi kuphwanya lamulo lachitatu la Malamulo Khumi, limene limaletsa ‘kutengera dzina la Ambuye pachabe.’ (Eksodo 20:7, King James Version) M’zaka za zana lachitatu C.E., Mishnah inalamula kuti “aliyense wotchula Dzina la Mulungu mmene limalembedwera” alibe “mbali m’dziko likudzalo.”—Sanhedrin 10:1.

Chodabwitsa n’chakuti akatswiri a maphunziro ambiri m’Dziko Lachikristu akumatsatira mwambo wachiyuda umenewu pomasulira Baibulo. Mwachitsanzo, mawu oyamba a The New Oxford Annotated Bible amati: “Kugwiritsa ntchito dzina lililonse la Mulungu mmodzi yekhayo, ngati kuti pali milungu ina imene Mulungu woona ayenera kusiyanitsidwa nayo, kunayamba kusiyidwa m’Chiyuda nyengo ya Chikristu isanakwane ndipo n’kosafunikira pachikhulupiriro cha Tchalitchi chachikristu padziko lonse.” Choncho, m’Baibulo limenelo liwu lakuti “Mbuye” lili m’malo mwa dzina la Mulungu.

Kodi Mulungu Amaganizapo Motani?

Koma kodi maganizo a otembenuza ndi akatswiri azaumulungu ameneŵa akufanana ndi maganizo a Mulungu? Ndiponsotu paja Mulungu sanafune kuubisira dzina lake mtundu wa anthu; m’malo mwake, analiulula kwa iwo. M’chigawo cha Chihebri cha Baibulo, chimene ambiri amachitcha Chipangano Chakale, dzina la Mulungu, Yehova, limapezekamo nthaŵi 6,800. Mbiri ya Baibulo imasonyeza kuti anthu aŵiri oyambirira Adamu, ndi Hava, anali ena mwa anthu amene amadziŵa ndiponso kugwiritsa ntchito dzina la Mulungu. Pamene anabala mwana wake woyamba, Hava anati: “Ndalandira munthu kwa Yehova.”—Genesis 4:1.

Patatha zaka mazana ambiri, pamene Mulungu anauza Mose kuti awatsogolere Aisrayeli powatulutsa muukapolo ku Aigupto, Mose anafunsa Mulungu kuti: “Onani, pakufika ine kwa ana a Israyeli, ndi kunena nawo, Mulungu wa makolo anu wandituma kwa inu; ndipo akakanena ndi ine, Dzina lake ndani? Ndikanena nawo chiyani?” Mwina Mose ankaganiza kuti Mulungu akazidziŵikitsa ndi dzina latsopano. Mulungu ananena ndi Mose: “Ukatero ndi ana a Israyeli, Yehova, Mulungu wa makolo anu, Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isake, ndi Mulungu wa Yakobo anandituma kwa inu; ili ndi dzina langa nthaŵi yosatha, ichi ndi chikumbukiro changa m’mibadwomibadwo.” (Eksodo 3:13, 15) Mwachionekere, Mulungu woona sanaganize kuti dzina lake linali loyera kwambiri koti anthu ake sangalitchule.

Ndiponsotu, atumiki okhulupirika a Mulungu a m’mibadwo yonse akhala akutchula dzina la Mulungu momasuka komanso mwaulemu. Boazi, mtumiki wokhulupirika wa Mulungu, kaŵirikaŵiri ankalonjera antchito ake kumunda ndi mawu akuti, “Yehova akhale nanu.” Kodi antchitowo ankadabwa nawo malonje oterowo? Ayi. Nkhaniyo ikuti: “Nam’yankha iwo, Yehova akudalitseni.” (Rute 2:4) M’malo moona malonje ameneŵa monga kunyoza Mulungu, anawaona monga njira yomupatsira ulemu m’zochita zawo zatsiku ndi tsiku. Ndi cholinga chofananacho Yesu anaphunzitsa ophunzira ake kupemphera motere: “Atate wathu wa Kumwamba, Dzina lanu liyeretsedwe.”—Mateyu 6:9.

Lamulo Lachitatu

Kodi nanga bwanji lamulo lachitatu la Malamulo Khumi? Eksodo 20:7 motsimikiza amati: “Usatchule dzina la Yehova Mulungu wako pachabe; chifukwa Yehova sadzamuyesa iye wosachimwa, amene atchula pachabe dzina lakelo.”

Kodi kwenikweni kutchula dzina la Mulungu “pachabe” kumatanthauza chiyani? The JPS Torah Commentary, yofalitsidwa ndi Bungwe la Jewish Publication Society, ikulongosola kuti liwu lachihebri limene pamwambapo latembenuzidwa “pachabe” ((lash·shaw’ʹ) lingatanthauze “monama” kapena “mopanda tanthauzo.” Buku la maumboni lomweli likupitiriza kuti: “Kukhala kwake ndi matanthauzo angapo kumachititsa [liwu lachihebri limeneli] kukhalanso [loletsa] anthu oimbana mlandu, kuphwanya lumbiro, kulumbira bodza, ndi kugwiritsa ntchito dzina la Mulungu mosayenera ndi molipeputsa.”

Buku landemanga limeneli lachiyuda lanena molondola kuti ‘kutchula dzina la Mulungu pachabe’ kumaphatikizapo kugwiritsa ntchito dzinalo m’njira yolakwika. Koma kodi kutchula dzina la Mulungu pophunzitsa ena za iye kapena pomufikira m’pemphero monga Atate wathu wakumwamba kungatchedwe molondola kukhala “kosayenera kapena kolipeputsa”? Yehova akunena maganizo ake kudzera m’mawu a pa Salmo 91:14 akuti: “Popeza andikondadi ndidzam’pulumutsa; ndidzam’kweza m’mwamba, popeza adziŵa dzina langa.”

Zili Ndi Ntchito Yanji?

Baibulo lotembenuzidwa m’Chingerezi chamakono lotchedwa The Five Books of Moses, lotembenuzidwa ndi Everett Fox, silitsata mwambo. Ilo silimagwiritsa ntchito “MBUYE”, koma “YHWH” kuimira dzina la Mulungu “n’chikhumbo chofuna kusonyeza chidziŵitso cha woŵerenga wachihebri.” Fox akutsimikizira motere: “Woŵerenga angaone mwamsanga kuti dzina lenileni la Mulungu wa Baibulo likupezeka m’buku limeneli monga ‘YHWH.’” Iye akuvomereza kuti maonekedwe a dzina la Mulungu angakhale “osakondweretsa” kwa woŵerengayo. Koma atachita ntchito yoyamikirikayi posabisa dzina la Mulungu potembenuza, akuwonjezera kuti: “Ndikulimbikitsa kuti mwa mwambo ‘MBUYE’ agwiritsidwe ntchito poŵerenga momveka, koma ena angakonde kutsata chizoloŵezi chawo.” Komabe, kodi chofunika ndi kungosankha zomwe munthu ukufuna, mwambo, kapena kutsata chizoloŵezi chako?

Ayi. Baibulo silimangolimbikitsa kugwiritsa ntchito dzina la Mulungu moyenera komanso limalamulira kutero! Pa Yesaya 12:4a, anthu a Mulungu akusonyezedwa akuimba mosakayika kuti: ‘Muyamikire Yehova, bukitsani dzina lake.’ Kuwonjeza pamenepa, wa masalmo akunena za amene ali oyenera chilango cha Mulungu motere: ‘Thirirani mkwiyo wanu pa akunja osadziŵa Inu, ndi pa maufumu osaitana pa dzina lanu.’—Salmo 79:6; onaninso Miyambo 18:10; Zefaniya 3:9.

Choncho ngakhale kuti ena apewa kutchula dzina laulemerero la Yehova chifukwa chosamvetsa lamulo lachitatu, amene amakondadi Mulungu amafuna kuitanira pa dzina lake. Inde, paliponse akapeza mwayi wotero, ‘amalalikira machitidwe ake mwa mitundu ya anthu, kunena kuti dzina lake lakwezedwa’!—Yesaya 12:4b.

[Mawu a M’munsi]

a M’chigawo cha Chihebri cha Baibulo (Chipangano Chakale), dzina la Mulungu likuimiridwa ndi zilembo zinayi zimene zingatembenuzidwe monga YHWH. Ngakhale kuti matchulidwe enieni a dzina la Mulungu n’ngosadziŵika, nthaŵi zambiri m’Chichewa limatchulidwa kuti “Yehova.”

[Zithunzi patsamba 30]

Mbali ya buku la Masalmo yochokera mu Mipukutu ya ku Nyanja Yakufa. Dzina la Mulungu, Yehova (YHWH), lalembedwa malembo achikale kwambiripo achihebri kusiyana ndi mbali zina zonse za mpukutuwo

[Mawu a Chithunzi]

Courtesy of the Shrine of the Book, Israel Museum, Jerusalem

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena