Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g99 12/8 tsamba 25-28
  • Kupenda Nkhanizo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kupenda Nkhanizo
  • Galamukani!—1999
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Angelo Sali Mmene Ambiri Amawaganizira
  • Angelo Amaganizira za Thanzi Lathu Lauzimu
  • Angelo Okhulupirika Satsutsana ndi Mawu a Mulungu
  • “Kuitana Angelo Onse!”
  • M’dzina la Angelo
  • Mmene Angelo Angakuthandizireni
    Nsanja ya Olonda—1998
  • Angelo—Kodi Amayambukira Moyo Wanu?
    Nsanja ya Olonda—1987
  • Kodi Angelo Ndi Otani?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Angelo Ndiwo “Mizimu Yotumikira Anthu”
    Nsanja ya Olonda—2009
Onani Zambiri
Galamukani!—1999
g99 12/8 tsamba 25-28

Kupenda Nkhanizo

NKHANI zamakono za kukumana ndi angelo zimakhudza anthu m’njira zosiyanasiyana. Choyamba n’chakuti pali anthu amene amazikhulupirira. Iwo amati chifukwa chakuti nkhani zoterezi n’zambiri ndiponso n’zofala, ndiye kuti n’zoona. Chachiŵiri n’chakuti pali ena amene amakayikira. Iwo amati palibe umboni weniweni wotsimikiza kuti nkhanizo n’zoona. Iwo amati ngati anthu ambiri akukhulupirira chinthu, sizitanthauza kuti n’choona. Ndiponsotu, nthaŵi ina m’buyomu anthu ankakhulupirira kuti pali nsomba za mutu ndi maŵere ngati a munthu wamkazi. Chachitatu n’chakuti pali ena amene alibe mbali. Polongosola maganizo a anthu opanda mbali ameneŵa, buku lotchedwa Angels—Opposing Viewpoints (Maganizo Otsutsana Ponena za Angelo) linalongosola kuti: “Anthu ambiri amati anaonapo angelo. Kaya anawaonadi n’zovuta kutsimikiza; omvera amangoti n’zoona chifukwa cha chikhulupiriro basi. Ndipo ngakhale okayikira sangathe kutsutsa, ndipo ndi oŵerengeka chabe amene amayesa kutero.”

Anthu ambiri amavomereza kuti Baibulo ndilo gwero lodalirika la chidziŵitso chonena za anthu auzimu.a Lingathe kutithandiza kupenda nkhani zamasiku ano za angelo. Mwina mukudziŵa kale, kuti Baibulo limatitsimikizira kuti angelo ndi enieni, amphamvu, ndiponso ndi zolengedwa zauzimu za ulemerero. Baibulo lili ndi nkhani za angelo amene anali kupereka mauthenga ndi kupulumutsa atumiki a Mulungu ku zinthu zovulaza.—Salmo 104:1, 4; Luka 1:26-33; Machitidwe 12:6-11.

Baibulo limasonyezanso kuti pali angelo ena oipa. Zolengedwa zauzimu zimenezi zimanyenga ndi kusocheretsa anthu, ndipo potero zimawachotsa kwa Mulungu. (2 Akorinto 11:14) Pachifukwa chabwino, Baibulo limachenjeza kuti: “Musamakhulupirire mawu ouziridwa alionse, koma yesani mawu ouziridwawo ngati achokera mwa Mulungu.” (1 Yohane 4:1, NW) Mwachitsanzo, tisanakhulupirire mawu oneneratu za m’tsogolo a anthu odzitcha okha aneneri, tingapende mwanzeru zimene akunena ndi kuziyerekezera ndi Mawu a Mulungu, amene iwo angamanene kuti akuimira. Ndithudi, tiyenera kuyembekezera kuti tikapenda nkhani zamasiku ano za kuonekera kwa angelo ziyenera kufanana ndi zakale. Koma kodi nkhani zamakono za kukumana ndi angelo zimafanana bwanji ndi zimene zinalembedwa m’Malemba?

Angelo Sali Mmene Ambiri Amawaganizira

Tiyeni tiyambe ndi kuthetsa mabodza aŵiri amasiku ano okhudza angelo. Mosiyana ndi zimene ambiri amakhulupirira, angelo sanayambe moyo wawo monga anthu. Iwo anakhalapo kumwamba kwa nthaŵi yaitali Mulungu asanalenge moyo padziko lapansi. Baibulo limati panthaŵi imene Mulungu ‘amaika maziko a dziko lapansi . . . , ana [aungelo] a Mulungu anafuula ndi chimwemwe’—Yobu 38:4-7.

Bodza lina lamakono n’lakuti angelo n’ngolekerera ndipo amalola kuchita zoipa. Koma zoona n’zakuti, angelo okhulupirika amasunga miyezo yolungama ya Mulungu ndipo amachita zinthu mogwirizana ndi lamulo lake. Amatumikira Mulungu, osati anthu.—Salmo 103:20.

Angelo Amaganizira za Thanzi Lathu Lauzimu

Mwa nkhani zina zamakono za angelo, pali zambiri zosimba za kupulumutsa anthu. M’buku lina loyenda malonda kwambiri, muli nkhani ya kamtsikana kamene kanatulutsidwa bwinobwino ndi dzanja losaoneka kuchokera m’nyumba imene imayaka. Buku lina linasimba nkhani ya ana asukulu aŵiri a kukoleji amene chimvula chamkuntho chinawatsekereza. Mwadzidzidzi, galimoto inabwera ndipo inawanyamula ndi kukawatula ali bwinobwino, koma osasiya mkukuluzi uliwonse ayi! Palinso nkhani ina yonena za Ann, amene ankadwala matenda a kansa. Patatsala masiku atatu kuti akaloŵe m’chipatala kukamuchita opaleshoni, munthu wosadziŵika wamtali anaima pakhomo pake. Ndiye anapereka malonje ponena kuti dzina lake ndi Thomas ndipo watumidwa ndi Mulungu. Thomas anakweza dzanja lake m’mwamba, ndipo Ann anamva kutentha, kuŵala kukuloŵa m’thupi mwake. Atapita ku opaleshoni, madokotala anadabwa kwambiri. Matenda ake a kansa anali atatha!

Nkhani zimenezi zimabweretsa funso loyeneradi lakuti, ngati munthu aliyense ali ndi mngelo wom’teteza, n’chifukwa chiyani anthu ena amapulumutsidwa, pamene ambiri satero? Anthu miyandamiyanda afa chifukwa cha matenda, nkhondo, njala, ndi ngozi zachilengedwe. Mosakayika, ambiri a iwo anapemphera kuti athandizidwe. N’chifukwa chiyani mngelo wowateteza sanawapulumutse?

Baibulo limapereka thandizo pafunso limeneli. Ilo limalongosola kuti Mulungu alibe tsankhu. (Machitidwe 10:34) Kuwonjezera apo, ngakhale kuti angelo okhulupirika a Mulungu amaganizira za thanzi lathu lakuthupi, iwo amaganizira kwambiri za thanzi lathu lauzimu. Mtumwi Paulo anakhudzapo mfundo imeneyi pofunsa funso lakuti: “Kodi [angelowo] siiliyonse mizimu yotumikira, yotumidwa kuti itumikire iwo amene adzaloŵa chipulumutso?” (Ahebri 1:14) Chithandizo chakuthupi chimapindulitsa kwa kanthaŵi chabe, koma chithandizo chauzimu chimapindulitsa kosatha.

Nkhani zambiri zosimba za angelo zimakhala zokhudza zinthu zosafunika kwenikweni. Angelo akuti anathandiza mayi wotopa ndi ntchito kusintha zofunda pabedi n’kuyalapo zina, kukumbutsa munthu wokagula zinthu kuti agule machesi, ndi kuthandiza oyendetsa galimoto kuti apeze malo oimitsapo galimoto zawo. Mtsikana wina ku Scotland ananena mawu awa uku akuseka: “Ndaimitsa galimoto yanga pamalo oletsedwa mu msewu wa St. Mary kwa masabata atatu tsopano ndipo ndapempha mngelo wanga kuti aiteteze ndi chikondi ndi kukoma mtima. Wapolisi aliyense akafikapo adzazidwa ndi chikondi chachikulu ndipo angoisiya salimbana n’kundipatsa mlandu. Sanandipatsepo chisamani.” N’zosadabwitsa kuti anthu ena amayerekezera angelo oteteza amasiku ano ndi mnzawo wachikondi kwambiri kapena Bambo wopereka mphatso kwa ana pa Khirisimasi yemwe akupereka kwa akulu.

Angelo Okhulupirika Satsutsana ndi Mawu a Mulungu

Mabuku a angelo ndi odzaza ndi miyambi ndi malangizo amene amati n’ngochokera kwa mizimu. Mwachitsanzo, buku lina limati lili ndi ziphunzitso zotumizidwa kuchokera kwa mngelo wamkulu Mikayeli kupita kwa mkazi wina ku Colorado, U.S.A. Zina mwa “zonena” zochokera kwa mikayeli ndi izi: “Misewu yonse imakafika kwa Mulungu. Zikhulupiriro zonse, ndiponso choonadi chonse cha kuwala chimakafika kwa Mulungu.” Motsutsana ndi zimenezi Yesu ananena kuti pali misewu iŵiri yokha yachipembedzo ndipo kuti ndi umodzi wokha mwa imeneyi umene ungamufikitse munthu poyanjidwa ndi Mulungu ndiponso kumoyo wosatha. Inayo imakafika kokakanidwa ndiponso kuchiwonongeko chosatha. (Mateyu 7:13, 14) Mwachionekere, zonena za anthu aŵiri ameneŵa sizingakhale zonse zoona.

Kodi “angelo” a “mkhalidwe wa uzimu watsopano” ameneŵa amati chiyani pankhani ya ukwati ndi khalidwe labwino? M’buku lina woŵerenga amapezamo nkhani ya Roseann, amene anauzidwa ndi “mngelo” wake kuti: “Uli ndi ambiri akuti uwapeze, ndipo moyo wako si ulinso pamene pali mwamuna wako. Umamukonda ndipo nayenso amakukonda, koma nthaŵi yakwana yosudzulana.” Anathetsa banja lake. Komatu, Baibulo limati Mulungu amadana ndi kusudzula popanda chifukwa chenicheni. (Malaki 2:16) Nkhani ina inasimba za mwamuna ndi mkazi amene amachita chigololo, poganiza kuti angelo amawayang’ana mosangalala ndipo amaika kampweya konunkhiritsa mowazungulira. Koma Baibulo limati: “Usachite chigololo.”—Eksodo 20:14.

Kodi mwina mauthenga amasiku ano ameneŵa akuwonjezera chidziŵitso chatsopano m’Baibulo? Ayi, Mawu a Mulungu sasintha. Mtumwi Paulo analembera kalata anthu ena a m’zaka za zana loyamba kuwauza kuti: ‘Ndizizwa kuti msanga motere mulikutunsika kwa iye amene anakuitanani m’chisomo cha Kristu, kutsata uthenga wabwino wina; umene suli wina; koma pali ena akuvuta inu, nafuna kuipsa Uthenga Wabwino wa Kristu. Koma ngakhale ife, kapena mngelo wochokera Kumwamba, ngati akakulalikireni uthenga wabwino wosati umene tidakulalikirani ife, akhale wotembereredwa.’—Agalatiya 1:6-8.

“Kuitana Angelo Onse!”

Kodi tiyenera kuitana angelo kuti atithandize kuthana ndi mavuto ndi zoopsa m’moyo? Umenewu ndiwo mutu wa nkhani wa mabuku ambiri. Nazi zitsanzo ziŵiri. Buku lakuti Ask Your Angels (Funsani Angelo Anu) akuti limasonyeza oliŵerenga ‘mmene angatengere mphamvu za angelo kuti apezenso maganizo awo enieni achibadwa amene atayika ndi kuti akwaniritse zolinga zawo. Buku lina langati limeneli n’lakuti Calling All Angels!: 57 Ways to Invite an Angel Into Your Life (Kuitana Angelo Onse!: Njira 57 Zoitanira Mngelo M’moyo Wanu).

Komabe, Baibulo silinena ngakhale pang’ono kuti tiziitana angelo. Yesu ananena mfundo imeneyi momveka bwino m’pemphero lachitsanzo. Iye anati: ‘Chifukwa chake pempherani inu chomwechi: Atate wathu wa Kumwamba . . . ’ (Mateyu 6:9) Chimodzimodzinso, mtumwi Paulo analemba kuti: “m’zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziŵike kwa Mulungu.”—Afilipi 4:6.

M’dzina la Angelo

“Mkhalidwe wauzimu watsopano” umagogomezera kwambiri kuphunzira mayina a angelo. Mabuku otchuka amapereka mayina zikwizikwi amene amati ndi a angelo. N’chifukwa chiyani amatero? Si chifukwa chakuti angowadziŵa chabe; koma kuti awaitanitse. Zimenezi n’zogwirizana kwambiri ndi matsenga. Encyclopedia of Angels (Insaikulopediya ya za Angelo) inanena kuti, “kugwiritsa ntchito ‘mayina obweretsa mphamvu,’ kapena mayina odziŵika a mizimu, [pamodzi ndi zida za mwambo, zamatsenga, ndi mapemphero] kumatulutsa mphamvu imene imatsegula chitseko chapakati pa anthu ndi mizimu, ndipo n’kutheketsa munthu wamatsenga kuti . . . alankhulitsane ndi mizimu.” Komatu, Baibulo limanena mosabisa kuti: “Musamachite matsenga.”—Levitiko 19:26, NW.

Baibulo lenilenilo limaulula mayina a angelo aŵiri okha okhulupirika, Mikayeli ndi Gabriyeli. (Danieli 12:1; Luka 1:26) Baibulo linapereka mayina ameneŵa kusonyeza kuti angelo ndi anthu osiyanasiyana a uzimu. N’chifukwa chiyani silinapereke mayina ambiri? Mwachionekere n’chifukwa choletsa anthu kukweza angelo kufika pomawapatsa ulemu wonyanyira, wakuti ngakhale angelowo saukhumba n’komwe. Choncho, pamene Yakobo anafunsa mngelo kuti aulule dzina lake, mngeloyo anakana. (Genesis 32:29) Kenaka, mngelo amene anaonekera kwa Yoswa anazidziŵikitsa osati mwa dzina koma ponena kuti anali “kazembe wa ankhondo a Yehova.” (Yoswa 5:14) Chimodzimodzinso pamene atate a Samsoni anafunsa mngelo dzina lake, anawauza kuti: “Mufunsiranji dzina langa, popeza liri lodabwitsa?” (Oweruza 13:17, 18) Angelo okhulupirika a Mulungu amafuna kuti ife tizilemekeza Mulungu ndi kuitana pa iye osati iwo.

[Mawu a M’munsi]

a Kuti mudziŵe chifukwa chimene Baibulo lili gwero lodalirika, onani bulosha lakuti Buku la Anthu Onse, lofalitsidwa ndi Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania.

[Mawu Otsindika patsamba 26]

“Kwa anthu amene amaona kuti akupanikizidwa kwambiri ndi Mulungu komanso malamulo ake, . . . angelo [A Mbadwo Watsopano] ndiwo amaloŵa mmalo mwake . . . ndi okoma mtima ndiponso saweruza. Ndipo amapezeka kwa aliyense, ngati mankhwala a mutu a asipirini.”—Magazini ya Time

[Bokosi patsamba 25]

“Kukumana” ndi Angelo Komanso Alendo Akuthambo Masiku Ano

Anthu ambiri masiku ano amati anaonapo angelo ndipo analankhulapo nawo. Ena amati apezanapo ndi anthu ochokera ku mapulaneti ena. Buku lotchedwa Angels—An Endangered Species linandandalika mbali zofanana za nkhani ziŵiri zimenezi, ndipo linati mbali zonsezo zingalongosoledwe mofanana.* Zotsatirazi ndi chidule cha mbali zofanana zimene zinandandalikidwa m’bukulo.

1. Angelo komanso anthu akuthambo amachokera ku mapulaneti ena.

2. Onse ali zamoyo zotsogola, kaya mwauzimu kapena pa zasayansi.

3. Mtundu wansangala wa anthu otereŵa umakhala ndi anthu amaonekedwe achinyamata ndiponso okongola, ndipo anthu ake amakhala a mtima wabwino ndipo achikondi chochuluka.

4. Onse savutika ndi chinenero, amalankhula bwinobwino m’chinenero cha amene akulankhula naye.

5. Onse ndi akatswiri a kuuluka.

6. Angelo komanso anthu akuthambo akaonekera amatsagana ndi kuwala kopha maso.

7. Onse amaoneka atavala mokwanira, nthaŵi zambiri amavala mikanjo, kapena zovala zothina. Mtundu woyera ndi wa buluwu ndiwo amakonda.

8. Nthaŵi zambiri onse amakhala amisinkhu yangati ya anthu.

9. Onse amasonyeza kukhudzidwa ndi mavuto a mtundu wa anthu ndi pulanetili.

10. Umboni wonse wa kukumana ndi anthu akuthambo kapena angelo umachokera kwa munthu amene anawaona.

[Mawu a M’munsi]

Malongosoledwe amodzi a zonsezi ndi onena kuti mizimu yoipa, kapena kuti ziwanda, ndi zimene mwachionekere zimapanga “kukumana” kotereku. Monga mmene Baibulo limanenera, “Satana yemwe adzionetsa ngati mngelo wa kuunika.” (2 Akorinto 11:14)—Onani Galamukani!, wa July 8, 1996 tsamba 26.

[Chithunzi patsamba 27]

Baibulo lili ndi nkhani zoona za angelo amene anali kuonekera kwa anthu

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena