Wamkulu Kwambiri Ndiponso Wamng’ono Kwambiri
“Musaphe Agulugufewo.”—WILLIAM BLAKE (1757—1827)
KODI munayamba mwaonererapo gulugufe akukupiza mapiko ake poteropo? Ndaninso wina koma munthu yekha wosachita chidwi ndi zinthu amene sangaime kuti aone kukongola komanso kusalimba kwa kachilombo kokoma m’maso kameneka? Ndipo amapezeka padziko lonse lapansi ndipo n’ngaakulu mosiyanasiyana komanso n’ngamitundu yosiyanasiyana kotero kuti akuti alipo pafupifupi mitundu 15,000 kufika 20,000!
Kodi gulugufe wamkulu kwambiri amene munamuonapo mumamutcha chiyani? Ngati mumakhala ku Papua New Guinea, ndiye kuti mwina munaona amene ali mtundu waukulu kwambiri padziko lapansi—wotchedwa Queen Alexandra’s birdwing, wokhala ndi mapiko aatali kufika mamilimita 280. Ngati kwanu kuli ku North kapena ku Central America, ndiye kuti mwina munakhalapo ndi mwayi woona wina wotchedwa Homerus Swallowtail wokhala ndi mapiko aatali kufika mamilimita150. Gulugufe wamkulu kwambiri mu Afirika ndi wotchedwa African giant swallowtail, amene ali ndi mapiko aatali kupitirira pang’ono mamilimita 230.
Nanga agulugufe aang’ono kwambiri ndi ati? Kodi amapezeka kuti? Buku lolongosola agulugufe lotchedwa The Illustrated Encyclopedia of Butterflies, lolembedwa ndi Dr. John Feltwell, likunena kuti “guluguge wotchedwa North American Pygmy blue . . . mwina ndiye gulugufe wamng’ono kwambiri padziko lonse, ndipo ali ndi mapiko okwana mamilimita oyambira pa 15 kulekeza pa 19.” Gulugufe wamng’ono kwambiri ku Britain ndi wotchedwa small blue, ndipo ali ndi mapiko okwana mamilimita 24.
M’mbali zambiri za dzikoli kuli nyumba za agulugufe zimene mukapita mumayendamo ndiye touluka tokongola timeneti timakuterani. Mungathe kuphunzira zambiri za zolengedwa zosangalatsa zimenezi ndi mbali za moyo wawo wonse, mmene amasinthira kuchokera ku kadzira kang’onong’ono n’kusanduka mphutsi n’kusanduka chombeza n’kusanduka gulugufe wamkulu bwino. Choncho mukadzaonanso gulugufe akukupiza mapiko ake poteropo, dzaimeni, dzachiteni naye chidwi, ndi kudabwitsidwa. Mudzakhala mukuyang’ana chozizwitsa—kaya adzakhala wamkulu kwambiri uja kapena wamng’ono uja!
[Chithunzi pamasamba 24, 25]
Gulugufe wamkulu kwambiri ndi wamng’ono kwambiri, otchedwa Queen Alexandra’s birdwing ndiponso pigmy blue (onseŵa ndi aakuludi chonchi)
[Mawu a Chithunzi]
Agulugufe: Allyn Museum of Entomology, Florida Museum of Natural History